Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 2/8 tsamba 16-18
  • Momwe Ndimakhalira Monga Wachibwibwi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Momwe Ndimakhalira Monga Wachibwibwi
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mphotho Zokhala Wotsimikiza Mtima Pochita Zinthu
  • Mmene Ena Angathandizire
  • Utumiki Wowonjezereka
  • Kodi Mungatani Kuti Muchepetse Vuto Lochita Chibwibwi?
    Galamukani!—2010
  • Kuchokera kwa Owerenga
    Galamukani!—2012
  • Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kulankhula Mosadodoma
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 2/8 tsamba 16-18

Momwe Ndimakhalira Monga Wachibwibwi

Yosimbidwa ndi Sven Sievers

NDAKHALA wachibwibwi chiyambire kale ndili mwana. Ndikalingalira zammbuyo, ndimasangalala ndi mmene makolo anga ankachitira chifukwa cha vuto langalo. Ndikamalankhula mwachibwibwi, nthaŵi zonse iwo ankayesetsa kutchera khutu kumvetsera zimene ndikufuna kunena m’malo moyesa kuwongolera kalankhulidwe kanga. Malinga nkunena kwa madokotala odziŵa za kulankhula, makolo omwe nthaŵi zonse amanenanena za mmene mwana wawo akuchitira chibwibwi akhoza kungokulitsa vutolo.a

Amayi anga anakhala a Mboni za Yehova pamene ndinali ndi zaka zitatu. Ndili pa unyamata ndinasankha zotengera chitsanzo chawo ndipo ndinathandizidwa kuphunzira bwino kwambiri Baibulo. Pa July 24, 1982, ndinabatizidwa monga mtumiki wodzipatulira wa Mulungu pamsonkhano wa ku Neumünster, Germany. Kenaka ndinasamukira ku South Africa, kumene ndinapitiriza kuchita nawo ntchito yolalikira, imene Akristu oona onse amalamulidwa kuchita. (Mateyu 28:19, 20) Mungadabwe kuti nanga ndimachita bwanji poti ndine wachibwibwi?

Mphotho Zokhala Wotsimikiza Mtima Pochita Zinthu

Ndiyenera kuvomereza kuti nthaŵi zina zimandivuta kuti ndichite zinthu motsimikiza mtima, koma ndapeza kuti kuchita zinthu ndi mtima wonse kumandithandiza kwambiri. Nkhani njakuti ndikhoza kuthapo ndithu kukambitsirana ndi ena nthaŵi zonse. Ngati sindichita kulankhula, ndimakambitsirana nawo molemba zimene ndikufunazo mwinamwake mwa kungosonyeza mabuku olongosola za m’Baibulo. Kukhala wotsimikiza mtima kumandithandiza kuthetsa vuto losoŵa momwe ndiyambitsire nkhani. Ndimayesetsa kupanga mawu oyamba kukhala aafupi. Kuchiyambi kwa makambitsiranowo, ndimalola mwini nyumba kulankhula momwe angathere. Anthu amakonda kulankhula, ndipo izi zinkandithandiza kuzindikira zimene amaganiza. Kenaka, ndimapitiriza makambitsiranowo mwa kunena zomwe zimawakondweretsa, ndi kumveketsa uthenga wa m’Baibulo. Kukhala wotchera khutu ku zimene akunena kumandithandiza kuiŵala vuto langa lakulankhula, motero ndimachita chibwibwi pang’ono.

Kutsimikiza mtima kumandithandizanso kuyankhapo pamisonkhano yachikristu. Ndapeza kuti pamene ndilankhulapo kwambiri pa makambitsirano a nkhani zonena za m’Baibulo, mpamene osonkhanawo ndi wochititsa phunziroyo amandizoloŵera ndipo amakhala ndi chidwi ndi zimene ndikunena osati mmene ndikunenera.

Kuti ndizisangalala ndi kupita kwanga patsogolo, ndiyenera kumayesayesabe. Izi zimandithandiza kuti ndisamadzimvere chisoni kwambiri ndi kukhala wokhumudwa. Kulimbana ndi kuti ndisamakhale wodzimvera chisoni ndi ntchito yosatha. Pali mawu akuti ngati munthu agwa pa kavalo, kungakhale kothandiza kwa iye kukweranso pa kavalopo kuti asamadzikayikire. Choncho ngati ndaleka kulankhula popereka ndemanga chifukwa chakuti chibwibwi chakwera, ndimayesanso kukwera kavalo, kunena kwake titero, mwa kuyankha funso lotsatira.

Mmene Ena Angathandizire

Ndikamachita telefoni kapena kufunsa za chidziŵitso china kwa alendo, ndimayamikira chithandizo chawo. Koma ena amachita chipongwe popereka chithandizocho, ndipo amanditenga monga mwana amene sangathe kulingalira zochita.

Ndimayamikiranso chithandizo cha mkazi wanga wokondedwa Tracy. Asanayambe ‘kundilankhulira,’ timayamba takambitsirana nkhaniyo mwatsatanetsatane ndipo amadziŵa chimene ndikufuna kunena. (Yerekezerani ndi Eksodo 4:10, 14, 15.) Mwanjira imeneyo, amandilemekeza monga mwamuna wake, ndipo amandipangitsa kumva kuti ndikukhalabe moyo wabwinobwino.

Chithandizo china chachikulu ndicho Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Pamsonkhano wa mlungu ndi mlungu umenewu, ophunzira amaŵerenga Baibulo ndi kukamba nkhani zifupizifupi mogwiritsa ntchito mitu ya nkhani ya m’Baibulo. Ndinadabwa kuona kuti kaŵirikaŵiri ndimatha kuŵerenga ndi kulankhula bwino pamaso pa omvetsera. Nkadakhala kuti sindinalembetse nawo m’sukulu imeneyi, mwina sindikanadziwa nkomwe kuti ndili ndi luso limeneli.

Pamene ndakhala ndi nkhani m’Sukulu Yautumiki Yaterokratiki, zimakhala zosangalatsa kwambiri pamene mlangizi akhala ndi chidwi ndi zimene ndikunena osati ndi mmene ndazinenera. Ndapindula kwambiri ndi Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki,b ngakhale kuti mfundo zina za m’bukuli nzovuta kwambiri kwa amene amalankhula mwachibwibwi koposa kwa amene amalankhula bwinobwino. Mwachitsanzo, nthaŵi zina, malinga ndi mmene ndachitira chibwibwi, sinditha kutsiriza nkhani yanga panthaŵi yomwe ndapatsidwa. Komabe zimandilimbikitsa kwambiri pamene mlangizi andisonyeza mfundo zimene ndikhoza kuzitha.

Utumiki Wowonjezereka

Kale, ndinali ndi mwaŵi woŵerenga poyera m’buku lachikristu limene tikuphunzira pamsonkhano. Ndinalinso ndi mwaŵi wochititsa phunziro pamene panalibe mtumiki aliyense woyenera ntchitoyo, ndipo tsopano ndimachita zimenezo nthaŵi zonse. Ngakhale kuti poyamba ndimakhala ndi mantha, ndaona kuti Mulungu amandithandiza pochita utumiki umenewo.

Komabe, kwa zaka zambiri ndinali ndi mwaŵi wochepa woŵerenga kapena kuphunzitsa ndili papulatifomu mumpingo. Izi zinali zomveka, chifukwa nthaŵi zina zinkanditengera nthaŵi yochuluka kwambiri kuti anthu amvetse zimene ndikunena. Motero ndinagwiritsira ntchito mphamvu zanga zonse pochita mautumiki ena. Poyamba, ndinatumikira ngati wothandiza kusamalira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a mpingo. Kenaka, nditaikidwa kukhala mtumiki wotumikira, ndinayamba kusamalira mabaibulo, mabuku, ndi zofalitsa zina. Kenaka, anandigaŵira kuti ndiziyang’ana makadi a gawo amene timagwiritsira ntchito pantchito yathu yochitira umboni poyera. Kuika nzeru zanga zonse pa mautumiki ameneŵa, ndikumayesa kuti ndiigwire bwino ntchitoyi, kunandisangalatsa kwambiri.

Kwazaka zisanu ndi zitatu zapitazo, ndatumikiranso ngati mlaliki wanthaŵi zonse pamodzi ndi Tracy. Ndithudi, pazimenezinso Yehova wandidalitsa kwambiri. Ndipo, nthaŵi zina ndimadabwa kuti kaya mwina Yehova akugwiritsira ntchito kufooka kwanga kolankhula mwachibwibwi. Mwa anthu asanu amene ndathandiza kufika pokhala Akristu odzipatulira, aŵiri ndi achibwibwi.

Ndimakumbukirabe mwachimwemwe tsiku limene ndinasankhidwa kutumikira monga mkulu mumpingo. Ngakhale kuti ndili ndi luso lochepa la kuphunzitsa papulatifomu, ndimaika mtima pakuthandiza aliyense payekha. Chibwibwi sichindilepheretsa kufufuza m’Malemba kuti ndithandize ena mumpingo omwe akukumana ndi mavuto aakulu.

Pazaka zisanu zapitazo, ndakhala ndikupemphedwa kulankhulapo pamisonkhano. Kuwonjezera pa kupereka nkhani m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki, ndakhala ndikumakwanitsa kupereka zilengezo zachidule pamisonkhano ina. Pang’onopang’ono kulankhula kwanga kwaongokera. Koma nthaŵi ina chibwibwi chinakulanso. Mwankhaŵa kwambiri, ndinaganiza kuti, ‘Sadzandigaŵiranso nkhani,’ koma zodabwitsa, dzina langa linaonekeranso pandandanda yotsatira ya okamba nkhani! Woyang’anira wotsogoza wa mpingo wathu ananena kuti ngati ndipeza kuti ndabanika kulephera kulankhula kwakuti sindingapitirize, ndingomuyang’ana iye ndipo abwera ku pulatifomu ndi kudzapitiriza. Ndinagwiritsira ntchito mwaŵi umenewu kamodzi kapena kaŵiri, koma m’miyezi yaposachedwa sindinachitepo zimenezo. Pamene ndinayamba kumalankhulako bwino, anayamba kumandigaŵira nkhani zazitalipo, kuphatikizapo nkhani zapoyera. Ndinazindikira bwino kwambiri kuti ndikulankhulako bwino posachedwa pamene anandipempha kuchita nawo zitsanzo ziŵiri pamsonkhano wadera wa Mboni za Yehova.

Kunena zoona, sindimvetsetsa bwino kuti nchifukwa ninji ndayamba kumalankhulako bwino. Mwina mtsogolo zikhoza kudzabwereranso. Ndipotu, ngakhale zikuoneka kuti ndasintha ndi kumalankhulako bwino pa pulatifomu, panthaŵi zina ndimabanika pamene ndikulankhula ndi anthu kwandekha. Motero sindinganene kuti tsopano ndili bwino kuti chibwibwi chatha. Ndikakhala kuti ndalephera kulankhula, ndimayesetsa kukumbukira kuti ndiyenera kulolera zokha zomwe ndingathe kuchita ndi “kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu.”—Mika 6:8.

Mulimonse mmene zidzakhalire mtsogolo, ndidzapitirizabe kuyesetsa pozindikira kuti m’dziko latsopano la Mulungu lomwe layandikira, chibwibwi chidzathetsedweratu. “Lilime la achibwibwi lidzalankhula zomveka msanga,” limatero Baibulo. Ndili ndi chikhulupiriro kuti zimenezi zidzachitikadi mwakuthupi ndiponso mwauzimu ndi kuti ‘wosalankhula adzaimba.’—Yesaya 32:4; 35:6.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Understanding the Fear of Stuttering,” mu Galamukani! yachingelezi ya November 22, 1997.

b Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 18]

Ndi mkazi wanga, Tracy

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena