Mungadzisankhire Tsogolo Lanu
KATSWIRI wina wa mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi, Joan Oates, anati: Ngakhale kuti kuwombeza maula kunali kuonedwa ngati “chinthu chanzeru kwambiri m’dziko lonse la anthu akale,” maula anali chinthu china chimene aneneri achihebri anali kuchiona ngati chopanda pake.” Chifukwa chiyani?
Ngakhale kuti Aisrayeli anali kukhala ndi anthu okhulupirira kuti chilichonse n’chikonzero cha Mulungu, iwowo anali kutsutsa zoti pali mphamvu ina yosadziŵika imene inali kutsogolera miyoyo yawo. Mulungu powalangiza anthuwo anati: ‘Asapezeke mwa inu munthu . . . wowombeza maula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga, kapena . . . wopenduza.’—Deuteronomo 18:10, 11.
Aisrayeli anali ndi chidaliro chakuti zinthu zidzawayendera bwino m’tsogolo, koma popanda kukhulupirira za chikonzero cha Mulungu kapena kudalira openduza. Buku la maumboni lotchedwa French Catholic Théo, linafotokoza chifukwa chake kuti, mtunduwo unali kukhulupirira kuti “munthu padziko lapansi samangotsogozedwa ndi mphamvu ina yosadziŵika. Mulungu ali n’cholinga ndi munthu.” Kodi cholinga chimenecho chinali chiti?
Chikonzero cha Mulungu Komanso Ufulu Wodzisankhira
Mulungu analonjeza Aisrayeli kuti akamvera malamulo ake adzawapatsa ufulu ndi mtendere. (Levitiko 26:3-6) Ndiponso, anali kuyembekezera Mesiya kuti ndiye amene adzakhazikitsa mikhalidwe yolungama padziko lapansi. (Yesaya, chaputala 11) Komabe, si kuti pamene Mulungu anawalonjeza zinthu zimenezo ndiye kuti iwo akanangokhala pansi n’kumadikira kuti zinthuzo zizichitika. Koma anauzidwa kuti: “Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako.”—Mlaliki 9:10.
Mfundo yaikulu pamenepo inali yakudzisankhira zochita. Aisrayeli anali ndi ufulu wakusankha kutumikira Mulungu ndi kudzikonzera tsogolo lawo. Mulungu anawalonjeza kuti: “Kudzakhala mukasamalira chisamalire malamulo anga amene ndikuuzani lerolino, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kum’tumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndidzapatsa mvula ya dziko lanu m’nyengo yake, ya myundo ndi ya masika, kuti mutute tirigu wanu, ndi vinyo wanu, ndi mafuta anu.” (Deuteronomo 11:13, 14) Aisrayeli analandira madalitso a Mulungu pamene anali omvera.
Aisrayeli atangotsala pang’ono kuloŵa m’dziko limene analonjezedwa, Mulungu anawapatsa mwayi wakusankha; Iye anati: “Tapenyani, ndaika pamaso panu lerolino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa.” (Deuteronomo 30:15) Munthu aliyense akanakhala ndi tsogolo labwino malingana ndi zochita ndiponso zosankha zake. Potumikira Mulungu akanadalitsidwa, pokana kum’tumikira akanavutika. Koma bwanji za lero?
Chochititsa ndi Zotsatirapo
Tili ndi malamulo ambiri achilengedwe amene anaikidwa kuti azitipindulitsa. Limodzi mwa ameneŵa ndilo lamulo lakuti chochitika chilichonse chili ndi chotsatirapo chake, kapena monga mmene Baibulo limanenera, kuti “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Tikangoimvetsetsa mfundo imeneyi, n’kotheka kulingalira za zinthu zimene zingadzachitike m’tsogolo.
Ngati timathamangitsa kwambiri galimoto, tingachite ngozi mosavuta, pomwe ngati tili osamala, tingaipeŵe. Ngati timasuta fodya, tingagwidwe msangamsanga ndi matenda a kansa, pomwe ngati sitisuta, sitingadwale kansa. N’zoona kuti zochitika monga kuukiridwa ndi zigaŵenga zimene tatchula kuchiyambi kwa nkhani ino sizikuoneka ngati zingatichitikire ifeyo, ndipo kungoyerekezera kokha kuti zingatichitikire n’kopanda tanthauzo. Komabe, kukhulupirira kuti zinthu zimachitika monga mwa chikonzero cha Mulungu sikungatipindulitse. Chikhulupiriro chimenecho sichimatithandiza kudziŵa za nthaŵi ino ngakhale yam’tsogolo. Kukhulupirira bodza sikumapatsa munthu chidaliro chenicheni chakuti m’tsogolo muli bwino. Ndiponso n’zosapindulitsa kukhulupirira kuti Mulungu ndiye amakonzeratu chochitika chilichonse.
Kodi M’tsogolo Mwanu Mudzakhala Motani?
M’tsogolo mwathu simunakonzedweretu koma zimene timachita tsopano lino n’zimene zimakonza tsogolo lathu. Ngakhale kuti moyo uli mphatso yochokera kwa Mulungu, Baibulo limanena momveka bwino kuti ifeyonso tili ndi mbali yaikulu yochita pakudzisankhira zochita tsopano lino ndi kudzikonzeranso tsogolo. Mfundo yakuti tili ndi ufulu wakukondweretsa Mulungu, kapena wakum’khumudwitsa, imasonyeza kuti Mulunguyo watipatsa ufulu wakudzilamulira m’moyo wathu.—Genesis 6:6; Salmo 78:40; Miyambo 27:11.
Ndiponso, Malemba Oyera amanena monenetsa kuti, tsogolo lathu limadalira pa kupirira kwathu limodzi ndi zochita zathu m’moyo, ndiye zonsezi zikanakhala zopanda tanthauzo ngati zinthu zinali zokonzedweratu kale. (Mateyu 24:13; Luka 10:25-28) Chabwino, ngati tisankha kukhala omvera Mulungu, ndiye kuti tingayembekezere kukhala ndi tsogolo lotani?
Baibulo limavumbula kuti anthu ali ndi tsogolo labwino kwambiri. Dziko lapansi lidzasandulidwa likhale paradaiso, ndipo mtendere ndi chisungiko zidzakhala zachikhalire. (Salmo 37:9-11; 46:8, 9) Tsogolo limeneli n’lotsimikizika chifukwa Mlengi wamphamvu yonse adzakwaniritsa lonjezo lake. (Yesaya 55:11) Koma kaya tidzadalitsidwa mwa kupatsidwa moyo m’Paradaiso kapena sitidzapatsidwa, si chifukwa chakuti zinthu zinakonzedweratu: tidzakhala nawo moyowo chifukwa chakuti timamvera Mulungu ndi kuchita chifuniro chake tsopano lino. (2 Atesalonika 1:6-8; Chivumbulutso 7:14, 15) Mulungu watipatsa ufulu wakusankha tokha ndipo akutilimbikitsa kuti: “Sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo.” (Deuteronomo 30:19) Nanga inuyo musankha chiyani? Zinthu sizinakonzedweretu iyayi, koma tsogolo lanu lili m’manja mwanu.
[Chithunzi patsamba 28]
Cholinga cha Mulungu n’chakuti anthu omvera akhale ndi tsogolo labwino kwambiri