Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 46 tsamba 187-190
  • Njira ya Kukhalira ndi Moyo Kosatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira ya Kukhalira ndi Moyo Kosatha
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Ungathe Kukhala M’dziko Latsopano la Mulungu Lamtendere
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Zingatheke Bwanji Kuti Mudzakhale ndi Moyo Wosatha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kukhala ndi Moyo Kosatha Siloto Chabe
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Tingakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 46 tsamba 187-190

Mutu 46

Njira ya Kukhalira ndi Moyo Kosatha

YEHOVA watipatsa ife mphatso zambiri zodabwitsa. Imodzi ya mphatso zache zabwino kopambana kwa ife ndiyo moyo. Popanda uwo ife sitikadachita chinthu chiri chonse, kodi tikadatha?—Koma ngati ife tikufuna kukhala nayobe mphatso imeneyo, pali zinthu zina zimene ife tiyenera kuzichita.

Inuyo muli kumachichita chimodzi cha zinthu zimenezo pa tsopano linoli. Inenso chimodzimodzi. Timachichita icho tsiku lonse ndi usiku wonse, ngakhale pamene ife tiri m’tulo. Ngati ife tikanati tileke, tikadafa nthawi yomweyo. Kodi mukuchidziwa chimenecho?—Inde, ife tiri kupuma mpweya.

Pali zinthu zina zimene ife timazichita tsiku liri lonse kuti tikhalebe ndi moyo. Kodi inu mungathe kuzichula zina za izo?—Ife timadya. Ife timamwa madzi. Ndipo ife timagona. Mulungu anatipanga ife kotero kuti ife sitingathe kukhala ndi moyo popanda zinthu zimenezi.

Palibe ziri zonse za izo ziri zobvuta kuzichita. Kunena zoona, ine ndimakonda kudya. Kodi sichoncho ndi inu?—Koma kodi ndi motani mmene chakudya chimatikhalitsira ife ndi moyo? Kodi mukudziwa? Kodi nchiani chimene chimachichitikira icho ife titachimeza?—

Thupi lathu limachipukusa chakudya kukhala tizidutswa tating’ono kwambirimbiri. Ndiyeno mwazi umazitengera zimenezi ku mbali iri yonse ya thupi lathu. Chakudya chimenechi chimagwiritsiridwa nchito m’njira yodabwitsa kuumbira pfupa latsopano, mnofu watsopano, tsitsi latsopano, zikhadabo, maso ndi mbali zina za thupi. Kodi inu munazidziwa zimenezo?—

Inuyo mungadabwe chimene chimazichitikira mbali za thupi zakalezo. Zimenezi zimafa pang’onopang’ono ndipo zimaturutsidwa monga zotayidwa. Zatsopanozo zimatenga malo ao.

Masinthidwe amenewa ali kumachitika kuli konse m’thupi mwathu. Sikumatenga nthawi yaitali kwambiri kufikira thupi lathu lonse litasinthidwa. Yehova analipanga thupi lathu kotero kuti ilo lizichita chimenechi. Iye analipanga ilo kotero kuti ilo likapitirizabe kumachichita icho kosatha. Inde, iye anampanga munthu kuti akhalebe ndi moyo kosatha.

Koma anthu amafa. Kodi nchifukwa ninji?—Chifukwa chakuti Adamu anamchimwira Mulungu. Ndipo ife tinaulandira uchimo kuchokera kwa Adamu. Iye anauononga unansi wabwino wa munthu ndi Mulungu. Ndipo moyo wathu umadalira pa Mulungu.

Kuti tikhale ndi moyo kosatha, ife tifunikira zoposa ndi mpweya ndi madzi ndi chakudya ndi tulo. Tifunikira kukhala ndi kaimidwe koyenera ndi Mulungu.

Palibe dotolo ali yense amene angathe kutipangitsa ife kukhala ndi moyo kosatha. Palibe mbulu uli wonse wa mankhwala amatsenga umene udzatiletsa ife kufa. Njira yokha imene ife tingathe kukhalira ndi moyo kosatha ndiyo mwa kumayandikira pafupi ndi Mulungu. Mphunzitsi Wamkuruyo amatiuza ife mmene ife tingachichitire chimenecho.

Tiyeni titenge Mabaibulo athu ndi kutsegula pa Yohane chaputara 17, vesi 3, NW. Panopo ife tikuchipeza chimene Yesu anachinena: “Ichi chitanthauza moyo wosatha, kuchilandira kwao chidziwitso cha inu, Mulungu woona yekha, ndi cha uyo amene munamtuma, Yesu Kristu.”

Kodi nchiani chimene Mphunzitsi Wamkuruyo anachinena kuti ife tikuchifunikira m’malo mwakuti tikhale ndi moyo kosatha?—Ife tifunikira kuchilandira chidziwitso. Chimenecho chikutanthauza kuti ife tifunikira kuphunzira. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene ife timaliphunzilira Baibulo.

Koma kodi ndi motani mmene kuphunzira za Yehova kudzatithandizira ife kukhala ndi moyo kosatha?—Kumbukirani, moyo wonse umachokera kwa iye. Kuti ife tikhale ndi chiyanjo chache, ife tiyenera kumlambira iye monga Mulungu yekha woona. Koma ife sitingathe kumlambira iye m’njira yoyenera kusiyapo ngati ife timvetsera chimene iye amachinena. Monga momwe ife timachifunira chakudya tsiku liri lonse, momwemonso tifunikira kuphunzira za Yehova tsiku liri lonse. Ukuko kumatiyandikizitsa ife pafupi ndi iye. Baibulo limati: ‘Munthu ayenera kukhala ndi moyo, osati ndi mkate wokha, koma ndi mau onse amene amaturuka pakamwa pa Yehova.’—Mateyu 4:4.

Ife tifunikiranso kuchilandira chidziwitso chonena za munthu wina kuphatikiza pa Mulungu. Kodi ameneyo ndani?—Yesu Kristu. Ichi chiri chifukwa chakuti Mulungu anamtumiza Yesu kudzauchotsa uchimo. Iye angathe kuuchotsa upandu umene Adamu anauchita pamene Adamu anamchimwira Mulungu. Yesu angathe kutithandiza ife kubweleranso mu unansi wabwino ndi Mulungu. Ndipo chimenecho sichiri chothekera m’njira ina iri yonse.

Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene Baibulo limanenera kuti: “Mulibe chipulumutso mwa munthu wina ali yense.” Ife tiyenera kuphunzira za Yesu ngati ife tikufuna kukhala ndi moyo kosatha. Ndipo ngati ife tiri nachodi chikhulupiliro mwa iye, ife tidzakhala okhoza kukhala ndi moyo kosatha. Pamene iye aibweretsa mikhalidwe yabwino ku dziko lonse lapansi, iye adzatithandiza ife kukhala ndi moyo kosatha ndi kukhala achimwemwe. Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene Baibulo limanenera kuti: “Iye amene asonyeza chikhulupiliro mwa Mwanayo ali ndi moyo wosatha.”—Machitidwe 4:12, Yohane 3:36, NW.

Tsopano, kodi kumatanthauzanji ‘kusonyeza chikhulupiliro’ mwa Yesu?—Kumatanthauza kuti ife timakhulupiliradi kuti ife sitingathe kukhalabe ndi moyo popanda iye. Kodi inu mukuchikhulupilira chimenecho?—

‘Kumasonyeza chikhulupiliro’ mwa Yesu kumatanthauzanso kanthu kenanso. Iko kumatanthauza kuti ife timamkhulupilira iye kwambirimbiri chakuti ife timachita chimene iye amachinena. Ife sitimangochita zinthu zina chabe ndipo osati zinazo. Ndipo ife timazichita izo chifukwa chakuti ife timafunadi kutero. Kodi chimenecho ndicho chimene inu mukufuna kuchita?—

Chimodzi cha zinthu zimene Mphunzitsi Wamkuruyo amatiuza ife kuzichita ndicho kulankhula ndi anthu ena ponena za Mulungu ndi ufumu wache. Chotero ngati ife taphunziradi kuchokera kwa Yesu, chimenecho ndicho kanthu kena kamene ife tidzakachita. Kodi inuyo mukuchichita chimenecho?—

Koma zimenezo sindizo zokha zimene ziri kanthu. Tsiku liri lonse ife tiyenera kuchita zinthu zimene Baibulo limati ziri zoyenera. Ife tiyenera kukhala osamala kusazichita zinthu zoipa. Ife tiyenera kusonyeza kuti ife timakondanadi wina ndi mnzache.

Ngati ife tizichita zinthu zimenezi, kukusonyeza kuti ife takhaladi tikumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo.

(Ophunzira enieni a Yesu Kristu adzakhaladi okhoza kukhala ndi moyo kosatha m’chimwemwe pa dziko lapansi pompano. Werengani chimene Baibulo limachinena ponena za chimenechi pa Salmo 37:29, 34 [36:29, 34 MO], Mateyu 19:16-21 ndi Aroma 6:23.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena