Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 3/13 tsamba 14-15
  • Robert Boyle

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Robert Boyle
  • Galamukani!—2013
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ANKAKONDA KWAMBIRI SAYANSI
  • ANKAKHULUPIRIRA MULUNGU
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2013
  • Baibulo la Bedell
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kusalolerana Zipembedzo Lerolino
    Galamukani!—1999
  • Magwero Apadera a Nzeru Yapamwamba
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
Onani Zambiri
Galamukani!—2013
g 3/13 tsamba 14-15

ZITHUNZI ZAKALE

Robert Boyle

Anthu ambiri okonda kuphunzira za mbiri yakale amamudziwa Robert Boyle kuti ndi wasayansi amene anatulukira zambiri zokhudza mmene gasi amagwirira ntchito. Asayansi ambiri akhala akutulukira zinthu zambiri potengera zimene Boyle anatulukirazi. Boyle ankadziwikanso kuti ankakhulupirira kuti kuli Mulungu komanso ankakhulupirira Mawu ake, Baibulo.

BOYLE anabadwa m’chaka cha 1627. Anabadwira m’banja lolemera ku nyumba yachifumu ya ku Lismore, m’dziko la Ireland. Imeneyi inali nthawi yomwe asayansi ena anayamba kufufuza zinthu n’cholinga choti anthu asamangokhulupirira zinthu zopanda umboni. Boyle anali m’gulu la asayansi amenewo. Moti pofotokoza za moyo wake ali wamng’ono ananena kuti anadzipatsa yekha dzina lakuti “Philaretus” kutanthauza kuti “Wokonda Choonadi.”

Boyle ankati akafufuza zinthu zinazake zatsopano, ankakonda kuuza aliyense zomwe watulukira. Iye analemba mabuku ambirimbiri ndipo zimene analembazo zinathandiza asayansi ambiri a m’nthawi yake, kuphatikizapo wasayansi wodziwika kwambiri, Sir Isaac Newton. M’chaka cha 1660, Boyle anakhala m’modzi mwa anthu amene anayambitsa bungwe lasayansi lotchedwa Royal Society, lomwe lidakalipo mpaka pano mu mzinda wa London m’dziko la England.

ANKAKONDA KWAMBIRI SAYANSI

Ena amakhulupirira kuti Boyle ndi amene anayambitsa sayansi yokhudza mmene zinthu zimapangidwira. Koma iye ankachita zosiyana ndi zimene asayansi ambiri ankachita nthawi imeneyo. Asayansi ambiri ankati akatulukira zinazake, ankazibisa kapena kuzilemba m’njira yoti anthu odziwa sayansi okha ndi amene angazimvetse, pomwe Boyle ankafalitsa zimene watulukira. Komanso m’malo mongokhulupirira zimene anthu ena ankanena, iye ankafufuza bwinobwino kenako n’kutsimikizira zoona zake.

Zimene Boyle anafufuza zinasonyeza kuti mfundo yoti chinthu chilichonse chinapangidwa ndi tizinthu ting’onoting’ono tolumikizana mosiyanasiyana ndi yoona.

Mfundo yoti asayansi asamangokhulupirira zinthu asanafufuze, anailemba m’buku lake lodziwika bwino lakuti The Sceptical Chymist. M’bukuli analembamonso kuti asayansi asamangokakamira mfundo zawo komanso azivomereza akalakwitsa. Iye analimbikitsanso asayansi ena omwe ankakakamira kuti mfundo zawo ndi zolondola, kuti azitha kusiyanitsa pakati pa zimene akudziwa kuti ndi zoona ndi zimene akungoganiza kuti ndi zoona.

Boyle analimbikitsa asayansi ena omwe ankakakamira kuti mfundo zawo ndi zolondola kuti azitha kusiyanitsa pakati pa zimene akudziwa kuti ndi zoona ndi zimene akungoganiza kuti ndi zoona.

ANKAKHULUPIRIRA MULUNGU

Boyle ankafufuzanso pa nkhani zokhudza Mulungu. Atafufuza za zinthu zodabwitsa zachilengedwe anayamba kukhulupirira kuti payenera kukhala winawake amene anazilenga. Zimenezi zinachititsa kuti asamagwirizane ndi anthu amene ankadziona ngati anzeru omwe ankakhulupirira kuti kulibe Mulungu. Boyle ananena kuti munthu wanzeru zake sanganene kuti kulibe Mulungu.

Komabe, Boyle ankaona kuti munthu payekha sangadziwe zoona pa nkhani zokhudza Mulungu. Ankaona kuti ndi Mulungu amene angamuthandize kuti adziwe zoona zake. Iye ananena kuti Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo, ndi amene angatithandize kudziwa zoona za Mulunguyo.

Boyle ankamva chisoni chifukwa anthu ambiri sankadziwa zimene Baibulo limanena komanso ankangokhulupirira chilichonse chimene awauza kutchalitchi kwawo popanda umboni. Iye ankadabwa kuti, “Zingatheke bwanji kuti munthu azingokhulupirira zinazake chifukwa chotengera makolo ake.” Zimenezi zinachititsa kuti Boyle ayambe kufunafuna njira zothandizira anthu kulidziwa bwino Baibulo.

Choncho, Boyle anapereka ndalama zothandizira pa ntchito yomasulira Baibulo m’zinenero zambiri. Zina mwa zinenero zimenezi zinali Chiarabu, Chiairishi, Chimalaya, Chitheki ndi zinenero zina za ku North America. Robert Boyle anali munthu wanzeru koma wodzichepetsa. Iye ankafunitsitsa kudziwa zoona pa nkhani ina iliyonse komanso ankafunitsitsa kuthandiza anthu ena kuti nawonso adziwe zoona.

DZIWANI IZI:

  • Robert Boyle anabadwa mu 1627 ku Ireland.

  • Amadziwika kuti ndi amene anayambitsa sayansi yoona mmene zinthu zosiyanasiyana zimapangidwira, ndipo akatswiri a masiku ano amatsatira zimene iye anayambitsa.

  • Anali wasayansi woyamba kufotokoza mwatsatanetsatane ndi kufalitsa njira zimene ankagwiritsa ntchito akafuna kutulukira zinthu zatsopano.

  • Sir Isaac Newton, yemwe anali wasayansi, ankatengera nzeru za Robert Boyle.

  • Anathandiza kuti Baibulo limasuliridwe m’zinenero zosiyanasiyana.

  • Anamwalira m’chaka cha 1691, ku England, ali ndi zaka 64.

ANATHANDIZA KUTI BAIBULO LIMASULIRIDWE M’CHIAIRISHI

Robert Boyle ankadziwa kuti mu 1573, panali anthu enaake omwe anayamba kumasulira Baibulo m’Chiairishi. Mu 1602, anthuwa anatulutsa Chipangano Chatsopano m’Chiairishi. Kenako, mu 1640, anamaliza kumasulira Malemba Achiheberi, omwe amadziwika kuti Chipangano Chakale, m’Chiairishi, koma anasindikiza mu 1685. Ntchitoyi inatheka Boyle atapereka ndalama zothandizira kuti lisindikizidwe. N’zochititsa chidwi kuti mabuku onse owonjezera a m’Baibulo anamasuliridwanso m’chinenerochi. Mabaibulo ena amakhala ndi mabuku amenewa ndipo amawaphatikiza ndi Baibulo n’kukhala buku limodzi. Komabe, Boyle anakana kufalitsa mabuku amenewa chifukwa ankaona kuti ndi abodza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena