Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 10/8 tsamba 26-27
  • Chithandizo Mapazi Akamaŵaŵa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chithandizo Mapazi Akamaŵaŵa
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukwana, Fashoni, ndi Mapazi
  • Malangizo Othandiza Pogula Nsapato
  • Kodi Nsapato Zanu Zimakukwanani Bwinobwino?
    Galamukani!—2003
  • Chisamaliro Kaamba ka Mapazi a Ana
    Galamukani!—1988
  • Kodi Miyendo Yake Inali Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1987
Galamukani!—1997
g97 10/8 tsamba 26-27

Chithandizo Mapazi Akamaŵaŵa

“MAPAZI anga akuŵaŵa, ndikufa ine!” Mwachionekere, uku ndiko kukuza zinthu ndi mkamwa. Komabe, matenda a kuŵaŵa kwa mapazi ndi ochuluka kwambiri ku United States mwakuti madokotala a mapazi sasoŵa ntchito.

Atapenda za maopaleshoni 2,000 amapazi amene anachita pazaka 14, Dr. Michael Coughlin, dokotala woongola mafupa a anthu opunduka, anapeza zodabwitsa. “Chodabwitsa,” iye anatero, “nchakuti ndinapeza kuti pafupifupi maopaleshoni onsewa anachitidwa pa azimayi.” Nchifukwa ninji azimayi ndiwo kwenikweni amapezeka ndi matenda a mapazi?

Kukwana, Fashoni, ndi Mapazi

Kufufuza pa azimayi 356 kunasonyeza kuti pafupifupi 9 mwa 10, pa avareji, ankavala nsapato zothina kumapazi awo! Mbali ina ya vutolo nchifukwa cha mmene amazipangira nsapato za azimayi. ‘Okonza nsapato sagwiritsiranso njira yoyesa ndi last zimene zikanamapangitsa kuti pazikhala chidendene chaching’ono bwino ndi phazi lalikulu m’mbali,’ akulongosola motero dokotala woongola mafupa a anthu opunduka Francesca Thompson.a

Motero, akamayesa nsapato, azimayi ambiri amapeza kuti pamene ikukwana bwino kutsogolo, chidendene nchosera; koma chidendene chikakwana bwino, kutsogolo nkothina. Ena amasankha yokwana chidendene koma yothina kutsogolo, chifukwa akatenga inayo ndiye kuti phazi lililonse lomwe aponye akamayenda nsapatoyo izingovuka.

Kukakamiza phazi m’nsapato yothina kutsogolo nkoipa kwambiri. Komanso okonza nsapato amatalikitsako chidendene ndi masentimita pang’ono. Ngakhale kuti zimatengedwa kukhala fashoni, nsapato yaitali chidendene imapanikiza mfundo ya chala chachikulu, ndipo imakankhira phazi kutsogolo kwa nsapato kumene kumakhala kothina kale. “Palibe nsapato yaitali chidendene yomwe ili yoyenera pathanzi la munthu,” akutero Dr. David Garrett, dokotala wa mapazi. Ena amati m’kupita kwa nthaŵi nsapato zazitali zidendene zimawononga mapazi, akakolo, akatumba, maondo ndi msana wa wozivalayo. Ndiponso zikhozanso kufupikitsa minofu ndi minyewa ya kumwendo, zimene zikhoza kuchititsa othamanga kukhala pangozi yovulala modetsa nkhaŵa.

Phazi la mzimayi silitha kuzoloŵerana bwino ndi nkhanza yomwe amalichitayo. Kunena zoona, pakapita zaka zambiri phazi limapwatalala—ngakhale munthuyo atakula. Koma sizitero ndi chidendene. “Chidendene chili ndi fupa limodzi lokha,” akutero Dr. Thompson, “ndipo limakhala laling’onobe ali ndi zaka 84 monga momwe linalili ali ndi zaka 14.” Izi zimapangitsa zinthu kuvutirapo kwa mayi kuti apeze nsapato imene ingamukwane kuyambira kuchidendene mpaka kuzala.

Malangizo Othandiza Pogula Nsapato

Malinga ndi kakwanidwe ndi fashoni za nsapato zawo zomwe zimawaika pangozi, kodi azimayi angatetezere bwanji mapazi kuti asamaŵaŵe? Yankho limayambira m’sitolo ya nsapato. Akatswiri ena amalimbikitsa zotsatirazi:

● Gulani nsapato chakumadzulo, pamene mapazi anu amakulirapo pang’ono.

● Yesani nsapato zonse—osati imodzi chabe.

● Onetsetsani kuti chidendene chikukwana bwino ndi kuti kutsogolo kwake kuli bwino muutali, mlifupi, ndi kukwera kwake.

● Kumbukirani kuti sitolo ingakhale ndi kapeti yawofuwofu kwambiri, kuchititsa ngakhale nsapato yothina kumveka bwino kwakanthaŵi.

● Pewani nsapato za chikopa chouma, chosalala ndi chong’anima kwambiri kapena zopangidwa ndi zinthu zosakhala zachikopa. Mosiyana ndi chikopa chofewa kapena chosasalaza, zinthu zimenezi sizinyutuka mukamayenda.

● Ngati mukugula nsapato yokhala ndi chidendene chachitali, yeserani kuikamo kachikopa kuti muwonjezere chiwofuwofu. Lingaliramponi zovala nsapato zazitali chidendene kanthaŵi, mukumasintha nthaŵi zina kuvala zazifupi chidendene.

Kowonjezera pa zili pamwambapazi, nthaŵi zonse kumbukirani kuti nsapato ziyenera kukukwanani bwino panthaŵi yogula. Mosiyana ndi ganizo lofala, siifeŵa pakapita nthaŵi. “Chonde, chonde osalola wogulitsa kukuchititsani kukhulupirira kuti nsapato yomwe ikukupwetekani phazi idzafewa bwino mutayamba kuivala,” akuchenjeza choncho Dr. Coughlin. “Chinthu chokha chimene chidzawonongeke ndi phazi lanu.”

Koma bwanji ngati palibe zina koma zothina kutsogolo zokwana bwino chidendene zokha kapena zokwana bwino kutsogolo koma zosera chidendene? Dr. Annu Goel, dokotala wa mapazi, akuti muyenera kusankha imene siivuta kukonza. “Pali njira ziŵiri zochitira zimenezi,” iye akutero. “Choyamba, mukhoza kugula nsapato zomwe zili zazikulu bwino kutsogolo ndi kuikamo zina kuti chidendene chizigwira bwino. . . . Njira yachiŵiri ndiyo kugula nsapato yachidendene chokwana bwino ndi kukakuza kutsogolo kwake kwa nsapatoyo. Komabe izi zimagwira ntchito pa nsapato zachikopa zokha.”

Popeza amayi ambiri amayenda mtunda wa makilomita ngati 15 patsiku, angachite bwino kuzipenda nsapato zawo. Monga momwe magazini ya American Health inanenera, “mwa kusunga mapazi bwino—makamaka povala nsapato zokwana bwino—mukhoza kuteteza matenda ambiri a mapazi kuti asachitike nkomwe.”

[Mawu a M’munsi]

a “Last” ndi chinthu chokonzedwa ngati phazi chomwe amagwiritsira ntchito kukonza mmene nsapato idzakhalire.

[Bokosi patsamba 26]

Matenda Anayi Ofala Amapazi

Bunions. Bunion ndi chotupa kunsi kwa chala chachikulu. Ngati sizotengera mwachibadwa, zotupazo zikhoza kupangika ndi nsapato zothina kapena zazitali chidendene. Kuthowapo kapena kuikapo ayezi kukhoza kuchepetsako kuŵaŵa kwakanthaŵi, koma opaleshoni ndiyo imafunika kuchotseratu chotupacho.

Hammertoes. Mungakhale ndi zala zokhotera pansi ngati muvala nsapato zopanikiza kwambiri kutsogolo kwa phazi. Pangafunike opaleshoni kuwongola pokhotapo.

Corns. Zotupa zabulungira m’zala, zochitika chifukwa cha kupekesana ndiponso kupanikizika, nthaŵi zina kochitika chifukwa cha kuvala nsapato zochepa m’mbali. Mankhwala a panyumba akhoza kungothandiza pang’ono, nthaŵi zambiri pamafunika opaleshoni kuti aongole zala zokhotazo zomwe zimachititsa kupekesana.

Calluses. Miyalo ya khungu lokhuthala, losamva kuŵaŵa imathandizira phazi pa kupekesana koŵirikiza. Kuviika m’madzi ofunda ndi a mchere wa Epsom kukhoza kulifeŵetsa. Koma musayese kucheka, popeza izi zikhoza kubweretsa matenda.

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

The Complete Encyclopedia of Illustration/J. G. Heck

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena