Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 6/8 tsamba 4-6
  • Kuduka Chiŵalo—Mmene Mungapeŵere Ngozi Yake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuduka Chiŵalo—Mmene Mungapeŵere Ngozi Yake
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Amafunikira Kuchita Maseŵera Olimbitsa Thupi
  • Kusamalira Ziŵalo Zopunduka
  • Peŵani Kuvulala
  • Kuduka Chiŵalo—Kodi Nanu Zingakuchitikireni?
    Galamukani!—1999
  • Vuto la Chithandizo Chake
    Galamukani!—2003
  • Zimene Mungachite Kuti Mupewe Matenda a Shuga
    Galamukani!—2014
  • “Mwana Wanu Ali ndi Matenda a Shuga!”
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 6/8 tsamba 4-6

Kuduka Chiŵalo—Mmene Mungapeŵere Ngozi Yake

N’KOTHEKA kupeŵa zinthu zambiri zimene zingapangitse munthu kudulidwa chiŵalo! Ndipo ngakhale anthu odwala matenda a peripheral Vascular (PVD), angapeŵenso zinthu zimenezo. Monga mmene tanenera m’nkhani yoyamba ija, chimachititsa PVD kaŵirikaŵiri ndi matenda a shuga.a Koma nkhani yabwino n’jakuti matenda a shuga ali ndi mankhwala.

Buku lotchedwa The Encyclopedia Britannica linati: “Kudya bwino ndiko mankhwala aakulu a matenda a shuga, kaya wodwalayo wapatsidwa mankhwala a insulin kapena ayi.” Dr. Marcel Bayol, wa ku Kings County Hospital ku New York City, anauza Galamukani! kuti: “Ngati anthu odwala matenda a shuga atatsimikiza kuti akufuna kuchira, namasamala ndi zimene amadya, ndipo namalolera kupimidwa kaŵirikaŵiri, angapeŵe kudzadulidwa chiŵalo monga mwendo.” Anthu odwala matenda a shuga a mtundu wachiŵiri amene amatsatira malangizo ameneŵa, tsiku lina adzaona kuti zizindikiro za matenda awo zikusintha.b

Amafunikira Kuchita Maseŵera Olimbitsa Thupi

Kuchita maseŵera olimbitsa thupi n’kofunikanso kwambiri. Kumathandiza thupi kusunga glucose, kapena shuga wa m’magazi, kuti akhalebe monga mmene amafunikira kukhalira. Ngati munthu wapezedwa ndi nthenda ya PVD, kulimbitsa thupi kumam’thandiza kupeza nyonga, ndipo thupi limamasuka, magazi amayenda bwino kufika kuziŵalo zowonongekazo. Maseŵera olimbitsa thupi amathandiza kuti odwalawo asamatsimphine kaŵirikaŵiri—chifukwa cha ululu umene anthu odwala PVD ameneŵa amamva m’mitsempha ya kumapazi, poyenda kapena polimbitsa thupi. Komabe, ayenera kumapeŵa maseŵera olimbitsa thupi amene amatopetsa kwambiri miyendo yawo. Maseŵera abwino kwambiri olimbitsa thupi angakhale kuyenda, kupalasa njinga, kupalasa bwato, kusambira, ndi maseŵera ena othamangitsa magazi. Munthu ayenera kuonana ndi dokotala asanayambe kumadzimana chakudya kapena asanaganize zoyamba kuchita maseŵera ena ake olimbitsa thupi.

Munthu amene akufuna kukhala ndi thanzi labwino ayenera kupeŵeratu kusuta fodya. PVD ndi nthenda imodzi mwa matenda ambiri amene amayambika kapena kukula chifukwa chosuta fodya. Dr. Bayol anati: “Kusuta fodya ndicho chifukwa chachikulu chimene chimapangitsa anthu kudulidwa ziŵalo, makamaka ngati wodwalayo alinso ndi matenda a shuga ndi PVD.” N’chifukwa chachikulu motani? Buku lolangiza anthu odulidwa ziŵalo mmene angazoloŵerere mkhalidwe wawo, linati: “Mwa anthu onse amene amafunikira kudulidwa ziŵalo, pamapezeka kuti chiŵerengero cha anthu osuta fodya chimaposa cha anthu osasuta fodya ndi 10.”

Kusamalira Ziŵalo Zopunduka

PVD ingachepetse magazi oyenda m’miyendo ndi m’mapazi, zikatero ndiye imayambitsa vuto lotchedwa neuropathy—kufa kapena kuuma kwa mitsempha. Ndiyeno zikatero ziŵalo sizichedwa kuvulazika, ngakhale pamene munthu wangogona pabedi. Mwachitsanzo, poti wodwalayo sangamve ululu, angapse kwambiri ngati bulangeti lake lamagetsi, lingatenthe kwambiri. N’chifukwa chake okonza zinthuzo amachenjeza odwala matenda a shuga kuti ayenera kusamala kwambiri pogwiritsira ntchito zinthu zimenezo.

Miyendo kapena manja amene ali opunduka nawonso sachedwa kuvulazika. Kungokandika pang’ono basi, pangadzakhale bala lalikulu, mwinanso kuyamba kuvunda. N’chifukwa chake kuli kofunika kusamala mapazi, povala nsapato zosathina ndiponso miyendo ndi mapazi ayenera kukhala oyera ndi ouma. Pali zipatala zambiri zimene zimaphunzitsa odwala kusamalira mapazi awo.

Pamene PVD yafika poipa poti palibenso kuchitira mwina koma kudula chiŵalocho, kaŵirikaŵiri madokotala amayesetsa kupeŵa kuchidula chiŵalocho. Njira ina ndiyo imene amati balloon angioplasty. Dokotala wa zamitsempha amaloŵetsa kanthu kena kofanana ndi mtsempha, kotchedwa catheter, kokhala ndi kathumba kunsonga kwake. Kenaka kathumbako amakauzira mpweya, ndiyeno kamawongola mtsempha umene unatsekeka. Njira inanso amati bypass surgery—kutenga mitsempha paziŵalo zina za thupi n’kuiika m’malo mwa mitsempha ina yowonongeka kwambiri.

Barbara, yemwe tsopano ali ndi zaka 54, wakhala ali ndi nthenda ya shuga ya mtundu woyamba imeneyi, kuyambira ali ndi zaka zinayi. Atangobala mwana wake woyamba, miyendo ya Barbara inagwidwa nthenda imeneyi ya PVD. Madokotala ena anamulangiza kuti aidulitse. Komabe, Barbara anapeza dokotala wina wa zamitsempha amene anagwiritsira ntchito angioplasty kupangitsa magazi kuyambanso kufika kumapazi. Njira ya angioplasty inam’thandiza kwa kanthaŵi, koma kenaka anadzafunikira kuchotsedwa mitsempha yowonongeka n’kuikidwa yabwino, ndipo anaterodi bwinobwino. Panopo Barbara amasamalira mapazi ake mwapadera kwambiri.

Peŵani Kuvulala

Kuvulala ndiko chinthu chachiŵiri chopangitsa munthu kudulidwa chiŵalo. Poti munthu sasankha kuti avulale chiŵalo chakutichakuti, angavulale chiŵalo chilichonse. Komabe, tikamaona moyo monga mmene Mulungu amauonera, munthu angamayesetsedi kupeŵa ngozi zovulaza. Akristu, kaya akugwira ntchito, kaya akuyendetsa galimoto, kaya akuseŵera, ayenera kumachita zinthu mokumbukira kuti matupi awo ndi mphatso imene Mulungu anawapatsa. Choncho, amasamala kwambiri mwakuchita zinthu mogwirizana ndi njira zoyenera zopeŵera ngozi ndipo amapeŵa kuchita dala zinthu zoika moyo pachiswe.—Aroma 12:1; 2 Akorinto 7:1.

Kodi anthu akuchitanji kuti achepetse ngozi m’mayiko ambiri amene munakwiriridwa mabomba? M’mayiko ambiri maboma akuphunzitsa anthu njira izi ndi izi zowathandiza kukhala osamala ndi mabomba. Malinga ndi mmene ananenera mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations, “anthu okhala pangoziwo . . . amaphunzitsidwa mmene angapeŵere kuponda bomba pamene akukhala ndi kugwira ntchito m’malo okumbiridwa mabomba.”

Lipoti lina lochokera ku bungwe la United Nations linati, n’zachisoni kuti “anthu amafika pongozoloŵera kuti kuli mabomba, ndiye amayamba kusasamala. Nthaŵi zina, zimene [anthuwo] amakhulupirira pachipembedzo chawo zimawalimbikitsa kunyalanyaza ngozi, chifukwa chokhulupirira kuti imfa n’njachilengedwe ndiye n’njosapeŵeka.” Komabe, Mawu a Mulungu amatsutsa anthu okhulupirira kuti poti imfa n’njosapeŵeka, kuyesa kupeŵa ngozi n’kosathandiza. M’malo mwake, Baibulo limalimbikitsa anthu kukhala osamala poopa ngozi.—Deuteronomo 22:8; Mlaliki 10:9.

Choncho, mutamasamala kwambiri pochita zinthu ndi kusamalanso thanzi lanu, mungapeŵedi ngozi zimene zingakupangitseni kudulidwa chiŵalo. Koma nanga bwanji anthu amene anadulidwa kale ziŵalo? Kodi angakhalebe ndi moyo wabwino?

[Mawu a M’munsi]

a Mavuto okhudza mitsempha ya kumapazi angayambike kapena kukula ngati munthu akuvala zovala zothina kwambiri m’munsi kapena kuvala nsapato zothina kwambiri, kapena ngati munthuyo amakhala pansi (makamaka atapinda miyendo) kapena kuimilira kwa nthaŵi yaitali.

b Anthu odwala matenda a shuga a mtundu woyamba, amapatsidwa mankhwala otchedwa insulin mwa kulasidwa jakisoni tsiku ndi tsiku. Koma aja odwala matenda a shuga a mtundu wachiŵiri (osadalira mankhwala a insulin) angamadzisamale mwa kudya bwino ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi. Ku United States, 95 peresenti ya anthu odwala matenda a shuga n’ngwodwala matenda a shuga a mtundu wachiŵiriwa.

[Chithunzi patsamba 4]

Kusuta fodya kungapangitse kudulidwa chiŵalo mosavuta kwambiri makamaka kwa anthu odwala matenda okhudza mitsempha

[Chithunzi patsamba 5]

Kuchita maseŵera olimbitsa thupi ndi kudya zakudya zabwino kumathandiza kukhala ndi mitsempha yathanzi labwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena