TB Yabweranso!
KUYAMBIRA m’ma 1950, chiŵerengero cha odwala tuberculosis (TB) chinatsika paliŵiro la 5 peresenti pachaka ku United States. Komabe, kuyambira 1985 pakhala chiwonjezeko cha 18 peresenti cha odwala TB odziŵika. Ndipo chimene chikuwopsa kwambiri nchakuti mtundu watsopano wa nthendayo umene wakhalako sukumva mankhwala. TB tsopano ikupha anthu pafupifupi mamiliyoni atatu chaka chilichonse. Kodi nchifukwa ninji nkhondo yolimbana ndi TB siikupambana?
Chifukwa china nchakuti odwala ambiri amangolephera kumwa mankhwala awo kwa nyengo yofunikira—nthaŵi zambiri miyezi isanu ndi umodzi kapena isanu ndi inayi. Mwachitsanzo, mu New York City kufufuza kwina kunasonyeza kuti 89 peresenti ya kagulu ka odwala TB okwanira 200 sanamalize mankhwala awo. “Zimenezo nzowopsa,” akutero Dr. Lee Reichman, pulezidenti wa American Lung Association, “chifukwa anthu amenewo (a) sadzachira, ndipo (b) mwinamwake adzakhala ndi TB yosamva mankhwala ofala amene akugwiritsiridwa ntchito.” Koma onyamula matendawo sangawononge thanzi lawo lokha. “Chifukwa cha kusamwa kwawo mankhwala,” akuwonjezera Dr. Reichman, “iwo akhoza kupatsira anthu ena matendawo.” Mosakayikira izi zathandizira kuwonjezeka kwa odwala pafupifupi mamiliyoni asanu ndi atatu opimidwa padziko lonse chaka chilichonse.
Ophunzira Baibulo akudziŵa kuti “miliri m’malo akutiakuti” ili mbali ya chizindikiro chakuti tikukhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo ili la zinthu. (Luka 21:11; 2 Timoteo 3:1) Kodi chidzatsatira nchiyani? Dziko lapansi latsopano, mmene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Inde, Yehova Mulungu akulonjeza, osati mpumulo wakanthaŵi, koma chimasuko chachikhalire ku matenda ndi imfa.—Chivumbulutso 21:1-4.