Zikhulupiriro—N’chifukwa Chiyani Zili Zoopsa Kwambiri?
KODI zikhulupiriro zingakuvulazeni? Ena angatsutse lingaliro limeneli kapena kuchepetsa kuopsa kwake. Komabe, Polofesa Stuart A. Vyse m’buku lake lakuti Believing in Magic—The Psychology of Superstition (Kukhulupirira Matsenga—Sayansi ya Zikhulupiriro) anachenjeza kuti: “Zikhulupiriro zitha kuwononga moyo ngati wina akuwonongera ndalama zambiri kwa asing’anga, kwa a maula, kwa a mayere, kapenanso ngati miyambo ya zikhulupiriro zakezo imalimbikitsa kutchova juga.” Kulola zikhulupiriro kuti zilamulire miyoyo yathu kungakhale ndi zotsatira zovulaza kwambiri.
Monga momwe taonera, zikhulupiriro zambiri n’zongofuna kuchotsa mantha a za m’tsogolo. Komabe, n’kofunika kupenda pakati pa zikhulupiriro ndi chidziŵitso chodalirika chonena za zimene zili m’tsogolo mwathu. Talingalirani za chitsanzo ichi.
Nkhani Yopatsa Chidziŵitso
Mu 1503, atafufuza kwa miyezi yambiri m’mphepete mwa gombe la Central America, Christopher Columbus anakocheza ngalawa zake ziŵiri zomwe anatsala nazo, pa chilumba chomwe tsopano chimatchedwa Jamaica. Poyamba, anthu a pa chilumbacho anawagaŵira amalinyero otopawo chakudya mwaulere. Komabe, patapita nthaŵi, chifukwa cha khalidwe loipa la amalinyerowo, anthuwo anasiya kuwapatsa chakudyacho. Zinthu zinafika povuta kwambiri, chifukwa chakuti nthaŵi yoti sitima ina idzabwere kudzaŵawombola inali kutali kwambiri.
Nkhaniyo imati, Columbus anaŵerenga m’buku lake la zanyengo ndipo anazindikira kuti pa February 29, 1504 mwezi udzada monga mwa chilengedwe. Pokhala kuti anthu a pa chilumbacho anali a zikhulupiriro, iye anatengerapo mwayi, ndipo anawaopseza kuti mdima udzaphimba mwezi ngati sapereka chakudya kwa gulu lake. Anthuwo ananyalanyaza chenjezo limeneli mpaka pamene mwezi unayamba kuda! Nthaŵi yomweyo, “anafuula ndi kulira kwakukulu, nanyamula zakudya kuthamangira komwe kunali sitimazo.” Kuchokera pomwepo oyendera malowo anali kulandira zakudya kwa nthaŵi yonse imene anakhala pamenepo.
Kwa anthu a pa chilumbacho, Columbus anali atachita matsenga amphamvu. Koma anaganiza zimenezi chifukwa cha zikhulupiriro zawo chabe. Choonadi n’chakuti zomwe “ananeneratuzo” zinachitika chifukwa cha momwe dziko, mwezi, ndi dzuŵa zimayendera nthaŵi zonse. Akatswiri a za kuthambo angalosere modalirika zinthu ngati kuda kwa mwezi nthaŵi yaitali sizinachitike, ndipo chidziŵitso chimenechi chimapezeka m’buku la zanyengo. Kuwonjezera apo, kuyenda kosaphonya kwa zinthu zakuthambo kumatheketsa akatswiri a za kuthambo ameneŵa kudziŵa malo enieni amene zili pa nthaŵi yakutiyakuti. Choncho, n’chifukwa chake pamene nyuzipepala yakwanuko ilengeza za nthaŵi ya kutuluka ndi kuloŵa kwa dzuŵa mumavomereza kuti n’zoona.
Mlengi Wamkulu wa zakuthambo ndiye gwero la chidziŵitso chonena za nthaŵi ya kuda kwa mwezi, kutuluka kwa dzuŵa ndi kuloŵa kwa dzuŵa. Koma zolosera za olosera mwayi, asing’anga, ndiponso a mayere, ndi zochokera ku magwero ena, amene ali otsutsana ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Taonani zomwe tikutanthauza.
Magwero Oopsa
Pa Machitidwe 16:16-19, pali nkhani yopatulika imene imanena kuti ‘namwali wina wantchito’ mumzinda wakale wa Filipi anapindulira mbuye wake zambiri chifukwa cha ‘kubwebweta kwake.’ Komabe, nkhaniyo imanena poyera kuti gwero la zolosera zakezo silinali Mlengi wamphamvuyonse, koma “mzimu wambwebwe.” N’chifukwa chake pamene mtumwi Paulo anatulutsa chiŵandacho, namwaliyo analibenso mphamvu za kulosera.
Tikazindikira kuti maulosi otereŵa amachokera kwa ziŵanda, timamvetsa chifukwa chake Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli chinanena kuti “Asapezeke mwa inu . . . munthu wosamalira mitambo, wamatsenga, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga, kapena wolodza anzake, kapena aliyense amene amapita kwa wobwebweta kapena wopenduza . . . Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:10-12, NW) Ndiponsotu, machitachita otere anali tchimo laimfa m’Chilamulo.—Levitiko 19:31; 20:6.
Mungadabwe kudziŵa kuti mizimu yoipa ndiyo imachititsa zikhulupiriro zonse zomwe mwina zingaoneke ngati zosaopsa kwenikweni. Komabe, Baibulo limanena kuti, “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.” (2 Akorinto 11:14) Satana pamodzi ndi ziŵanda zimene zili pansi pa ulamuliro wake angachititse mikhalidwe yoopsa kuoneka ngati yosavulaza, mwinanso kuoneka ngati yopindulitsa. Nthaŵi zina, angachititse maula kuchitikadi moona, kuti asokeretse anthu oona kuti aziganiza kuti maula ameneŵa achokera kwa Mulungu. (Yerekezani ndi Mateyu 7:21-23; 2 Atesalonika 2:9-12.) Zimenezi zikusonyeza chifukwa chake zolosera za anthu ena omwe amadzinenera kuti ali ndi mphamvu yapadera nthaŵi zina zimachitikadi.
Ndithudi, ambiri, mwinanso onse, amene amadzinenera kuti ali ndi mphamvu zapadera amakhala onyenga, akathyali, ongofuna kudyera masuku pamutu opusa. Komabe kaya akhale wonyenga kapena ayi mfundo n’njakuti akugwiritsidwa ntchito ndi Satana kuti asokoneze anthu kupandukira Yehova, ndi kuwachititsa khungu ku “Uthenga Wabwino wa ulemerero.”—2 Akorinto 4:3, 4.
Zithumwa za “Mwayi” ndi Mafano
Kodi tinganenepo chiyani pa zithumwa za “mwayi” ndiponso zikhulupiriro zozoloŵereka zimene anthu amagwiritsa ntchito kuti asachite mantha ndiponso kuti adziteteze pa zinthu zongowagwera? Zimenezi zimabweretsa ngozi zambiri zovuta kuzizindikira. Chifukwa choyamba n’chakuti munthu wozikhulupiriroyo kwenikweni angakhale akupereka moyo wake kuti uzilamulidwa ndi mizimu yosaoneka. Amasiya kuganiza zanzeru ndi za luntha, m’malo mwake amaopa zinthu zopanda maziko.
Wolemba wina anatulukira vuto lina lachibadwa chathu. Iye anati: “Ngati munthu amadalira chithumwa kaamba ka chitetezo ndipo chithumwacho chalephera kugwira ntchito munthuyo angayambe chizoloŵezi choloza ena chala kuti ndiwo akuchititsa masokawo m’malo modziloza chala iye mwini.” (Yerekezani ndi Agalatiya 6:7.) N’zosangalatsa kumva zomwe Ralph Woldo Emerson wolemba zimangirizo ananena zakuti: “Amuna opepera ndi amene amakhulupirira zinthu zochitika mwamwayi . . . Koma amuna enieni amakhulupirira kuti zochita zimakhala ndi zotsatira zake.”
“Zochita ndi zotsatira zake” m’miyoyo yathu kaŵirikaŵiri zimakhala zinthu zadzidzidzi—“nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika” zimene zimafikira tonsefe. (Mlaliki 9:11, NW) Zinthu zongotigwera sizichitika chifukwa cha “tsoka.” Akristu amadziŵa kuti zikhulupiriro ndi zithumwa sizimakhudza zinthu zongotigwera. Pamene zichitika, timakumbukira choonadi cha Baibulo chakuti: “Simudziŵa chimene chidzakugwereni mawa. Pakuti ndinu nkhungu yoonekera kwa kanthaŵi ndipo kenaka imazimiririka.”—Yakobo 4:14, NW.
Komanso, Akristu oona amadziŵa kuti kaŵirikaŵiri zithumwa komanso miyambo ya zikhulupiriro imalambiridwa. N’chifukwa chake Akristu amaona zinthu zonse zotere monga mafano, omwe amaletsedwa poyera m’Mawu a Mulungu.—Eksodo 20:4, 5; 1 Yohane 5:21.
Mmene Tingadziŵire za M’tsogolo
Zimenezi sizikutanthauza kuti Akristu sadera nkhawa za m’tsogolo. Koma kuganiza mosamala kumasonyeza poyera kuti kudziŵa za m’tsogolo n’kofunika ndipo n’kwa mtengo wapatali kwabasi. Ngati tadziŵiratu zomwe ziti zichitike m’tsogolo, tingachitepo kanthu moyenerera, ndipo tingapindule ife eni pamodzinso ndi okondedwa athu.
Komabe, m’pofunika kufunafuna chidziŵitso cha nkhaniyi ku magwero oyenera. Mneneri Yesaya anachenjeza kuti: “Anthu adzakuuza iwe kufunsira mauthenga kwa alauli ndi obwebweta . . . Ndipo iwe uziwayankha kuti, ‘Tamverani zimene Ambuye akukuphunzitsani! Musamvere obwebweta—zomwe akuuza inu sizidzakupindulirani.’”—Yesaya 8:19, 20, Today’s English Version.
Magwero oona a chidziŵitso chodalirika chonena za m’tsogolo ndiwo Wolemba wa Baibulo. (2 Petro 1:19-21) Buku louziridwa limeneli lili ndi maumboni ochuluka osonyeza kuti maulosi amene Mulungu wamphamvuyonse, Yehova, analosera n’ngodalirika—indedi n’ngodalirika ngati kuyenda kwa zinthu za kuthambo “zonenedweratu” m’mabuku ambirimbiri a zanyengo. Kuti mumvetse bwino kuti maulosi a Baibulo ndi olongosoledwa mwatsatanetsatane ndiponso mosaphonya, talingalirani chitsanzo ichi. Tayerekezerani kuti munthu wina wotchuka kwambiri lerolino akulengeza poyera ndipo akuneneratu zomwe zidzachitike zake 2000 kutsogoloku m’chaka cha 2199. Mawu ake oneneratu zam’tsogolo ali ndi ndondomeko yotere:
◻ Nkhondo yaikulu kwambiri idzabuka pakati pa mayiko amphamvu a dziko lapansi omwe padakali pano sali paudani, ndipo zotsatira zake zidzasintha mbiri.
◻ Imodzi mwa njira zimene adzagwiritse ntchito idzakhala ntchito yaluso imene idzapatutse mtsinje waukulu kwambiri.
◻ Dzina la wogonjetsayo likutchulidwa—zaka zambiri iye asanabadwe.
◻ Mapeto a wogonjayo akufotokozedwa, motero mawu onenedweratuwo akutalikitsidwa kufika zaka zambiri kutsogolo.
Ngati zinthu zonsezi zingachitikedi, kodi sizingachititse kuti anthu ayembekezere zinthu zina zimene munthu ameneyu wanena kuti zichitika m’tsogolo?
Zomwe talongosola kumenezi zinachitikadi. Zaka pafupifupi 200 Babulo asanagonje kwa Amedi ndi Aperisi, Yehova kupyolera mwa mneneri Yesaya analosera zotsatirazi:
◻ Nkhondo yaikulu idzabuka pakati pa Amedi mogwirizana ndi Aperisi kulimbana ndi Babulo.—Yesaya 13:17, 19.
◻ Imodzi mwa njira zomwe adzagwiritse ntchito idzakhala ntchito ya kuumitsa mtsinje wachitetezo wonga chingalande chachikulu. Komanso, zipata zoloŵera m’mzinda wotetezedwa umenewo zidzakhala zosatseka.—Yesaya 44:27–45:2.
◻ Wogonjetsayo dzina lake lidzakhala Koresi—linatchulidwa zaka 150 iye asanabadwe.—Yesaya 45:1.
◻ M’kupita kwa nthaŵi, Babulo adzasanduka bwinja.—Yesaya 13:17-22.
Mawu onenedweratu onseŵa anachitikadi. Ndiyeno kodi si kwanzeru kuyembekezera maulosi ena amene Yehova wanena m’Mawu ake olembedwa?
Tsogolo Labwino Limene Mulungu Walonjeza
Kodi Baibulo limalosera chiyani? Baibulo limalosera kuti m’dziko latsopano la Mulungu, simudzakhala wina wovutika chifukwa cha kukhala ndi mantha a kusadziŵa zam’tsogolo. Taonani chitsimikizo cha Mulungu kwa nzika za m’nthaŵi imeneyo: “Sipadzakhala wakuwawopsa [anthu anga].”—Mika 4:4.
Baibulo limalonjezanso kuti Mulungu ‘adzaolowetsa dzanja lake, nakwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.’ (Salmo 145:16) Kodi kukwaniritsidwa kwa maulosi ameneŵa kuli kutali? Ayi ndithu! Baibulo linalosera kale kuti zochitika zomwe tikuona tsopano padziko lapansi ndi umboni wokwanira wakuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a dongosolo loipali la zinthu.—2 Timoteo 3:1-5.
Posachedwapa Mlengi wachikondi adzathetsa mikhalidwe yoipayi. Adzathetsa nkhondo zonse, zimene zimachititsa dziko lonse nthumanzi komanso zimabweretsa mavuto. Kuwonjezera apo, udani, kudzikonda, upandu, ndi chiwawa zidzakhala zinthu zakale mpaka kalekale. Baibulo limalonjeza kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:10, 11.
Ena mwa madalitso amene anthu adzasangalala nawo m’dziko latsopano ndi thanzi labwino. Ngakhale imfa ndi chisoni chomwe imfa imabweretsa kudzakhala kulibe. Mulungu iyemwini anati: “Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.”—Chivumbulutso 21:4, 5.
Panthaŵiyo palibe munthu adzakumana ndi zinthu zongomugwera zimene zimasintha ndi kuwononga miyoyo lerolino. Satana ndi ziwanda zaka zoipa amene amayambitsa zikhulupiriro ndi mabodza, adzakhalanso atachotsedwa. Choonadi chosangalatsa chimenechi chimapezeka m’Baibulo.
[Zithunzi patsamba 25]
Zikhulupiriro ndi zochitika zokhulupirira mizimu n’zogwirizana kwambiri
[Mawu a Chithunzi]
Kusiyapo mkazi amene ali m’chigalasi choloselerayo: Les Wies/Tony Stone Images
[Chithunzi patsamba 26]
Dziko latsopano la Mulungu lidzakhala lopanda zikhulupiriro