Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 8/09 tsamba 29-31
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
  • Galamukani!—2009
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chalakwika N’chiyani Pachithunzichi?
  • Zithunzi Zoti Ana Apeze
  • Kuchokera M’magazini Ino
  • Kodi Mukudziwa Chiyani Zokhudza Woweruza Ehudi?
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2009
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2009
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2009
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Galamukani!—2009
g 8/09 tsamba 29-31

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Chalakwika N’chiyani Pachithunzichi?

Werengani Machitidwe 3:1-10. Ndiyeno yang’anani chithunzichi. Kodi n’chiyani chalakwika? Lembani mayankho anu m’mizere ili m’munsiyi.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

KAMBIRANANI:

N’chifukwa chiyani atumwi ankachita zozizwitsa? Kodi zimenezi zikusonyeza kuti m’tsogolomu mudzachitika chiyani?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Chivumbulutso 21:3, 4; 22:2.

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pachithunzi chilichonse.

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 5 Kodi chimachitika n’chiyani mnyamata kapena mtsikana akaphunzitsidwa bwino kuyambira ali mwana? Miyambo 22:․․․

TSAMBA 5 Kodi Mulungu anapanga chiyani kuchokera mwa munthu mmodzi? Machitidwe 17:․․․

TSAMBA 11 Kodi mawu abwino amathandiza bwanji? Miyambo 12:․․․

TSAMBA 23 Kodi ndani amakhala wamkulu pakati pa Akhristu? Luka 9:․․․

Kodi Mukudziwa Chiyani Zokhudza Woweruza Ehudi?

Werengani Oweruza 3:12-30. Ndiyeno yankhani mafunso otsatirawa.

4. ․․․․․

Kodi anachokera fuko liti?

5. ․․․․․

Kodi iye anapulumutsa Aisiraeli kwa wolamulira uti?

6. ․․․․․

Zoona kapena zonama? Anakhala ndi moyo Mfumu Davide isanabadwe.

KAMBIRANANI:

Werengani Oweruza 3:15, 28. N’chifukwa chiyani Yehova anasankha Ehudi? Kodi Ehudi anatamanda ndani zinthu zitamuyendera bwino kunkhondo? Kodi muyenera kuchita chiyani mukamakumana ndi mavuto, ndipo n’chifukwa chiyani?

◼ Mayankho ali patsamba 29

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Petulo ndi Yohane anali pomwepo.

2. Munthuyo anali wolumala, osati wosaona.

3. Munthu wolumalayo anali pafupi ndi chipata cha pakachisi osati m’dziko lomweli.

4. Benjamini, Oweruza 3:15.

5. Egiloni, Oweruza 3:14.

6. Zoona.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena