Stroko!
STROKO ndiyo imapha ndi kupundula anthu kwambiri kumaiko otukuka a Kumadzulo. Matenda ameneŵa amagwira ubongo mwadzidzidzi. Kanthaŵi aka ukhoza kukhala uli bwino, kenaka, ungomva ngati kuti mphezi yakugwera—stroko yamphamvu ingasinthe moyo wanu modzidzimutsa ndipo kwambiri. Ikhoza kukupundulani mwankhanza, kukupangitsani kukhala wosalankhula, wodandaula, kusintha umunthu wanu ndi luso lanu la kuzindikira zinthu, ndi kukuikani pankhondo yosatha yoyesa kukhalanso ndi moyo womwe inu ndi banja lanu munali nawo kale.
Talingalirani za Ellen Morgan.a Lachitatu, Ellen anali munthu wazaka 64 wathanzi ndi wamphamvu. Lachinayi, akugula zinthu ndi mwamuna wake, mwadzidzidzi Ellen sanathenso kulankhula, ndipo nkhope yake inapotoka. Thupi lake linafooka, ndipo anali kumangodzandira monga waledzera. Ellen anagwidwa ndi stroko yamphamvu!
Pambuyo pa strokoyo, Ellen anali wopuwala mwakuti anali kulephera kuchita zinthu zing’onozing’ono monga kusamba kapena kuvala. Pokhala wosatha kulemba, kuluka, kapena kusoka, anayamba kumangolira mosatonthozeka ndiponso anali kukhala wolefuka kwambiri. Ellen sanasokonezeke nzeru; komabe, anali kukhumudwa akamubwerera malingaliro akuti mwina ena akumuona monga wosokonezeka. Pambuyo pake, Ellen ananena kuti: “Ndi ochepa amene amazindikira mmene kusintha kwamwadzidzidzi kumeneku kumakhudzira mtima ndi maganizo a munthu. Ndinatsala pang’ono kuganiza kuti amenewo ndiwo anali mapeto anga.”
Kodi chimapangitsa stroko nchiyani? Kodi aliyense amene ali ndi stroko amamva chimodzimodzi? Kodi amene apulumuka atha bwanji kupirira ndi nthendayi? Kodi mabanja omwe ali ndi odwala stroko amakhala bwanji? Kodi ena tonsefe tingathandize motani? Galamukani! ino ikuyankha mafunso ameneŵa ndipo ikuthandizani kumvetsetsa miyoyo ya opulumuka stroko ndiponso mabanja awo amene amavutika nawo.
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena asinthidwa poganizira odwalawo ndi mabanja awo.