Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 6/8 tsamba 28-31
  • “Ana ndi Osalimba”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ana ndi Osalimba”
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malangizo Apamwamba
  • Zimene Zikuchitika Lerolino
  • Yankho Lenileni
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kumanga Banja Lolimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Thandizani Ana Anu Kukula Bwino
    Galamukani!—1997
  • Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 6/8 tsamba 28-31

“Ana ndi Osalimba”

‘Ana ndi osalimba; ndiziyenda pang’onopang’ono’ malingana ndi kuyenda kwa anaŵa.’—Yakobo, bambo wa ana ambiri, wa m’zaka za zana la 18 B.C.E.

KUZUNZA ana si kwatsopano. Mitundu ina yakale ya anthu—monga ngati ya Aaziteki, Akanani, Ainka, ndi Afoinike—ndi yodziŵika chifukwa cha kupereka nsembe ana awo. Zinthu zimene zinakumbidwa m’nthaka kumene kunali mzinda wa chifoinike wa Carthage (umene tsopano uli kunja kwa mzinda wa Tunis, ku North Africa) zinavumbula kuti pakati pa zaka za zana lachisanu ndi lachitatu B.C.E., ana okwanira 20,000 anaperekedwa nsembe kwa mulungu wotchedwa Baala ndiponso mulungu wachikazi wotchedwa Tanit! Ameneŵa ndi ana ochuluka kwambiri kwenikweni tikaganizira kuti mzinda wa Carthage utafika pachimake pa kukula unali ndi anthu 250,000 basi.

Komabe, panali mtundu wina wa anthu akale umene unali wosiyana ndi mitundu imeneyi. Ngakhale kuti mtundu wa Israyeli unkakhala pakati pa mitundu ina imene inkachitira ana awo nkhanza, unkalera ana mosiyana kwambiri. Tate wa mtundu umenewu, Yakobo ndi amene anapereka chitsanzo. Malingana ndi buku la m’Baibulo la Genesis, pamene Yakobo ankabwerera kumudzi kwawo, anauza anthu onse amene ankayenda naye kuti aziyenda pang’onopang’ono kuti ana asavutike paulendopo. “Ana ndi osalimba,” iye anatero. Pamene ankayankhula zimenezo n’kuti ana ake ali ndi zaka zapakati pa 5 ndi 14. (Genesis 33:13,14) Mbadwa zake, Aisrayeli, anasonyeza kuti ankaona ana monga ofunika ndipo ankawapatsa zofuna zawo.

N’zoona kuti ana m’nthaŵi za Baibulo ankachita ntchito zambiri. Akamakula, anyamata ankaphunzitsidwa ntchito zamanja ndi atate awo; monga ulimi, kapenanso ntchito zaluso monga ukalipentala. (Genesis 37:2; 1 Samueli 16:11) Atsikana, adakali pakhomo pa makolo awo ankaphunzitsidwa ntchito za pakhomo zimene zinali zofunika kuzidziŵa akadzakhala paokha. Rakele, mkazi wake wa Yakobo, anali woweta nkhosa pamene anali mtsikana. (Genesis 29:6-9) Atsikana ankagwira ntchito m’minda ndi m’minda ya mpesa nthaŵi yokolola. (Rute 2:5-9; Nyimbo ya Solomo 1:6)a Nthaŵi zambiri ntchito yotereyi inkachitidwa moyang’aniridwa ndi makolo achikondi ndipo mophunzitsidwa.

Komanso, ana ambiri ku Israyeli ankasangalala ndi kuchita maseŵera’. Mneneri Zekariya anatchulapo za ‘m’misewu ya mudzi mokhala ana amuna ndi akazi akusewera.’ (Zekariya 8:5) Ndipo Yesu Kristu anatchulapo za ana akukhala m’mabwalo a malonda amene ankaimba zitoliro ndi kumavina. (Mateyu 11:16, 17) Kodi n’chiyani chimene chinkachititsa kuti ana azikhala nawo bwino motero?

Malangizo Apamwamba

Nthaŵi yonse imene Aisrayeli ankamvera malamulo a Mulungu, sankavutitsa ana awo kapena kuwazunza. (Yerekezani Deuteronomo 18:10 ndi Yeremiya 7:31.) Ankaona ana awo aamuna ndi aakazi monga “cholandira cha kwa Yehova,” “mphotho.” (Salmo 127:3-5) Kholo linkaona ana ake monga ‘timitengo ta azitona tozinga podyera pake’—ndipotu mitengo ya azitona inali yamtengo wapatali kwambiri kwa mtundu wa anthu odalira ulimi amenewa! (Salmo 128:3-6) Wolemba mbiri wina Alfred Edersheim akunena kuti kuphatikiza pa mawu akuti mwana wamwamuna ndi mwana wamkazi, chiyankhulidwe cha Chihebri chakale chinali ndi mawu asanu ndi anayi otanthauza ana, liwu lililonse linkaimira msinkhu winawake wa anawo. Iye akutsiriza motere: “N’zosakayikitsa kuti anthu ameneŵa, oonetsetsa moyo wa ana mwachidwi chonchiwa, mpaka n’kumatha kusiyanitsa misinkhu imeneyi ana akangosintha pang’ono, ankakonda ana awo kwambiri.”

M’nyengo ya Chikristu, makolo ankalangizidwa kuti ayenera kukhala bwino ndi ana awo ndiponso ayenera kuwalemekeza. Yesu anapereka chitsanzo chabwino cha zimene tingamachite kwa ana a anthu ena. Nthaŵi ina atatsala pang’ono kutsiriza utumiki wake wa padziko lapansi, anthu anayamba kum’bweretsera ana awo. Koma ophunzira ake poganiza kuti Yesu anali wotanganidwa kwambiri kotero kuti anawo akanam’sokoneza, anayesa kuwaletsa anawo. Koma Yesu anatsutsa ophunzira akewo: “Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.” Mpaka Yesu “anatiyangata.” Sitingakayikire ayi kuti iye ankaona kuti ana anali amtengo wapatali ndipo ofunika kuwachitira chifundo.—Marko 10:14, 16; Luka 18:15-17.

Kenaka, mtumwi Paulo ananena izi kwa atate: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.” (Akolose 3:21) Mogwirizana ndi lamulo limenelo, makolo achikristu nthaŵi imeneyo, ngakhalenso a lero, sangalole kuti ana awo azigwira ntchito m’mikhalidwe yozunza. Amazindikira kufunika kwa chikondi, chisamaliro, ndi chitetezo kuti ana akule bwino, akhwime m’maganizo, ndipo kuti akule mwauzimu. Makolo ayenera kuonetsa chikondi chenicheni mwa zochitika. Kutanthauza kuti mwa zinthu zina ayenera kuteteza ana awo ku ntchito zofoola nyonga.

Zimene Zikuchitika Lerolino

N’zoona kuti tikukhala “m’nthaŵi zowawitsa.” (2 Timoteo 3:1-5) Chifukwa cha mikhalidwe yovuta ya zachuma, m’mayiko ambiri ngakhale makolo achikristu angaone kuti ndi bwino kulola ana awo kuyamba ntchito. Mmene taonera kale, palibe cholakwa ngati ana akugwira ntchito imene ili yabwino komanso imene akuphunzirapo kanthu. Ntchito yotereyi ingathe kupititsa patsogolo kukula kwa mwana, kukhwima maganizo kwake, kukula muuzimu, m’makhalidwe, kapena kudziŵa kukhala ndi anthu koma si isokoneza maphunziro, maseŵera oyenera, ndi kupuma.

Mosakayikira, makolo achikristu angakonde kuti ana awo azigwira ntchito moyang’aniridwa ndi iwo, osati ndi anthu ena opanda chifundo kapena opulukira amene angawalembe ntchito ngati akapolo. Makolo otereŵa amaonetsetsa kuti ntchito iliyonse imene ana awo akugwira siikuwachititsa kuti azunzidwe mwa kumenyedwa, kaya kuchitidwa nkhanza monga mwa kugwiriridwa, kapena kuvutitsidwa maganizo. Ndiponso amafuna kuti ana awo akhale nawo pafupi. Mwanjira imeneyi iwo angathe kukwaniritsa ntchito yawo yonenedwa m’Baibulo ya uphunzitsi wa zauzimu: “Muziwaphunzitsa [Mawu a Mulungu] mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.”—Deuteronomo 6:6, 7.

Ndiponsotu, Mkristu amaphunzitsidwa kuti ayenera kukhala wachifundo, wokondana ndi abale, ndi kukhala wachisoni. (1 Petro 3:8) Amalimbikitsidwa kuti ‘achitire onse chokoma.’ (Agalatiya 6:10) Ngati mikhalidwe ya umulungu imeneyi iyenera kusonyezedwa kwa anthu alionse, nanga bwanji ana athu enieni! Mogwirizana ndi lamulo lalikulu la makhalidwe—“zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero”—Akristu sangalole kuti agwiritse ntchito mwankhanza ana a ena, kaya ndi Akristu anzawo kapena ayi. (Mateyu 7:12) Kuwonjezeranso apo, chifukwa chakuti Akristu ndi anthu osunga lamulo, amafuna kuonetsetsa kuti sakuphwanya malamulo a boma oletsa anthu kugwira ntchito ngati asanafike pa msinkhu winawake.—Aroma 13:1.

