Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/10 tsamba 3
  • Kodi Nthawi Imakucheperani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nthawi Imakucheperani?
  • Galamukani!—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Vuto Limene Limakhalapo: Kupanikizika
    Galamukani!—2015
  • Kodi Ndingachitenji ndi Homuweki Yochuluka Motero?
    Galamukani!—1993
  • Mfundo 20 Zothandiza Kuti Muzikhala ndi Nthawi Yokwanira
    Galamukani!—2010
  • Mangani Moyo Wanu pa Utumiki wa Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—2010
g 4/10 tsamba 3

Kodi Nthawi Imakucheperani?

NGATI mwachonga bokosi lachiwiri kapena lachitatu pa mafunso omwe ali kumanjaku, ndiye kuti nthawi imakucheperani. Ndipo dziwani kuti simuli nokha. Pafupifupi kulikonse padzikoli, anthu amapanikizika kuchita zinthu zambiri ngakhale kuti zina n’zosawakhudza n’komwe. Zikhoza kukhala zinthu monga kukonza galimoto, kuchita zimene bwana wanena komanso zinthu zina zosayembekezereka. Pofuna kuchita zinthu zonsezi, mungadzione kuti zimakuvutani kugwiritsa ntchito bwino nthawi. Mungayambenso kuona kuti palibe chimene mukuchita.

Komabe mwina mumaona kuti simuchedwa kuthana nazo zinthuzo ndipo muyambanso kukhala ndi nthawi yokwanira yochita zinthu zofunika kwambiri, zothandiza inuyo, banja lanu ndiponso anzanu. Koma kodi nthawi imeneyi mudzaipeza liti? Kodi mukuona kuti muyamba kupeza mpata liti? Lero, mlungu uno kapena mwezi wamawa?

Kunena zoona, n’zovuta kuti zinthu zisinthe zokha padzikoli. Koma inuyo ndi amene mungapangitse kuti muzikhala ndi nthawi yokwanira. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

[Bokosi patsamba 3]

Kodi mumakhala ndi mpata wochita zinthu zofunika kwambiri?

◯ Ndimakhala nawo tsiku lililonse

◯ Ndimakhala nawo kumapeto kwa mlungu uliwonse

◯ Sindipeza mpata

Kodi tsiku lililonse

◯ Mumakwanitsa kuchita zimene munaganiza kuti muchite?

◯ Mumalephera kukukwaniritsa zolinga zanu chifukwa chakuti nthawi zambiri mumatanganidwa ndi ntchito?

◯ Mumasiya nthawi yomweyo zimene mukuchita kuti mukachite zinthu zina zogwa mwadzidzidzi?

Kodi tsiku lililonse mumaona kuti

◯ Mumachita zinthu popanda kupanikizika?

◯ Anthu ena amakupanikizani ndi zinthu zosafunika?

◯ Muli ndi ntchito yambiri yoti muchite?

Kodi tsiku likamatha, mumaona kuti

◯ Mwakwanitsa kuchita zinthu zofunika zimene mumafuna kuchita?

◯ Mwamaliza ntchito yanu, ngakhale kuti simunaigwire bwino?

◯ Munalibe nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri kwa inu?

Kodi nthawi zambiri mumamva bwanji tsiku likamatha?

◯ Ndimaona kuti zonse zayenda bwino

◯ Ndimakhala kuti ndatoperatu

◯ Palibe chomwe ndachita chaphindu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena