Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 7/8 tsamba 3
  • Kodi Moyo Wanu Ungakhale ndi Ngozi Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Moyo Wanu Ungakhale ndi Ngozi Zotani?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Pali Moyo Wabwinopo?
  • Mmene Mungatetezere Thanzi Lanu
    Galamukani!—1999
  • Kusiyana m’Zathanzi kwa Padziko Lonse—Vuto Lomakula
    Galamukani!—1995
  • Umoyo Wabwino—Kodi Mungachitenji Ponena za Iwo?
    Galamukani!—1989
  • Kodi Umoyo Nchiyani?
    Galamukani!—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 7/8 tsamba 3

Kodi Moyo Wanu Ungakhale ndi Ngozi Zotani?

M’NJIRA zambiri umoyo wabwino wakhala wovuta kuupeza kwake. Lipoti la bungwe la World Health Organization (WHO) la chaka cha 1998 linati: “Anthu ambiri lero kuposa kale lonse ali ndi zipatala pafupi, madzi abwino ndi zimbudzi zaukhondo.” Kunena zoona, anthu ambiri padziko lonse akukhalabe moyo wovutika kwambiri, komabe malinga ndi mmene wailesi ya British Broadcasting Corporation inanenera, “umphaŵi wachepetsedwa kwambiri padziko lonse m’zaka 50 zokha zapitazi kuposa mmene unachepetsedwera m’zaka 500 zam’buyomu.”

Kupita patsogolo kwa njira zosamalira umoyo kwawonjezera zaka zimene anthu amayembekezera kukhala ndi moyo padziko lonse. Mu 1955 ambiri ankakhala zaka 48. Mu 1995 zaka zimenezi zinakwera n’kufika pa 65. Chifukwa chimodzi chimene chachititsa kukwera kumeneku ndicho kupita patsogolo kumene kwachitidwa polimbana ndi matenda ogwira ana.

Zaka 40 zokha m’mbuyomu, ana osafika zaka zisanu ankakwana 40 peresenti ya imfa zonse. Koma pomafika 1998, chifukwa cha kubwera kwa akatemera, ana ambiri padziko lapansi anali atatetezedwa ku matenda aakulu ogwira ana. Motero, chiŵerengero cha imfa ya ana osafika zaka zisanu chatsika mpaka kufika pa 21 peresenti ya imfa zonse. Malingana ndi kunena kwa bungwe la WHO “pali chifukwa chooneka bwinobwino chimene chikuchititsa anthu kukhala ndi moyo wabwinopo komanso wautalipo.”

N’zoona kuti moyo wautalipo koma wopanda kusintha kwabwino kwenikweni ndi wopanda tanthauzo. Pofunafuna mikhalidwe yabwinopo anthu ambiri amayamba kuika zinthu zakuthupi patsogolo. Komabe, moyo woterowo ungakhale ndi ngozi zake ku thanzi.

Kodi Pali Moyo Wabwinopo?

Kupita patsogolo kwa zachuma komanso kwa zakakhalidwe kwachititsa kusintha kwakukulu kwa moyo wa anthu. Tsopano anthu ambiri okhala m’mayiko olemera angathe kugula zinthu ndi kutha kuchita zinthu zina zimene kale anthu olemera okha ndi amene ankazikwanitsa. Ngakhale kuti kupita patsogolo kumeneku kwabweretsa chiyembekezo chokhala ndi moyo wautalipo, anthu ambiri kwawaloŵetsa m’moyo wodziwononga.

Mwachitsanzo, chifukwa chokhala ndi ndalama zokwanira, anthu mamiliyoni akhala akugula zinthu zosafunika monga ngati mankhwala osokoneza bongo, moŵa, ndi fodya. Ndipo zotsatirapo zodziŵikiratuzo n’zomvetsa chisoni. Magazini yotchedwa World Watch inanena kuti: “Pa thanzi la anthu, chinthu chimene chikupitiriza kuopsabe mwaliwiro si nthenda ayi, koma chinthu chogulitsidwa.” Magaziniyo ikuwonjezera kunena kuti: “Zaka 25 zikubwerazi, matenda oyamba chifukwa chosuta fodya akuoneka kuti adzavutitsa anthu kwambiri padziko lonse kuposa matenda opatsirana.” Ndiponsotu, magazini ya Scientific American inanena kuti: “N’zochititsa mantha kwambiri kuti 30 peresenti ya anthu odwala matenda a kansa yakupha inawayamba chifukwa cha kusuta, ndipo anthu enanso ochuluka chimodzimodzi inawayamba chifukwa cha moyo wawo, makamaka kadyedwe ndi kusachita maseŵera olimbitsa thupi.”

Mosakayikitsa, zimene timasankha kuchita m’moyo wathu zimakhudza thanzi lathu kwambiri. Chilichonse chimene timachita chimakhudza thanzi lathu—kaya ndi chokhudza zimene timalowetsa m’maganizo athu, thupi lathu, kapena zimene timachita kuti tikhale ndi thupi lolimba. Ndiye nanga tingapitirize bwanji kukhalabe ndi thanzi labwino kapena kuti likhale labwinopo? Kodi kudya bwino ndi kuchita maseŵera olimbitsa thupi n’kokwanira? Ndipo, kodi maganizo ndi zinthu zauzimu zimam’thandiza bwanji munthu kukhala ndi moyo wathanzi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena