Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g18 No. 3 tsamba 6-13
  • Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa​—Zimene Mungachite Panopa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa​—Zimene Mungachite Panopa
  • Galamukani!—2018
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • 1: MUZICHEZA NDI ACHIBALE KOMANSO ANZANU
  • 2: MUZIDYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI KOMANSO KUCHITA MASEWERA OLIMBITSA THUPI
  • 3: MUZIGONA MOKWANIRA
  • 4: MUZIUZA ENA MMENE MUKUMVERA
  • 5: MUZIPEWA ZINTHU ZOMWE ZINGAWONONGE THANZI LANU
  • 6: MUZIPEZA NTHAWI YOCHITA ZINTHU ZINA
  • 7: MUZICHITA ZINTHU MMENE MUNKACHITIRA POYAMBA
  • 8: MUSAMAPUPULUME POSANKHA ZOCHITA PA NKHANI ZIKULUZIKULU
  • 9: MUZIKUMBUKIRA MALEMUYO
  • 10: MUTHA KUCHOKAPO KWA MASIKU ANGAPO
  • 11: MUZITHANDIZA ANTHU ENA
  • 12: MUZIONANSO BWINO ZIMENE MUMACHITA
  • Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa | Mfundo Zachidule
  • Kodi Ndingakhale Motani ndi Chisoni Changa?
    Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira
  • “Kodi Ndingakhale Bwanji ndi Chisoni Changa?”
    Galamukani!—1988
  • Mfundo Zothandiza Amene Aferedwa
    Galamukani!—2018
  • N’chiyani Chingakuthandizeni Ngati Mwaferedwa?
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—2018
g18 No. 3 tsamba 6-13
Anthu ali kunyanja, ena akuulutsa kayiti ndipo ena akujambulana

MFUNDO ZOTHANDIZA AMENE AFEREDWA

Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa—Zimene Mungachite Panopa

Pali malangizo ambirimbiri othandizira anthu omwe aferedwa ndipo ena amakhala othandiza kuposa ena. Mwina zimenezi zili choncho chifukwa monga tinafotokozera poyamba paja, anthufe timasonyeza chisoni mosiyanasiyana. Choncho zomwe zingakhale zothandiza kwa wina sizingakhale zothandizanso kwa wina.

Komabe pali mfundo zina zomwe anthu ambiri anaziona kuti n’zothandiza. Mfundozi ndi zomwe kawirikawiri akatswiri othandiza anthu omwe aferedwa, amapereka ndipo zimagwirizana kwambiri ndi mfundo za m’Baibulo.

1: MUZICHEZA NDI ACHIBALE KOMANSO ANZANU

  • Anthu ali kunyanja, ena akuulutsa kayiti ndipo ena akujambulana

    Akatswiri ena amaona kuti njira imeneyi ndi yabwino kwambiri ukafuna kuchepetsa chisoni. Komabe nthawi zina mungaone kuti ndi bwino kungokhala panokha. Mwinanso anthu ena akamakuthandizani mungamamve ngati akungokutopetsani. Umu ndi mmenenso ena amamvera.

  • Musaganize kuti mukufunika kukhala limodzi ndi anzanu nthawi zonse. Komanso sibwino kuwathamangitsa chifukwa nthawi ina mudzafuna thandizo lawo. Choncho muziwauza mwaulemu zimene mukufuna ndi zimene simukufuna pa nthawiyo.

  • Muyenera kugawa bwino nthawi yokhala ndi anzanu komanso yochita zinthu panokha mogwirizana ndi mmene mukumvera.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Awiri amaposa mmodzi . . . Ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.”​—Mlaliki 4:9, 10.

2: MUZIDYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI KOMANSO KUCHITA MASEWERA OLIMBITSA THUPI

  • Zakudya za magulu onse zingakuthandizeni kuti muthe kupirira mukakhala ndi chisoni. Muzidya zipatso, ndiwo zamasamba komanso zakudya zokhala ndi mapulotini.

  • Muzimwa madzi ambiri komanso zakumwa zina zopatsa thanzi.

  • Mukaona kuti simukulakalaka kudya, muzingodya pang’ono koma pafupipafupi. Mukhozanso kupempha a dokotala kuti akupatseni mankhwala othandiza kubwezeretsa zofunika m’thupi.a

  • Muziyenda mwandawala kapena kuchita masewera enaake olimbitsa thupi kuti muchepetseko nkhawa. Nthawi zina kuchita masewera olimbitsa thupi kungakupatseni mpata woganizira za womwalirayo kapenanso zinthu zina.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”​—Aefeso 5:29.

3: MUZIGONA MOKWANIRA

  • Bedi

    Nthawi zonse kugona mokwanira n’kofunika kwambiri makamaka kwa anthu amene aferedwa. Tikutero chifukwa chisoni chimapangitsa munthu kumva kutopa mwachilendo.

  • Musamamwe kwambiri khofi kapena mowa chifukwa zakumwa zimenezi zimachititsa kuti munthu azisowa tulo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”​—Mlaliki 4:6.

4: MUZIUZA ENA MMENE MUKUMVERA

  • Mkazi amene anaferedwa akulankhula ndi mnzake

    Muzikumbukira kuti anthufe timamva chisoni mosiyanasiyana. Ndiyeno mumafunika kudziwa njira yomwe ingakuthandizeni inuyo.

  • Anthu ena akakhala ndi chisoni amaona kuti amamvako bwino akauza ena mmene akumvera. Pomwe ena amaona kuti imeneyi si njira yabwino. Koma akatswiri ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Mukaona kuti mukufunika kuuza winawake mmene mukumvera koma mukukayikakayika, mukhoza kuyamba ndi kufotokoza zinthu zing’onozing’ono kwa mnzanu yemwe mumamudalira.

  • Anthu ena amaona kuti kulira kumawathandiza kuti achepetseko chisoni pamene ena sachita kufunika kuti alire kwambiri.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Mtima umadziwa kuwawa kwa moyo wa munthu.”​—Miyambo 14:10.

5: MUZIPEWA ZINTHU ZOMWE ZINGAWONONGE THANZI LANU

  • Bambo akumwa mowa

    Anthu ena akaferedwa amaganiza kuti kumwa mowa kwambiri komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kungawachepetsere nkhawa. Komatu zimenezi zimawononga thanzi lawo. Mtendere womwe amapezawo umangokhala wa kanthawi kochepa koma pamapeto pake zimawabweretsera mavuto aakulu. Choncho mukakhala ndi nkhawa muzipeza njira zabwino zomwe zingakuthandizeni.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi.”​—2 Akorinto 7:1.

6: MUZIPEZA NTHAWI YOCHITA ZINTHU ZINA

  • Ena amaona kuti zimakhala zothandiza kuti pa nthawi imene ayamba kumva kwambiri chisoni, azichita zinazake zomwe zingawachititse kuti asamaganizire kwambiri za malemuyo.

  • Mukhozanso kuchepetsako nkhawa mukamacheza ndi anzanu, kupeza anthu atsopano ocheza nawo, kuphunzira zinthu zatsopano komanso kuchita zinthu zina zosangalatsa.

  • Nthawi ikamadutsa zinthu zimasintha ndipo mudzaona kuti mwayamba kuiwalako moti zikhoza kumakutengerani kanthawi kuti muyambirenso kuganizira za womwalirayo. Zikatere ndiye kuti chisoni chanu chayamba kuchepa.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chilichonse chili ndi nthawi yake, . . . Nthawi yolira ndi nthawi yoseka. Nthawi yolira mofuula ndi nthawi yodumphadumpha mosangalala.”​—Mlaliki 3:1, 4.

7: MUZICHITA ZINTHU MMENE MUNKACHITIRA POYAMBA

  • Mayi watenga kalendala ndipo akulemba zomwe akufuna azichita

    Musachedwe kuyambanso kuchita zinthu ngati kale.

  • Mukayambiranso kugona pa nthawi imene munkagona poyamba, kugwira ntchito komanso kuchita zinthu zina zomwe munkachita, sizingakuvuteni kuti muyambirenso kuzolowera.

  • Mukamatanganidwa ndi kuchita zinthu zofunika, mudzachepetsa chisoni chanu.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pakuti zowawa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukira kawirikawiri, chifukwa Mulungu woona akuchititsa kuti mtima wake uzisangalala.”​—Mlaliki 5:20.

8: MUSAMAPUPULUME POSANKHA ZOCHITA PA NKHANI ZIKULUZIKULU

  • Anthu ambiri amene amasankha zochita pa nkhani zikuluzikulu wokondedwa wawo atangomwalira kumene, amadzanong’oneza bondo.

  • Ngati n’kotheka muzidikira kaye kuti padutse nthawi yokwanira musanasamuke, kusintha ntchito yomwe munkagwira, kuwononga kapena kupatsa ena katundu wa malemuyo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira, koma aliyense wopupuluma, ndithu adzasauka.”​—Miyambo 21:5.

9: MUZIKUMBUKIRA MALEMUYO

  • Bambo akuonetsa anzake zithunzi za mkazi wake amene anamwalira

    Anthu ambiri omwe anaferedwa, amamvako bwino akamachita zinthu zomwe zimawathandiza kukumbukira womwalirayo.

  • Zikhozanso kukuthandizani ngati mutasunga zithunzi komanso zinthu zina kuti muzikumbukirabe malemuyo. Mungakhalenso ndi buku loti muzilembamo nkhani zomwe mukufuna kuti muzizikumbukira.

  • Mungasungenso zinthu zomwe zingamakukumbutseni zinthu zabwino zokhudza malemuyo kuti mudzazione nthawi ina mtima ukadzakhala m’malo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kumbukirani masiku akale.”​—Deuteronomo 32:7.

10: MUTHA KUCHOKAPO KWA MASIKU ANGAPO

  • Mukhoza kukonza zoti mukapitidweko mphepo kwinakwake.

  • Ngati simungakwanitse kupita kwinakwake kwa masiku angapo, mukhoza kungochita zinthu zina zoti musangalale nazo kwa tsiku limodzi kapena awiri. Mwina mungapite kunyanja kapena kukaona malo enaake.

  • Ndipotu ngakhale kungochita zinthu zina zosiyana ndi zomwe mumachita nthawi zonse, kungakuthandizeni kuchepetsako chisoni.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”​—Maliko 6:31.

11: MUZITHANDIZA ANTHU ENA

  • Mtsikana akuthandiza mayi wachikulire kugula zinthu kumsika

    Muzikumbukira kuti nthawi iliyonse imene mukuthandiza ena, nanunso mumasangalala.

  • Mungayambe ndi kuthandiza anthu enanso omwe akhudzidwa ndi imfa ya wokondedwa wanuyo, monga achibale ndi anzanu.

  • Mukathandiza ena komanso kuwalimbikitsa pa nthawi yomwe muli ndi chisoni, zingakuthandizeni kuti muyambirenso kusangalala.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

12: MUZIONANSO BWINO ZIMENE MUMACHITA

  • Mukaferedwa, mumakhala ndi mpata woganizira zinthu zofunika kwambiri.

  • Muzipezeraponso mwayi woganizira zimene mumachita pa moyo wanu.

  • Ngati n’kotheka sinthani zina ndi zina zomwe mumachita.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ndi bwino kupita kunyumba yamaliro kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyerero, chifukwa amenewo ndiwo mapeto a anthu onse. Chotero munthu amene ali moyo aziganizira zimenezi mumtima mwake.”​—Mlaliki 7:2.

Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa | Mfundo Zachidule

  • 1: MUZICHEZA NDI ACHIBALE KOMANSO ANZANU

    Nthawi ina mukhoza kuchezako ndi anzanu komanso kukhalako panokha. Muzichita zinthu mogwirizana ndi mmene mukumvera.

  • 2: MUZIDYA ZAKUDYA ZOPATSA THANZI KOMANSO KUCHITA MASEWERA OLIMBITSA THUPI

    Ndi bwino kudya zakudya zopatsa thanzi, kumwa madzi okwanira komanso kuchitako masewera olimbitsa thupi.

  • 3: MUZIGONA MOKWANIRA

    Kugona mokwanira kumathandiza ngati munthu akumva kutopa chifukwa chosokonezeka maganizo ndi chisoni.

  • 4: MUZIMASUKA KUUZA ENA MMENE MUKUMVERA

    Popeza kuti anthufe timamva chisoni mosiyanasiyana, ndi bwino kudziwa njira yomwe ingakuthandizeni.

  • 5: MUZIPEWA ZINTHU ZOMWE ZINGAWONONGE THANZI LANU

    Musamamwe kwambiri mowa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo chifukwa zimenezi zimangowonjezera mavuto.

  • 6: MUZIPEZA NTHAWI YOCHITA ZINTHU ZINA

    Muzipeza nthawi yocheza ndi anzanu komanso yochitako zosangalatsa.

  • 7: MUZICHITA ZINTHU MMENE MUNKACHITIRA POYAMBA

    Muziyesetsa kuchita zinthu zomwe munkachita kale ndipo nthawi ikamapita mudzayambanso kuzolowera.

  • 8: MUSAMAPUPULUME POSANKHA ZOCHITA PA NKHANI ZIKULUZIKULU

    Ngati n’zotheka dikirani kaye kwa chaka kapena kuposerapo, musanasankhe zochita pa nkhani zikuluzikulu kuti musadzanong’oneze bondo.

  • 9: MUZIKUMBUKIRA MALEMUYO

    Muzilemba komanso kusunga zithunzi ndi zinthu zina zomwe zingakuthandizeni kuti muzikumbukirabe malemuyo.

  • 10: MUTHA KUCHOKAPO KAYE KWA MASIKU ANGAPO

    Muyenera kupeza nthawi yokachitako zinthu zina zosiyana ndi zomwe mumachita nthawi zonse kaya kwa tsiku limodzi kapena kwa maola angapo.

  • 11: MUZITHANDIZA ANTHU ENA

    Mungachepetseko chisoni pothandiza anthu enanso omwe angafunikire thandizo. Ena mwa anthuwa angakhalenso omwe akhudzidwa ndi imfa ya wokondedwa wanuyo.

  • 12: MUZIONANSO BWINO ZIMENE MUMACHITA

    Nthawiyi ingakupatseninso mpata woganizira zinthu zofunika kwambiri. Ngati n’kotheka mungathe kusintha zina ndi zina zomwe mumachita pa moyo wanu.

Kunena zoona, sizingatheke kuti chisoni chanu chidzatheretu. Komabe anthu ambiri amene okondedwa awo anamwalira, anapeza umboni woti kutsatira mfundo zoyenera monga zomwe zili m’nkhaniyi kumawathandiza kuti azisangalala. Ndipotu si kuti nkhaniyi yafotokoza njira zonse zomwe munthu angatsatire kuti achepetseko chisoni. Koma ngati mutayesa kugwiritsa ntchito mfundo zomwe zafotokozedwazi, mukhoza kuona kuti chisoni chanu chayamba kuchepa n’kuyambiranso kukhala osangalala.

a Magazini ya Galamukani! sisankhira anthu thandizo la mankhwala.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena