Phunziro 37
Kukhazikika Maganizo ndi Maonekedwe a Munthu
1-9. Tanthauzirani kukhazikika maganizo ndi chidaliro, ndipo fotokozani mmene munthu angapezere zimenezo.
1 Mlankhuli wokhazikika maganizo amalankhula momasuka. Iye amakhala wodekha ndi wosatekeseka chifukwa ali ndi chidaliro chonse. Koma kusakhazikika maganizo kumasonyeza kupanda chidaliro. Ziŵirizo zimayendera pamodzi. Ndicho chifukwa chake “Chidaliro ndi kukhazikika maganizo” zaphatikizidwa pamodzi monga mfundo imodzi pasilipi la Uphungu wa Kulankhula.
2 Pamene kuli kwakuti chidaliro ndi kukhazikika maganizo zili zofunika kwa mlankhuli, zimenezo sizikutanthauza kudzidalira mopambanitsa, kumene kumaonekera mwa kuima monyada kapena kuti monyang’wa kapenanso kuti moyerekedwa. Mwinanso kukhala wosakhazikika bwino pampando kapena kuyedzamira mopanda ulemu kufelemu la pakhomo mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba. Ngati kanthu kena pokamba nkhani yanu kasonyeza mzimu wodzidalira mopambanitsa, mosakayikira woyang’anira sukulu adzakupatsani uphungu wam’seri, chifukwa cholinga chake ndicho kukuthandizani kuthetsa mzimu uliwonse woterowo umene ungapangitse ulaliki wanu kukhala wosagwira mtima.
3 Komabe, ngati ndinu mlankhuli watsopano, n’koyembekezeka kuti mungachite mantha ndi manyazi pamene mupita kupulatifomu. Nthaŵi zina mukhoza kuchita mantha kwambiri ndi kumangika thupi moti mungaganize kuti simudzatha kukamba nkhani yogwira mtima. Komatu musakhale ndi maganizo amenewo ayi. Chidaliro ndi kukhazikika maganizo zimadza mwa kuyesetsa mwakhama ndi kudziŵanso chifukwa chake izo zikusoŵeka.
4 Nanga n’chifukwa ninji alankhuli ena amakhala alibe chidaliro? Makamaka pali chifukwa chimodzi kapena ziŵiri. Choyamba, kusakonzekera bwino kapena kusamvetsa bwino nkhani yawo. Chachiŵiri, kudzikayikira kuti saali alankhuli okhoza bwino.
5 Kodi chingakupatseni chidaliro n’chiyani? Kwenikweni, ndicho kudziŵa kapena kukhulupirira kuti mudzakhoza kukwaniritsa cholinga chanu. Ndicho chitsimikizo chakuti mkhalidwewo mutha kuchita nawo ndi kuulamulira. Papulatifomu zimenezo zingafune kuzoloŵera. Popeza mwalankhulapo nkhani zingapo, mungakhale ndi chidaliro chakuti imeneyinso mudzailankhula bwino. Koma ngakhale muli wachatsopano, nkhani zanu zoyambirira ziyenera kukulimbikitsani, ndipo posachedwapa mudzakhoza kuonetsa luso limeneli pamlingo wokulirapo.
6 China chofunika kuti mukhale ndi chidaliro, kaya muli wozoloŵera kapena ayi, ndicho kuidziŵa bwino nkhani yanu komanso kukhala ndi chitsimikizo chakuti nkhani imeneyo n’njopindulitsadi. Zimenezo zimafuna osati kukonzekera chabe nkhani yanu pasadakhale komanso kukonzekeranso mosamalitsa kakambidwe kake. Ngati muzindikira kuti zimenezo n’zokuthandizani kupita patsogolo mwateokalase komanso n’zophunzitsa abale omwe alipowo, mudzapita ku pulatifomu ndi maganizo apemphero. Mudzatengeka maganizo ndi nkhaniyo ndipo mudzaiŵala za inumwini ndi mantha anu. Mudzangoganiza za kukondweretsa Mulungu, osati anthu.—Agal. 1:10; Eks. 4:10-12; Yer. 1:8.
