Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g25 No. 1 tsamba 10-11
  • Muzikhutira Ndi Zomwe Muli Nazo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzikhutira Ndi Zomwe Muli Nazo
  • Galamukani!—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?
  • ZIMENE MUNGACHITE
  • Kodi ‘Mwaphunzira Chinsinsi’ Chokhala Wokhutira?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Kodi Munthu Angakhaledi Wokhutira ndi Zimene ali Nazo?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Zimene Tingachite Kuti Tikhale Okhutira
    Galamukani!—2021
  • Kulimbana Ndi Mavuto a M’dziko Lokonda Kutaya Zinthu
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—2025
g25 No. 1 tsamba 10-11
Zithunzi: 1. Bambo waweruka kuntchito ya zomangamanga ndipo akumwetulira. 2. Kenako akusewera ndi ana ake awiri komanso galu ndipo mkazi wake akusangalala.

ZIMENE MUNGACHITE PA VUTO LA KUKWERA MITENGO KWA ZINTHU

Muzikhutira Ndi Zomwe Muli Nazo

Anthu amene amakhala okhutira amasangalala ndi zinthu zomwe ali nazo. Ndipo zinthu zikasintha, nawonso amasintha n’kuyamba kukhala moyo wogwirizana ndi mmene zinthu zilili.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?

Katswiri wina wamaganizo dzina lake Jessica Koehler ananena kuti anthu amene amakhala okhutira amakhala osangalala. Anapezanso kuti anthu oterewa, sachitira nsanje kwenikweni anzawo. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu amene amakhala okhutira sada nkhawa kwambiri. Ndipo ena mwa anthu amene amasangalala kwambiri ndi omwe alibe zinthu zambiri. Zili chonchonso makamaka kwa anthu amene amaona kuti kucheza ndi anthu am’banja lawo komanso anzawo n’kofunika kwambiri.

“Ngati tili ndi chakudya, zovala ndi pogona, tizikhala okhutira ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteyo 6:8.

ZIMENE MUNGACHITE

Muzipewa kudziyerekezera ndi ena. Mukamadziyerekezera ndi munthu wina amene akuoneka ngati akukhala moyo wawofuwofu, mukhoza kukhala wosakhutira komanso wansanje. N’kuthekanso kuti zimene mukuganizazo si zoona chifukwa munthu winayo akhoza kukhala kuti ali ndi ngongole yaikulu. Mayi wina wa ku Senegal dzina lake Nicole, ananena kuti: “Sikuti ndimafunika zinthu zambiri kuti ndikhale wosangalala. Ndikakhala wokhutira ndikhoza kumasangalala ngakhale kuti anthu ena ali ndi zambiri kuposa ineyo.”

Tayesani izi: Muzipewa otsatsa malonda komanso zinthu zomwe anthu amaika pamalo ochezera zomwe zimangosonyeza katundu komanso ndalama zimene anthu ena ali nazo.

“Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera mʼzinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.


Muziyamikira. Anthu amene amakhala ndi mtima woyamikira amakhala okhutira ndipo sakhala ndi maganizo oti akufunika kuchitiridwa zambiri. Roberton wa ku Haiti ananena kuti: “Ndimaganizira zinthu zabwino zimene ena andichitira ineyo komanso anthu am’banja langa ndipo kenako ndimawayamikira. Ndimaphunzitsanso mwana wanga wazaka 8 kuti akapatsidwa chilichonse, azithokoza.”

Tayesani izi: Tsiku lililonse muzilemba chinthu chimene mukufuna kuyamikira. Chikhoza kukhala moyo wathanzi, banja logwirizana, anzanu abwino kapenanso kulowa kwa dzuwa kokongola.

“Munthu amene ali ndi mtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.”—Miyambo 15:15.

Tonsefe nthawi zina timavutika kukhala okhutira ndi zomwe tili nazo. Koma kuchita zimenezi n’kothandiza. Tikasankha kukhala okhutira, timakhala osangalala, ndipo kusangalalako sitingakugule ndi ndalama.

Erik.

“M’banja lathu taphunzira kukhala okhutira ndipo zimenezi zatithandiza kwambiri. Zachititsa kuti tisamakhalenso otanganidwa ngati kale, tizikhala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu limodzi komanso tizisangalala ndi zinthu zomwe tili nazo.”—Erik, U.S.A.

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena