Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g00 8/8 tsamba 14-15
  • Kodi Chisoni Chiyenera Kusonyezedwa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chisoni Chiyenera Kusonyezedwa?
  • Galamukani!—2000
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mkulu Wolongosola za Maliro Waona
  • Chikhalidwe N’chosiyana, Zochita Nazo N’zosiyana
  • “Kodi Ndingakhale Bwanji ndi Chisoni Changa?”
    Galamukani!—1988
  • Mfundo Zothandiza Amene Aferedwa
    Galamukani!—2018
  • Kupirira Panthawi Yachisoni
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Ndingakhale Motani ndi Chisoni Changa?
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
Onani Zambiri
Galamukani!—2000
g00 8/8 tsamba 14-15

Kodi Chisoni Chiyenera Kusonyezedwa?

M’BUKU lake lotchedwa On Children and Death, Dr. Elisabeth Kūbler-Ross anati: “Anthu ambirimbiri amavutika chifukwa mpaka pano sanagonjetse zovuta za pa ubwana wawo. Motero ana ayenera kuloledwa kulira popanda kuwanena kuti n’ngoliralira kapena achisasati, kapena kuwauza mawu opusa akuti ‘anyamata salira.’”

Kuona zinthu m’njira imeneyi n’kosiyana ndi maganizo opezeka m’madera ena akuti munthu sayenera kusonyeza chisoni chake m’njira iliyonse.

Zimene Mkulu Wolongosola za Maliro Waona

Kusiyana kumeneku kukusonyezedwa ndi mawu a Robert Gallagher, amene ali mkulu wolongosola za maliro ku New York. Iye anacheza ndi atolankhani a Galamukani! ndipo anamufunsa ngati anaona kusiyana kulikonse pa mmene mbadwa za ku United States ndi anthu ochita kusamukirako kuchokera kumayiko achilatini amasonyezera chisoni.

“Inde ndaona kuti pali kusiyana. Pamene ndinayamba ntchito imeneyi cha m’ma 1950, m’dera lathu tinali ndi mabanja ambiri achitaliyana osamukira kuno. Anali anthu achisoni kwambiri. Masiku ano kukakhala maliro timapezana ndi ana awo ndi zidzukulu zawo, ndipo chisoni chija sichionekanso. Sasonyeza kwambiri chisoni chawo.”

M’nthaŵi za m’Baibulo Ahebri anali kusonyeza kudandaula ndiponso chisoni chawo. Taonani mmene Baibulo limalongosolera zimene Yakobo anachita pamene anakhulupirira kuti mwana wake Yosefe wadyedwa ndi chilombo cholusa: “Yakobo ndipo anang’amba malaya ake, navala chiguduli m’chuuno mwake nam’lilira mwana wake masiku ambiri. Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti am’tonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anam’lilira.” (Genesis 37:34, 35 Tapendeketsa mawu ndife.) Inde, Yakobo sanachite manyazi kulilira mwana wake amene anasowa.

Chikhalidwe N’chosiyana, Zochita Nazo N’zosiyana

N’zoona kuti chikhalidwe chimasiyanasiyana. Mwachitsanzo, m’madera ambiri ku Nigeria, ngakhale kuti mabanja amakhala ndi ana ambiri ndipo maliro amachitika pafupipafupi chifukwa cha matenda osiyanasiyana, “kumakhala kulira kwadzaoneni mwana akafa, makamaka akakhala mwana woyamba ndipo amachita kunyanya mwanayo akakhala wamwamuna,” anatero wolemba wina amene wakhala zaka 20 ku Africa. “Kusiyana kwake n’kwakuti ku Nigeria anthu amasonyeza chisoni kwa kanthaŵi kochepa koma chimakhala chadzaoneni. Sichikhala kwa miyezi kapena zaka.”

M’madera a ku Mediterranean kapena ku Latin America, anthu anazoloŵera kusonyeza chisoni mmene munthuwe ukumvera. Kumeneko, chisangalalo ndiponso mkwiyo amazisonyeza poyera. Moni suthera pachanza chokha; koma amakumbatirananso mwachikondi. Momwemonso, chisoni amachisonyeza poyera mwa kulira ndiponso kubuma.

Wolemba wotchedwa Katherine Fair Donnelly ananena kuti, bambo woferedwa “amavutika maganizo chifukwa cha imfa ya mwana wake ndiponso chifukwa choopa kuti sakhala mwamuna weniweni akasonyeza chisoni chake pagulu.” Komabe iye anatsutsa zimenezi ponena kuti, “palibe malire a zinthu zololeka ndi zosaloleka posonyeza chisoni pamene munthu waferedwa mwana. Kuziziritsa mtima polira n’kofanana ndi kufinya chilonda kuti muchotsa mafinya.”

Choncho, tingati chisoni amachisonyeza kwambiri kumadera ena kuposa ena. Koma sitiyenera kuona kuti kusonyeza chisoni ndiponso kulira ndi chizindikiro cha kufooka. Ngakhale Yesu Kristu “analira” chifukwa cha imfa ya mnzake Lazaro, ngakhale kuti iye anali kudziŵa kuti amuukitsa posachedwa.—Yohane 11:35.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Yakobo sanachite manyazi kulilira mwana wake amene anasowa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena