Kuithetsa Padziko Lonse Kodi Nkotheka?
AKATSWIRI akuvomereza kuti TB ndi vuto lapadziko lonse loyenera kuthandizana. Palibe dziko lomwe lingathetse TB palokha, chifukwa anthu mamiliyoni amayenda kudutsa malire mlungu uliwonse.
Ambiri amakhulupirira kuti mgwirizano wa maiko onse umalira kuti maiko olemera athandize maiko osauka, amene amakhudzidwa kwambiri ndi TB. Monga momwe Dr. Arata Kochi akunenera, “zidzawakhaliranso bwino maiko olemera ngati athandiza maiko osauka kulimbana ndi TB, isanafalikire ku maiko awo.”
Koma maiko olemera, poona zomwe amaganizira kuti ndizo zofunika choyamba ndiponso mavuto aakulu, sanachitepo kanthu mwamsanga kuthandiza. Maiko ena osauka amanyalanyaza za thanzi la anthu, m’malo mwake nkumawonongera ndalama zambiri pogula zida. Pofika chapakati pa 1996, ndi 10 peresenti yokha ya anthu odwala TB padziko lonse lapansi amene anali kuthandizidwa mwa kugwiritsira ntchito njira ya DOTS, ochepa kwambiri kosati nkulepheretsa mliriwu kufala.
Bungwe la WHO linati: “Nzeru ndi mankhwala osakwera mtengo ochiritsa TB zakhalapo kwazaka makumi ambiri. Chomwe dziko lifunikira ndicho kuti anthu audindo, otha kulimbikitsa zinthu ndi achifundo, achitepo kanthu mwamphamvu ndi kutsimikizira kuti mankhwalawa akugwiritsidwadi ntchito padziko lonse lapansi.”
Kuthetsa Komwe Kudzakhalapo
Kodi tingadalire anthu audindo ndi otha kulimbikitsa zinthu kuti adzathetsa vutoli? Wamasalmo a m’Baibulo wouziridwa analemba kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” Tsono ndani amene tiyenera kumkhulupirira? Lembalo likupitiriza kuti: “Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake; amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m’mwemo.”—Salmo 146:3, 5, 6.
Monga Mkonzi ndi Mlengi wadziko lapansi, Yehova Mulungu ali ndi zonse mphamvu ndi nzeru moti akhoza kuthetsa nthenda. Kodi Iye ali ndi chifundo? Kupyolera mwa mneneri wake wouziridwa, Yehova akulonjeza kuti: “Ndidzawaleka [“ndidzawachitira chifundo,” NW] [anthu anga] monga munthu aleka [“achitira chifundo,” NW] mwana wake womtumikira.”—Malaki 3:17.
Chaputala chomalizira cha Baibulo chimalongosola masomphenya omwe anaperekedwa kwa mtumwi Yohane. Iye anaona “mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziŵiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi.” Mitengo yophiphiritsira imeneyi ndi zipatso zimene imabala zimaimira makonzedwe a Mulungu amene adzatheketsa anthu kukhala kosatha padziko lapansi.—Chivumbulutso 22:2.
Popitiriza, Yohane analemba kuti: “Masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nawo amitundu.” Masamba ophiphiritsira ameneŵa amaimira madalitso ochokera kwa Mulungu amene adzachiritsa mtundu wa anthu, mwauzimu ndiponso mwakuthupi. Motero, tingatsimikizire kuti m’dziko latsopano lolungama mu ulamuliro wa Mulungu, TB idzathetsedwa kwamuyaya.—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Mulungu akulonjeza kuchiritsa mtundu wa anthu kwamuyaya