7 Zimenezo zimafuna kuti mukhale otsimikiza ponena za zonse zimene mudzanena. Tsimikizani zimenezo pokonzekera. Ndipo mutachita zonse zotheka pokonza nkhani yosangalatsa ndi yaumoyo, ngati mukuonabe kuti siinafike pokometsetsa kapena ili yozizirirapo, kumbukirani kuti omvetsera aumoyo adzapangitsa nkhani yanu kukhalanso yaumoyo. Choncho pangitsani omvetsera anu kukhala aumoyo ndi kalankhulidwe kanu, ndipo chidwi chawo chidzakupatsani chidaliro m’zimene mukunenazo.
8 Mongadi muja dokotala amafufuzira zizindikiro za matenda, phungu wanunso adzaona zizindikiro zimene zimasonyeza mosalakwa kuti muli wosakhazikika maganizo. Ndiponso monga muja dokotala wabwino amayesetsera kuchiritsa nthenda yeniyeni m’malo mwa zizindikiro zake chabe, phungu wanunso adzayesetsa kukuthandizani kugonjetsa zenizenizo zokusoŵetsani chidaliro ndi kukhazikika maganizo. Komabe, kuzidziŵa zizindikiro ndi kuphunzira mmene mungaziletsere kudzakuthandizani kugonjetsa zenizeni zochititsa zizindikiro zimenezo. Kodi izo n’chiyani?
9 Kunena mwachisawawa, zilipo njira ziŵiri zosonyeza mantha ndi kumangika thupi. Tikhoza kuziika m’magulu aŵiri monga zisonyezero zathupi ndi zam’mawu. Pamene zimenezi zionekera pamlingo uliwonse, timati munthuyo sali wokhazikika maganizo.
10, 11. Kodi kaimidwe ka munthu kangasonyeze motani kuti iye alibe chidaliro?
10 Kukhazikika maganizo kuonekera m’kaimidwe ka munthu. Pamenepo, umboni woyamba wa kukhazikika maganizo umaoneka m’kaimidwe kanu. Nazi zinthu zina zimene zidzaulula ngati mulibe chidaliro. Choyamba taganizirani manja anu: kugwira manja anu mutawapindira kumbuyo, kuwafumbata mwamphamvu kumbali kwanu kapena kugwira zolimba gome lolankhulirapo; kupisa ndi kutulutsa manja m’matumba kaŵirikaŵiri, kumanga ndi kumasula mabatani a jekete, kugwiragwira ku tsaya, mphuno, magalasi a maso popanda cholinga chenicheni; kulankhula ndi manja kosamaliza; kuseŵeretsa wochi, pensulo, mphete kapena notsi. Kapena ganizirani za kusunthasuntha mapazi, kuyendetsayendetsa thupi; msana wongoti gwa ngati kapirimwana wa msampha kapena kupindapinda mawondo; kunyambitanyambita milomo, kumezameza mate kapena malovu, ndi kupuma mofulumira komanso kwapamwamba.
11 Zizindikiro zonsezi za kusakhazikika maganizo mutha kuzilamulira kapena kuzichepetsa mwa kuyesetsa kwakhama. Ngati muyesetsa kuchita zimenezo mudzaoneka kuti muli wokhazikika m’kaimidwe kanu. Choncho pumani mwachibadwa komanso mosafulumira, ndipo yesetsani kumasuka thupi. Yambani mwakhazika mtima pansi, osangofikira kulankhula. Omvetsera anu ali okonzeka kulabadira, ndipo zimenezo zidzakuthandizani kupeza chidaliro chimene mukuchifuna. Sumikani maganizo pa nkhani yanu, osadera nkhaŵa za omvetsera kapena kuganiza kwambiri za inumwini.
12-14. Ngati mawu a munthu asonyeza kupanda chidaliro, kodi angachitenji kuti akhazikike maganizo?
12 Kukhazikika maganizo kuonekera mwa kulamulira mawu. Zizindikiro za m’mawu zosonyeza mantha ndizo kukweza kwambiri mawu, mawu onjenjemera, kukhosomola kapena kutsokomola kaŵirikaŵiri koyeretsa pakhosi, kuchepetsa mawu kosakhala kwachibadwa chifukwa chomangika thupi. Mavuto ameneŵa ndi zizoloŵezizo mutha kuzigonjetsa mwa kuyesetsa kwakhama.
13 Popita ku pulatifomu musayende mofulumira kwambiri kapena pokonza bwino notsi zanu, koma khalani wodekha ndi wosangalala pofuna kugaŵirako ena zimene mwakonzekera. Ngati mudziŵa kuti mumachita mantha poyamba kulankhula, yesetsani kulankhula pang’onopang’ono mawu anu oyamba komanso ndi mphamvu ya mawu yocheperapo kuposa ya masiku onse. Zimenezo zidzakuthandizani kulamulira mantha anu. Mudzapeza kuti kugwiritsa ntchito manja polankhula ndi kupuma zidzakuthandizani kuti mumasuke thupi.
14 Koma simuyenera kuyembekezera tsiku lopita papulatifomu kuti muyesetse kuchita zinthu zimenezo. Phunzirani kukhala wokhazikika maganizo ndi wodziletsa m’kulankhula kwanu kwa tsiku ndi tsiku. Kudzakuthandizani kwambiri pokhala ndi chidaliro papulatifomu ndi mu utumiki wanu wakumunda, kumene chidalirocho chimakhala chofunika kwambiri. Kulankhula modekha kudzapangitsa omvetsera kukhala okhazikika m’mitima mwawo ndi kutchera khutu ku nkhani yanu. Kuyankha nthaŵi zonse pamisonkhano kudzakuthandizani kukhala wozoloŵera kulankhula pamaso pa anthu ambiri.
**********
15. N’chifukwa chiyani maonekedwe abwino a munthu ali ofunika kwambiri?
15 Maonekedwe anu abwino angakuthandizeninso kukhazikika maganizo, koma maonekedwe n’ngofunikanso pazifukwa zina. Ngati mlaliki sanasamale bwino maonekedwe ake, angaone kuti maonekedwewo akusokoneza omvetsera moti sangapereke maganizo ku zimene akunena. Zimenezo zidzakopera maganizo a omvetsera kwa iyemwini, chinthu chimene ngakhale iye sakufuna kuchita. Ngati munthu ali wosasamala kwambiri za maonekedwe ake, angachititse ena kunyoza gulu lonse limene iye alinso mbali yake ndi kukana uthenga umene akuupereka. Zimenezo siziyenera kuchitika konse. Choncho, ngakhale kuti “Maonekedwe a munthu” aikidwa pothera pafomu ya Uphungu wa Kulankhula, sayenera kuonedwa monga osafunikira kwenikweni.
16-21. Kodi ndi uphungu wotani umene ukuperekedwa pa kavalidwe ndi kapesedwe koyenera?
16 Kavalidwe ndi kapesedwe kabwino. Tiyenera kupeŵa kuvala mopambanitsa. Mlaliki wachikristu sayenera kutengera masitaelo a dziko odzionetsera. Iye ayenera kupeŵa kuvala mowonjeza, kapena kwadzaoneni moti maganizo a anthu akupita ku zovala zake. Ndipo ayeneranso kusamala kuti asavale modzichotsera ulemu. Kuvala bwino sikutanthauza kuti wina mpaka atavala suti yatsopano, koma munthu atha kukhala waudongo ndi waukhondo nthaŵi zonse. Thalauza iyenera kusitidwa komanso tayi ivalidwe moongoka bwino. Izi ndi zinthu zoti wina aliyense atha kuchita.
17 Uphungu wonena za kavalidwe umene mtumwi Paulo analemba pa 1 Timoteo 2:9, ulinso woyenera kwa akazi achikristu lerolino. Kwa abalenso n’chimodzimodzi, sayenera kuvala m’njira yodzionetsera, ndiponso n’kosayenera kuti iwo aloŵerere kwambiri m’masitaelo a kavalidwe ka dziko amene ali umboni wa kusadekha.
18 Komabe, tiyenera kukumbukira kuti anthu onse sangavale mofanana. Sitiyenera kuwayembekezera kutero. Zokonda zimasiyana, ndipo zimenezo n’zoyenera. Komanso kamene tikuti kavalidwe koyenera kamasiyananso m’madera osiyanasiyana a dziko lapansi. Chofunika nthaŵi zonse ndicho kupeŵa mavalidwe amene angapereke chithunzi chosayenera kwa omvetsera ndi pofunanso kupeŵa kukhumudwitsa aja amene amabwera kumisonkhano yathu.
19 Ponena za kavalidwe koyenera kwa abale popereka nkhani m’sukulu kapena pamsonkhano wa utumiki, tinganene kuti ayenera kuvala m’njira yooneka bwino mofanana ndi mbale amene akukakamba nkhani yapoyera. Ngati uli mkhalidwe wa kwanuko kuvala tayi ndi suti pokamba nkhani yapoyera, kameneko ndiko kavalidwe koyenera ngakhale pokamba nkhani m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase, chifukwa mukuphunzitsidwa kulankhula nkhani poyera.
20 Chinanso chofunika ndicho kusamala kapesedwe. Tsitsi losapesa lingapereke chithunzi choipa. M’pofunika kudzisamala pankhani imeneyi kuti muoneke waudongo. Ndiponso, pamene amuna mumpingo apereka nkhani pamisonkhano, ayenera aonetsetse kuti apala ndevu zawo bwinobwino.
21 Ponena za uphungu pankhani imeneyi ya kavalidwe ndi kapesedwe koyenera, ngati mpata wakhalapo woti wina ayamikiridwe pambali imeneyi, nthaŵi zonse zimenezo zingachitidwe kuchokera pa pulatifomu. Ndi iko komwe, pamene ena akuyamikiridwa pakavalidwe ndi kapesedwe koyenera, zimalimbikitsa ena kutengera chitsanzo chabwino chimenecho. Komabe, ngati pakufunikira kuti wina awongolere kavalidwe ndi kapesedwe, ndi bwino kuti woyang’anira sukuluyo apereke maganizo amenewo m’njira yachifundo m’seri, osati am’patsire uphungu papulatifomu pomwepo ayi.
22-28. Fotokozani mmene kaimidwe ka munthu kangayambukirire maonekedwe.
22 Kaimidwe koyenera. Kaimidwe koyenera kakuphatikizidwanso m’kaonekedwe kanu. Apanso, si kuti anthu onse amaima mofanana, ndipo sitiyenera kupangitsa abale kuima mwa njira inayake yakutiyakuti. Komabe, m’pofunika kuonetsetsa ndi kuwongolera kapena kuchotsa maimidwe ena ake okopera chidwi kwa munthuyo ndi kudodometsa uthenga umene ukuperekedwa.
23 Mwachitsanzo, sikuti tonse timaika miyendo mofanana tikaimirira, ndipo kaŵirikaŵiri zimenezo sizikhala n’kanthu, malinga taima mowongoka. Koma ngati mlankhuli aima motangalala ngati kuti ali pahachi kaya kuti kavalo, zimenezo zingakhale zosokoneza kwambiri.
24 Komanso, ngati mlankhuli aima choŵeramira kutsogolo, osati mowongoka bwino, omvetsera angam’mvere chisoni poganiza kuti mwina wadwala, ndipo zimenezo zingamawapangitse iwo kusapindula kwenikweni ndi nkhani yake. Maganizo awo sakhala pa zimene iye akunena koma amangoganiza za iyeyo.
25 Kuima ndi mwendo umodzi, winawo utakoloŵekedwa kumbuyo kwa unzake, kumapereka umboni wa kusakhazikika maganizo, monga momwe kumakhalira kuima mutapisa manja m’matumba. Izi ndi zinthu zofunikira kupeŵa.
26 Ndiponso, ngakhale kuti sikulakwa pamene mlankhuli aika manja nthaŵi zina pagome lolankhulirapo, ngati lilipo, iye sayenera kuyedzamira pagomepo, mofanana ndi mmene wofalitsa mu utumiki wakumunda sayenera kuyedzamira kufelemu ya pakhomo. Sikupereka chithunzi chabwino.
27 Komabe, tinenetse pano kuti anthu n’ngosiyana. Sikuti anthu onse amaima mofanana, ndipo kuchita mopambanitsa ndiko kokha kumasokoneza nkhani, ndiponso n’kumene kuyenera kuyang’aniridwa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase.
28 Kuti munthu awongolere kaimidwe kake mankhwala ake n’kukonzekera basi. Ngati mukufuna kuwongolera mbali imeneyi, muyenera kuganiziratu pasadakhale ndi kudziŵiratu kuti pamene mukwera pa pulatifomu muyenera kuima mowongoka bwino musanayambe kulankhula. Ichinso n’chinthu china chimene tingawongolere mwa kuyesetsa kuima bwino tsiku ndi tsiku.
29-31. N’chifukwa chiyani zipangizo zathu ziyenera kukhala zosamalika bwino?
29 Zipangizo zosamalika bwino. Ngati, pamene wina akulankhula pakhomo kapena popereka nkhani papulatifomu, kenako mapepala ena n’kugwera pansi kuchokera m’Baibulo limene akugwiritsa ntchito, zimenezo n’zosokoneza. Zimapereka chithunzi choipa. Panopa sitikutanthauza kuti sitiyenera kuika chilichonse m’Baibulo, koma ngati payamba kukhala mavuto amene asokoneza nkhani, ndiye kuti m’pofunika kuperekapo chisamaliro chokulirapo pa kaonekedwe ka munthu. Ndi bwinonso kupenda maonekedwe a Baibulo lanu. Chifukwa cha kuligwiritsa ntchito kwambiri, likhoza kuda kapena kung’ambika moti n’kusaonekanso bwino. Choncho tingachite bwino kuonetsetsa ngati Baibulo limene timaligwiritsa ntchito papulatifomu mu utumiki wakumunda lingakhumudwitse aja amene timafuna kuwathandiza.
30 Zili chimodzimodzi ndi chola kapena kuti chikwama chathu chonyamulira mabuku. Zilipo njira zosiyanasiyana zimene tingapakirire zinthu mwaukhondo m’chola chathu. Koma ngati tichita kusanthulasanthula m’mapepala m’cholamo kuti tipeze buku limene tikufuna kutulutsa, kapena ngati pamene tifuna kutulutsa magazini zinthu zinanso n’kugwera pakhomo, pamenepo tiyenera kuchitapo kanthu.
31 Zingakhalenso zosokoneza kwa omvetsera ngati wolankhulayo alongedza m’thumba lakunja la chovala chake mabolopeni, mapensulo ndi zinthu zina zoonekera kwambiri. Palibe lamulo limene liyenera kupangidwa la kumene munthu angasungire zinthuzo, koma pamene ziyamba kukopa maganizo ndi kuwachotsa ku nkhani, pamenepo m’pofunika kuti pakhale kuwongolera kwinakwake.
32-34. Kodi maonekedwe a nkhope amathandiza chiyani pamaonekedwe athu?
32 Musasonyeze nkhope yosemphana ndi nkhani. Pokonza nkhani ndi bwino kuganizira za mzimu wake wa nkhaniyo. Mwachitsanzo, polankhula za imfa ndi chiwonongeko, n’kosayenera kuonetsa nkhope yomwetulira. Momwemonso, polankhula za mikhalidwe yosangalatsa ya m’dongosolo latsopano la zinthu, sikungakhale koyenerera kupangira omvetsera tsinya.
33 Kaŵirikaŵiri kumakhala kosavuta kuonetsa nkhope yakutiyakuti, ndipotu anthu ena n’kwachibadwa kuonetsa nkhope yosakondwa kuposa ena. Komabe, chomwe tiyenera kuchipeŵa ndicho kuchita mopambanitsa moti n’kuipitsa nkhani. Ngati maonekedwe a nkhope angapangitse omvetsera kukayikira zimene mlankhuliyo akunena, nkhope imeneyo n’njosafunikira.
34 Choncho ndi bwino pokonza nkhani kuganizira za mzimu umene nkhaniyo iyenera kulankhulidwa nawo. Ngati ili nkhani yoopsa, yonena za kuwonongedwa kwa anthu oipa, ilankhulidwe ndi mzimu womwewo. Ndipo ngati mukuganizira nkhaniyo ndi kuikumbukira, mwachibadwa nkhope yanu idzasonyeza mzimu wake. Ngati ili nkhani yosangalatsa, yoyenera kukondweretsa omvetsera, ikambidwe mwansangala. Ndipo ngati mukhala womasuka thupi papulatifomu, kaŵirikaŵiri nkhope yanu idzasonyeza chisangalalo chimenecho.