Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 2/8 tsamba 4-8
  • Stroko—Chomwe Chimaiyambitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Stroko—Chomwe Chimaiyambitsa
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zotsatira Zake
  • Vuto pa Kulankhulana
  • Kusintha Mtima ndi Umunthu
  • Apabanja Nawonso Amavutika
  • Kupirira Nsautso Yobwera Pambuyo Pake
    Galamukani!—1998
  • Stroko!
    Galamukani!—1998
  • Ubongo—“Woposa Kompyuta”
    Galamukani!—1988
Galamukani!—1998
g98 2/8 tsamba 4-8

Stroko—Chomwe Chimaiyambitsa

“UBONGO ndiwo chiŵalo chofeŵa kwambiri m’thupi,” anatero dokotala wa za mitsempha yotumiza mauthenga m’thupi Dr. Vladimir Hachinski, wa pa Yunivesite ya Western Ontario ku London, Canada. Uli maperesenti aŵiri chabe a kulemera kwa thupi lonse, koma ubongo uli ndi mitsempha yoposa mamiliyoni zikwi khumi yotumiza mauthenga imene imapatsirana uthenga nthaŵi zonse kuti ipangitse malingaliro, kuyenda ndi kuzindikira kwathu zinthu kwa tsiku ndi tsiku. Popeza umadalira okosijeni ndi glucose, ubongo umalandira zimenezi mosalekeza kudzera m’mitsempha yolukanalukana.

Komabe, pamene mbali ina ya ubongo imanidwa okosijeni kwa masekondi oŵerengeka, mitsempha yotumiza mauthenga yofeŵayo imaleka kugwira ntchito yake. Ngati izi zipitirira kwa mphindi zingapo, zotsatira zake zimakhala kuwonongeka kwa ubongo pamene maselo ake amafa kuphatikizaponso ntchito yawo. Izi zimatchedwa ischemia, kupereŵera kwa okosijeni kochitika chifukwa cha kutsekeka kwa mtsempha. Minofu ya ubongo imawonongekanso popeza kupereŵera kwa okosijeni kumasokoneza makemikolo a mu ubongo ndipo nzoopsa. Zotsatira zake zimakhala stroko. Nthaŵi zina stroko imachitikanso pamene mitsempha ya magazi isweka, zikumapangitsa magazi kudzaza mu ubongo ndipo zimenezi zimatseka mitsempha ina. Izi zimasokoneza kayendedwe ka makemikolo ndi mphamvu yamagetsi kupita ku minofu ndipo zimapangitsa minofu ya ubongoyo kuvulazika.

Zotsatira Zake

Stroko iliyonse imasiyana ndi inzake, ndipo stroko imakhudza anthu mwanjira zosiyanasiyana. Ngakhale kuti palibe yemwe zimamchitikira zonse zomwe stroko imachita, zotsatira zakezo zimakhala kuyambira pa zosavuta ndipo zosaoneka kwenikweni kufika zoipirapo, zoonekeratu kuti nzoŵaŵa kwambiri. Thupi limalephera kugwira ntchito malinga ndi mbali ya ubongo komwe stroko yachitikako.

Nthaŵi zambiri munthu amafooka kapena kupuwala manja ndi miyendo. Kaŵirikaŵiri, izi zimachitika mbali imodzi ya thupi, mbali yomwe ubongo sunagwidwe stroko. Motero, ubongo ukawonongeka kudzanja lamanja thupi limapuwala kudzanja lamanzere, ndipo ubongo ukawonongeka kudzanja lamanzere thupi limapuwala kudzanja lamanja. Ena angathe kugwiritsira ntchito dzanja kapena mwendo wawo, kumangodabwira kuti minofu ikunjenjemera kwambiri kwakuti mwendo kapena dzanjalo limangopezeka likupita kwina osati kumene amafunako. Wodwalayo amaoneka ngati wochita maseŵera a skate akuyesayesa kudzilimbitsa kuti asagwe. Dr. David Levine wa ku New York University Medical Center anati: “Luso lawo lakuzindikira kuti mwendo kapena dzanja lawo likuyenda ndi kuti lili pati limakhala litatha.”

Kufika mpaka 15 peresenti ya opulumuka nthendayi nthaŵi zambiri amakonda kudwala mwadzidzidzi, zotsatira zake zimakhala kunjenjemera, ndipo kukomoka kaŵirikaŵiri. Komanso nzofala kuti thupi lawo limachita chidzanzidzanzi. Wopulumuka stroko wina yemwe manja ndi miyendo yake imachita chidzanzidzanzi anati: “Masiku ena usiku chinachake chimandikhudza miyendo ndipo ndimadzuka chifukwa zimakhala ngati shoko yamagetsi ikundigwira.”

Zotsatira za stroko zingaphatikizepo kumaona chinthu chimodzi ngati ziŵiri ndiponso vuto pomeza. Ngati zawonongeka ndi zomwe zimawongolera pakamwa ndi pakhosi, pangakhale zina zochititsa manyazi kwa odwala stroko, monga kuchucha dovu. Zikhoza kusokoneza mphamvu ya kuona, kumva, kununkhiza, kulaŵa, ndi kukhudza.

Vuto pa Kulankhulana

Yerekezani inu nokha kuti anthu aŵiri akulu matupi omwe simuwadziŵa akukulondolani mumsewu kuli kamdima. Mutayang’ana m’mbuyo, mukuwaona akukuthamangirani. Pamene mukuyesera kukuwa kuti anthu akuthandizeni, mawu anu atsekeka! Kodi mukuona mmene mungakhalire okhumudwa kwambiri zitakhala motero? Izi ndizo zimene ambiri mwa odwala stroko amamva pamene modzidzimutsa amakhala osathanso kulankhula.

Kukhala osatha kunena zomwe mukuganiza, momwe mukumvera, zomwe mukuyembekeza ndiponso mantha anu—mmawu ena kupatukana ndi banja—ndicho chotsatirapo chimodzi chowononga kwambiri cha stroko. Wina yemwe anapulumuka stroko anazilongosola motere: “Nthaŵi iliyonse ndikafuna kuti ndinene kanthu, palibe mawu amamveka. Ndinakakamizika kumangokhala chete ndipo sindinkatha kutsatira malangizo kaya olankhulidwa kapena olembedwa. Mawu ankangomveka . . . ngati kuti anthu omwe ndili nawo pafupi akulankhula chilankhulidwe chachilendo. Sindinali kumva ndipo sindinali kulankhula.”

Koma Charles anali kumva zonse zomwe anali kumuuza. Koma kuti ayankhe, iye analemba kuti: “Ndinali kukhala nazo zoti ndinene, koma ndinkalankhula zosamveka ndipo zosalongosoka. Zikatero, ndinkaona ngati ndine womangika.” M’buku lake lakuti Stroke: An Owners Manual, Arthur Josephs akunena kuti: “Minofu yosiyanasiyana yoposa zana imalamulidwa ndi kugwirizana panthaŵi yolankhula ndipo uliwonse wa minofu imeneyo umalamuliridwa ndi mitsempha yonyamula mauthenga m’thupi yokwana zana pa avareji. . . . Pamachitika zinthu zokwana 140,000 m’mitsempha yonyamula mauthenga kuti pakhale kulankhula kwa sekondi imodzi. Kodi kungakudabwitseni kuti kuvulala kumbali ina yochepa ya ubongo yomwe imalamulira minofu imeneyi kukhoza kupangitsa munthu kulankhula zosamveka bwino?”

Stroko imasokoneza kwambiri chigawo chimene chimalamulira kulankhula. Mwachitsanzo, munthu yemwe sangathe kulankhula akhoza kumatha kuimba. Wina akhoza kunena mawu modzidzimukira koma osati pamene iye wafuna, mwina nthaŵi zina amalankhula mosalekeza. Ena amangobwerezabwereza mawu kapena kugwiritsira ntchito mawu mosayenerera, kumati inde pamene akutanthauza kuti ayi kapena ayi akutanthauza kuti inde. Ena amadziŵa mawu amene akufuna kunenawo, koma ubongo sungathe kulamulira pakamwa, milomo, ndi lilime kuwanena. Mwina akhoza kumalankhula zosamveka bwino chifukwa cha kufooka kwa minofu. Ena akhoza kumakuwa apa ndi apo mobwerezabwereza polankhula.

Nthaŵi zina stroko ingawononge mbali ya ubongo imene imalamulira mphamvu ya mawu. Zotsatira zake ndizo kulankhula mawu opanda mphamvu. Mwina wodwalayo sangazindikire kusiyana kwa mphamvu ya mawu a ena. Zopinga kulankhulana zimenezi kuphatikizapo zimene tatchulapo kale zimagaŵanitsa banja, monga mwamuna ndi mkazi. Georg akunena kuti: “Popeza stroko imakhudza kaonekedwe ka nkhope ndiponso kayendetsedwe ka manja polankhula, ndithudi umunthu wonse, mwadzidzidzi sitinalinso kumvana ngati kale. Kwa ine zinkaoneka ngati ndili ndi mkazi wina yemwe anafunikira kuti ndichitenso kumzoloŵera.”

Kusintha Mtima ndi Umunthu

Kusinthasintha kakhalidwe mosayenera, kulira kapena kuseka mosayembekezereka, kukwiya kwambiri, kukayikira zinthu kwachilendo, ndi kuchita chisoni konyanyira ndiko kusintha kwa mtima ndi umunthu zimene opulumuka stroko ndiponso mabanja awo ayenera kulimbana nazo.

Gilbert wodwala stroko, anati: “Nthaŵi zina ndimakhudzidwa mtima kwambiri, mwina kumaseka kapena kulira pa zinthu zochepa. Nthaŵi zina ndikaseka, wina amatheka kundifunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ukuseka?’ ndipo sinditha kuwauza ayi.” Zimenezi, kuphatikizapo kuyenda modzandira ndi kutsimphina pang’ono, zinampangitsa Gilbert kunena kuti: “Ndingoona ngati ndili m’thupi lina, ngati kuti ndine wina, osati yemwe uja ndinali stroko isanandigwire.”

Omwe malingaliro ndi thupi lawo zimasinthasintha, ndi oŵerengeka chabe ngati alipo nkomwe omwe sapsaipsa mtima. Hiroyuki, amene stroko inampangitsa kusamalankhula bwino ndiponso kupuwala pang’ono, anati: “Sindinakhalebe bwino ngakhale kuti panapita nthaŵi. Nditazindikira kuti sindingathenso kupitiriza kumagwira ntchito yanga ngati kale, ndinakhala wokhumudwa. Ndinayamba kumangoimba mlandu chilichonse ndi anthu omwe ndipo ndinamva ngati kuti mtima wanga uphulika. Sindinkachita zinthu monga mwamuna.”

Sichachilendo kwa munthu wa stroko kukhala ndi mantha ndi nkhaŵa. Ellen akuti: “Ndimadzimva wosatetezereka ndikamva ngati kulemera m’mutu mwanga kumene kumasonyeza kuti ndidzagwidwanso stroko mtsogolo. Ndimachita mantha kwambiri ndikamalingalira zimenezo.” Ron akulongosola za nkhaŵa zimene ali nazo: “Nthaŵi zina sizitheka kuti ndilingalire kanthu kufika pomanga mfundo yakutiyakuti. Zimakhala zokhumudwitsa ndikati ndiyese kulingalira zinthu ziŵiri kapena zitatu zochepa panthaŵi imodzi. Ndimaiŵala zinthu msanga kwambiri mwakuti nthaŵi zina sindikumbukira zomwe ndinaganiza mphindi pang’ono zapitazo. Zotsatira zake, ndimalakwitsa zinthu kwambiri, ndipo zimandikhumudwitsa ine mwini ndi ena. Kodi ndidzakhala bwanji zaka pang’ono chabe kutsogoloku? Kodi sindizidzatha kukambitsirana ndi ena mwanzeru kapena kuyendetsa galimoto? Kodi ndidzavutitsa mkazi wanga?”

Apabanja Nawonso Amavutika

Nzoonekeratu kuti si ogwidwa stroko okha amene amavutika ndi zotsatirapo zowonongazo. Mabanja awonso amavutika. M’zochitika zina amavutika ndi maganizo kuona yemwe kale amatha kulankhula, munthu wabwinobwino mwadzidzidzi, iwo ali chipenyere wafooka, nkukhala ngati kamwana kumangodalira ena. Maunansi a m’banja amasokonezeka chifukwa ena mwina amafunikira kuchita zomwe sankachita kale.

Haruko akulongosola zotsatirapo zoipazo motere: “Mwamuna wanga anaiŵala pafupifupi kalikonse kofunika. Mosayembekezera tinasiya kampani imene tinali kuyendetsa ndipo tinaluza nyumba ndi katundu wathu. Chinandiŵaŵa kwambiri chinali kusatha kulankhulanso bwinobwino ndi mwamuna wanga ndi kusamfunsanso malangizo. Popeza samathanso kuzindikira kuti ndi usiku kapena ndi usana, kaŵirikaŵiri nsalu zovala usiku ngati mateŵera amazivula. Ngakhale kuti tinkadziŵa kuti nthaŵi idzafika pamene adzakhala wotero, nzovutabe kuti ife tizoloŵere mmene alilimo. Kakhalidwe kathu kasinthiratu, chifukwa tsopano mwana wanga wamkazi ndi ine ndife tsopano amene timasamalira mwamuna wanga.”

“Kusamalira yemwe ali ndi stroko—mosasamala kanthu mmene mumamkondera—nthaŵi zina kungakutopetseni,” akutero Elaine Fantle Shimberg m’buku lake lakuti Strokes: What Families Should Know. “Mavuto ndiponso ntchito imeneyi siitha.” Nthaŵi zina chisamaliro chimene ena m’banjamo amapereka chingakhale chowononga thanzi, chosautsa mtima, ndiponso chosokoneza uzimu wawo. Maria analongosola kuti stroko ya amayi ake inavutitsa moyo wake kwambiri: “Ndimakawachezera tsiku lililonse ndipo ndimayesa kuwalimbikitsa mwauzimu, kuŵerenga ndi kupemphera nawo pamodzi, ndiye kenaka kuwasonyeza chikondi, kuwakumbatira, ndi kuwapsompsona. Ndikabwera kunyumba, ndimakhala nditapsinjika maganizo—masiku ena mpaka kusanza.”

Chinthu chovuta kwambiri kuchipirira kwa osamalira anzawo ena ndicho kusintha kwa khalidwe. Dr. Ronald Calvanio, dokotala wa za mitsempha yonyamula mauthenga, anauza Galamukani! kuti: “Ngati pali matenda ogwira ubongo—ndiko kuti, mmene munthu amaganizira, khalidwe lake, mtima wake—zikukhudza umunthu wa munthuyo, motero mwanjira ina kusokonezeka kwa zinthu m’maganizo kumene kumachitika kumasinthadi kwambiri kakhalidwe ka banja.” Yoshiko akunena kuti: “Ndinaona ngati kuti mwamuna wanga wasinthiratu atangodwala, amakalipa mosayembekezereka pa zinthu zazing’ono. Nthaŵi imeneyo ndimavutika kwambiri.”

Kaŵirikaŵiri, omwe si a m’banjamo sangaone kusintha kwa khalidweko. Motero, ena mwa amene amasamala odwala otero amaona ngati kuti anyanyalidwa ndipo amachita ntchitoyo okhaokha. Midori akunena kuti: “Nthenda ya stroko yapundula maganizo ndi mtima wa mwamuna wanga. Ngakhale kuti amafunikira kwambiri chilimbikitso, sanena zimenezo kwa wina aliyense ndipo amangodzivutikira yekha. Choncho zimanditsalira ine kumamlimbikitsa. Kumaona mmene mwamuna wanga waukira kuti kaya ndi wosangalala kapena ndi wodandaula tsiku ndi tsiku kumandidetsa nkhaŵa ndipo nthaŵi zina ndimachita mantha.”

Kodi ambiri amene anapulumuka nthenda ya stroko ndiponso mabanja awo atha bwanji kumakhala ndi kusintha kumene stroko imabweretsa? Kodi ndi motani mmene aliyense wa ife angathandizire amene akuvutika nkupuwala kochitika ndi stroko? Nkhani yathu yotsatira idzalongosola zimenezi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

Zizindikiro Zochenjeza

• Kufooka kwa mwadzidzidzi, kumva ngati wachita chidzanzidzanzi, kupuwala kwa nkhope, dzanja, kapena mwendo, makamaka mbali imodzi ya thupi

• Mwadzidzidzi kuyamba kuona zinthu mwachimbuuzi kapena kumaona ngati kuli kamdima, makamaka diso limodzi; kumaona chinthu chimodzi ngati ndi ziŵiri

• Kumavutika kuti ulankhule kapena kuti umve ngakhale kachiganizo kochepa

• Chizungulire kapena kumadzandira kapena kusagwirizana kwa miyendo poyenda, makamaka ngati zichitikira nthaŵi imodzi ndi chizindikiro china

Zizindikiro Zosafala Kwenikweni

• Kuŵaŵa kwambiri kwa mutu kwa mwadzidzidzi—kaŵirikaŵiri konenedwa kuti “kuŵaŵa kwa mutu koposa kwina konse”

• Mwadzidzidzi kufuna kusanza ndiponso kutentha kwa thupi—kosiyana ndi kochitidwa ndi mavairasi chifukwa cha kuyambika kwake mofulumira (m’mphindi kapena maola chabe m’malo mwa masiku ambiri)

• Kusazindikira zinthu kwa kanthaŵi kapena kukhala watulotulo kwa kanthaŵi (kukomoka ndi kusokonekera maganizo)

Musanyalanyaze Zizindikiro

Dr. David Levine akunena mwamphamvu kuti ngati muona zizindikirozi, wodwalayo ayenera “kupita kuchipatala mwamsanga ndithu. Pali umboni wakuti ngati mupatsa mankhwala odwala stroko maola ochepa oyambirirawo, siiwononga kwambiri.”

Nthaŵi zina zizindikirozi zikhoza kungooneka kwa kanthaŵi kochepa kenaka nkuleka. Zochitika zotere zimatchedwa TIA kapena kuti transient ischemic attacks. Musazinyalanyaze, chifukwa zimenezi zingasonyeze kuti muli pangozi kwambiri yogwidwa stroko, ndipo pambuyo pake stroko yamphamvu ingakugwireni. Dokotala akhoza kuchitapo kanthu pa zopangitsazo ndi kuthandiza kuchepetsa ngozi yoti mukanadwalanso stroko mtsogolo.

Tatengera pa malangizo operekedwa ndi National Stroke Association, Englewood, Colorado, U.S.A.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena