ZIMENE MUNGACHITE PA VUTO LA KUKWERA MITENGO KWA ZINTHU
Muzikhala Wopatsa
Ngati mukuvutika chifukwa cha kukwera mitengo kwa zinthu, mukhoza kuganiza kuti simungakhale wopatsa. Koma kukhala wopatsa kungakuthandizeni kuti musamavutike kwambiri ndi vuto la kukwera mitengo. N’zotheka ndithu kukhala wopatsa koma osawononga ndalama.
N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?
Kukhala wopatsa, ngakhale pa zinthu zing’onozing’ono, kumatithandiza kukhala wosangalala komanso kuti tisamadzikayikire. Ndipotu kafukufuku amasonyeza kuti kukhala wopatsa kumathandiza kuti tikhale ndi moyo wathanzi komanso tiziganiza bwino. Mwachitsanzo, zimathandiza kuti tisamade nkhawa, BP isakwere komanso tisamamve kuphwanya thupi. Kumatithandizanso kuti tizigona tulo tabwino.
Tikamapatsa anthu ena ndalama kapena zinthu zina, zimakhala zosavuta kuti tidzalandire thandizo tikadzafunikira. Howard, yemwe amakhala ku England, anati: “Tikamayesetsa kukhala opatsa komanso kuthandiza ena, ine ndi mkazi wanga sitiona kuti tikuvutitsa anthu ikafika nthawi yoti nawonso atithandize.” N’zoona kuti anthu amene amapereka zinthu kuchokera mumtima, sayembekezera kuti anthu adzawabwezere. Koma kupatsa kumawathandiza kuti apeze anzawo apamtima omwe angawathandize akavutika.
ZIMENE MUNGACHITE
Muzigawira ena zomwe muli nazo. Ngakhale mutakhala kuti mulibe zinthu zambiri, mukhoza kukhala ndi kenakake komwe mungagawire anthu ena. Mwachitsanzo, mukhoza kuwaitana kuti adzadye chakudya. Duncan ndi banja lake, omwe amakhala ku Uganda, ndi osauka koma ali ndi mtima wopatsa. Duncan anati: “Lamlungu, ine ndi mkazi wanga timakonda kuitana munthu kunyumba n’kudya naye chakudya chosafuna zambiri. Timasangalala kucheza ndi anthu.”
Komabe tiyenera kukhala osamala pa nkhani yopatsayi. Si bwino kumangopereka zinthu kwa ena mpaka banja lanu kumavutika.—Yobu 17:5.
Tayesani izi: Itanani munthu wina kunyumba kwanu kuti mudzadye naye chakudya chosafuna zambiri kapena kumwa naye zakumwa. Ngati muli ndi zinthu zomwe simuzigwiritsa ntchito, mukhoza kupatsa anzanu kapena maneba omwe angazigwiritse ntchito.
Mukhoza kukhala wopatsa m’njira zinanso. Mphatso zina zabwino kwambiri sitichita kugula. Mwachitsanzo, tingapatule nthawi yathu kuti tichite zinthu zina zothandiza anthu ena. Mawu abwino akhozanso kukhala mphatso. Choncho muziyamikira anthu ena komanso kuwauza kuti mumawakonda.
Tayesani izi: Thandizani anthu ena ntchito zapakhomo, kukonza zomwe zawonongeka kapena kukawagulira zinthu. Lembani khadi kapena meseji kwa mnzanu, ngakhale yongomuuza kuti mukumuganizira.
Mukakhala wopatsa, mumadalitsidwa kwambiri.