Chisamaliro Kaamba ka Mapazi a Ana
“TIKUBALA mtundu wa opunduka,” akudera nkhawa tero Adrian Grier katswiri wodziŵa za matenda a mapazi wa mu mzinda wa Luton, England. M’chigawo cha m’chipatala chake, iye amawona ana achichepere a zaka zisanu ndi chimodzi za kubadwa okhala ndi mapazi osapangidwa bwino. Chochititsa: Nsapato zosalinga bwino. M’chaka chimodzi chokha, pa ana oposa 3,000 ofufuzidwa ndi Grier, 600 a iwo anali ndi vuto la mapazi lochititsidwa ndi nsapato zomwe sizinalinge bwino. “Kufulumira kumene ana amayamba kuvala nsapato zokometsera kumakhalanso kufulumira kwa kubwera kwa kusapangidwa bwino ndipo kudzakhalanso tero kuipa kwake,” analongosola tero Grier mu Luton Herald. Koma nsapato zosalinga bwino siziri kokha chochititsa kaamba ka kusapangidwa bwino kwa mapazi. Mapazi a makanda angakhale osapangidwa bwino pachiyambi ngati makolo awaika iwo mu nsapato zogwira kwambiri, ndipo masokisi omwe ali ang’ono kwambiri angakhale ovulaza chimodzimodzi, anatero Grier.
Kukhala ogalamuka ku ngozi ndi kutenga kafikiridwe ka nzeru m’kugula kwa nsapato zopangidwa bwino kudzachita zambiri kuchinjiriza kulemalako, kupunduka kwa zala, zotupa, ndipo ngakhale zilonda za m’mapazi mu moyo wotsatira. Grier akulingalira kuti nsapato kaamba ka ana zikhale zotalika mainchi 3/4 (2 cm) kuposa phazi la mwana (kuti chilole kaamba ka kukula) ndi kukhala ndi zala zowulungana bwino.
Chitadza ku zovala, limodzinso ndi nsapato, chidule cha malingaliro otsimikizirika a pa nthaŵi yakechi kwa akazi Achikristu chingakhale chothandiza kwa onse: ‘Khalani oyenera ndi anzeru ponena za zovala zanu.’—1 Timoteo 2:9, Today’s English Version.