Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 8/8 tsamba 19
  • Kuvutika ndi Mantha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuvutika ndi Mantha
  • Galamukani!—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Kuthetsa Mantha Oopa Kucheza ndi Anthu
    Galamukani!—1998
  • Kodi Mungatani Kuti Muthandize Odwala Matenda Oda Nkhawa?
    Galamukani!—2012
  • Pamene Zioneka Ngati Kuti Anthu Onse Akungokupenyetsetsa
    Galamukani!—1998
  • Muzimutulira Yehova Nkhawa Zanu Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 8/8 tsamba 19

Kuvutika ndi Mantha

“Kaŵirikaŵiri mantha akhala nkhani yoseketsa. Koma ‘sizoseketsa’ konse.”—Jerilyn Ross, mkulu wa malo operekera chithandizo kwa odwala matenda a nkhaŵa

MAWUWO akuti “mantha” amatanthauza kuopa kwambiri chinthu china, kaya kuopa chinthu chomwe palibe, kapena zinthu zomwe sizinachitike, kapena kumangodzimva wamantha basi. Koma kungonena tanthauzo lake chabe sikungathandize kuti mumvetse mmene munthu amaopera ndi mmene amakhalira wosungulumwa, zimene zimadziŵikitsa mantha ameneŵa. Raeann Dumont, amene wakhala akuthandiza anthu amantha kwazaka makumi aŵiri, anati: “Anthu amantha amaopa kupita m’malo osiyanasiyana mwakuti amangokhala panyumba, mwina angamakhale ndi nkhaŵa zosatha nthaŵi zonse, mwina angamathetse nkhaŵa zawo mwa kumwa moŵa umene ungamawonjezerenso mavuto.”

Mantha amaikidwa m’gulu la matenda otchedwa kuti matenda a nkhaŵa.a Akuti 12 peresenti ya chiŵerengero cha anthu akuluakulu mu United States adzavutikapo ndi mantha panthaŵi ina m’moyo wawo. Ambiri a iwo amavutika mwachinsinsi kwazaka zambiri. Malinga nkunena kwa Anxiety Disorders Association of America, “Mwatsoka, pafupifupi anthu atatu mwa anayi alionse amene ali ndi mantha salandira chithandizo. Anthu ambiri amene ali ndi mantha safuna kupeza chithandizo chifukwa amachita manyazi. Ena sadziwa chimene chikuŵavuta kapena sadziŵa kumene angapeze chithandizo, ndipo ena amaopa chithandizo chenichenicho.”

Pali mantha osiyanasiyana amitundu mazanamazana, koma akatswiri amawagaŵa m’magulu atatu. Mantha ochepa a simple phobia amachitika chifukwa cha zinthu wamba kapena mmene mkhalidwe ulili, monga kachilombo, nyama, kukwera ndege, ndi kukhala m’malo otsekeredwa. Mantha a Agoraphobia nthaŵi zonse amachitika pakakhala kuti wapanikizika ndi zina zake. Wovutikayo amaopa kuti apanikizikenso ndi kanthu kena mwakuti amapewa kupita malo onse kumene poyamba mavutowo anachitikira. Chizindikiro cha mantha a kucheza ndi anthu chimakhala kuopa kuchititsidwa manyazi pagulu, monga kulankhula pagulu.

Lingalirani chimodzi mwa zinthu zitatu zimenezi—mantha oopa kucheza ndi anthu. The Washingtonian inati: “Ngakhale mutaphatikiza pamodzi mantha ochepa ena onse monga kuopa njoka kapena kukwera ndege, safanana ndi mantha oopa kucheza ndi anthu pakuvutitsa.” Kodi izi nzoonadi? Ngati zilidi choncho, nchifukwa ninji? Tiyeni tione.

[Mawu a M’munsi]

a Matenda ena a nkhaŵa ndi monga kupanikizika maganizo, obsessive-compulsive disorder, kuopa masoka akale, ndi matenda ena a nkhaŵa. Kuti mumve zambiri, onani Galamukani! yachingelezi ya February 8, 1996, “Compulsive Behavior—Does It Control Your Life?” ndi June 8, 1996, “Coping With Panic Attacks.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena