Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gh mutu 13 tsamba 116-123
  • Chimasuko ku Imfa Kumka ku Moyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimasuko ku Imfa Kumka ku Moyo
  • Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MWANA ADZA PA DZIKO LAPANSI
  • KUFAFANIZA MANGAWA A UCHIMO
  • CHISONYEZERO CHACHIKULU CHA CHIKONDI
  • KUPEREKA MPHATSO YA MOYO
  • Yesu Kristu, kupyolera mwa Amene Mulungu Adzawadalitsa Anthu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Dipo
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Yesu Kristu—Kodi Anatumidwa ndi Mulungu?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Dipo la Kristu Njira ya Mulungu ya Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
gh mutu 13 tsamba 116-123

Mutu 13

Chimasuko ku Imfa Kumka ku Moyo

1. Monga momwe kwalongosoledwera pano, kodi n’chiani chimene chingachitikire banja la ana amasiye chimene chikawapatsa chifukwa chokhalira othokoza?

NKHONDO zankhanza za m’zaka zino za zana la makumi awiri zachititsa ana amasiye ambiri. Tayerekezreani banja la ana amasiye amene ataya makolo onse. Opanda nyumba kapena njira zopezera zosowa, iwo ali obvutika-bvutika ndi umphawi m’moyo—anjala, odwala ndi opanda chiyembekezo cha m’tsogolo. Komabe, tiyeni tiyerekezere kuti mwamuna wina waufulu wokoma mtima aona kubvutika kwao, ndipo akusonyeza chikondi kwa iwo. Iye akulangiza mwana wake, amene ali wosakwatira, kuchita ubwenzi ndi ana amasiye amene’wa ndi kubwera nawo m’nyumba. M’menemo iye akuwasambitsa, kuwadyetsa ndi kuwabveka, ndi kuwalipirira ngongole zao. Akumakhala monga atate weni-weni kwa iwo, mwana wake’yo akuwachititsa kusangalala ndi moyo wokwanira. Kodi ana amasiye amene’wo sayenera kukhala othokoza kwa mwamuna waufulu wokoma mtima amene’yu ndi mwana wake’yo? Ndithudi, iwo ayenera kuwathokoza!

2. Kodi ndi motani m’mene tonsefe takhalira ngati “ana amasiye”? (Aroma 5:12)

2 Kodi mumazindikira kuti inu muli chiwalo cha banja la ana amasiye lotero’lo? Inde, pakuti inu ndinu mbadwa za Adamu, atate wa anthu onse, amene mwa uchimo wake wadala anasiya banja lonse laumunthu liri mu mkhalidwe wa chisoni mu umene lirimo lero lino. Mongofananandi ana amasiye amene’wo, ife ‘tagulitsidwa mu ukapolo ku uchimo,’ tikumalandira mkhalidwe wachisoni umene’wu kuchokera kwa Adamu.—Aroma 7:14.

3. Kodi n’chifukwa ninji tiri opanda mphamvu ya kudziombola? (Salmo 51:5)

3 Popeza kuti timabadwa tiri ochimwa, anthu tonsefe tiri mu mkhalidwe woonekera kukhala ngati wopanda chiyembekezo wolongosoledwa pa Salmo 49:7 wakuti:

“Kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kum’perekera dipo kwa Mulungu.”

Ngati munthu wina wochokera kunja kwa banja la anthu akanapanda kutithandiza, ife tonse tikanafa ndi kukhala akufabe kwamuyaya. Pakuti Mulungu sangalole zolengedwa zimene zimapitirizabe kuperewera, kapena “kuphonya chandamale,” cha chilungamo chake kukhalabe ndi moyo kosatha. Iwo akakhala mphamvu yoipitsa m’chilengedwe chonse choyera.

4. (a) Kodi n’chiani chimene chimasonyeza kuti Mulungu amasamalira anthu? (1 Yohane 4:9, 10) (b) Kodi “Mwana’yo” ndani?

