Sanaleme
Pa October 5, 1995, Matt Tapio, wazaka 14, anachitidwa opaleshoni yochotsa chotupa paubongo wake. Chotupacho chinali chachikulu. Opaleshoniyo inali yoyamba, mwa maopaleshoni ena ambiri oti achitidwe m’zaka zina ziŵiri ndi theka. Ndiyeno anayamba kupatsidwa mankhwala a chemotherapy ndi njira zina zochiritsira monga ya radiation.
Matt ankakhala ku Michigan, U.S.A., nkumenenso ankaloŵa sukulu ndi misonkhano yachikristu. Ankagwiritsira ntchito mipata yolankhula ndi aphunzitsi ake ndi am’kalasi anzake ponena za zikhulupiriro zake ngakhalenso kugwira ntchito yakufikira ena mu utumiki wapoyera. Pamasiku onse amene iye anali kugonekedwa kaŵirikaŵiri m’chipatala—anatha miyezi 18 ya zaka ziŵiri ndi theka zotsirizira za moyo wake m’zipatala—onse amene anali kukumana nawo kumeneko anawagaŵira mazanamazana a zofalitsa zonena za Baibulo.
Nthaŵi zambiri zinkaoneka ngati kuti Matt sadzachira, koma nthaŵi iliyonse ankachira. Tsiku lina, popita kuchipatala, anakomoka ndipo analeka kupuma. Ndiyeno anayamba kumuuzira mpweya m’mphuno, kenaka anatsitsimuka. Pamene anatsitsimuka, anayamba kulira ndi kufuula akumati: “Ndichira basi! Ndichira basi! Sindingafe!” Anthu ankatero kuti chimene chinali kumthandiza Matt kukhala nthaŵi yaitali choncho chinali chifukwa chakuti ankakhulupirira Mulungu.
Pa January 13, 1996, Matt anakhutiritsa chikhumbo cha mtima wake pamene anabatizidwa posonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova Mulungu. Anambatizira padziŵe layekha, kuopera kuti angafalitse matenda. Patangotha masiku oŵerengeka, anabwereranso kuchipatala kukachitidwa opaleshoni inanso. Mu August, 1997, Matt ankasanza mosalekeza kwa milungu ingapo, koma anadzaleka atachitidwa opaleshoni inanso.
Komabe pazonsezo, Matt anangokhalabe munthu wanthabwala, namaseleula ndi adokotala ndi manesi. Iwowo sankadziŵa chifukwa chake iye anali wanthabwala modabwitsa choncho. Mmodzi mwa adokotalawo anamuuza kuti: “Matt, ineyo ndikanakhala iwe, ndikanaphimba bedi langa ndi nsalu, nkufunda mutu wanga, nkuuza aliyense kutuluka.”
Mu February 1998, Matt anabwerera kunyumba kuchokera kuchipatala imodzi mwa nthaŵi zotsirizira. Anali wachimwemwe kwambiri kuti anali moyo ndi kutinso anali kunyumba, moti atangoloŵa kumene pakhomo anati: “Ndakondwa kwambiri! Tiyeni tipemphere.” Ndiyeno anamlongosolera Yehova kuti anali ndi chimwemwe. Patatha miyezi iŵiri, pa April 19, potsirizira Matt anamwalira ndi kansa ija.
Zisanachitike zimenezo, Matt ankafunsidwa mafunso namamjambula mawu, ndipo tepiyo anaimvetsera pamsonkhano wa Mboni za Yehova pa Nyumba ya Ufumu ya kwawoko. Anafunsidwa kuti: “Ungatiuze chiyani enafe amene tili ndi thanzi labwinopo ponena za utumiki wathu ndi misonkhano yachikristu?”
Matt anayankha kuti: “Chitani zimene mungathe tsopano lino. . . . Simungadziŵe zimene zingachitike. . . . Koma kaya kudzachitikanji, musadzaleke kumchitira Yehova umboni.”