Kuthetsa Mantha Oopa Kucheza ndi Anthu
“Chinthu chofunika kwambiri chimene anthu amantha ayenera kukumbukira nchakuti akhoza kuchira. Si chinthu chakuti ayenera kumangopitirizabe kuvutika nacho.”—Dr. Chris Sletten.
MOSANGALATSA, anthu ambiri amene ali ndi mantha oopa kucheza ndi ena athandizidwa kuthetsa nkhaŵa zawo ndipo mwina kutha kumakhala pagulu limene ankaliopa kwambiri kwa zaka zambiri. Ngati inu mumavutika ndi mantha oopa kucheza ndi anthu, tsimikizirani kuti nanunso mukhoza kuphunzira njira zothandiza zothetsera vuto limeneli. Kuti muchite zimenezi muyenera kudziŵa (1) zizindikiro zimene mumasonyeza (2) zikhulupiriro zimene muli nazo ponena za zinthu zimene mumaopa, ndipo (3) khalidwe limene mantha anuwo amapangitsa.
Mapulinsipulo a Baibulo akhoza kuthandiza. Nzoona kuti Mawu a Mulungu si buku la zamankhwala, ndiponso silitchulapo nkomwe mawu akuti “mantha oopa kucheza ndi anthu.” Komabe Baibulo likhoza kukuthandizani ‘kusunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira’ pamene mukulimbana ndi mantha anu.—Miyambo 3:21; Yesaya 48:17.
Kudziŵa Zizindikiro Zimene Mumasonyeza
Zizindikiro za kuopa anthu zimasiyana kwa munthu wina ndi mnzake. Kodi thupi lanu limachita bwanji pamene mukuyandikira malo amene mumaopa? Kodi manja anu amanjenjemera? Kodi mtima wanu umagunda kwambiri? Kodi m’mimba mumakuŵaŵani? Kodi mumatuluka thukuta kapena kutentha thupi, kapena mumauma mkamwa?
Kunena zoona, ndi chinthu chosasangalatsa kulingalira za kutuluka thukuta, kuchita chibwibwi, kapena kunjenjemera pamaso pa ena. Koma kukhala ndi nkhaŵa chifukwa cha zomwe mukulingalira kuti zitha kuchitika sikungathandize. Yesu anafunsa bwino kuti: “Ndani wa inu ndi kudera nkhaŵa angathe kuwonjezera pa msinkhu wake mkono umodzi?” (Mateyu 6:27; yerekezerani ndi Miyambo 12:25.) Ndithudi, kumangolingalira zomwe zimakuchitikirani ndiponso pa zimene ena angalingalire ponena za izo kukhoza kungopangitsa zinthu kuipiraipira. “Kulingalira kuti ena amaona kuti mukunjenjemera ndi mantha kumapangitsa anthu a mantha oopa kucheza ndi anthu kukhala ndi nkhaŵa kwambiri,” inatero The Harvard Mental Health Letter. “Amayamba kulingalira zotsatirapo zoipa ndi kuti sangapange zolongosoka—chiyembekezo chomwe chimapangitsa kuti mantha awonjezereke pamene akufika pamalo amene amaopawo.”
Mukhoza kuchepetsako zizindikiro zomwe mumasonyeza mwa kupuma pang’onopang’ono. (Onani bokosi lakuti “Samalani Kapumidwe Kanu!”) Komanso chinthu china chothandiza ndicho kupanga maseŵera olimbitsa thupi ndi kukhala omasuka thupi. (1 Timoteo 4:8) Mungafunikirenso kusintha khalidwe lanu. Mwachitsanzo, Baibulo limapereka uphungu wakuti: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja aŵiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:6) Motero onetsetsani kuti mukupumula mokwanira. Kuwonjezera apo, samalani za chakudya chanu. Musamaphonye chakudya kapena kudya panthaŵi zosakhazikitsidwa bwino. Zingakhale bwino kuchepetsa zakudya zokhala ndi caffeine, chifukwa zingathe kuyambitsa nkhaŵa.
Koposa zonse, khalani wofatsa mtima. (Mlaliki 7:8) Gulu lina la madokotala linati: “Mkupita kwa nthaŵi, mudzaona kuti ngakhale kuti nthaŵi zonse mumakhala ndi nkhaŵa pakakhala zochitika zina zochitikira pagulu, kukula kwa zizindikiro zomwe thupi lanu limasonyeza zidzacheperako ndithu. Chachikulu koposa, pamene mukuyesayesa, mudzakulitsa kudzidalira kwanu ndipo mudzakhala okonzekera bwino kukhala pa anthu amene mumaopa.”
Kupenda Zomwe Mumakhulupirira Chifukwa cha Mantha Anu
Kumanenedwa kuti simungamve kanthu kena m’thupi lanu ngati simunayambe mwakalingalira. Zimenezi zimaoneka kukhala zoona pankhani ya mantha oopa kucheza ndi anthu. Choncho, kuti muchepetse zizindikiro zomwe thupi lanu limasonyeza, muyenera kuona bwino za “malingaliro amene amakusokonezani” ndi kukuchititsani kukhala ndi mantha.—Salmo 94:19.
Akatswiri ena amati mantha oopa kucheza ndi anthu angokhala chabe kuopa kuti anthu anganyoze zimene ungachite. Mwachitsanzo, pamene mwasonkhana, munthu woopa kucheza ndi anthu akhoza kumadziuza kuti, ‘ndikuoneka wopusa. Anthu ayenera kuti akuzindikira kuti sindiyenera kukhala pano. Ndikhulupirira kuti aliyense akundinyoza.’ Munthu wina woopa kucheza ndi anthu wotchedwa Tracy anali ndi malingaliro ngati amenewo. Komabe, mkupita kwa nthaŵi anafufuza bwino zomwe ankakhulupirirazo. Anazindikira kuti anthu ali ndi zinthu zina zofunika zoti achite ndi nthaŵi yawo koposa kumalingalira za iye. “Ngakhale ngati nditanena zinazake zosasangalatsa,” Tracy anatero, “kodi nkoyenera kuti munthu wina andione monga wopanda pake chifukwa cha zimenezo?”
Monga Tracy, muyenera kupenda kalingaliridwe koipa kakuti zimene mukuganizazo zichitika—ndiponso kuti zikhala zoipa kwambiri—kuti ena pagulu akuonani ngati achabechabe. Kodi pali zifukwa zabwino zokhulupirira kuti anthu akukwiyirani ngati zimene mumaopazo zachitikadi? Ngakhale ngati ena atatero, kodi pali chifukwa chakuti inu mulingalire kuti simungathe kupirira vutolo? Kodi zolingalira za munthu wina muganiza zingasinthedi umunthu wanu? Baibulo limalangiza mwanzeru kuti: “Mawu onsetu onenedwa usawalabadire.”—Mlaliki 7:21.
Gulu lina la madokotala linalemba zotsatirazi ponena za anthu omwe amachita mantha kucheza ndi anzawo: “Vuto limakhalapo pamene anthu alingalira kwambiri za zovuta zomwe zimakhalapo mosalephereka pamoyo. Kulephera zinazake kungakhale kokhumudwitsa kwambiri. Kukhoza kukuŵaŵani mtima. Koma sikuyenera kukuŵaŵani mtima monyanyira. Si vuto lalikulu kwambiri kusiyapo ngati inu mwini mulikulitsa.”
Baibulo limatithandiza kuti ife eni tizidziona bwino mmene tilili. Ilo limati: “Timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri.” (Yakobo 3:2) Ndithudi, palibe amene sasonyezapo kulephera chifukwa cha kupanda ungwiro ndipo nthaŵi zina zimakhala zochititsa manyazi. Kuzindikira zimenezi kumatithandiza kuvomereza zolakwa za anzathu, ndipo kumalimbikitsa kuti ena azitha kumvetsa zomwe timachita. Mulimonse, Akristu amadziŵa kuti amene kuvomereza kapena kukana kwake kuli nkanthu ndiye Yehova Mulungu—ndipo iye sayang’anira zolakwa zathu.—Salmo 103:13, 14; 130:3.
Kudziŵa Mantha Anuwo ndi Kuthana Nawo
Kuti muthetse vuto la kuopa kucheza ndi anzanu mudzafunikira kulimbana ndi mantha anu. Poyamba, kuchita zimenezi kungakuopseni. Kufikira tsopano lino, mwina mwakhala mukupeŵa kukhala pagulu limene limakuopsani. Komabe mosakayikira, zimenezi zingangokulandani kudzidalira kwanu ndi kuwonjezera mantha anu. Ndi zifukwa zomveka bwino Baibulo limati: “Wopanduka afunafuna chifuniro chake, nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.”—Miyambo 18:1.
Mosemphana ndi zimenezo, kulimbana ndi mantha anu kukhoza kuchepetsa nkhaŵa zomwe muli nazo.a Dr. John R. Marshall anati: “Kaŵirikaŵiri timalimbikitsa odwala matenda a kusakonda kucheza ndi anzawo—makamaka amene mantha awo ali ocheperapo monga kuopa kulankhula pagulu—kuti ayenera kudzikakamiza kumachitapo kanthu m’mikhalidwe ndi m’mabungwe amene zochita zake zimafunikira kuchitira pamodzi ndi ena.”
Kulimbana ndi zinthu zomwe mumaziopa kudzakupangitsani kukhulupirira (1) kuti kulephera kuchita zinazake mochititsa manyazi sikuti nthaŵi zonse anthu ena adzakuonani monga opanda pake (2) kuti ngakhale ngati atakuonani monga opanda pake, sizitanthauza kuti mwalephereratu. Kumbukirani kuti muyenera kukhala odekha kuona mmene mungawongolere zinthu. Sikuti vutolo lidzatha tsiku limodzi, ndiponso si kwanzeru kulingalira kuti zizindikiro zonse zosonyeza mantha ocheza ndi anthu zidzatheratu. Malinga ndi Dr. Sally Winston, cholinga cha chithandizochi, sikuti nkuthetsa zizindikiro zomwe mumasonyeza, koma kukupangitsani kuti muziziona monga nkhani yaing’ono. Iye anati ngati mumaziona kuti sinkhani yaikulu, zimatha kapena kusintha.
Akristu ali ndi zifukwa zamphamvu zakuti athetsere mantha oopa kucheza ndi anthu. Ndithudi, iwo amauzidwa kuti ‘aganizirane wina ndi mnzake kuti afulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwawo pamodzi.’ (Ahebri 10:24, 25) Popeza ntchito ya Akristu imakhala yochitira zinthu pamodzi ndi ena, kulimbikira kwambiri kuthetsa mantha a kucheza ndi ena kukhoza kuthandiza kuti mupite patsogolo mwauzimu. (Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 2:42; 1 Atesalonika 5:14) Nenani nkhaniyo kwa Yehova Mulungu m’pemphero popeza iyeyo akhoza kukupatsani “ukulu woposa wamphamvu.” (2 Akorinto 4:7; 1 Yohane 5:14) Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuona moyenerera mmene ena amakuonerani ndi kukulitsa luso loyenera lakuchita zimene iye amafuna.
Kunena zoona, aliyense wokhala ndi mantha ameneŵa payekha ali ndi mavuto apadera, ndipo aliyense ali ndi zovuta zake zomwe ayenera kulimbana nazo ndiponso mphamvu zosiyana zothetsera mavutowo. Ena awongokera kwambiri mwa kugwiritsira ntchito mfundo zimene talongosolazi. Pali ena amene amafunikira chithandizo chowonjezereka. Mwachitsanzo, ena athandizidwa mwakumwa mankhwala.b Ena anafuna chithandizo cha katswiri wa za maganizo. Galamukani! siiyamikira kapena kulimbikitsa mankhwala amtundu wina uliwonse. Kaya Mkristu afuna mankhwala amtundu umenewo ayenera kusankha yekha. Komabe, ayenera kuchenjera kuonetsetsa kuti chithandizo chimene alandirecho sichikutsutsana ndi mapulinsipulo a Baibulo.
Anthu “Akumva Zomwezi Tizimva Ife”
Baibulo lingathe kulimbikitsa kwambiri, chifukwa lili ndi zitsanzo za anthu amene anagonjetsa zovuta zomwe anakumana nazo kuti achite zimene Mulungu ankafuna kwa iwo. Lingalirani za Eliya. Monga mmodzi wa aneneri oyambirira a Israyeli, anasonyeza kulimba mtima kumene munthu wamba sangasonyeze. Komabe, Baibulo limatitsimikizira kuti “Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife.” (Yakobo 5:17) Sikuti iyeyo sankachitako mantha kaya kukhala ndi nkhaŵa nthaŵi zina.—1 Mafumu 19:1-4.
Mtumwi Paulo, Mkristu, anapita ku Korinto “mofooka ndi m’mantha ndi monthunthumira mwambiri,” mwachionekere chifukwa cha kudzikayikira paluso lake. Ndipo anakumana ndi anthu ochulukirapo amene anamuona monga wopanda pake. Ndipo, ena mwa otsutsa ananena zotere za Paulo: “Maonekedwe a thupi lake ngofooka, ndi mawu ake ngachabe.” Komabe palibe chomwe chimasonyeza kuti Paulo analolera malingaliro olakwika a ena kuti akhudze mmene iye mwini ankadzionera kapena mmene amaonera maluso ake.—1 Akorinto 2:3-5; 2 Akorinto 10:10.
Mose analibe chikhulupiriro chakuti angathe kuonana ndi Farao, akumanena kuti ndi “wa mkamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.” (Eksodo 4:10) Ngakhale pamene Yehova Mulungu analonjeza kuti akamthandiza, Mose anapempha kuti: “Ayi, Ambuye, tumizani wina wake.” (Eksodo 4:13 Today’s English Version) Mose sanazindikire luso limene anali nalo, koma Yehova ankadziŵa. Iye anaona kuti Mose anali ndi nzeru ndi nyonga yochitira ntchito imeneyo. Komabe, mwachikondi Yehova anampatsa Mose womthandiza. Sanakakamize Mose kukaonana ndi Farao ali yekha.—Eksodo 4:14, 15.
Nayenso Yeremiya ndi chitsanzo chabwino pankhani imeneyi. Pamene anatumidwa monga mneneri wa Mulungu, munthu wachinyamata ameneyu anayankha kuti: ‘Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithayi kunena pakuti ndili mwana.” Yeremiya analibe mphamvu yakuti agwirire ntchito imeneyi. Komabe Yehova anali naye. Anathandiza Yeremiya kukhala “mudzi walinga, mzati wachitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse.”—Yeremiya 1:6, 18, 19.
Chotero ngati mantha ndi nkhaŵa zimakuvutani, musalingalire kuti mulibe chikhulupiriro kapena kuti Yehova wakukanani. M’malo mwake, “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”—Salmo 34:18.
Ndithudi, zitsanzo za m’Baibulo zimene tatchula pamwambapo zimasonyeza kuti ngakhale amuna okhala ndi chikhulupiriro chachikulu ankavutika ndi kudzimva kuti ndi osakwanira. Ngakhale kuti sankafuna zoposa zomwe aliyense payekha angathe, Yehova anathandiza Eliya, Paulo, Mose, ndi Yeremiya kukwanitsa kuchita zambiri koposa zomwe ankayembekezera. Popeza Yehova “adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife pfumbi,” tsimikizirani kuti angathe kukuchitirani zofananazo.—Salmo 103:14.
[Mawu a M’munsi]
a Madokotala ena amati ngati muona kuti kuchita zimenezi nkovuta, kaziyesezani ngati kuti mukuchita zimene mumaziwopazo. Yerekezerani mukumalingalira zinthuzo mwadongosolo lake bwinobwino. Nkhaŵa yanu ikhoza kuyambika; koma pitirizani kumadzikumbutsa kuti zitheka kuti ena satsutsa zimene mufuna kuchita, kapena ngati angatsutse, sizikhala zoipa kwambiri kusiyana ndi zimene mukuganiza ndipo lingalirani mapeto a zochitikazo ngati kuti zatha mmene mumafunira.
b Amene afuna kumwa mankhwala ayenera kuonetsetsa kusiyana pakati pa kuipa ndi ubwino wake. Ayeneranso kuona ngati mantha awo ndi akulu mwakuti nkoyenera kumwa mankhwala. Akatswiri ambiri amaona kuti mankhwala angagwire ntchito bwino ngati mutaŵaphatikiza ndi chithandizo chokhudza mantha ndi khalidwe la munthuyo.
[Bokosi patsamba 24]
Samalani Kapumidwe Kanu!
ANTHU ena oopa kucheza ndi anzawo amatha kuchepetsa zizindikiro za manthawo mwa kusamala kapumidwe kawo. Poyamba, zimenezi zingaoneke zachilendo. Chifukwa chake nchakuti aliyense amadziŵa kupuma! Koma akatswiri amati anthu ambiri omwe ali ndi nkhaŵa samapuma bwino. Kaŵirikaŵiri amapuma mosakoka mpweya wambiri, ndipo amatero mofulumira, kapena amatulutsa mpweya wambiri m’chifuwa.
Yeserani kukoka mpweya ndi kuutulutsa pang’onopang’ono. Kupumira m’mphuno osati mkamwa kukhoza kupangitsa zimenezi kukhala zosavuta. Komanso, phunzirani kupuma kuchokera pansi pa chifuŵa chifukwa kupuma kochokera chapamwambamwamba kukhoza kungowonjezera mpata wakuti muyambe kupuma mofulumira kwambiri. Kuti muyese ngati mungathe zimenezi, taimirirani ndiye, ikani dzanja lanu pamimba panu ndi linalo pakati pa chifuwa chanu. Pamene mukupuma, onani ndi dzanja liti limene likuyenda kwambiri. Ngati ndi dzanja lanu lomwe lili pachifuŵa, muyenera kuzoloŵera kupuma kuchokera pansi m’chifuwa mwanu.
Nzoonadi kuti simungapume kuchokera pansi pa chifuwa chanu nthaŵi zonse. (Mungapume kuchokera pansi pa chifuwa nthaŵi zinayi kwa imodzi imene mudzapuma kuchokera pamwamba pa chifuwa, komanso nthaŵi zina zimasintha.) Choncho, mpofunika chenjezo: Amene ali ndi vuto losatha lokhudza ziwalo zawo zopumira—monga matenda a emphysema kapena phumi—ayenera kuwonana kaye ndi dokotala wawo asanatengere kapumidwe kalikonse.
[Bokosi patsamba 25]
Pamene Mantha Amapanikiza Munthu
KWA anthu ena omwe amaopa kucheza ndi anzawo, amakhala ndi nkhaŵa kwambiri mwakuti amapanikizika. Mantha adzidzidzi ndiponso ofooketsa ameneŵa amachititsa munthu kupuma nkhwezakweza, kumva ngati akufuna kukomoka, ndi kuganiza kuti wadwala matenda a kuleka kugwira ntchito kwa mtima.
Akatswiri amati kuli bwino kusalimbana ndi kupanikizika kumeneku. M’malo mwake, amalangiza wovutikayo ‘kungopirira’ nkhaŵayo kufikira itatha. “Simungaithetse ikayambika,” anatero Jerilyn Ross. “Iyenera kuchitika kufikira itatha. Mungodziŵa kuti imapangitsadi nthumanzi, koma siyoopsa. Ikutha.”
Melvin Green, mkulu wa bungwe lothandiza anthu a mantha oopa malo atetete opanda kanthu otchedwa agoraphobia, akuyerekezera zimenezi ndi funde laling’ono limene munthu angaone likuyandikira kugombe. “Izi zimaimira mmene mumamvera nkhaŵazo zikayamba,” iye anatero. “Pamene funde likuyandikira mtunda limanka nlikulirakulira. Izi zimaimira mmeme nkhaŵa yanu imakulira. Posapita nthaŵi fundelo limakula kwambiri. Kenaka limayamba kuchepa kufikira litatha pagombe. Zimenezi zimaimira kuyambika ndi kutha kwa nkhaŵayi.” Green anati ovutikawo sayenera kulimbana ndi mmene akumvera koma kungoleka kufikira zitatha.
[Zithunzi patsamba 24]
Kuti muchepetse nkhaŵa zanu, samalani za chakudya chanu muzichita maseŵera olimbitsa thupi nthaŵi zonse, ndiponso muzipumula mokwanira
[Chithunzi patsamba 26]
Yehova anathandiza anthu monga Mose kuti akwanitse kuchita zambiri mu utumiki wawo kuposa zomwe ayenera kuti ankayembekezera