4 Komabe, mofanana ndi mwamuna waufulu wokoma mtima’yo wolongosoledwa pamwambapo, yehova Mulungu wasonyeza kuti iye amasamalira anthu, ndipo iye wachita monga momwe Baibulo limatiuzira kuti:

“Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.” (Yohane 3:16)

Mwana amene’yu akulongosoledwa kukhala “Mwana wobadwa yekha” chifukwa chakuti iye ndiye woyamba ndi yekha amene analengedwa mwachindunji ndi Mulungu. Monga momwe taonera kale, iye anagwira ntchito pambali pa Yehova monga “mmisiri” m’kupanga zolengedwa zina zonse. Monga wolankhulira wamkulu wa Mulungu, iye akuchedwa’nso “Mau.”—Yohane 1:1-3.

MWANA ADZA PA DZIKO LAPANSI

5. (a) Kodi ndi motani m’mene Mwana’yo anakhalira munthu pa dziko lapansi? (Luka 1:30-35) (b) Kodi Yesu analingana ndi Adamu wangwiro’yo m’njira yotani?

5 Yehova analinganiza kutumiza Mwana amene’yu pa dziko lapansi kuchokera kumwamba. Mulungu ‘anam’konzera thupi,’ thupi langwiro laumunthu, mwa kusamutsira mphamvu ya moyo ya Mwana’yo m’mimba ya namwali, Mariya, mbadwa ya Davide, kuchokera m’malo a kumwamba, ndipo chotero itatha miyezi isanu ndi inai iye anam’bala pano pa dziko lapansi monga “Mwana wa munthu.” (Ahebri 10:5; Yohane 3:13) Pamene iye anakula kukhala wachikulire monga mwamuna, Mwana amene’yu, Yesu, anafanana ndendende ndi mwamuna woyambirira, Adamu. Monga momwe’di mwamuna wangwiro’yo Adamu anasonyezera ulemerero wa Mulungu, chotero Yesu tsopano anasonyeza ulemerero umene’wo:

“Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.”—Yohane 1:14.

6. (a) Kodi n’chifukwa ninji Yesu anayenera kukhala munthu wangwiro? (1 Timoteo 2:5,6) (b) Kodi n’chifukwa ninji Yesu sanatulutse banja la iye mwini? (c) Kodi ndi motani m’mene Yesu, monga woimira wa Mulungu, anagulira anthu? (1 Petro 1:18, 19)

6 Yesu sanali theka Mulungu, theka lina munthu. Iye sanali Mulungu wathupi. Kuti alipirire “kulakwa kwa munthu mmodzi [Adamu],” “munthu mmodzi Yesu Kristu” anayenera kufanana ndendende ndi Adamu wangwiro pa nthawi ina’yo. Iye anayenera kukhala munthu wangwiro, wosaposa pamenepo, kapena kuchepera pamenepo. (Aroma 5:15) Mofanana ndi Adamu, Yesu akanatha kukwatira ndi kutulutsa banja la iye mwini, lopangidwa potsirizira pake ndi mabiliyoni ambiri a anthu angwiro. Koma chimene’cho sichinali chifuniro cha Atate kaamba ka iye. Chifuniro cha Mulungu chinali chakuti Yesu akhalebe wopanda mwana ndi kudzipereka monga nsembe yangwiro yaumunthu. Mwazi wake wotsanulidwa mu imfa ukaimira moyo wake wangwiro waumunthu wofanana ndendende ndi moyo wa Adamu, ndipo umene’wu akaugwiritsira ntchito m’kugula banja la Adamu kukhala lake. Motero Yesu akakhala “atate” kwa banja lamasiye limene’li, “ambiri” amene iye akuwanena pa Mateyu 20:28:

“Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.”

KUFAFANIZA MANGAWA A UCHIMO

7 (a) Kodi ndi motani m’mene Yesu anapezera “ndalama za pathumba” kuti afafanize mangawa a anthu a uchimo? (b) Kodi ndi motani m’mene iye anakhalira wokhoza kudzipereka kwa Yehova? (1 Akorinto 15:45)

7 Mongofanana ndi mwana wamwamuna wa munthu waufulu wokoma mtima’yo m’chitsanzo chathu’cho, amene analipira mangawa a banja la ana amasiye, Yesu akanatha kufafaniza mangawa a uchimo amene banja la anthu linawalandira kuchokera kwa Adamu. Komabe, Yesu choyamba ayenera kukhala nao chire mtengo wa moyo wake, mofanana ndi “ndalama za pa thumba,” kuti alipire ngongole imene’yo. Iye anayenera kufa monga munthu m’malo mwakuti atulutse kuyenera kwake kwa moyo waumunthu kuti kugwiritsiridwe ntchito kwina kuli konse. Ndi cholinga chimene’chi, iye mofunitsitsa anabvomereza imfa yankhanza yochititsidwa ndi adani a Mulungu. Koma adani amene’wa sakanatha kuchotsa kwa iye kuyenera kumeneku kwa moyo waumunthu. Tsopano kunakhala ngati “ndalama” za m’manja. Pamene Mulungu anamuukitsa “mu mzimu” ndipo anakwera’nso kumwamba, iye anali nazobe “ndalama’ zimene’zo pamanja kuti akazipereka kwa Yehova monga “dipo.” Motero iye akanatha kuombola chimene Adamu anataya-moyo kaamba ka ana onse a Adamu.—1 Petro 3:18; Aroma 3:24.

8. Kodi ndi chitsanzo chotani cholosera chimene Baibulo limapereka ponena za kutetezera uchimo wa anthu? (Levitiko 16:34)

8 Mofanana ndi m’chochitika cha banja la ana amasiye lolongosoledwa poyambirira’lo, Yesu, monga woimira wa Mulungu, anachitapo kanthu kumasula anthu ku mkhalidwe wao wobvutika’wo. Kwa zaka zoposa chikwi chimodzi mphambu mazana asanu Yesu asanapereke nsembe yake yaikulu, Yehova anachititsa Aisrayeli kuchita, chaka ndi chaka, chitsanzo cholosera cha kachitidwe kamene’ko. Pa tsiku la chaka ndi chaka la chitetezero, mkulu wa ansembe Wachiisraeyli anapha nyama zina zopanda chirema natenga mwazi wake kumka nawo m’chihema cholambirira (pambuyo pake, kachisi) ndipo m’menemo anauwaza pamaso pa chotetezera, chimene chinaimira mpando wa chiweruzo wa Yehova Mulungu iye mwini. Mwa njira imene’yi iye anatetezera machimo a anthu kwa chaka china.

9. Kodi ndi motani m’mene yesu anakwaniritsira chitsanzo chakale’cho?

9 M’kalata yake kwa Ahebri, mtumwi Paulo akulongosola mwatsatane-tsatane m’mene Yesu anakwaniritsira chitsanzo chakale chimene’cho kuti:

“Kristu sanalowa m’malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oona’wo; komatu m’Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife; kosati kuti adzipereke yekha kawiri-kawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m’malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake; chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawiri-kawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsiriziro cha nthawi’zo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha. Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro; kotero Kristu’nso ataperekedwa nsembe kamodzi [chifukwa cha uchimo wa Adamu] kukasenza machimo a ambiri.” (Ahebri 9:24-28)

Chotero kumwamba Yesu anatsiriza kachitidwe kalamulo kamene iye sakangomasula kokha anthu ku machimo ao olandiridwa kuchokera kwa Adamu, koma’nso akawalandira monga banja la iye mwini, kwa amene iye tsopano angathe kupereka moyo wosatha.

CHISONYEZERO CHACHIKULU CHA CHIKONDI

10. (a) Kodi n’chifukwa ninji dipo liri chisonyezero chachikulu kwambiri cha chikondi? (Yohane 15:9, 13) (b) Kodi ndi motani m’mene tingasonyezere chiyamikiro kaamba ka makonzedwe amene’wa, ndipo limodzi ndi chotulukapo chotani kwa ife? (Akolose 3:17)

10 Ha, ndi mtengo waukulu chotani nanga umene Yesu anali wofunitsitsa kuulipira m’malo mwakuti aombole anthu ku uchimo! Ha, ndi okondwa chotani nanga m’mene tingakhalire kuti Atate ndi Mwana apanga makonzedwe a chikondi amene’wa kaamba ka banja laumunthu! Chiri’di chisonyezero chachikulu cha chikondi chao kwa anthu, ndipo ife tiyenera kusonyeza chiyamikiro chathu pamenepo mwa kulandira mokondwera makonzedwe onse a Mulungu kaamba ka moyo mogworizana ndi zofuna Zake. Awo osonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu ‘angakhale’di’ ndi moyo wosatha, monga momwe Yesu anasonyezera kuti:

“Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. inde, ndipo mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi.”- Yohane 6:47, 51.

11. (a) Kodi n’chiani chimene chikufunika kwa awo amene amafuna moyo wosatha? (Aroma 12:2) (b) Kodi n’chiani chimene chimatulukapo kuchokera m’kulandira kuolowa manja kwa banja la Mulungu?

11 M’fanizo la ana athu amasiye, ana osowa pogona amene’wa anayenera kubvomereza miyezo ya moyo m’banja lao latsopano’lo. Iwo anayenera kusamba. Ziri chimodzi-modzi ndi awo amene amasonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya yesu ndi amene ama’mfuna kukhala ‘Atate wao wamuyaya.’ (Yesaya 9:6) Monga momwe Yesu ananenera kwa ophunzira ake kuti:

“Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.” (Mateyu 16:24)

Sitiyenera kulingalira kuti zimene’zi ziri zobvuta kwambiri, pakuti, kumbukirani, Yesu anati’nso: “Gori langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:30) Ndipo ngati tilandira kuolowa manja kwa banja la Mulungu, ndi kutumikira m’menemo ndi mtima wonse, tidzakhala ndi zisangalalo zosaneneka. Monga momwe’di mwana anadyetsera ana amasiye amene’wo, ndi kuthandiza kuwasambitsa ndi kuwabveka, momwemo’nso Yesu adzatidyetsa chakudya chauzimu chochokera m’Mau a Mulungu, Baibulo, ndi kutithandiza kubvala umunthu watsopano, amene “analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.”—Aefeso 4:24.

KUPEREKA MPHATSO YA MOYO

12. (a) Kodi Yesu akuchita ntchito yotetezera machimo choyamba kaamba ka yani, ndipo kaamba ka chifuno chotani? (b) Kodi n’chiani chimene chimatulukapo kwa awo olowetsedwa “m’pangano latsopano”? (Ahebri 8:10)

12 Kwa zaka zikwi zisanu ndi chimodzi tsopano, imfa “yalamulira monga mfumu” pa anthu. Imene’yo yakhala mphotho ya uchimo wolandiridwa kuchokera kwa Adamu, koma tsopano Mulungu akupereka kwa ife “mphatso yaulere [ya] moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 5:14; 6:23) Kodi ndi motani m’mene phatso imene’yi ikuperekedwera? Choyamba, Yesu akuchita ntchito yotetezera machimo kaamba ka “kagulu kankhosa” kake ka atsatiri osunga umphumphu, okwanira 144,000, amene “anagulidwa mwa anthu, monga zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa [Yesu],” ndi amene ayenera “kulamulira monga mafumu pa dziko lapansi” pamodzi ndi Kristu Yesu. (Luka 12:32; Chibvumbulutso 14:4; 5:9, 10, NW) Pa maziko a nsembe ya Yesu, amene’wa amalowetsedwa “m’pangano latsopano” ndi Mulungu monga ziwalo za Israyeli wauzimu, ndipo ali yense wa iwo ayenera kutsiriza njira yake pa dziko lapansi mokhulupirika, pambuyo pake iye amakhala ndi phande m’chiukiriro cha moyo wa kumwamba. (Ahebri 8:8) Otsalira apang’ono a “kagulu ka nkhosa” kamene’ka akutumikirabe pa dziko lapansi.

13. (a) Kodi ndi gulu lina liti limene laonekera m’nthawi zaposachedwapa? (Aroma 8:21, 22) (b) Kodi ndi chiyembekezo chosangalatsa chotani chimene chiri patsogolo pa amene’wa? (Chibvumbulutso 7:15-17)

13 Koma taonani! M’nthawi zaposachedwapa “khamu lalikulu” laonekera pa dziko lapansi, “ochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwa,” okwanira zikwi mazana ochuluka. Amenewa’nso amasonyeza chikhulupiriro “m’mwazi wa Mwanawankhosa,” Yesu, ndi kutsimikizira umphumphu ku ulamuliro wa Mulungu. Posachedwapa, iwo ayenera kupyola “chisautso chachikulu” chimene Mulungu adzaononga nacho dongosolo la zinthu loipa la Satana, ndi kulowa m’dziko lapansi loyeretsedwa limene lidzasandulizidwa kukhala paradaiso. (Chibvumbulutso 7:9-14) Kupyolera mwa kulamulira kwachikondi kwa ufumu wake, Kristu Yesu pamenepo adzagwiritsira ntchito phindu la nsembe yake yaikulu kaamba ka iwo kotero kuti awafikitse pa chizindikiro cha ungwiro waumunthu. Awo amene amamatira ku ulamuliro wa Mulungu poyesedwa adzalowa m’moyo wosatha.

14. (a) Kodi n’chiani chimene Chibvumbulutso 20:11-13 chimalongosola? (Yohane 5:28, 29) (b) Kodi ndi motani m’mene oukitsidwa’wo adzaweruzidwira? (Machitidwe 24:15)

14 Ndipo kachiwiri’nso, taononi! pamene paradaiso akubwezeretsedwa pa dziko lapansi, onani kukwaniritsidwa kwa Chibvumbulutso 20:11-13:

“Ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera [m’mwamba], ndi Iye wakukhalapo [Yehova Mulungu], . . . Ndipo ndinaona akufa, akulu ndi ang’ono alinkuima ku mpando wachifumu; ndipo mabukhu anatsegulidwa; . . . ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabukhu, monga mwa ntchito zao.”

Unyinji wa anthu umene uli m’manda uyenera kubwezeretsedwa ku moyo pa dziko lapansi. Iwo’nso, ali pakati pa “ambiri” a banja la Yesu, ogudwa ndi nsembe yake, ndi amene kupanda ungwiro kwao iye akukuchotsa tsopano. (Ahebri 9:28) Iye akuwaweruza, osati mogwirizana ndi machimo ao akale, koma monga mwa ntchito zao m’kugwirizana ndi zimene ‘zalembedwa m’mabukhu’-zofunika za Mulungu zoti apezere moyo m’dziko lapansi la paradaiso.

15. Kodi ndani amene akupanga makonzedwe odabwitsa amene ‘wa, ndipo chotero kodi ndi motani m’mene moyenera tinganenere? (1 Akorinto 15:55, 57)

15 Mofanana ndi munthu waufulu wokoma mtima ndi mwana wake wamwamuna m’fanizo lathu lija, Atate wa kumwamba, Yehova, ndi Mwana wake, Kristu Yesu, akuchita’di utumiki wodabwitsa wachikondi m’kuombola anthufe ku mkhalidwe wonga wa mwana wamasiye ndi kutibwezera ku moyo weni-weni. Polingalira makonzedwe abwino kwambiri amene’wa, timanena modabwa kuti:

“Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulika’di maweruzo ake, ndi njira zake n’zosalondoleka!”-Aroma 11:33.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena