Kodi Thanzi Labwino Mungalipeze Motani?
MANKHWALA ndi nkhani ya tsiku ndi tsiku. Zimaoneka kuti pafupifupi bwenzi lililonse kapena wachinansi ali ndi mankhwala amene amakonda pamatenda alionse. Choncho nzomveka kuti anthu amakhala ndi chilakolako chofuna kumwa mankhwala paokha. Komabe, pali anthu amene “amafuna dokotala pokhapokha pamene zinthu zavuta kwambiri,” anatero dokotala wa ku Brazil. “Akhoza kukhala ndi zotupa pakhungu lawo zimene sizipola ngakhale kuti amwa mankhwala paokha kwa miyezi yambiri. Akapita kwa dokotala, amakapezeka ali ndi kansa imene akanachiritsidwa akanabwera poyamba pomwe.”
Popeza kuti kupimitsa mwamsanga kumapulumutsa miyoyo, kuchedwa kungakutayitseni zambiri. “Mayi wina wazaka 30 anachedwa kupita ku mwezi ndiponso ankamva kuŵaŵa m’mimba. Anamwa mankhwala ambiri oletsa kumva kuŵaŵa ndi oletsa kutupa payekha, ndipo kuŵaŵako kunacheperako,” anatero dokotala. “Koma patapita masiku atatu, anakomoka chifukwa cha kuchepa kwa magazi m’thupi ndipo mwamsanga anamtengera kuchipatala. Nthaŵi yomweyo ndinamchita opaleshoni ndi kupeza kuti anali ndi mimba yomwe inakhala malo oipa, mu Fallopian tube. Iye anapulumuka panthaŵi yake!”
Mayi wina wachitsikana ku Sao Paulo anaganiza kuti analibe magazi okwana m’thupi, koma matenda ake anali kufooka kwakukulu kwa impso yake. Popeza anachedwa kupita kuchipatala, kunapezeka kuti njira yokha yomthandizira ndi kuchotsa impso yakeyo ndi kuikamo ina. Dokotalayo anamaliza nkunena kuti: “Kaŵirikaŵiri wodwala amakayikira zopita ku chipatala, ndiye amamwa mankhwala payekha kapena kufunsira kwa anthu osadziŵa za mankhwala, mapeto ake amakhala kudwala kwambiri.”
Ndithudi, sitifuna kunyalanyaza zizindikiro zimene thupi lathu limasonyeza. Komabe tingachitenji kuti tisamalingalire kwambiri za chipatala kapena kumwa mankhwala patokha? Kukhala ndi thanzi labwino kumalongosoledwa kuti ndi “kupeza bwino m’thupi, malingaliro, kapena maganizo” kapenanso monga “kukhala wopanda matenda mwakuthupi kapena chowawa chilichonse.” Chokondweretsa nchakuti masiku ano nzodziŵika kuti matenda ambiri akhoza kupewedwa. Malinga nkunena kwa Dr. Lewis Thomas, “m’malo mopangidwa osalimba, tili ndi matupi olimba modabwitsa, athanzi kwambiri.” Motero, m’malo ‘molola nkhaŵa ya thanzi kutipangitsa kudandaula mpaka kudwala,’ tiyenera kugwirizana ndi thupi ndi mphamvu zake zapadera zodzichiritsa lokha. Dokotala wodziŵa bwino ntchito yake akhoza kutithandiza.
Pamene Tiyenera Kufuna Chithandizo cha Dokotala
Dokotala wa ku Brazil anati tiyenera kupita kuchipatala “ngati zinthu monga kutentha kwa thupi, kuŵaŵa kwa mutu, kusanza, kapena kuŵaŵa kwa m’mimba, m’chifuwa, kapena m’chiuno sizikutha ndi mankhwala ndipo zikuyambiranso kaŵirikaŵiri popanda zifukwa zodziŵika bwino kapena ngati kuŵaŵako nkwakukulu koma kotha mwamsanga kapena kotenga nthaŵi yaitali kwambiri.” Dokotala wina anati tiyenera kupita kuchipatala nthaŵi iliyonse pamene tikukayikira zoti tichite ndi zizindikiro zamatenda kapena kuti zikusiyana ndi mmene zimakhalira nthaŵi zina. Iye anawonjeza kuti: “Pamene mwana wadwala, m’malo mompatsa okha mwanayo mankhwala, kaŵirikaŵiri makolo amasankha kupita kuchipatala.”
Koma kodi mankhwala ngofunika nthaŵi zonse? Kodi kugwiritsira ntchito mankhwala kungakudwalitseni m’malo mochiritsa? Kodi pamakhala zotsatirapo zina zoipa, monga zilonda m’mimba kapena kuwonongeka kwa chiwindi kapena impso? Kodi salimbana ndi mankhwala ena? “Ndi odwala oŵerengeka okha amene amaona mavuto awo modekha kapena kuwamvetsetsa bwino,” inatero The New Encyclopædia Britannica. Koma dokotala wabwino akhoza kutiuza kuti mankhwala onse akhoza kuvulaza ndi kuti pali mankhwala ochepa chabe omwe amagwiritsidwa ntchito makono omwe sawononga m’thupi. Mukadzagula mankhwala tsopano, mudzaŵerenge palebulo za chenjezo la ngozi yomwe ingakhalepo mutamwa mankhwalawo! Ngakhale mankhwala omwe amagulitsidwa m’masitolo akhoza kukuvulazani kapena kupha ngati agwiritsidwa ntchito molakwa kapena kwa nthaŵi yaitali.
Richard A. Knox analemba mu The Boston Globe za kufunika kwa kukhala ochenjera kuti: “Mamiliyoni omwe amadwala kuphwanya kwa m’maondo ndi akasukusuku amene masiku onse amamwa mankhwala oletsa kuŵaŵa ali pangozi ya kudwala mwadzidzidzi matenda a kutuluka magazi kwa mkati, malinga ndi lipoti la ofufuza pa Stanford University.” Iye anawonjezera kuti: “Ndiponso ofufuza amachenjeza kuti kumwera pamodzi mankhwala oletsa kuŵaŵa ndi mankhwala ochotsa asidi kapena mapilisi otsekereza asidi sizilepheretsa mavuto am’mimba ndipo mwina zingangopititsa patsogolo mavutowo.”
Nanga bwanji za kumwa mankhwala pawekha kofalaku? Dokotala ku Ribeirao Preto ku Brazil anati: “Ndilingalira kuti zingakhale bwino ngati aliyense angamasunge mankhwala pang’ono . . . . m’nyumba. Komabe mankhwala ameneŵa ayenera kugwiritsiridwa ntchito mwanzeru.” (Onani bokosi, patsamba 7.) Komanso, maphunziro a zaumoyo amathandiza kuti anthu akhale ndi moyo wabwino. Popeza kakhalidwe kamasiyana pakati pa munthu wina ndi mnzake, Galamukani! sinenapo kanthu kulimbikitsa mankhwala akutiakuti, za kuchiritsa kwakuti, kapena mankhwala azitsamba alionse.
Thanzi Labwino—Mungalipeze Motani?
“Madokotala abwino m’dziko lapansi ndi a Dokotala Chakudya Chabwino, a Dokotala Kupumula Koyenera, a Dokotala Chisangalalo,” analemba choncho Jonathan Swift, mlembi wa m’zaka za zana la 18. Ndithudi, chakudya cha magulu atatu, kupumula koyenera, ndi chimwemwe nzofunika pathanzi labwino. Poyerekezera ndi zimenezi, ngakhale kuti osatsa malonda anzeru amawanenerera, sitingagule thanzi mwa kungomwa mankhwala. “Kugwiritsira ntchito mankhwala mosayenera ndi kwangozi” kukhoza kuchepetsa chitetezo cha m’thupi.—Dicionário Terapêutico Guanabara.
Komabe, pozindikira kuti tili ndi udindo wosankha mmene tizikhalira ndi kupewa kumwa mankhwala mosayenerera, kusuta, kumwa moŵa mwauchidakwa, ndi kudzipanikiza kwambiri, tikhoza kuchita zambiri kuwongolera thanzi lathu. Marian, amene ali ndi zaka za m’ma 60 ndipo watumikira monga mmishonale kwa nthaŵi yaitali ku Brazil anati: “Ndakhala ndi thanzi labwino mwa kudya zakudya zosiyanasiyana zopatsa thanzi.” Iye analongosolanso kuti: “Ndimakonda kudzuka mmamawa, choncho kugona mwamsanga nkofunika.” Sitiyenera kunyalanyaza kuchita zinthu mwanzeru ndi kukhala ndi makhalidwe abwino, ngakhalenso kupita kukapimidwa nthaŵi ndi nthaŵi ndi kukambitsirana kwabwino ndi dokotala wodziŵa ntchito yake amene amathandiza banja lathu.
Ngakhale kuti amafunabe kukhala ndi thanzi labwino, Marian ali tcheru kusanyalanyaza kapena kudera nkhaŵa kwambiri za thanzi lakelo. Iye anati: “Ndimapempheranso kwa Yehova kuti andithandize pamene ndikufuna kuchita chilichonse chokhudza thanzi langa, kuti ndichite zomwe zingakhale zothandiza kwa nthaŵi yaitali osati kuti ndithere nthaŵi yambiri ndi ndalama kuyesayesa kuwongolera thanzi langa.” Iye anawonjezera kunena kuti: “Popeza kukhala wotangwanika ndi ntchito nchinthu chofunika, ndimapemphera kuti Mulungu andithandize kuti ndizisamala mmene ndimagwiritsira ntchito nthaŵi ndi mphamvu yanga, kuti ndisamadzipanikize mosayenerera ndiponso kuti ndisamapambanitse.”
Kuti tikhaledi achimwemwe, sitinganyalanyaze za mtsogolo. Ngakhale kuti tingakhale ndi thanzi labwino tsopano, matenda, zoŵaŵa, kuvutika, ndiye kenaka kumwalira zidzachitikabe. Kodi pali chiyembekezo chilichonse chakuti tidzakhala ndi moyo wopanda matenda?
[Bokosi patsamba 6]
Ubwino wa Kudzisamalira Koyenera
Mbali yaikulu thanzi lanu limadalira pa zimene mumadya ndi kumwa. Ngati mutayesera kuyendetsa galimoto mutathira madzi m’petulo kapena kuthiramo shuga, posapita nthaŵi mudzaononga injini. Chimodzimodzinso ngati mungamadye zakudya ndi zakumwa zosapatsa thanzi, simudzakhala ndi thanzi labwino. Zili monga zomwe zimachitika ndi kompyuta. Ngati mulembamo zolakwika, iyo idzapereka mayankho olakwika.
Dr. Melanie Mintzer, profesa wa mankhwala akumwa panyumba, analongosola kuti: “Pali mitundu itatu ya odwala: omwe amapita kuchipatala chifukwa cha zinthu zomwe akanatha kudzithandiza okha panyumba, omwe amapita kuchipatala panthaŵi yoyenera, ndi omwe sapita kuchipatala ngakhale pamene anafunikira kutero. A m’gulu loyambalo kaŵirikaŵiri amatayitsa nthaŵi madokotala ndi kudzitayiranso nthaŵi ndi ndalama zawo. A m’gulu lachitatu amaika miyoyo yawo pangozi mwa kuchedwa kukaonana ndi dokotala. Madokotala amati kukanakhala bwino anthu ambiri akadakhala m’gulu lapakatilo.”
“Njira zisanu ndi ziŵiri zokhalira ndi thanzi loyenera ndi: kudya ndi kumwa zamagulu atatu, kupanga maseŵera olimbitsa thupi nthaŵi zonse, osasuta fodya, muzipumula mokwanira, yesetsani kusadzipanikiza ndi zochita, pitirizani kukondana ndi anzanu, ndiponso yesetsani kuchita zinthu mwanzeru kupewa zomwe zingakudwalitseni kapena kukuvulazani.”—Before You Call the Doctor—Safe, Effective Self-Care for Over 300 Medical Problems, yolembedwa ndi Anne Simons, M.D., Bobbie Hasselbring, ndi Michael Castleman.
[Bokosi patsamba 7]
Bokosi la Mankhwala la Panyumba
“Kwayerekezeredwa kuti pafupifupi 90 peresenti ya zizindikiro za matenda—kuphwanya m’thupi, kupweteka, zotupatupa, ndi zizindikiro zina zakuti sukupeza bwino kapena uli ndi matenda—zomwe anthu athanzi amazimva amangozinyalanyaza osauza wina. . . . Kaŵirikaŵiri amagwiritsira ntchito mankhwala a mwamsanga, monga mibulu iŵiri ya asipulini pofuna kuthetsa kuŵaŵa kwa mutu.”
“Chimapangitsa kuti zimenezi zitheke ndi bokosi la mankhwala la panyumba. Limathandiza kuti pasakhale maulendo osayenera odya ndalama zambiri opita kwa dokotala kapena kuchipatala.”—Complete Home Medical Guide, lolembedwa pa Columbia University College of Physicians and Surgeons.
Buku lomwelonso limalimbikitsa kuti ndi bwino kuti m’bokosi la mankhwala la panyumba muzikhalanso mapulasitala, mabandeji a tizibowotizibowo, thonje, mankhwala odzola osiyanasiyana, mankhwala ophera mabakiteriya, masizasi, chida chopimira kutentha kwa thupi (thermometer ya mkamwa), ndi zinthu zina zofunika.
Pa mankhwala, bukulo limalimbikitsa kukhala ndi mapilisi oletsa kutentha ndi kuphwanya kwa thupi, mankhwala ochotsa asidi, mankhwala a chifuwa, ma antihistamine ndi decongestant, mankhwala othandiza ukadzimbidwa, mankhwala oletsa kutsegula m’mimba.
[Bokosi patsamba 8]
Chenjezo
“Ngakhale kuti ma OTC [mankhwala omwe mumagula kusitolo] safunikira kuti dokotala achite kukulemberani, iwo ndi mankhwala enieni. Monga mankhwala a kuchipatala, ena mwa iwo safunikira kumwera pamodzi ndi a mtundu wina kapena pamodzi ndi zakudya zina kapena moŵa. Monga mankhwala ena onse, ena akhoza kupangitsa mavuto ena ambiri kapena akhoza kusanduka chizoloŵezi kumangomwa mankhwalawo. Ndipo nthaŵi zina mankhwala ogula kusitolo asamaloŵe m’malo kupita kuchipatala.
“Komabe, ambiri ndi abwino ndipo othandiza . . . Amathandiza kwambiri.”—Using Medicines Wisely.
[Zithunzi patsamba 7]
Kumbukirani kuti palibe mankhwala azitsamba kapena achizungu amene alibe zovuta zilizonse
1. Mosungira mankhwala mwa ogulitsa wamba
2. Wogulitsa mankhwala pabwalo
3. Matumba a mankhwala azitsamba