Kuchuluka kwa Akufa Kofanana ndi Akufa Pankhondo
PAMENE Marilyn wazaka 23 anawonda ndipo anadzimva wofooka, analingalira kuti mwina chinali chifukwa cha kukhala kwake ndi pathupi kwaposachedwa. Analinso kutsokomola kosalekeza, zimene analongosola kwa dokotala wake. Dokotalayo anamuuza kuti ndi matenda a m’mphuno, nkhwiko ndi kholingo. Pambuyo pake, pamene anayamba kutuluka thukuta kwambiri usiku, Marilyn anada nkhaŵa kwambiri. Anapitanso kwa dokotala wake, yemwe anati ampime pachifuwa ndi makina a X ray.
Zoderadera zoonekera pa X ray zinasonyeza kuti anayenera kuchitapo kanthu mwamsanga, koma sizinali zotheka kulankhula ndi Marilyn patelefoni. “Dokotalayo anafikira amayi anga ndi kuwauza kuti ndinali wodwaladi kwambiri,” anatero Marilyn. “Amayi anga anabwera kudzandifuna ndi kundiuza kuti ndifunika kupita kwa [Dokotala] mwamsanga. Iye ananditumiza kuchipatala kumene anandipimanso ndi X-ray ndi kundigoneka.”
Marilyn anadabwa kumva kuti anali ndi chifuwa cha TB. Analingalira kuti adzafa, koma atapatsidwa mankhwala a TB, posapita nthaŵi anachira.
Nzomveka kuti Marilyn anadabwa kuti anali ndi chifuwa cha TB. Ngakhale akatswiri a zachipatala ankaganiza kuti chifuwa cha TB chathetsedwa m’maiko otukuka mpaka chaposachedwa. “Ndinkaganiza kuti chatha monga matenda a chaola,” anatero wogwira ntchito m’chipatala pachipatala china ku London. “Koma pamene ndinayamba kugwira ntchito kuno, ndinapeza kuti chilipo ndipo chikupitirizabe kuwonjezereka mofulumira m’mizinda yochulukana anthu.”
M’malo amene chifuwa cha TB chinatha, chayambanso; kumene chinalikobe, chawonjezeka. M’malo moti ithetsedwe, TB ndi yakupha mofanana ndi nkhondo ndiponso njala. Talingalirani:
◼ Ngakhale kuti mankhwala amakono ndi apamwamba, pazaka zapita zoposa zana limodzi, chifuwa cha TB chapha anthu pafupifupi mamiliyoni 200.
◼ Chifuwa cha TB chimapha akulu ambiri kuposa matenda ena onse kuwaphatikiza pamodzi. Kufika mpaka anthu mamiliyoni zikwi ziŵiri—chigawo chimodzi mwa zitatu za anthu padziko lapansi—ali kale ndi bakiteriya yoyambitsa TB. Ndiponso, munthu mmodzi pa sekondi iliyonse amagwidwa ndi chifuwa cha TB!
◼ Mu 1995 chiŵerengero cha anthu omwe anali kudwala chifuwa cha TB anali mamiliyoni 22. Pafupifupi mamiliyoni atatu anamwalira, ambiri a iwo m’maiko otukuka kumene.
Mankhwala amphamvu ochiritsira chifuwa cha TB alipo, nanga nchifukwa chiyani matenda ameneŵa akupitirizabe kukhala mliri pakati pa anthu? Kodi adzaŵagonjetsa? Kodi pali njira yoti mungadzitetezere ku matendaŵa? Nkhani zotsatirazi zidzayankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
New Jersey Medical School—National Tuberculosis Center