Mutu 22
Kulambira Koona—Njira ya Moyo
1. Kodi ndi ciyembekezo cotani cimene ciri patsogolo pathu tsopano, koma kodi nciani cimene tiyenera kucicita kuti ticigwiritsitse?
CIYEMBEKEZO ca kukhala ndi moyo kwamuyaya m’kulamulira kwa ufumu wa Mulungu ciri pamaso panu. Monga momwe mwaonera, ciyembekezo cimeneci cazikidwa kwakukurukuru pa coonadi ca Mau a Mulungu mwiniyo. Kuli kothekera kuti inuyo mungaupeze uwo ngati inu mumamkondadi Mulungu ndi kumlambira iye mwa “kumayenda m’coonadi.”—2 Yohane 1-4.
2. Kodi kulambira koona kunadziwidwa mwa dzina lotani pakati pa Akristu oyambirira? Ncifukwa ninji?
2 Kulambira koona kumatanthauza zambiri koposa kungodziwa coonadi kokha. Kumatanthauza zambiri koposa kumangocilankhula ndi kumangocilalikira coonadico kwa ena. Kumatanthauza kucikhulupirira ndi kumacita mogwirizana ndi coonadico, “kumayenda m’coonadi” mwa kumacigwiritsira ico nchito m’miyoyo yathu tsiku ndi tsiku. (Yakobo 1:22-25) Kulambira koona kunaisonkhezera kwambiri miyoyo ya Akristu oyambirira kwakuti kunadziwidwa kukhala “Njirayo” ndiponso “njira ya coonadi.” (Macitidwe 9:2; 2 Petro 2:2) Iri “njira” yosonyezedwa ndi Mulungu yakuti alambiri onse oona akhale mogwirizana nayo pamene iwo akucimenyera nkhondo colinga cao ca moyo wamuyaya.
3. Ncifukwa ninji tiyenera kugwiritsira nchito coonadi ca Mau a Mulungu m’mbali iriyonse ya moyo?
3 Cotero, kulambira kwathu Yehova Mulungu sikungakhale kanthu kena kosiyana ndi mbali yinayo ya moyo wathu. Koma, tiyenera kugwiritsira nchito coonadi ca Mau ace m’mbali iriyonse ya moyo. “Mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31; onaninso Akolose 3:17) Macitidwe athu alionse ayenera kugwirizana ndi coonadi ca Mau a Mulungu, ndipo motero kupereka ulemerero kwa Mulungu. Ici cidzakhala kaamba ka cimwemwe cathu cokhalitsa. Maprinsipulo olungama a Mau ace samasintha mogwirizana ndi malo kumene munthuyo amakhalako kapena mikhalidwe ya munthuyo. Iwo nthawi zonse amakhala oona, nthawi zonse oyenera.—Salmo 119:142 [118:142, Dy].
4. Kodi nciani cimene cikuphatikizidwamo m’kumaubvala umunthu watsopano?
4 Ngati mumakucitadi kulambira koona, kodi kudzatanthauzanji kwa inu tsopano? Uko kudzaupangitsa moyo wanu wonse kugwirizana ndi njira ya Mulungu. Mau ace amatiuza ife kuti: “Mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, . . . koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimubvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’cilungamo, ndi m’ciyero ca coonadi.” (Aefeso 4:22-24) Kubvala umunthu watsopano kumatanthauza kukusiya kulankhula kotukwana ndi konama ndi kuyamba kumalankhula zolongosoka ndi zoona. Kumatanthauza kusiya kuledzera ndi cigololo ndi kumakhala ndi khalidwe loongoka ndi lolemekezeka. Kumatanthauza kusiya dyera, ndi kumakukulitsa kupanda dyera ndi kuolowa manja.—Akolose 3:5-10.
5. Kodi kuli kothekera kuisonyeza mikhalidwe yaumulungu pa nthawi zonse? Motani?
5 Ha, ndi motani nanga mmene kukhalira kotonthoza maganizo pamene mikhalidwe yaumulungu ikusonyezedwa kwa anthu amene munthuyo amakumana nawo tsiku ndi tsiku—kwa apabanja lace, kwa atsamwali ace ocitira nawo bizinesi limodzi, kwa mabwenzi ace a pamtima ndi alendo! (Akolose 3:12-14, 18-23) Koma, kodi mukukulingalira uko kukhala kobvuta kukupanga kusintha kumeneku, ndi kukucirikiza uko tsiku ndi tsiku? Mwa cithandizo ca mzimu wa Mulungu inu mungacite. Kupyolera mwa kulambira koona inu mungazibale zipatso zodabwitsa za mzimu wa Mulungu m’moyo wanu.—Agalatiya 5:19-24.
6. (a) Kodi ndi motani mmene kulambira koona kumakuyambukirira kumazipanga zosankha kwa munthu? (b) Talongosolani za mmene kulambira koona kumaiyambukirira nchito ya Mkristu ndi masewera ace.
6 Pamene kulambira koona kumafikira kukhala njira yanu ya moyo uko kudzakhala citsogozo canu cosalekeza. Pa kumazipanga zosankha, zazikuru kapena zazing’ono, inu mudzaphunzira kudzifunsa nokha kuti: “Kodi nciani cimene cidzakhala comkondweretsa Yehova Mulungu? Kodi nciani cimene maprinsipulo a m’Mau ace amasonyeza kukhala kacitidwe koyenera ndi kanzeru? (Salmo 119:105 [118:105, Dy]; Miyambo 3:1-6) Mwacitsanzo, Mkristu woona adzakhala wodera nkhawa kuti nchito yace yakuthupi siinayenera kuudodometsa utumiki wace wa kwa Yehova Mulungu, kapena iyo iri imene imaphatikizapo macitacita amene Baibulo limawakana. (Ahebri 13:5, 18; Yesaya 2:3, 4; Cibvumbulutso 18:4) Ngakhale pamene tifika pa nkhani ya kusewera, Mau a Mulungu ayenera kutsogolerapo m’kumacisankha cinthu colimbikitsa, coyera. (Afilipi 4:8) Palibe cinthu ciriconse m’moyo wanu cimene sicidzakhala cosonkhezeredwa mu njira yopindulitsa ndi kulambira koona.
MFUPO YACIMWEMWE KAAMBA KA CIPIRIRO
7. (a) Kodi ncifukwa ninji kungakhale kobvuta kupitirizabe kumayenda “m’njira ya coonadi”? (b) Pamene mukumana ndi citsutso, kodi kacitidwe koyenera ndi kotani, malinga ndi kunena kwa Ahebri 10:36?
7 Komabe, cifukwa ca zitsenderezo zimene dziko limazidzetsa pa Akristu olimba, kungakhale kobvuta kupitirizabe kumayenda mokhulupirika mu “njira ya coonadi.” Yesu anacenjeza kuti Akristu oona adzadedwa ndi kuzunzidwa, monga momwe iye adacitidwira. (Yohane 15:18-20; 2 Timoteo 3:12) Zocitika zingabuke zimene zimapereka upandu wa kukudodometsa kuphunzira kwanu Baibulo kokhazikika kapena kusonkhana kwanu ndi Akristu anzanu pa misonkhano ya mpingo. Citsutso cingaipangitse nchito ya kulalikira kukhala yobvuta, ngakhale yaupandu. Kodi nciani cimene mudzacita? Baibulo limapereka uphungu wakuti: “Pakuti cikusowani cipiriro, kuti pamene mwacita cifuniro ca Mulungu, mukalandire lonjezano.” (Ahebri 10:36) Cotero, kacitidwe kokha koyenera ndiko ka kumamatirabe mu utumiki wa Mulungu, mukamadalira mwa Iye kuti akucirikizeni inu.—Salmo 55:22 [54:23, Dy]; Ahebri 6:11, 12.
8. Ncifukwa ninji ife tingakhale ndi cisangalalo ceniceni ngati tilimbana naco ciyeso ca cikhulupiriro cathu cimene cimadza ndi citsutso?
8 Wophunzira Yakobo anawalembera Akristu oyambirira kuti: “Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m’mene mukugwa m’mayesero a mitundumitundu; pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro canu cicita cipiriro.” (Yakobo 1:2, 3) Inde, tingakhale ndi cisangalalo ceniceni ngati, pokumana ndi citsutso, ife tilimbana naco ciyeso ca cikhulupiriro cathuco. Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti mwa cipiriro ife timaicirikiza mbali ya Atate wathu wakumwambayo mu nkhani yaikuruyo imene iri pamaso pa cilengedwe caponseponseci. Kuonjezerapo, Mwana wa Mulungu amatitsimikizira ife kuti: “Mudzakhala nao moyo wanu m’cipiriro.” Inde, mwa cipiriro inu mudzaipeza mfupo ya moyo wamuyaya.—Luka 21:16-19; 1 Petro 2:21-23; 2 Atesalonika 1:4, 5.
9. (a) Ncifukwa ninji tikukhala ndi moyo mu nthawi yodalitsika kwambiri mu mbiri yonse ya kukhalapo kwa anthu? (b) Kodi ndi ciyembekezo cosangalatsa cotani cimene ciri mtsogolomo kwa awo amene samaisiya konse njira ya coonadi?
9 Ife tikukhala mu nthawi yodalitsika kwambiri mu mbiri yonse ya kukhalapo kwa anthu. Posacedwapa tsopano Yehova limodzi ndi Mwana wace, Kristu Yesu, adzawacotsa mu cilengedwe caponseponseci adani onse a ufumu wa Mulungu. Ha, ndi motani nanga mmene kudzakhalira kosangalatsa, nkhondo imeneyo itatha, kumakhala m’mikhalidwe yolungama m’dziko lapansi lauparadaiso, losabvutika, lopanda cisoni ndi imfa! Inu mungakhale ndi cidaliro cotheratu mu ciyembekezo cimeneco, cifukwa cakuti “Mulungu . . . sanganame.” (Tito 1:2, NW) Pamenepo, yembekezerani ciyembekezo codalitsika cimeneco, ndipo musakusiye konse kulambira Yehova Mulungu woonayo. Ipitirizenibe njira ya coonadi, pakuti “dziko lapansi lipita, ndi calakolako cace; koma iye amene acita cifuniro ca Mulungu akhala ku nthawi yonse.”—1 Yohane 2:17.