Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 2/8 tsamba 8-12
  • Kupirira Nsautso Yobwera Pambuyo Pake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupirira Nsautso Yobwera Pambuyo Pake
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chithandizo cha Banja ndi Mabwenzi
  • Kuphunzira Kuthandiza
  • Kupirira, Pothandizidwa ndi Yehova Mwachikondi
  • Opereka Chithandizo Alimbikitsidwa
  • Kupirira Zolepheretsa Zambiri
  • Stroko—Chomwe Chimaiyambitsa
    Galamukani!—1998
  • Stroko!
    Galamukani!—1998
  • Nyengo ya Kuchira
    Galamukani!—1996
  • Kusamala Wosamala Ena Mmene Ena Angathandizire
    Galamukani!—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 2/8 tsamba 8-12

Kupirira Nsautso Yobwera Pambuyo Pake

ALI chigonere pa bedi m’chipatala mwendo ndi dzanja zitapuwala, Gilbert anafunsa dokotala wake kuti: “Kodi mwendo ndi dzanja langali zidzayambanso kugwira ntchito?” Gilbert anamva yankho loopsa lakuti: “Pamene ulimbikira kwambiri mpamenenso zidzayambe kugwiranso ntchito mwamsanga.” Iye anayankha kuti: “Ndine wokonzekera kutero!” Pausinkhu wa zaka 65, mothandizidwa ndi zochitachita zolimbitsa thupi za kuchipatala pamodzinso ndi khama lake zinamthandiza kuchoka pa mpando wamawilo nkuyamba kuyenda ndi chothandizira kuyenda, kenaka ndi ndodo kenaka kubwereranso kuntchito.

“Zolimbitsa thupi zomwe amachita pothandiza omwe anadwala stroko zimasonyeza kuti ngati mbali ina ya ubongo yawonongeka, mbali zina za ubongo zikhoza kuyamba kugwira ntchito imene mbali yowonongekayo inali kuchita. Cholinga cha chithandizochi ndicho kupangitsa mbali zimene sizinkagwira ntchito imeneyo kuti ziyambe kugwira ntchitoyo ndi kuti ubongo uzindikire zimenezo ndi kuzoloŵera,” anatero Weiner, Lee, ndi Bell omwe anafufuza za nkhaniyo. Komabe kuti achire pali zifukwa zinanso, monga mbali ya ubongo yomwe yawonongekayo ndi ukulu wa strokoyo, thanzi lake la munthuyo, chisamaliro cha kuchipatala ndiponso mmene ena amamlimbikitsira.

Chithandizo cha Banja ndi Mabwenzi

Erikka anali kuchita zolimbitsa thupi kwazaka zitatu, kuphunzira kuyenda ndi kugwiritsira ntchito dzanja lake lamanja kuti azitha kuchita zinthu mosadaliranso dzanja lamanzere lomwe linapuwala. Iye akulongosola chomwe chinamthandiza kupirira: “Makamaka nchifukwa chakuti mwamuna wanga ndi anzanga sananditaye. Chifukwa chozindikira kuti amandikonda ndinapeza mphamvu, ndipo pamene ankandiuza kuti ndisataye mtima, zimenezo zinandilimbikitsa.”

Apabanja amakhala othandiza kwambiri kuti wokondedwa wawo achire. Iwo ayenera kufunsira kwa madokotala ndi kuyang’anitsitsa kuti adziŵe chithandizo chonse choyenera kuchitidwa panyumba kuti zinthu zisabwererenso m’mbuyo pa kuwongokera komwe kunachitika kale. Kudekha, kukoma mtima, kukhala womvetsetsa zinthu, ndi chikondi zomwe apabanja ndi mabwenzi amasonyeza zimamlimbikitsa ndi kupereka mpata wabwino woti aphunzirenso kulankhula, kuŵerenga, ndiponso maluso ena a tsiku ndi tsiku.

Akumasamala kuti asachite ngati akumkakamiza kapenanso kumnyengerera konyanyitsa, John anagwira ntchito mwamphamvu kuthandiza mkazi wake Ellen kuchita maseŵera olimbitsa thupi ndi kutsata malamulo a ku chipatala. Iye akulongosola khama la banja lake kuti: “Sitinafune kulekerera Ellen kukhala wachisoni kwambiri. Nthaŵi zina tinkachita ngati tikumukakamiza kuchita zinthu, komabe tinkaona pomwe angathere ndipo tinkamthandiza. Iye sachedwa kukhumudwa, choncho ndimayesetsa kuti ndisamvutitse maganizo.”

Pamene Ellen ankaphunziranso kulankhula ndi chithandizo cha dokotala wodziŵa za kalankhulidwe, John anali kumthandiza. “Zinali zolimbikitsa kuchitira zinthu pamodzi, motero tinkaŵerengerana Baibulo mokweza, zimene zinamthandiza kumalankhulako bwino. Komanso, tinayamba kumachita nawo utumiki, popeza ndife a Mboni za Yehova ndipo tinkachita pang’onopang’ono poyambapo. Mwanjira imeneyi Ellen ankatha kuuzako ena chiyembekezo chathu chamtsogolo. Kwa Ellen, awa anali mankhwala paokha.” Pakutha kwa zaka zitatu, Ellen anali atawongokera kwambiri.

Chilimbikitso chomwe mabwenzi amapereka musachiderere popeza chikhoza kuthandiza kwambiri kuti wodwala stroko achire. Nyuzipepala ya zachipatala yotchedwa Stroke inanena kuti “chilimbikitso cha mabwenzi chinapezeka kuti chimapangitsa kuchira mwamsanga ndi kusintha mwamsanga pa kachitidwe ka zinthu, ngakhale kwa odwala amene anagwidwa stroko yamphamvu.”

Bernie anayamikira kwambiri chithandizo chimene anzake anampatsa. Iye akutikumbutsa kuti: “Nzolimbikitsa kwambiri anzako akamadzakuona. Mawu osonyeza kumvera chisoni ndi kukusamalira zimakupangitsa kulimba maganizo. Ngakhale kuti sikoyenera kuti wina azingonena za zomwe ukulephera kuchita, kunena za zomwe wayamba kuchitako bwino nkolimbikitsa kwambiri.” Kodi nchiyani chimene tonsefe tiyenera kuchita kuti tithandize omwe akuvutika ndipo akupirira nsautso yobwera ndi stroko? “Atengereni maluŵa kapena kambani nawo nkhani ya m’Malemba. Zimenezo zinandithandiza kwambiri,” Bernie akutero.

Melva, wachikulire yemwe anapulumuka stroko, anaziona kukhala zothandiza kuti mmodzi wa abale ake achikristu azipemphera naye pamodzi. Nayenso Gilbert anavomereza zimenezi, ananena kuti: “Zimasonyeza kuti mumamganiziradi wina ngati mupemphera naye.” Peter, yemwe stroko inampangitsa kuti asamaone bwino, amayamikira ngati ena akumvetsa zimene iye sangathe kuchita ndipo akumamuŵerengera.

Kuthandiza wina kupita ndi kubwera kuchipatala kumasonyeza chikondi. Kutsimikiza kuti nyumba ya wodwala stroko ndi yosamalika nkofunikanso. Iye angamagwe nthaŵi iliyonse ngati kuimirira kumamvuta. Mwachitsanzo, Gilbert, anayamikira kwambiri chithandizo cha anzake amene kuwonjezera pakumuchitira zinthu zina anamuikira chogwirira m’chipinda chosambira kuti azigwirira.

Kuphunzira Kuthandiza

Kusinthasintha kwakuti pena nkukondwa pena nkukhala odandaula ndiponso kukonda kwawo kulira nthaŵi zambiri kumakhala kokhumudwitsa kwa omwe anadwala stroko ndiponso kumakhala kosokoneza kwa omwe amazipenyawo popeza sazindikira choti achite. Komabe, mwa kuphunzira kukhala othandiza, mabwenzi akhoza kuthandiza kuteteza wodwala stroko kuti asaloŵerere nkukhala wodzipatula, zomwe nthaŵi zina zingachitike. Kaŵirikaŵiri khalidwe loliralira limachepako. Koma ngati alira, khalani chete ndipo musachokepo, ndi kumanena zomwe mukadakonda kumva zidakakhala kuti ndinu mukudwalayo.

Choposa apo, kulitsani chikondi chaumulungu kwa amene matenda awo awasintha umunthu wawo umene munawadziŵa nawo poyamba. Iwo amaona mmene inu zimakukhudzirani ndipo zimenezi zimakhudza mmene iwo azichitira kwa inu. Errika ananena kuti: “Sizidzathekanso kuti ndikhale monga mmene ndinalili kale. Koma aliyense sayenera kuyembekezera zotero kwa wodwala stroko. Achibale ndi mabwenzi ayenera kuphunzira kumakonda munthuyo monga mmene alili. Ngati atapenda bwino kwambiri za umunthu wake, adzapeza kuti khalidwe labwino lakale lija lidakalipo.”

Pamene munthu sakutha kulankhula ndipo anthu sakumumva zimene akunena, kudzilemekeza kwawo kumachepa kwambiri. Mwakuyesetsa kulankhula nawo, abwenzi ayenera kupangitsa omwe sakutha kulankhula bwino kuona kuti ndi anthu ofunika mwa kuyesetsa kulankhula nawo. Takashi anati: “Zomwe ndimaganiza ndi kulingalira mumtima sizinasinthe. Komabe, anthu amandithaŵa chifukwa sangathe kulankhulana nane bwinobwino. Zimandivuta kwambiri kuti ndilankhule ndi anthu, koma ngati wina abwera kudzalankhula nane, zimandilimbikitsa ndipo zimandisangalatsa kwambiri!”

Otsatiraŵa ndi malangizo othandiza kwa tonsefe omwe angatithandize kuchirikiza ndi kulimbikitsa omwe ali ndi vuto la kulankhula.

Kaŵirikaŵiri stroko siisokoneza nzeru za munthu. Ambiri mwa omwe anadwalapo stroko amakhalabe ndi nzeru, ngakhale kuti zomwe amanena zingakhale zovuta kumva. Osawalankhula mwachipongwe kapena kuchita nawo ngati mukulankhula ndi ana. Apatseni ulemu.

Mvetserani modekha. Iwo angafunikire nthaŵi kuti atsimikize zoti anene kapena kuti atchule liwu, kapena chiganizo chonse. Kumbukirani kuti munthu yemwe ali ndi chidwi chomvetsera sachita zinthu mothamangitsa.

Musamanamizire kuti mwamva pamene simunamve. Modekha nenani kuti: “Pepani. Kuoneka kuti sindinamvetse. Tikambiranenso nthaŵi ina.”

Lankhulani pang’onopang’ono ndipo momveka bwino ndi mawu aakulu bwino.

Nenani ziganizo zifupizifupi ndi mawu ozoloŵereka.

Funsani mafunso omwe angapangitse munthu kuyankha kuti inde kapena ayi ndipo limbikitsani kuti ayankhe. Dziŵani kuti mwina angakhale kuti sakumva mawu anu.

Yesetsani kuti pasakhale phokoso lina.

Kupirira, Pothandizidwa ndi Yehova Mwachikondi

Ngakhale kuti nzofunika kudziŵa chimene chinapangitsa stroko yanu, popeza zimenezi zimathandiza kuti muchitepo kanthu ndi kuchepetsa ngozi yodzadwalanso stroko mtsogolo, nkofunika kuthetsa mantha amene angabwerepo. Ellen anati: “Mawu a Mulungu apa Yesaya 41:10 amanditonthoza kwambiri. Pamenepo Iye anati: ‘Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.’ Yehova wakhaladi weniweni kwa ine, motero akumandipangitsa kusakhala ndi mantha.”

Baibulo limamthandizanso Anand kulimba mtima atathedwa nzeru: “Limandilimbikitsa kwambiri, popeza nthaŵi zonse linandipatsa nyonga ndi kunditsitsimula.” Vuto la Hiroyuki linali lakuti sankatha kupindula ndi Malemba popeza sankatha kusumika maganizo. Iye anatiuza kuti: “Ndimasangalala ndikamamvetsera mabuku a Baibulo akuŵerengedwa pa kaseti.”

Mtumwi Paulo ananena kuti: “Pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.” (2 Akorinto 12:10) Unali mzimu wa Yehova umene unathandiza Paulo kuchita zimene sakanatha kuchita pa iye yekha. Amene anapulumuka stroko nawonso akhoza kudalira pa Yehova kuti awalimbikitse mwauzimu. Erikka ananena kuti: “Pamene tili ndi thanzi ndipo timachita chilichonse ndi mphamvu yathu, sitimpatsa mpata waukulu Yehova kuti atithandize. Koma kupunduka kwanga kwandipangitsa kulimbitsa ubwenzi wanga ndi iye mwanjira yapadera.”

Opereka Chithandizo Alimbikitsidwa

Opereka chithandizo ayenera kulimbikitsidwa pantchito yawo yovutayi. Kodi nkuti kumene angapeze chithandizo? Malo amodzi ndiwo m’banja lawo. Aliyense m’banjamo ayenera kuthandizapo popereka chithandizo. Yoshiko ananena mmene ana ake aamuna amamlimbikitsira: “Ankamvetsera mavuto anga monga kuti ndi awo.” Am’banjamo ayenera kudziŵa bwino zambiri zomwe angathe ncholinga choti adziŵe momwe angasamalire wodwala strokoyo ndiponso mmene angachitire malinga nkusintha kwa umunthu wa wokondedwa wawoyo.

Kodi ndani winanso yemwe angapereke chithandizo? David ndi banja lake anapempha kuti abale awo auzimu mumpingo wa Mboni za Yehova awathandize pa mavuto a Victor: “Iwo anatithandizadi. Mosinthanasinthana amabwera kudzagona kunyumba kwathu kudikirira Victor usiku wonse m’malo mwa ife.”

Aliyense amene amasamalira wodwala ayenera kuona chikondi ndi chithandizo cha abale ake auzimu. Koma ena amaziona kukhala zovuta kuti apemphe thandizo. Haruko akunena kuti: “Nthaŵi zambiri amandiuza kuti: ‘Ngati pali kanthu ukufuna kuti tikuthandize, osalephera kutiuza.’ Koma ndikaona mmene aliyense alili wotangwanika, ndimalephera kupempha thandizo. Ndingakondwe ngati anthu angamandipatse thandizo mwanjira ina monga kumati: ‘Ndikhoza kukuthandizani kusesa. Ndi tsiku liti lomwe mungakonde?’ ‘Ndikhoza kukakugulirani zinthu, kodi zingakhale bwino nditabwera kunyumba kwanu tsopano?’”

Mkazi wa Kenji anagwidwa stroko; komabe Kenji ankatha kumpatsa mkazi wakeyo chisamaliro chomwe ankafunikira. Anapeza kuti mwa pemphero ankatha kutulira Yehova nkhaŵa zake. Kenaka, mkazi wake analeka kulankhula, ndiye zitatero, Kenji analibenso mzake woti nkulankhula naye. Koma ankaŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Iye anati: “Limandikumbutsa za chisamaliro cha Yehova kwa osweka mzimu, ndipo zimenezi zandithandiza kuti ndisapsinjike maganizo ndi kukhala wosungulumwa.”

