ZIMENE MUNGACHITE PA VUTO LA KUKWERA MITENGO KWA ZINTHU
Muzigwiritsa Ntchito Bwino Ndalama Zanu
Tonsefe timavutika ndi kukwera mitengo kwa zinthu. Koma sikuti tilibiretu mtengo wogwira. Pali zinthu zina zimene mungachite kuti zinthu ziziyendako bwino.
N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?
Ngati simungagwiritse ntchito ndalama zanu mwanzeru, ndalamazo zikhoza kutha mosadziwika bwino ndipo izi zingakuwonjezereni nkhawa. Ngakhale zitakhala kuti mumapeza ndalama zochepa, pali zinthu zina zimene mungachite zomwe zingakuthandizeni.
ZIMENE MUNGACHITE
Muzikhala moyo wogwirizana ndi ndalama zimene mumapeza. Mukamachita zimenezi, mtima wanu uzikhala m’malo ndipo simungavutike ngati patagwa zadzidzidzi.
Kuti musamagwiritse ntchito ndalama zambiri kuposa zimene mumapeza, muyenera kukhala ndi bajeti. Mukamakonza bajetiyo, muziganizira zinthu zofunika kwambiri. Ndiye muziyesetsa kutsatira bajeti yanuyo, ndipo muzisintha ngati mitengo ya zinthu yakwera kapena ngati ndalama zimene mumapeza zasintha. Ngati muli pa banja, muzikambirana ndi mwamuna kapena mkazi wanu mukamapanga bajeti.
Tayesani izi: Ngati n’zotheka, muzipewa kugula zinthu pa ngongole. Anthu ambiri amaona kuti kuchita zimenezi kumawathandiza kuti azigula zinthu zomwe zili pabajeti komanso azipewa ngongole. Komanso muzipeza nthawi yoona masitetimenti anu akubanki. Kudziwa ndalama zimene mwatsala nazo kungakuthandizeni kuti muchepetse nkhawa.
Kukhala moyo wogwirizana ndi ndalama zimene mumapeza kungakhale kovuta. Koma kukhala ndi bajeti yabwino kungakuthandizeni kwambiri. Kungakuthandizeninso kuti musamangokhalira kudera nkhawa nkhani zokhudza ndalama.
Muzichita zinthu mosamala kuti musachotsedwe ntchito. Kodi mungatani kuti musachotsedwe ntchito? Zina zomwe mungachite ndi izi: Muzifika kuntchito pa nthawi yake ndipo muzikhala ndi maganizo oyenera okhudza ntchito yanu. Muzithandiza ena, muzilimbikira ntchito, muzichita zinthu mwaulemu, muzitsatira malamulo a ntchito yanu komanso muziwonjezera luso lanu.
Muzipewa kuwononga ndalama. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimawononga ndalama pa zinthu zosathandiza?’ Mwachitsanzo, anthu ena amawononga ndalama zomwe azivutikira, pa zinthu monga kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, juga, kusuta kapena kumwa mowa mwauchidakwa. Makhalidwe amenewa akhozanso kuwononga thanzi la munthu komanso kuchititsa kuti achotsedwe ntchito.
Muzisunga ndalama kuti mudzagwiritse ntchito pa zinthu zadzidzidzi. Ngati mungathe, muzisunga ndalama zoti mudzagwiritse ntchito pa zinthu zadzidzidzi. Ndalama zimenezo zingathandize kuti musade nkhawa kwambiri ngati inuyo kapena munthu wina wa m’banja lanu atadwala, mutachotsedwa ntchito kapena patachitika vuto lina losayembekezereka.