Mtendere ndi Bata Kodi Zidzakhalakodi?
PAMENE anthu ena anafunsidwa chimene anakafuna pomakachitira tchuthi chawo kumaiko ena, pafupifupi atatu mwa anayi alionse mwa alendo achibritishi anayankha kuti anakafuna, “Mtendere ndi bata.” Koma chifukwa cha vuto la phokoso kuzungulira dziko lonse, ambiri amakhulupirira kuti mtendere weniweni ndi bata ndi loto chabe.
Ngakhale kuti pakhala zoyesayesa zamphamvu kuti achepetseko phokoso, mungafunse kuti, Kodi tiyenera kukhulupirira kuti tsiku lina padzakhala palibiretu phokoso lina lililonse? Bwanji za ena amene alibe nkhaŵa ngati yanuyo?
Zopinga Zoyenera Kuchotsedwapo
Nkovuta kulankhula ndi anthu amakani. Ndipo nkovuta kwambiri kuwachititsa kuti amvetse malingaliro anu. Pamene gulu lina la achinyamata laphokoso kwambiri linasonkhana panja pa nyumba imene Ron anali kukhalamo, iye anangopanga nzeru yopalana nawo ubwenzi. Anadziŵa maina awo. Ndipo anawathandiza ngakhale kukonza imodzi ya njinga zawo. Chiyambire pamenepo, iwo sanamvutitsenso.
Titenge chitsanzo cha Marjorie, mayi wopanda mwamuna koma amene ali ndi mwana wachitsikana, ndipo amakhala m’fulati yozingidwa ndi anansi aphokoso. Okhala pamwamba pake alibe kapeti m’nyumba. Chifukwa cha chimenecho, ana a m’nyumbamo amamsokosera kwambiri Marjorie pamene amathamangathamanga m’nyumbamo ndi nsapato zamaŵiro, kuzanditsa mpira pansi, ndipo ngakhale kulumpha kuchokera pabedi kumamsokosera. Kuphatikiza pa zimenezo, mayi wa anawo amavala nsapato zazitali panyumba. Marjorie anakafikira mnansi wakeyo mwaulemu nampempha kuchepetsako phokoso, komano mnansiyo sankatha kulankhula bwino Chingelezi moti sizinaphule kanthu. Antchito a boma anati adzatumiza womasulira kuti akathandize kuthetsa vutolo. Choncho Marjorie akuyembekeza kuti mwina zinthu zingakhale bwino.
M’nyumba yapansi pake m’makhala mwamuna amene amaimba nyimbo pa wailesi mopokosera kwambiri pakati pa 7 ndi 8 koloko mmaŵa uliwonse. Ndipo nyimbozo zimapanga phokoso logunda mosalekeza. Ngakhale kuti Marjorie anafikira mwamunayo mosamala ndithu, iye poyankha anati nyimbo zakezo zinali zofunika kwambiri ‘kukonzekeretsa maganizo ake kuti agwire bwino ntchito.’ Kodi Marjorie athana nazo bwanji zimenezo?
Iye akuti: “Ndikulimbikira kudziletsa ndi kupirira. Ndasintha programu yanga, ndimakhala pansi ndi kuŵerenga mosasamala kanthu za phokosolo. Ndimapeza kuti mwamsanga ndimamwerekera ndi buku langalo. Basi ndikatero, phokoso lija sindimalimva kwenikweni.”
Koma Heather amakhala m’fulati yoyang’anizana ndi naitikalabu, mmene mumakhala phokoso kwambiri usiku wonse mpaka nthaŵi yotseka m’ma 6 koloko mmaŵa. Ngakhale kuti pomalizira pake anakapereka lipoti ku boma, palibe zenizeni zimene zachitidwa kuthetsa vutolo.
Kutha kwa Phokoso?
“Anthu ambiri amanena kuti kukangoti zii kopandiratu phokoso lina lililonse, kumakhala konyong’onya kwambiri ndi koopsa,” anatero Dr. Ross Coles wa bungwe la Institute of Hearing Research limene ndi nthambi ya Medical Research Council ya ku Britain. Nyimbo zokoma za mbalame, kugavira kosangalatsa kwa mafunde pagombe, nsangala yokondweretsa ya ana—ndi mapokoso ena amatisangalatsa. Ngakhale kuti panopo tingakhumbe kuti phokoso lonse lithe, timasangalala kukhala limodzi ndi mabwenzi abwino amene timacheza nawo. Mulungu walonjeza mtendere ndi bata kwa atumiki ake okhulupirika.
M’Baibulo wamasalmo analengeza kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) Boma la Ufumu wakumwamba wa Mulungu posachedwapa lidzaloŵerera m’zochita za anthu. (Danieli 2:44) Pamenepo, padzakhala “mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi,” mu ulamuliro wa Kristu Yesu.—Salmo 72:7; Yesaya 9:6, 7.
Mungathe kukhala ndi chitsimikizo chakuti kuloŵapo kwa Mulungu kudzadzetsa mtendere ndi bata zimene tonsefe tikukhumba, mogwirizana ndi ulosi wa Yesaya mneneri wa Mulungu wakuti: “Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthaŵi zonse. Ndipo anthu anga adzakhala . . . mopuma mwa phe.”—Yesaya 32:17, 18.
Ngakhale tsopanoli, mutha kupeza mtendere wauzimu ndi bata pamisonkhano ya Mboni za Yehova kwanu komweko. Ngakhale kuti nthaŵi zina zikwi makumimakumi amasonkhana m’misonkhano yaikulu—ndipo pamisonkhanoyi pamakhala ‘phokoso la amuna, akazi, ndi ana’—phokoso lakelo si lija losokosera, koma losangalatsa. (Mika 2:12) Kadzionereni nokha mwa kusonkhana ndi Mboni kwanuko kapena mwa kuwalembera pa keyala imodzi mwa ondandalikidwa patsamba 5 a magazini ino. Sangalalani ndi mtendere weniweni ndi bata potsagana nawo lero ndipo mwina mpaka kunthaŵi zonse.