Kudalira mzimu wa Yehova kukhoza kuthandiza pamene zikuoneka kuti malingaliro akutivuta. Yoshiko, amene akupirira kusintha kwa umunthu wa mwamuna wake ndi kukalipakalipa kobwera pambuyo pogwidwa ndi stroko, ananena kuti: “Nthaŵi zina ndimangoona ngati ndingokuwa ndi mawu anga onse. Zikafika pamenepo nthaŵi zonse ndimapemphera kwa Yehova, ndipo mzimu wake umandipatsa mtendere.” Pothokoza chifukwa cha kukhulupirika kwa Yehova kwa iye, salola kuti kanthu kena kasokoneze khalidwe lake lachikristu. Nthaŵi zonse amapezeka pamisonkhano yachikristu, amapita mu utumiki, ndipo amakhala ndi phunziro la Baibulo laumwini. Yoshiko ananena kuti: “Popeza ndimachita mbali yanga, ndidziŵa kuti Yehova sadzandisiya.”

Munthu atada nkhaŵa, nthaŵi zonse Yehova amakhala wokonzeka kumvetsera. Midori, yemwe mwamuna wake anadwalapo stroko, amatonthozedwa ndi mfundo yakuti, mophiphiritsira, Yehova waika misozi yake yonse yomwe wakhetsa ‘m’nsupa yake.’ (Salmo 56:8) Iye akukumbukira mawu a Yesu akuti: “Musadere nkhaŵa za maŵa.” Ndipo akunena kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti ndidikire mpaka dziko lapansi latsopano litafika.”—Mateyu 6:31-34.

Kupirira Zolepheretsa Zambiri

Nzoona kuti panyengo yawo yakuongokera, ena amachirako ndithu, koma ena zimangowongokera pang’ono chabe. Kodi chingathandize amene zimangowongokera pang’ono chabewo kuti angokhala mozoloŵera kuchita zomwe angathe nchiyani, ngakhale kuti zolepheretsazo zingakhale zoŵaŵa ndi zosatha?

Bernie, yemwe sathanso kuyenda chifukwa cha stroko, akuyankha kuti: “Kukhala kwanga ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha m’paradaiso yemwe akudzayo padziko lapansi ndiponso pemphero kwa Atate wanga wakumwamba, Yehova, ndizo zinandithandiza kulolera ndi mtima wofatsa kuchita zokha zomwe ndingathe.”

Chiyembekezo chomwecho chinathandiza Erikka ndi mwamuna wake Georg, kuti alolere kumangochita zokhazo zomwe angathe komabe nkumasangalala ndi moyo. Georg akunena kuti: “Tili ndi malonjezo a Mulungu kuti adzachiritsa anthu tsiku lina. Motero sitilingaliranso kwambiri za kulumalako. Nzoona, timachitabe zonse zomwe tingathe kuthandiza Erikka kuti akhale wathanzi. Koma munthu ukhoza kuphunzira kumakhala nkumalingalira zinthu zina zothandiza ngakhale minofu ya m’thupi lako siigwira ntchito bwino.”—Yesaya 33:24; 35:5, 6; Chivumbulutso 21:4.

Pamene kuchira kwanu nkosalongosoka kwenikweni, thandizo la achibale ndi mabwenzi limakhala lofunika kwambiri. Akhoza kuthandiza wodwalayo kupirira kufikira itakwana nthaŵi ya Mulungu yochiritsa matenda onse.

Kuzindikira kuti mtsogolo zinthu zidzawakhalira bwino odwala stroko ndi mabanja awo pamene onse adzachira kumawathandiza kumaona zochitika za tsiku limodzi palokha. Motero iwo angayembekeze kuti adzachira pa kuvutika kwawo konse m’dziko latsopano la Mulungu lomwe libwera posachedwa. (Yeremiya 29:11; 2 Petro 3:13) Padakali pano, onse amene amayang’ana kwa Yehova akhoza kukhala ndi chikhulupiriro kuti ngakhale tsopano iye adzawathandiza ndi kuwalimbikitsa kupirira zovuta zomwe amakumana nazo chifukwa cha kupunduka kwawo kochitika ndi stroko.—Salmo 33:22; 55:22.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

A m’banja ndi mabwenzi akhoza kuthandiza wovutikayo kuti apirire kufikira itakwana nthaŵi yomwe Mulungu adzachiritsa odwala onse

[Bokosi/Chithunzi patsamba 10]

Mmene Tingapewere Stroko

“NJIRA yabwino koposa yolimbanirana ndi stroko ndiyo kuyesayesa kuipewa,” akutero Dr. David Levine. Ndipo chinthu choyamba chomwe chimapangitsa stroko ndicho matenda a BP.

BP mwa anthu ambiri ingaletsedwe mwa kudya chakudya chokhala ndi potassium wambiri ndi mchere pang’ono, mafuta ndi ma cholesterol pang’ono. Kuchepetsako kamwedwe ka zoledzeretsa nakonso kungakhale kofunika. Kuchita maseŵera olimbitsa thupi nthaŵi zonse mogwirizana ndi usinkhu ndiponso mphamvu zanu kungathandize kuchepetsako thupi lanu ndipo zotsatira zake zikhoza kukhala kuchepetsako kuthamanga kwa magazi. Muyeneranso kumwa mankhwala—mopatsidwa malangizo ndi dokotala, popeza pali mankhwala amitundu yambiri.

Matenda a mitsempha yotchedwa Carotid artery imene imapita kumutu amachepetsa mtsempha womwe umatengera magazi ku ubongo ndipo ndicho chopangitsa chachikulu cha stroko. Malinga ndi mmene watsekekera, zingakhale bwino kuchita opaleshoni yotchedwa carotid endarterectomy kuti atsegule mitsempha yotsekekayo. Kufufuza kwasonyeza kuti anthu amene anali kusonyeza zizindikiro zakuti mitsempha yawo itsekeka ndipo inalidi pafupi kwambiri kutsekeka anachira atawachita opaleshoni pamodzi ndi kumwa mankhwala ena. Komabe, pakhoza kukhala mavuto ena obwera chifukwa cha opaleshoni, motero muyenera kuzilingalira bwino.

Matenda a mtima akhoza kukuikani pangozi kwambiri yodwala stroko. Atrial fibrillation (kugunda molakwika kwa mtima), kumene kukhoza kupangitsa magazi kuundana ndi kuyenda kupita ku ubongo, kukhoza kuchizidwa ndi mankhwala osungunula magazi. Matenda ena a mtima angafunikire opaleshoni ndi mankhwala kuti mpata wogwidwa stroko uchepe. Matenda ashuga amapangitsa anthu ambiri kugwidwa stroko, motero kuwapewa kumathandiza kumaletsa stroko.

Zizindikiro zooneka kwa kanthaŵi kochepa zotchedwa kuti transient ischemic attacks, TIAs, ndi chenjezo loonekeratu lakuti stroko ichitika. Onetsetsani kuti musazinyalanyaze. Kaonaneni ndi dokotala wanu, ndipo thetsani zopangitsazo, popeza zizindikiro za TIA zimawonjezera ngozi yodwala stroko.

Moyo wathanzi, ndiponso kakhalidwe kabwino zikhoza kuthandiza kwambiri kupewa stroko. Kudya chakudya cha magulu atatu ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi ndiponso kuchepetsa kumwa zakumwa zoledzeretsa ndi kulekeratu kusuta fodya zikhoza kuthandiza mitsempha kukhala yabwino ndipo mwina kungathandize ngakhale yomwe inali yowonongeka kuti ikhaleko bwino. Malinga nkufufuza kosiyanasiyana, kudya zipatso ndi ndiwo zamasamba ndi zakudya zina za m’gulu la chimanga kwathandiza kuchepetsa ngozi yodwala stroko.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena