Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 8/8 tsamba 20-22
  • Pamene Zioneka Ngati Kuti Anthu Onse Akungokupenyetsetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Zioneka Ngati Kuti Anthu Onse Akungokupenyetsetsa
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhaŵa za Munthu Woopa Kucheza ndi Ena
  • Kodi Amachitanji Poyesa Kuthetsa Manthawo?
  • Kuthetsa Mantha Oopa Kucheza ndi Anthu
    Galamukani!—1998
  • Kuvutika ndi Mantha
    Galamukani!—1998
  • Kodi Malo Ochezera a pa Intaneti Akusokoneza Moyo Wanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Mungatani Kuti Muthandize Odwala Matenda Oda Nkhawa?
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 8/8 tsamba 20-22

Pamene Zioneka Ngati Kuti Anthu Onse Akungokupenyetsetsa

Jerry anazitcha zimenezi “chizunzo.” Iye anati: “Nthaŵi zonse ndikamaloŵa m’kalasi, ndinkatuluka thukuta kwambiri, mkamwa mwanga munkachita ngati mwadzaza thonje, ndipo sindinkaganizanso kuti nditha kulankhula—ngakhale ngati zimenezo zinali zofunika pamoyo wanga. Ndiye kenaka ndinkamva ngati kuti kutentha kwambiri kumeneku kukukwera mmanja ndi mmiyendo ndi kumaso kwanga ndiye thupi langa linkafiira kwambiri.”

JERRY amavutika ndi mantha a kuopa kucheza ndi anthu, vuto lomwe chizindikiro chake ndi kuopa kwambiri kuti ena azikuyang’ana zomwe ukuchita ndi kuchititsidwa manyazi pagulu. “Munthu amene amaopa kucheza ndi anthu amakhulupirira kuti onse akumyang’anitsitsa,” kanatero kabuku kofalitsidwa ndi bungwe la Anxiety Disorders Association of America. “Nkhaŵayo ikhoza kupangitsa kuti aoneke ngati wopanikizika kuphatikizapo zizindikiro zina monga, kugunda kwa mtima, kufooka, kupuma mofulumira, ndi kutuluka thukuta kwambiri.”

Ena akhoza kusuliza mantha omwe anthu oopa kucheza ndi ena ali nawo, akumati iwo ayenera kungodzilimbikitsa ndi kuwaiŵalako za manyazi awo ndi “kuyamba kumacheza ndi anthu.” Nzoona kuti mbali imodzi yothetsera mantha a kucheza ndi anthu ndiyo kulimbana ndi mantha anu. Komabe, pali kusiyana kwakukulu pakati pa manyazi ndi kuopa kucheza ndi anthu. “Mosiyana ndi manyazi wamba,” anatero Jerilyn Ross, “mantha oopa kucheza ndi anthu amakhala aakulu kwambiri mwakuti amasokoneza zochita zatsiku ndi tsiku, kuntchito, kusukulu, ndiponso paliponse pamene umachita zinthu ndi anthu ena.”

Kufufuza kumasonyeza kuti miyoyo ya anthu mamiliyoni imasokonezeka chifukwa cha kuopa kucheza ndi anthu.a Lingalirani za mantha ena amene amakhudzana ndi vuto lofoola limeneli.

Nkhaŵa za Munthu Woopa Kucheza ndi Ena

Kulankhula pagulu. Doug akukumbukira kuti ankaopa pamene ankalankhula nkhani yachidule kwa kagulu ka anthu akwawo. “Mwadzidzidzi ndinayamba kutuluka thukuta ndi kumva kuzizira,” iye anatero. “Mtima wanga unali kugunda kwambiri. Ndinali kunjenjemera. Ndinamva kukhosi kwanga ngati kuti kukutsekeka, zikumapangitsa kukhala zovuta kuti ndilankhule.” Inde pafupifupi munthu aliyense amanjenjemera akamalankhula pagulu. Koma munthu woopa kucheza ndi ena amachita mantha kwambiri, ndipo sasintha ngakhale kuti wakhala akuchita chinthu chimodzimodzicho kwa nthaŵi yaitali. Doug anafika pomaona ngakhale kulankhula wamba monga chinthu choopseza moyo wake.