Yankho Lenileni

Kodi m’tsogolo muli zotani? M’tsogolo muli nthaŵi zabwino kwa ana ndi akulu omwe. Akristu oona ndi otsimikiza kuti chimene chidzachotse kotheratu mchitidwe wogwiritsa ntchito ana mwankhanza ndi boma limene likubwera la padziko lonse lapansi limene Baibulo limalitcha kuti “Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 3:2) Anthu oopa Mulungu akhala akulipempherera ponena kuti: “Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

Mwa zinthu zina, Ufumu umenewu udzachotsa mikhalidwe imene imayambitsa mchitidwe wogwiritsa ntchito ana mwankhanza. Udzachotseratu umphaŵi. “Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.” (Salmo 67:6) Ufumu wa Mulungu udzatsimikiza kuti aliyense ndi ophunzira mokwanira maphunziro ozikidwa pa mikhalidwe ya umulungu. “Pamene maweruziro [a Mulungu] ali pa dziko lapansi, okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.”—Yesaya 26:9.

Boma la Mulungu lidzachotseratu umbombo pa chuma umene umachititsa kuti pasakhale chilungamo. Kusankhana chifukwa cha mtundu, makhalidwe, msinkhu, kapena chifukwa choti wina ndi mkazi kapena ndi mwamuna sikudzakhalaponso nthaŵi imeneyo, chifukwa lamulo lalikulu kwambiri la Ufumu umenewo lidzakhala lamulo la chikondi, pamwamba pa lamulo loti: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.” (Mateyu 22:39) Pansi pa boma lolungama lotereli, vuto la mchitidwe wogwiritsa ntchito ana mwankhanza lidzatheratu!

[Mawu a M’munsi]

a Zimenezi sizinachititse kuti akazi asanduke anthu otsikirapo m’mabanja, kuti iwo ndi oyenera ntchito za m’nyumba kapena za kumunda basi. Zimene Baibulo limafotokoza za “mkazi wangwiro” m’buku la Miyambo zimaonetsa kuti mkazi wokwatiwa sankangosamalira banja lokha komanso ankasamalira zinthu zambiri za pakhomo, ankalima n’kumapeza chakudya chokwanira, ndiponso kugulitsa malonda.— Miyambo 31:10, 16, 18, 24.

[Bokosi patsamba 30]

Dona Alola Atsikana Ake Kupita

KWA zaka 15, Ceciliab anali ndi nyumba zokhala mahule ku chilumba china cha ku Caribbean zimene ankaziyang’anira. Ankagula atsikana 12 kapena 15 nthaŵi imodzi, ambiri ankakhala osafika zaka 18. Atsikana ameneŵa ankagwidwa asakufuna chifukwa cha ngongole za makolo awo. Cecilia ankawalipirira ngongolezo ndiye kenaka ankatenga atsikanawo kuti azikamugwirira ntchito. Pa ndalama zimene iwo ankapeza, iye ankatengapo zina n’kumawagulira chakudya komanso n’kumawasamalira ndipo zina ankaziika padera kuti zidzakwane pa ndalama zimene anawagulira. Pankatha zaka kuti iwo adziwombole n’kukhala pa ufulu. Atsikanawo sankaloledwa kutuluka m’nyumbamo pokhapokha ngati ali ndi mlonda.

Cecilia akukumbukira bwino zimene zinachitika nthaŵi ina. Amayi a mtsikana wina, hule, ankabwera sabata iliyonse kudzatenga mapukusi a chakudya—chakudya chimene chapezeka chifukwa cha “ntchito” ya mwana wake. Mtsikana ameneyo anali ndi mwana wake wamwamuna. Anali atalephera kulipira ngongole zake ndipo analibiretu chiyembekezo chodzamasulidwa. Tsiku lina anadzipha, atalemba kalata yonena kuti mwana wake azimusamalira ndi adona akewo. Cecilia analera mnyamatayo pamodzi ndi ana ake anayi.

Mwana wina wa Cecilia anayamba kuphunzira Baibulo ndi amishonale a Mboni za Yehova. Cecilia analimbikitsidwa kuti aziphunzira nawo koma poyamba anakana chifukwa chakuti sankadziŵa kulemba kapena kuŵerenga. Komabe, pang’onopang’ono, chifukwa chomamvetsera makambirano ochokera m’Baibulo, anayamba kuona chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kwake ndipo anakonda kukhululukira kwake. (Yesaya 43:25) Chifukwa chofuna kuphunzira Baibulo payekha, msangamsanga anayamba kuphunzira kuŵerenga ndi kulemba. Ndipo atayamba kudziŵa zambiri za m’Baibulo, anaona kuti anafunikira kugwirizana ndi miyezo yapamwamba ya Mulungu.

Tsiku lina atsikanawo anadabwa kwambiri iye akuwauza kuti angathe kumapita! Iye anawauza kuti zimene iwo ankachita zinali zoipa kwambiri pamaso pa Yehova. Palibe aliyense wa iwo amene anamubwezera ngongole yake. Komabe, aŵiri a iwo anasamuka kuti azikakhala naye kunyumba kwake. Pambuyo pake winanso anakhala Mboni yobatizidwa. Tsopano, Cecilia wakhala mphunzitsi wa nthaŵi zonse wa Baibulo kwa zaka 11, n’kumaphunzitsa anthu ena kuti asiye mikhalidwe yosalemekeza Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

b Si dzina lake lenileni.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena