Pamene Anthu Amakhalanso ndi Chiyembekezo ndi Chikondi
MAKOLO, aphunzitsi, ndi ena onse amene amagwira ntchito zokhudza ana amazindikira kuti kaya iwo kapena anawo kapena wina aliyense sangathe kusintha dzikoli. Pali vuto limene lili ngati kusefukira kwa nyanja yomwe siphwetseka. Komabe, pali zambiri zimene tonsefe tingachite kupangitsa kuti achinyamata akhale achimwemwe, athanzipo, ndipo ozoloŵera kukhala m’dzikoli.
Popeza kuti kuteteza kuli bwino kuposa kuchiritsa, makolo ayenera kulingalira bwino ponena za mmene khalidwe lawo ndi zimene amakonda zingakhudzire khalidwe la ana awo. Kuŵasonyeza kuti amaŵakonda panyumba kumaŵapangitsa kudzimva kuti ndi otetezereka, chinthu chimene chingathandize kuti asamalingalire zodzipha. Chinthu chimodzi chimene achinyamata amasoŵa ndicho kukhala ndi wina wake amene angamawamvetsere. Ngati makolo samvetsera, mwina munthu wina wamakhalidwe oipa ndiye adzawamvetsera.
Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani kwa makolo lerolino? Pezani nthaŵi yokhala ndi ana anu pamene iwo akufuna—pamene adakali aang’ono. M’mabanja ambiri zimenezi si chinthu choti nkuchitika mosavuta. Amayesetsa kuti apangitse zinthu kuyenda bwino panyumba mwanjira yokagwira ntchito makolo onse aŵiri. Amene asonyeza kufunitsitsa akwanitsa kusiya kuchita zinthu zina ncholinga choti azikhala ndi mpata wocheza ndi ana awo kaŵirikaŵiri apindula kuona ana awo zinthu zikuwayendera bwino. Komabe, monga momwe tanenera kale, nthaŵi zina ngakhale makolo atayesetsa, mavuto akulu okhudza ana adzabukabe.
Mabwenzi ndi Achikulire ena Angathe Kuthandiza
Nkhondo, kugwirira chigololo, ndi kuvutitsa achinyamata kumalira kuti makolo amene amasamalira ana agwirirepo ntchito mwakhama kuti awatetezere. Ana amene asokonezeka maganizo chifukwa cha zinthu zoipa zimene anakumana nazo sangasinthe ngakhale pali zoyesayesa zofuna kuwathandiza. Pamafunikira kutayirapo nthaŵi yambiri ndiponso kukhala wakhama. Kunena zoona si chanzeru ndiponso si chikondi kuwaderera kapena kuŵataya. Kodi sitingayese kuwasonyeza kukoma mtima ndi chikondi moolowa manja kuti tithandize amene ali pangozi?
Sikuti ndi makolo okha komanso mabwenzi ngakhale achibale ayenera kukhala maso kuona makhalidwe mwa achinyamata amene angasonyeze kufooka ndi kusonyeza kukhala okhumudwa. (Onani bokosi lakuti “Pafunikira Odziŵa Bwino za Vutolo Kuti Athandize,” patsamba 8.) Ngati asonyeza zizindikiro zimenezo, fulumirani kuwamvetsera. Ngati kungatheke, yesetsani kupangitsa achinyamatawo kulankhula kuti akuuzeni vuto lawo mwakuwafunsa mafunso osonyeza kukoma mtima kuti muwasonyeze kuti ndinu bwenzi lenileni. Mabwenzi odalirika ndiponso achibale angathe kuthandiza makolo kulimbana nazo pamene zinthu zafika povuta; komabe, ayenera kusamala kuti asatenge udindo wa makolo. Kaŵirikaŵiri achinyamata akamafuna kudzipha kumakhala kuli kuthedwa nzeru ndiye amakhala akupempha kusamalidwa—kuti makolo awasamale.
Mphatso yabwino koposa imene wina aliyense angapatse achinyamata ndiyo chiyembekezo cha m’tsogolo mwachimwemwe, chinthu chomwe chingawalimbikitse kuti apitirize kukhala ndi moyo. Achinyamata ambiri afika pozindikira kuti zimene Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa kudzakhala dongosolo ladziko labwinopo nzoona.
Kupulumutsidwa Pamene Anafuna Kudzipha
Ku Japan, mayi wina wachitsikana amene nthaŵi zambiri ankalingalira zodzipha ananena zoterezi: “Ndakhala ndikulingalira kuchita zimenezi kwa nthaŵi yaitali. Pamene ndinali mwana wamng’ono, munthu wina amene ndinkamkhulupirira anandigona mokakamiza. . . . kale lonseli, ndakhala ndikulemba makalata onena kuti ‘ndikufuna kufa’ mwakuti sindikumbukira kuti ndi angati. Tsopano ndinakhala wa Mboni za Yehova, ndipo tsopano ndimatumikira monga mlaliki wanthaŵi zonse, komabe malingaliro ameneŵa amandibwererabe nthaŵi zambiri. . . . Koma Yehova wandilola kukhalabe moyo, ndipo amaoneka ngati kuti amandiuza ndi mawu otsitsa kuti, ‘Pitiriza kukhala ndi moyo.’”
Mtsikana wina wazaka 15 wa ku Russia anati: “Pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi zitatu, ndinayamba kumadzimva ngati kuti palibe ankandifuna. Makolo anga sankapeza nthaŵi nkomwe yoti nkulankhula nane, ndipo ndinkayesetsa kuthetsa mavuto anga ndekha. Ndinkangokhala kwandekha. Ndinali kukangana ndi makolo anga nthaŵi zonse. Kenaka ndinayamba kulingalira zodzipha. Ndine wosangalala kuti ndinakumana ndi Mboni za Yehova!”
Cathy wa ku Australia amene tsopano ali m’zaka zake za m’ma 30 anapereka ndemanga zolimbikitsa zosonyeza kuti kutaya mtima kukhoza kusintha nkukhala chiyembekezo chabwino: “Nthaŵi zonse ndinkalingalira njira zosiyanasiyana zodziphera ndipo potsiriza ndinayesera kudzipha. Ndinkafuna kuthaŵa dziko lokhumudwitsali, lokwiyitsa ndi lopanda phindu. Chifukwa cha kupanikizika maganizo zinali zovuta kuthetsa mavuto amene ndinali nawo. Motero kudzipha ndiko kunkaoneka kukhala njira yothetsera mavuto panthaŵiyo.
“Pamene ndinamva zakuti dziko likhoza kukhala paradaiso, lamtendere, kuti onse adzakhala ndi moyo wachimwemwe, ndinalakalaka dziko lotero. Komabe zinkaoneka ngati maloto osatheka. Koma kenaka pang’onopang’ono ndinayamba kumvetsetsa mmene Yehova amaonera moyo ndipo mmene amaonera aliyense wa ife kukhala wofunika. Ndinayamba kukhulupirira kuti tiyenera kuyembekezera zam’tsogolo. Potsiriza, ndinapeza njira yothetsera mavutowo. Koma kuti ndiwaiwale chinali chinthu chovuta kwambiri. Nthaŵi zina ndinkakhala wopanikizika maganizo kwambiri, ndipo ndinkakhala wosokonezeka maganizo kosaneneka. Komabe, kupanga Yehova Mulungu kukhala wofunika kwambiri m’moyo wanga kunandipangitsa kuti ndiyandikire kwambiri kwa iye ndipo ndinkaona kukhala wotetezereka. Ndimayamikira Yehova chifukwa cha zonse zimene wandichitira.”
Sikudzakhalanso Munthu Kufa Adakali Wachinyamata
Mwakuphunzira Baibulo, wachinyamata angafike pakuzindikira kuti kutsogolo kuli chinthu china chabwino choyenera kuyembekezera—chimene Paulo, mtumwi wachikristu amachitcha kuti “moyo weniweniwo.” Iye analangiza wachinyamata wotchedwa Timoteo kuti: “Lamulira iwo achuma . . . asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo; kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino . . . nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.”—1 Timoteo 6:17-19.
Uphungu wa Paulo umasonyeza kuti tiyenera kumadera nkhaŵa za anthu ena, kuwathandiza kuti akhale ndi chiyembekezo cholimba ponena zamtsogolo. “Moyo weniweniwo” ndi umene Yehova walonjeza m’dziko lake lapansi latsopano la “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.”—2 Petro 3:13.
Achinyamata ambiri amene kale ankaika moyo wawo pachiswe anafika pomvetsetsa kuti kumwa mankhwala osokoneza bongo ndi chiwerewere ndi zinthu zopanda pake zonga njira yaitali ndi yolemetsa yomka nayo kuimfa, koma chidule chake nkukhala kungodzipha. Iwo anazindikira kuti dziko lino, ndi nkhondo zake, chidani, khalidwe lovutitsa ena, ndi kusoŵa chikondi zidzatha posachedwapa. Iwo aphunzira kuti dongosolo lino lazinthu silingakonzekenso. Iwo amakhulupirira kwambiri kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo chinthu chokha chodalirika choti nkuyembekeza, chifukwa udzabweretsa dziko latsopano mmene osati achinyamata okha koma anthu onse omvera sadzafanso—Inde, sadzalakalakanso kufa.—Chivumbulutso 21:1-4.
[Bokosi patsamba 8]
Pafunikira Odziŵa Bwino za Vutolo Kuti Athandize
The American Medical Association Encyclopedia of Medicine imati “oposa 90 peresenti mwa amene amadzipha amatero chifukwa cha matenda amalingaliro.” Limandandalika matenda otsatiraŵa monga kupanikizika maganizo (pafupifupi 15 peresenti), matenda a schizophrenia (pafupifupi 10 peresenti), uchidakwa (pafupifupi 7 peresenti), matenda a kusakonda kucheza ndi ena (pafupifupi 5 peresenti), ndi mtundu wina wa matenda a neurosis (ochepera pa 5 peresenti). Iyo imapereka uphungu uwu: “Aliyense amene wapezeka kuti anali kuyesayesa kudzipha muyenera kumuyang’anira bwino. Kuyambira 20 peresenti kufika 30 peresenti ya amene ankafuna kudzipha amayeseranso kutero mkati mwachaka chomwecho.” Dr. Jan Fawcett analemba kuti: “Oposa 50 peresenti ya amene amadzipha [ku United States] ndi anthu amene sanakumanepo ndi dokotala wazamaganizo.” Ndipo maumboni ena amati: “Chithandizo chogwira mtima kwambiri nchakuti munthuyo akaonane ndi katswiri wodziŵa zamaganizo mwamsanga kuti amthandize kuthetsa kupanikizika maganizo kumene ali nako.”