Kudya pali anthu ena. Popeza anthu owopa kucheza ndi ena amakhulupirira kuti ena akuŵayang’anitsitsa, ngakhale kudya kwenikweniku kumakhala chinthu chovuta. Amadera nkhaŵa kuti manja awo azinjenjemera, kuti agwetsa zakudya kapena aziphonya pakamwa, mwina ngakhale kuti asanza. Manthawo amapangitsa kuti zimene akuganiza zichitikedi. Buku lakuti Dying of Embarrassment linati: “Pamene ukuopa kuti uchita china chake chochititsa manyazi, ndipo pamenenso umakhala ndi nkhaŵa kwambiri. Pamene ukhala ndi nkhaŵa kwambiri, ndipo mpamenenso mpata umakula wakuti uyambe kunjenjemera kapena kumatakataka. Vuto limeneli likhoza kukula mpaka kufika poti zingakuvuteni kuika chakudya kapena chakumwa pakamwa panu popanda kugwetsapo kapena kutayirapo pansi.”

Kulemba pamaso pa anthu ena. Poopa kuti mwina manja awo azinjenjemera kapena kuti anthu aŵaona akulemba zosaŵerengeka, anthu ambiri oopa kucheza ndi ena amamangika kwambiri pofuna kusaina cheke kapena ntchito ina iliyonse yolemba pomwe anthu akuŵaonerera. Mwachitsanzo, Sam anachita manyazi pamene womlemba ntchito ankafuna kuti iye azisaina buku la kuntchito pamaso pa alonda asanayambe ntchito tsiku lililonse. “Sindinkatha,” Sam anatero. “Dzanja langa linkanjenjemera kwambiri mwakuti ndinkachita kuligwira ndi dzanja linali kuti ndilembe pamzere ndipo zomwe ndinkalembazo zinali zosaŵerengeka.”

Kugwiritsira ntchito telefoni. Dr. John R. Marshall ananena kuti ambiri mwa odwala ake anavomereza kuti amapewa kugwiritsira ntchito telefoni nthaŵi zonse pamene kuli kotheka kutero. “Nkhaŵa yawo inali yakuti mwina satha kuyankha zolongosoka,” iye anatero. “Ena ankaopa kuti, chifukwa chakuti sakadziŵa chonena, angakhale chete kwambiri mochititsa manyazi ndipo pamene kukambitsiranako kuima, nkhaŵa idzapangitsa kuti mawu awo asinthe, nkumalankhula monjenjemera, kapena mokweza kwambiri. Ankaopa kuti mwina akhoza kumadodomadodoma, kuchita chibwibwi, kapena mwanjira ina yochititsa manyazi kusonyeza kuti ndi osokonezeka maganizo.”

Kukhalira pamodzi ndi ena. Anthu oopa kucheza ndi ena amawopa malo alionse amene angakhale ndi ena. Kaŵirikaŵiri, amaopa kuyang’anizana maso ndi maso ndi ena. “Anthu oopa kucheza ndi ena amadera nkhaŵa kuti kaya maso awo ayang’ane kuti ndiponso kodi achite chiyani ngati ena awayang’ana,” inatero The Harvard Mental Health Letter. “Iwo amaopa kuyang’anizana ndi ena chifukwa amadziona kuti sadziŵa kuti ndi nthaŵi iti pamene ayenera kuyang’anizana ndipo ndi nthaŵi iti ayenera kuyang’ana kwina. Iwo amalingalira kuti ena atanthauzira molakwa kuyang’ana kwawoko.”

Palinso mantha ena okhudzana ndi kuopa kucheza ndi anthu. Mwachitsanzo, ambiri amaopa kuloŵa m’zimbudzi za anthu onse. Ena amaopa kugula pamene wogulitsa akuwayang’anitsitsa. “Ndimalingalira za ine mwini kwambiri mwakuti sindiona chinthu chomwe ndikuchiyang’ana,” anatero mayi wina. “Nthaŵi zonse ndimayembekezera kapena kulingalira kuti munthu yemwe ali kukauntala anena kuti ndingonena chimene ndikufuna kuti ndi saŵatayire nthaŵi.”

Kodi Amachitanji Poyesa Kuthetsa Manthawo?

Anthu amene alibe vuto limeneli zimawavuta kumvetsa chimene chimavuta anthu oopa kucheza ndi ena. Munthu wina wovutika ndi mantha ameneŵa analongosola zomwe amakumana nazo monga “chinthu chochititsa manyazi kwambiri kuposa chilichonse chimene munthu wina angaganize!” Wina anavomera kuti: “Nthaŵi zonse ndimalingalira zodzipha.”

Mwachisoni, anthu ambiri omwe amaopa kucheza ndi ena amayamba kumwa moŵa ncholinga chofuna kuchepetsako nkhaŵa zawo.b Ngakhale kuti ungathandize pakanthaŵi kochepa, m’kupita kwa nthaŵi, kumwa kwambiri moŵa kumangowonjezera mavuto kwa wovutikayo. Dr. John R. Marshall anati: “Ambiri mwa odwala anga amene sanayambe amwapo pagulu akhala akuledzera ncholinga chakuti achotse mantha asanachite kanthu kapena mkati mwa zochitika zapagulu, zotsatira zake zimangokhala kuwonjezera kudzinyozetsa pamaso pa ena, chinthu chomwe amaopa kwambiricho.”

Mwinamwake njira yofala kwambiri imene anthu oopa kucheza ndi anzawo amatsata podzitetezera ndiyo kupewa. Inde, ambiri sayandikira pamene pakuchitika zimene amaopazo. “Ndimapewa chilichonse momwe ndingathere, mwina ngakhale kulankhula patelefoni,” anatero Lorraine wamanthayo. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, ambiri mwa ovutikawo amapeza kuti kupewa kumangowamanga ukapolo m’malo mowatetezera. “Pakapita nthaŵi,” anatero Lorraine, “kusungulumwa kumandifooketsa kwambiri.”

Kupewa kukhoza kukhala “msampha umene mwadzitchera nokha,” anachenjeza motero Jerilyn Ross. “Ndipo machitidwe alionse akupewa,” anaonjezera motero, “amapangitsa kuti msamphawo ukugwereni nthaŵi yotsatira kufikira kupewako kumakhala chizoloŵezi.” Anthu ena ovutika mwamtundu umenewu amakana akaitanidwa kuchakudya kapena amakana ntchito imene imakhudza kugwirira pamodzi ndi anthu. Zotsatira zake, saphunzira kulimbana ndi mantha awo ndi kuwagonjetsa. Monga mmene Dr. Richard Heimberg ananenera, “miyoyo yawo ndi yodzazidwa ndi zongoganiza kuti sadzaloledwa zimene sizimachitika ndiponso amalingalira kuti sangathe ntchito zina zomwe sanaziyesepo chifukwa chakuti amazipewa.”

Komabe pali nkhani yabwino kwa omwe amaopa kucheza ndi anzawo: Nkotheka kuchiritsidwa. Nzoona kuti, nkosatheka—mwina ngakhale kosafunika nkomwe—kuthetseratu nkhaŵa iliyonse imene munthu amakhala nayo. Komabe amene amavutika ndi mantha a kucheza ndi ena akhoza kuphunzira kuwalamulira, ndipo Baibulo lili ndi uphungu umene ungathandize.

[Mawu a M’munsi]

a Muyenera kuzindikira kuti pafupifupi aliyense amawopako anthu mwamtundu wina. Mwachitsanzo, anthu ambiri amada nkhaŵa akalingalira zolankhula pagulu. Komabe, kuti muzindikire kuti munthuyu amaopa kucheza ndi anthu ndi kwa okhawo amene mantha awo ali aakulu kwambiri kufika pakuti nkuŵalepheretsa kuchita zinthu molongosoka.

b Kufufuza kumasonyeza kuti anthu oopa kucheza ndi anzawo amamwa kwambiri moŵa ndi kuti pakati pa zidakwa pali anthu ambiri oopa kucheza ndi anzawo. Kodi chimayambirira nchiti? Amati mmodzi mwa zidakwa zitatu zilizonse anali ndi vuto lopanikizika maganizo kapena mtundu wina wa mantha ocheza ndi ena asanayambe kumwa.

[Zithunzi patsamba 21]

Kwa anthu oopa kucheza ndi ena, kuchitira pamodzi zinthu ndi ena ndi chinthu chovuta kwambiri

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena