ZIMENE MUNGACHITE PA VUTO LA KUKWERA MITENGO KWA ZINTHU
Zinthu Zina Zimafunika Kungovomereza
Mitengo ya zinthu ikamakwera pang’onopang’ono mwina sitingazindikire, makamaka ngati malipiro athunso akukwera. Koma ngati mitengo yakwera kamodzin’kamodzi ndipo malipiro athu sanasinthe, tingayambe kuda nkhawa, makamaka ngati tili ndi banja.
Sitingaletse kuti zinthu zisakwere. Koma kungovomereza kuti zinthu zakwera mitengo, kungatithandize.
N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?
Anthu amene amadziwa kuti sangaletse kukwera mitengo kwa zinthu, savutika . . .
kukhalabe odekha. Tikakhala odekha, timaganiza bwino komanso timasankha zinthu mwanzeru.
kupewa kuchita zinthu zosathandiza. Mwachitsanzo, zingakhale zosathandiza kuzemba kulipira mabilu kapena kuwononga ndalama pa zinthu zosafunika.
kupewa kukangana ndi anthu am’banja lathu pa nkhani za ndalama.
kupeza njira zothandiza kupirira vutoli zomwe zingaphatikizepo kugwiritsa ntchito ndalama zochepa komanso kuona zinthu zimene tikufunikadi kugula.
ZIMENE MUNGACHITE
Muzikhala okonzeka kusintha. Zinthu zikakwera mitengo, ndi nzeru kuchepetsa zimene timagula, ngati zingatheke. Anthu ena amafuna kuti azikhalabe moyo wapamwamba kuposa ndalama zimene amapeza. Choncho amakhala ngati akuyesa kusambira mumtsinje umene madzi ake akuthamanga kwambiri. Kuchita zimenezi kumangowatopetsa. Ngati muli ndi banja, muyenera kuti mumadera nkhawa za mmene mungapezere zofunika pa moyo za banja lanu ndipo izi n’zomveka. Koma kumbukirani kuti anthu am’banja lanu amafuna chikondi chanu komanso nthawi yanu kuposa china chilichonse.
Kufuna kumakhalabe moyo wapamwamba zinthu zitakwera mtengo, kuli ngati kuyesa kusambira mumtsinje umene madzi ake akuthamanga kwambiri