Mwana Atchedwa Wosauka
M’MUDZI waung’ono wa mu Afirika, munthu wotchedwa kuti Okot ndi mkazi wake, Matina, anasangalala pamene mwana wawo woyamba, wamkazi, anabadwa. Achibale ndi mabwenzi anayenda kupita ku mudzi umene amakhalawo kukapereka mphatso ndiponso mafuno abwino akuti mwanayo adzakhale ndi moyo wautali ndiponso wachimwemwe.
Banja limeneli linkakhala movutika kwambiri. Ankalima kamunda kakang’ono, ndipo nyumba yawo mmene Matina anaberekeramo mwanayo, inali yanjerwa zosawotcha, yofoleredwa ndi udzu. Analingalira zogwira ntchito mwakhama kuti mwana wawo woyambayo asadzavutike monga mmene anachitira iwo. Pofuna kumakumbukira cholinga chawochi, anamutcha mwana wawo wamkaziyo Acan, kutanthauza kuti “Ndine Wosauka.”
Kodi Acan ali ndi tsogolo lotani? Ngati adzakhala monga mmene anthu ambiri m’dzikomo amakhalira, ndiye kuti sadzaphunzira kuŵerenga ndi kulemba. Akati adzapeze ntchito atadzakula, azidzalandira ndalama zoposa pang’ono $190 pachaka. Ndipo m’dzikomo, anthu amakhala ndi moyo pafupifupi zaka 42 basi.
Vuto la Acan si lachilendo. Pa anthu pafupifupi 6 biliyoni okhala padziko lapansi, pafupifupi 1.3 biliyoni amapeza ndalama zosakwana $370 pachaka. M’maiko olemera pa avareji amapeza $21,598. Tsiku ndi tsiku, chiŵerengero cha anthu osauka chimawonjezereka ndi 67,000, pafupifupi 25 miliyoni chaka chilichonse. Ambiri amapezeka m’maiko otukuka kumene—mu Afirika, Asia, ndi ku Latin America. Koma ngakhale m’maiko olemera, muli anthu osauka mwa apo ndi apo. Ndipo anthu 7 mwa 10 osauka kwambiri pa dziko ndi akazi.
Anthu ambiri sangathe kupewa umphaŵi wadzaoneni. Amalephera kupeza zinthu zofunika kwambiri pa moyo wawo—chakudya, zovala, ndi nyumba. Amakhala mosasangalala, monyozeka, osaphunzira, ndiponso osakhala ndi thanzi labwino. Bungwe la World Health Organization limati: “Umphaŵi umavutitsa kwambiri munthu m’moyo wake wonse, kuyambira atangobadwa kufikira panthaŵi yoikidwa m’manda. Umayendera pamodzi ndi matenda akupha ndi oŵaŵa kwambiri kuzunza moyo wa onse ogwidwa nawo.”
Koma kodi sizoona kuti kakhalidwe m’maiko otukuka kumene kakupita patsogolo? M’maiko ena, nzoonadi. Mu ena ambiri, ayi. Magazini onena za chitukuko otchedwa Choices ananena zakuti “osauka ali pafupi kufanana ndi olemera” ndi ‘nthanthi yoopsa.’ M’malo mwake, anati: “Zoona zenizeni nzakuti tikukhala m’dziko limene muli kusiyana kwakukulu pazachuma, pakati pa maiko ndiponso mkati mwamaiko.”
Kodi umphaŵi udzapitiriza kuvutitsa anthu kwa nthaŵi zonse? M’nkhani ziŵiri zotsatira, Galamukani! ikupenda nkhani yovutayi ndi kusonyeza mmene umphaŵi udzathere.