Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Ndingakhale Motani Wopanda Makolo?
“Makolo anga anasudzulana pamene ndinali ndi zaka zitatu, mlongo wanga ali ndi zaka zinayi. Tinakakhala ndi amayi khoti litagamula kuti amayi ndiwo atitenge anafe. Zimenezi zinachitika atalimbana ndithu m’khoti. Komabe, pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, ine ndi mlongo wanga tinakakhala ndi atate.”—Horacio.
PATATHA zaka zingapo, atate ake a Horacio ndi chibwenzi chawo anasamuka—kumsiya Horacio ndi mlongo wake. Horacio akukumbukira kuti: “Ndimo mmene pa usinkhu wazaka 18, ndinakhalira wamkulu m’banja lathu la anthu angapo, ineyo, mlongo wanga wazaka 19 ndi mlongo wanga wa mimba ina wazaka 12—amene anatsala nafe.”
Monga mmene nkhani yakumbuyoku inasonyezera, padziko lonse ana mamiliyoni ambiri alibe makolo.a Mofanana ndi Horacio, achinyamata ena asiyidwa. Komanso ena makolo awo anamwalira kapena analekana nawo chifukwa cha nkhondo kapena masoka achilengedwe. Mulimonse mmene zingakhalire, kukhala wopanda makolo ndi kovuta ndiponso kosautsa. Ndipo zingakupatseni ntchito yochuluka.
‘Adzandisamala Ndani?’
Mmene mungachitire ndi vuto limeneli zimadalira pa usinkhu wanu ndi mmene zinthu ziliri. Mwachionekere, zinthu zimakhala zovuta kwambiri ngati mudakali mwana. Ngakhale zili choncho, mwina muli ndi ena amene angakusamaleni. Mwinamwake amalume, azakhali, achimwene kapenanso achemwali anu akufuna kuti muzikakhala nawo.
Kusamalira ana ndi amayi amasiye ndi mbali ya kulambira kwa Mboni za Yehova. (Yakobo 1:27; 2:15-17) Ndipo nthaŵi zambiri, ena mumpingomo amathandizapo. Mwachitsanzo, Horacio ndi alongo ake anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anali kufika pamisonkhano yawo. Banja lachikristu limene anakumana nalo kumeneko linayamba kuwathandiza. “Ndikuyamika Yehova chifukwa cha chitsogozo ndi chisamaliro chake chachikondi cha tsiku ndi tsiku!” akutero Horacio. “Tinali ndi mwayi kwambiri wothandizidwa ndi banja lauzimu mumpingo limene munali anyamata a usinkhu wathu. Tingatero kuti anatileradi. Choncho, mosiyana ndi kale, tinaona ngati tili a m’banja lomwelo, limene tinalidalira.”
Komabe, si achinyamata onse amene ali ndi mwayi umenewu. Lipoti la United Nations Children’s Fund likuti: “Nthaŵi zina ana opanda owasamala amatengedwa ndi mabanja ena amene amakawazunza, kuwagwiritsa ntchito yopanda malipiro kapenanso yosawapatsa mpata wotukuka, kuwatuma kukachita uhule kapenanso kuwapanga akapolo.” Choncho ngati muli ndi wina amene akukusamalani bwino, muziyamika.
Kunena zoona, kukhala wopanda makolo ndi chinthu chopweteka kwambiri. Ndipo mwachibadwa mungaŵaŵidwe mtima posakhala nawo kuti akusamaleni. Kuuzidwa zochita ndi wachibale kapena mbale wanu wamkulu zingawonjezere mkwiyo wanu. Koma osathetsera mkwiyowo pa awo amene akukusamalani. Baibulo limati: “Muchenjere, mkwiyo ungakunyengeni muchite mnyozo . . . Chenjerani, musalunjike kumphulupulu.” (Yobu 36:18, 21) Kumbukirani mtsikana wa m’Baibulo wotchedwa Estere. Monga wamasiye, analeredwa ndi msuwani wake wamkulu, Moredekai. Ngakhale sanali kholo lake lombereka, Moredekai ‘adaika malamulo pa iye,’ amene anawamvera ngakhale pamene anali wachikulire! (Estere 2:7, 15, 20, NW) Khalani womvera, ndipo zidzathandiza kwambiri kuchepetsa mavuto ndi kupangitsa moyo wa aliyense m’banjamo kukhala wosavuta.
Udindo wa Banja
Ngati muli ndi mbale wanu wamkulu—kapena ngati inuyo ndiye wamkulu—mwina inu ndi abale anu mutha kukhala panokha. Mwinanso mungakhale mutu m’banjamo—udindo waukulu kwambiri! Komabe, m’mikhalidwe ngati imeneyi achinyamata ambiri achita ntchito yochititsa kaso polera abale awo.
Ndithudi, mungakhale ndi maganizo ena oipa. Komabe, kuganiza mofatsa kuti mumasamala abale anu ndipo mumawakonda kudzakuthandizani kukhala ndi maganizo abwino. Kuona ntchito yosamala iwo monga yopatsidwa ndi Mulungu kudzakuthandizaninso. Ndiponso, Akristu amalamulidwa kusamalira mbumba yawo. (1 Timoteo 5:8) Komabe ngakhale muyeseyese chotani kukhala amayi kapena atate wa abale anu, simungakhale makolo awo.
Si kwanzeru kuyembekezera kuti abale anu azikumverani monga anali kuchitira kwa makolo anu. Ndiponso, kungatenge nthaŵi yaitali kuti azoloŵere mkhalidwewu ndi kuyamba kukumverani. Chotero padakali pano, musakwiye. Peŵani “chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano.” Mwa zochita zanu, phunzitsani abale anu kukhala ‘okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha.’—Aefeso 4:31, 32.
Horacio akuvomereza kuti sanali kuchita bwino: “Nthaŵi zina ndinali kuwaletsa abale anga mopambanitsa. Kumbali ina, chinali chitetezo, ndipo tinasunga khalidwe labwino kwa Yehova.”
Kudzisamala Wekha
Ngati ulibe makolo okusamala, ndithudi kudzakhala kovuta kwambiri kudzisamala wekha mwakuthupi. Mwinamwake anthu achikulire mumpingo wachikristu angakuphunzitse iwe ndi abale ako, ngati uli nawo kuphika, kuyeretsa zinthu, ndi kusamalira zinthu za panyumba zimene ukufunika kudzisamalira. Koma kodi udzachita chiyani kuti upeze ndalama? Kapena sungachitire mwina koposa kupeza ntchito.
Komabe, ntchito ndi zosoŵa kwa achinyamata amene sanapite patali m’maphunziro, sanagwirepo ntchito, kapena alibe maluso a ntchito. Choncho ngati kungatheke kuti umalize maphunziro—kapena kupeza maphunziro owonjezereka a ntchito—n’kwanzeru kutero. Horacio akukumbukira kuti: “Ine ndi mlongo wanga wamkulu tinali kugwira ntchito kuti tithe kulipira sukulu yanga ndi ya mlongo wanga wa atate ena.” Ngati ukukhala m’dziko lomatukuka, uyenera kugwiritsa ntchito nzeru kuti upeze ntchito—Onani “Kudzipangira Ntchito m’Maiko Otukuka,” mu kope la Galamukani! ya November 8, 1994.
M’mayiko olemera kwambiri, kungakhale kotheka kupeza chithandizo cha ndalama kuchokera ku boma. Nthaŵi zambiri, pamakhala mabungwe a boma kapena a anthu amene cholinga chawo ndi kuthandiza ana amasiye kapena osiyidwa. Mwachitsanzo mabungwe ena angakuthandize kupeza chakudya kapena nyumba. Ndithudi, thandizo la ndalama lililonse limene ungalandire uyenera kuligwiritsa ntchito moyenera. “Ndalama zitchinjiriza,” limatero Baibulo. (Mlaliki 7:12) Ndalama mofulumira ‘zingamere mapiko ndi kuuluka,’ ngati susamala popanga bajeti ndi poigwiritsa ntchito.—Miyambo 23:4, 5.
Ngati wachikulire akukusamala, kupeza zinthu zina sikungakhale kovuta kwenikweni. Komabe, nthaŵi idzafika pamene udzafunikira kudzisamala wekha. Popeza ulibe makolo oti n’kukulimbikitsa pa maphunziro, pafunika khama kuti uike maganizo pa maphunziro. Langizo la mtumwi wachikristu Paulo kwa Timoteo lonena za kupita patsogolo kwauzimu lingagwirenso ntchito pa maphunziro akusukulu: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.” (1 Timoteo 4:15) Mwa kuchita zimenezi, udzawaonetsa chitsanzo chabwino kwa anthu okhala nawo pafupi komanso zidzakuthandiza.
Chofunika choposa zonse ndicho kusamalira zosoŵa zako zauzimu. Yesa kukhala ndi chizoloŵezi chabwino chochita zinthu zauzimu. (Afilipi 3:16) Mwachitsanzo, ndi chizoloŵezi cha mabanja a Mboni za Yehova kukambirana lemba la m’Baibulo tsiku ndi tsiku. Bwanji osapanga mbali imeneyi kukhala chizoloŵezi chakonso? Chizoloŵezi chophunzira Baibulo ndi chofika kumisonkhano yachikristu nthaŵi zonse chidzakuthandiza kukhala wolimba mwauzimu.—Ahebri 10:24, 25.
Kulimbana ndi Vutolo
N’zoona, kukhala wopanda makolo n’kovuta, komabe sizitanthauza kuti moyo udzakhala wamavuto okhaokha. Paola amene tsopano ali ndi zaka 20, mayi wake anamwalira pamene iye anali ndi zaka 6. Atate ake anamwalira pamene iye anali ndi zaka 10. Iye ndi abale ake anayi anapatsidwa nyumba ndi mayi wina wokoma mtima. Kodi moyo wake wakhala wachisoni chokhachokha? Ayi. Paola akuti: “Zoona banja lathu si lokwanira, koma timakhala ndi moyo wabwino. Komanso, chikondi chomwe tili nacho pakati pathu ndi cholimba kuposa cha m’mabanja ambiri.”
Mlongo wa Paola, Irene akuwonjezera kuti: “Ngakhale tilibe makolo, tili ofanana ndi achinyamata ena.” Kodi akuwauza chiyani awo amene ali mu mkhalidwe wofananawu? “Osaganiza kuti muli ndi tsoka.” Ndiponso Horacio akuti: “Mkhalidwe umenewu unandipangitsa kukula m’maganizo mwamsanga.”
Munthu akatayikidwa makolo ake zimakhala zoŵaŵa kwambiri. Komabe, khalani otsimikiza kuti ndi chithandizo cha Yehova, mungakhalebe ndi moyo ndi kulandira madalitso ake.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani ya “Achinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Nchifukwa Chiyani Ndikukhala Wopanda Makolo?,” mu kope la Galamukani! ya December 8, 1998.
[Chithunzi patsamba 14]
Mungapeze chithandizo kwa akulu achikristu