Kodi Moyo Wopanda Matenda ndi Maloto Chabe?
KODI munayamba mwadwalapo kwambiri kapena anakuchitanipo opaleshoni yaikulu? Ngati zimenezi zinakuchitikiramponi, nzachionekere kuti tsopano mumayamikira moyo kwambiri. Koma mulimonse mmene thanzi lanu lingakhalire, kodi mumakhulupirira kuti nzotheka kukhala ndi thanzi langwiro? Izi zingaoneke zosatheka chifukwa chakuti pali matenda ambiri ofooketsa monga kansa kapena matenda a mtima. Ndithudi, ambiri a ife timadwala nthaŵi ndi nthaŵi. Komabe, kukhala ndi moyo wosadwala nkomwe si maloto chabe.
Munthu analengedwa kuti azisangalala ndi moyo wathanzi, osati kumavutika ndi matenda ndi imfa. Motero, pofuna kuthetsa matenda ndi imfa, Yehova anapereka maziko a moyo wathanzi langwiro ndi moyo wosatha mwa nsembe ya dipo ya Kristu Yesu. “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Amene adzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu sadzavutika ndi kudwaladwala kapena ukalamba. Popeza zidzakhala motero, nanga matenda adzapita kuti?
Mpumulo ku Matenda
Chitsanzo timachipeza panjira imene Yesu ankachiritsira odwala. Za machiritso amenewo zinanenedwa motere: “Akhungu alandira kuona kwawo, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphaŵi ulalikidwa uthenga wabwino.” (Mateyu 11:3-5) Inde onse opunduka amene anamfikira Yesu “anachiritsidwa.” (Mateyu 14:36) Zotsatira zake, “khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziŵalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.”—Mateyu 15:31.
Zoonadi, ngakhale kuti palibe aliyense lerolino amene angachiritse motero, tingathe kukhala ndi chikhulupiriro kuti pansi pa ulamuliro wa Mulungu anthu adzafika ku ungwiro, adzachiritsidwa matenda awo onse akuthupi ndi amalingaliro. Lonjezo la Mulungu linalembedwa pa Chivumbulutso 21:3, 4: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”
Lingalirani za dziko lapansi mmene mulibe chifukwa chokhalira ndi indasitale yopanga mankhwala, zipatala, opaleshoni kapena kulandira mankhwala! Kuwonjezera apo, m’Paradaiso wobwezeretsedwa, kupsinjika maganizo ndiponso kuzungulira mutu zidzakhala zinthu zakale. Moyo udzakhala wosangalatsadi, ndipo chimwemwe chidzakhala khalidwe la nthaŵi zonse. Ndithudi, mphamvu yopanda malire ya Mulungu idzapangitsa kudzibwezeretsa kwa thupi kuyamba kugwira ntchito bwino, ndipo mapindu a nsembe ya dipo adzachotsa zotsatirapo za uchimo zomwe zimatifooketsa. “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
Ndi chiyembekezo chabwino chotani nanga—kumasangalala ndi thanzi langwiro lakuthupi ndi lauzimu pansi pa Ufumu wa Mulungu! Pamene mukukhala ndi moyo wabwino ndi wodzisamala tsopano lino, yembekezani madalitso omwe adzakhalako m’dziko latsopano la Mulungu. Yehova ‘akhutitse m’kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu’!—Salmo 103:5.