Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 4/8 tsamba 12-14
  • Thanzi Langwiro kwa Onse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Thanzi Langwiro kwa Onse
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chochititsa Chachikulu
  • Njira Yopulumukira
  • Thanzi Langwiro Lidzakhalapodi
  • Kodi Moyo Wopanda Matenda ndi Maloto Chabe?
    Galamukani!—1998
  • Dipo la Kristu Njira ya Mulungu ya Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Yesu Kristu—Kodi Anatumidwa ndi Mulungu?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Thanzi Labwino kwa Onse—Lifika Posachedwapa!
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 4/8 tsamba 12-14

Thanzi Langwiro kwa Onse

MOFANANA ndi kakhalidwe, malo, ndi zipatala, kaumbidwe ka thupi lathu kamayambukiranso thanzi lathu. Kaumbidwe kameneko kamachititsidwa ndi chibadwa ndi matenda amene tingakhale nawo pambuyo pake chifukwa cha kukhala ndi matendawo m’majini.

“Thupi limene mumaloŵa nalo m’dziko,” dokotala wina akutero, “ndilo limene limasonyeza makamaka ngati mudzakhala ndi thanzi labwino, ndi zaka zambiri, kapena ngati mudzakhala ndi moyo nkomwe.”

Matenda a mutu, kulimba minofu, minyewa yokumbudzuka, mafupa osalimba, kudwala mtima, ndi ena, zilibe kanthu kuti tinawalandira motani, amatikumbutsa masiku onse kuti thanzi lathu limayambukiridwa moipa ndi thupi ndi maganizo osakhala bwino. Kodi chochititsa matenda ofala ameneŵa chachikulu nchiyani?

Chochititsa Chachikulu

Dokotala wina wotchedwa Luka wa m’zaka za zana loyamba C.E. anayankha funso limeneli m’nkhani youziridwa yonena za Yesu Kristu imene analemba. Tsiku lina, Luka analemba motero, anthu anabweretsa munthu wina wamanjenje kwa Yesu kuti amchiritse. Yesu anati kwa wamanjenjeyo: “Machimo ako akhululukidwa.” Ndiyeno, kuti Yesu asonyeze kuti analidi ndi mphamvu ya kukhululukira machimo, analamula wamanjenjeyo nati: “Tauka, nusenze kama wako numuke kunyumba kwako.” Munthuyo anatero! Chifukwa chake, “chizizwo chinagwira anthu onse” amene anaona kuchiritsa kumeneko, ndipo “analemekeza Mulungu.”—Luka 5:17-26.

Kodi Yesu analankhula za tchimo liti? Yankho limatithandiza kumvetsetsa chifukwa chake timadwala, kukalamba, ndi kufa. Popeza kuti tili ndi chidaliro chakuti “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu,” tingayembekezere Baibulo kutiyankhira funsolo. (2 Timoteo 3:16; 2 Petro 1:21) Ilo limatiuza kuti munthu woyambayo, Adamu, analengedwa wangwiro. Kukhala kwake ndi thanzi labwino kunadalira pa kumvera Mlengi wake.

Komabe, Adamu anasankha kuswa lamulo la Mulungu. Mwa kusamvera ndi kupandukira dala Mlengi wake, iye anali kuchimwa. Chifukwa chake, anakhala wopanda ungwiro, wodwala, ndipo anafa m’kupita kwa nthaŵi. Chotero, uchimo ndiwo unachititsa kuti Adamu adwale ndi kufa.

Monga momwe makolo amapatsira matenda ena kwa ana awo chifukwa cha mmene malamulo a majini amagwirira ntchito, momwemonso Adamu anapatsira mbadwa zake, fuko la anthu, kupanda ungwiro ndi kudwala kotsatirapo. Motero, matenda onse alipo chifukwa cha uchimo woyambirira wa Adamu. (Genesis 2:17; 3:1-19; Aroma 5:12) Kodi pali njira yopulumukira?

Njira Yopulumukira

Kusintha kwa thanzi langwiro kukhala loipa kunachititsidwa ndi uchimo—kupandukira lamulo la Mulungu kwa Adamu. Kusintha thanzi loipa kukhalanso langwiro kungachitike kokha mwa kuchotsapo uchimo. (Aroma 5:18, 19) Motani? Munthu wina wangwiro, wofanana ndendende ndi Adamu pamene anali wangwiro, anayenera kupereka moyo wake nsembe monga dipo. Lamulo la Mulungu nlakuti “moyo kulipa moyo,” kutanthauza kuti, moyo udzaloŵa m’malo mwa moyo unzake.—Deuteronomo 19:21.

Komabe, panalibe ndi mmodzi yense mwa mbadwa za Adamu amene akanapereka dipo lotero. Motero, Yehova yekha mwachikondi anapereka Yesu Mwana wake monga munthu wangwiro kuti apereke moyo wake “dipo la anthu ambiri” kuti “tikhale ndi moyo mwa iye.”—Salmo 49:7; Mateyu 20:28; 1 Yohane 4:9.

Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anasonyeza kuti Atate wake, Yehova, anampatsa mphamvu ya kuchotsa machimo pamene anauza wamanjenje uja kuti, “machimo ako akhululukidwa,” munthu wochirayo napita kunyumba. Kaŵirikaŵiri Yesu anagwiritsira ntchito mphamvu imeneyi yochokera kwa Mulungu mwa kuchiritsa kamodzinkamodzi akhungu, ogontha, ndi ena ambiri odwala matenda osiyanasiyana.

Baibulo, ponena za machiritso ozizwitsa a Yesu ameneŵa, limati: “Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziŵalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, ndi opunduka ziŵalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya.” (Mateyu 15:30, 31) Kuukitsa akufa kumene Yesu anachita kunalinso kodabwitsa kwambiri. Baibulo limasimba za ziukiriro zingapo zimenezi.—Luka 7:11-16; 8:49-56; Yohane 11:14, 38-44.

Machiritso ozizwitsa ameneŵa amatitsimikizira kuti palibe nthenda iliyonse imene mphamvu ya Yesu ya kuchiritsa ingalephere. Kodi iye adzagwiritsiranso ntchito mphamvu yopatsidwa ndi Mulungu imeneyi? Kodi tingapindule nayo?

Thanzi Langwiro Lidzakhalapodi

Maulosi a Baibulo amasonyeza kuti Yesu wayamba kale kulamulira monga Mfumu m’boma lakumwamba la Mulungu. Mulungu wampatsa mphamvu ya kuchotsa maboma onse a anthu amene alipowa ndi kulamulira dziko lonse lapansi. (Salmo 110:1, 2; Danieli 2:44) Pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake lidzakwaniritsidwa: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Mu ulamuliro wa Ufumu wakumwamba umenewo, mbali ya chifuniro cha Mulungu pa dziko lapansi idzakhala kuwongolera kwambiri thanzi la banja la anthu.

Ndiyeno, mwakuthupi ndi mwauzimu, “maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba.” “Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24; 35:5, 6.

Mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu, thanzi langwiro lidzatanthauza kuti anthu sadzafa monga momwe timachitiramu. Mawu a Mulungu amalonjeza: “Yense wakukhulupirira iye [adzakhala] nawo moyo wosatha.” “Mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Yohane 3:16; Aroma 6:23) Inde, kalekale salmo louziridwa linalonjeza: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29) Ndiyeno, monga momwe Yesu anachitira pamene anali pa dziko lapansi, iye adzaukitsa akufa ndi kuwapatsa mpata wa kupindula ndi thanzi langwiro. Baibulo limalonjeza: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.”—Machitidwe 24:15.

Dziko lapansili lidzakhala lachonde mu ulamuliro wa Ufumuwo kotero kuti njala, imene imachititsanso thanzi loipa, sidzakhalaponso. Maulosi a Baibulo amatiuza: “Mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zawo, ndi nthaka idzapereka zipatso zake, ndipo adzakhazikika m’dziko mwawo.” (Ezekieli 34:27) “Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.” (Salmo 67:6) “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.” (Salmo 72:16) “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa.”—Yesaya 35:1.

Buku la ulosi lomaliza la Baibulo, pofotokoza mwachidule mkhalidwe umene udzakhalamo m’dziko latsopano la Mulungu, limati: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”—Chivumbulutso 21:4.

Kodi mukunena kuti, ‘Zimenezo nzovuta kukhulupirira’? Pamenepo, talingalirani zotsatirazi. Adamu asanachimwe, anali ndi thanzi langwiro. Talingalirani kuti kunali kotheka kwa munthu wina kulankhula naye panthaŵiyo ndi kumuuza kuti tsiku lina dziko lapansi likadzala ndi anthu omva zoŵaŵa, omadwala ndi omakalamba. Kodi simuganiza kuti zimenezo zikanamvuta Adamu kukhulupirira? Komabe, ndimmene zilili tsopano.

Mosiyana ndi zimenezi, thanzi langwiro lidzakhalapodi mu Ufumu wa Mulungu. Mawu a Yehova amatitsimikizira: “Mawu aŵa ali okhulupirika ndi oona.” (Chivumbulutso 21:5) Zimene Mulungu wanena kuti zidzachitika zidzachitikadi chifukwa chakuti “Mulungu sakhoza kunama.”—Ahebri 6:18.

Kodi muyenera kuchitanji tsopano kuti mudzalandire madalitso alinkudza ameneŵa? Njira ya kumoyo wosatha wa thanzi langwiro inasonyezedwa bwino lomwe ndi zimene Yesu ananena m’pemphero kwa Atate wake: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.

Pemphani kuti Mboni za Yehova zizichita nanu phunziro la Baibulo panyumba panu. Zidzakhala zokondwa kukuthandizani kuphunzira zambiri ponena za malonjezo a Mulungu abwino koposa. Ndiko kudzakhala kuyamba kwanu kuloŵa panjira yopita ku thanzi langwiro!

[Chithunzi patsamba 14]

M’dziko latsopano la Mulungu, anthu onse adzakhala ndi thanzi langwiro

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena