Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • go mutu 8 tsamba 121-149
  • Masiku Osonyezedwa M’kati mwa “Nthawi ya Mapeto”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masiku Osonyezedwa M’kati mwa “Nthawi ya Mapeto”
  • Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • TSOPANO BUKHU LATSEGULIDWA
  • “NTHAWI ZOIKIDWIRATU” ZITATU NDI THEKA
  • MASIKU 1,290 NDI MASIKU 1,335
  • CHIMWEMWE PAMBUYO PA MASIKU 1,335
  • Masiku aulosi a Danieli ndi Chikhulupiriro Chathu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kuzindikira Alambiri Oona M’nthaŵi ya Chimaliziro
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Yehova Alonjeza Danieli Mphotho Yodabwitsa
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Woimira Wamkulu wa Mulungu m’Boma la Dziko
    Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
Onani Zambiri
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
go mutu 8 tsamba 121-149

Mutu 8

Masiku Osonyezedwa M’kati mwa “Nthawi ya Mapeto”

1. Kodi “nthawi ya mapeto” ikusonyezedwa ndi nyengo za nthawi zotani?

“NTHAWI ya mapeto” iri ndi mapeto ake kapena pothera. Mapeto ake akulu ali mu “nthawi ya masautso” imene palibe yofanana nayo imene mitundu inakumana nayo ndi kale lonse ndipo sidzakumana nayo kachiwiri’nso. M’kati mwa “nthawi ya mapeto” yonenedwa’yo pali masiku osonyezedwa. Amene’wa ndi nyengo za nthawi zimene zimayambukira “opatulika a Wam’mwamba-mwamba’yo,” otsalira otsirizira a ophunzira obadwa ndi mzimu a Kristu amene aikidwa kukhala ndi phande limodzi ndi Yesu kumwamba. “Masiku” amene’wa anali ofunika kwambiri kwakuti n’kuchulidwa kwa mneneri wokalamba Danieli wa m’nthawi zakale.—Danieli 7:25.

2. Kodi ndi motani m’mene mitundu yozunza “oyera” idzakhalira potsirizira pake?

2 M’mbali yotsirizira ya chaputala cha khumi ndi chimodzi cha ulosi wake, Danieli molosera akusonya ku zaka zathu za zana la makumi awiri zino ndi kulimbana kwakukulu pakati pa gulu la mitundu ya demokratiki, yaufulu, ndi yololeza kuchita bizinesi ndi mtundu wa mitundu yosaloleza kuchita bizinesi. Magulu onse a mitundu’wo akhala ozunza otsala a “oyera” obadwa ndi mzimu a Yehova Mulungu, tsopano ochedwa mboni Zachikristu. (Yesaya 43:10-12; 44:8) Danieli akumaliza chaputala cha khumi ndi chimodzi ndi chithunzithunzi cholosera cha kuzinga kotsirizira kochitidwa ndi “mfumu ya kumpoto” Yachikomunisti’yo molimbana ndi otsalira a Mboni zobadwa ndi mzimu, ndiyeno akuti: “Koma adzafikira chimariziro chake wopanda wina wakum’thandiza.” Okanganira nawo ake ulamuliro wa dziko a ndale za dziko, “mfumu ya kumwela” ya demokratiki, naye’nso adzafikitsidwa ku mapeto amene’wa popanda wina wothandiza ndi kum’pulumutsa.—Danieli 11:45.

3, 4. Kodi ndani amene anali Mikaeli ndi “ana a anthu” a Danieli”?

3 Kodi ndi motani m’mene chionongeko chotheratu chotero’cho cha “mfumu ya kumpoto” ndi “mfumu ya kumwela” chidzadzera? Mngelo wa Yehova wolosera’yo anazilongosola kwa Danieli, kuti: “Ndipo nthawi yomweyi adzauka Mikaeli kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako; ndipo padzakhala nthawi ya masautso, siinakhala yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija; ndipo nthawi yomweyo anthu ako adzapulumutsidwa, yense amene am’peza wolembedwa m’bukhu.”—Danieli 12:1.

4 M’mabukhu ena a Watch Tower Society kwatsimikiziridwa kuti Mikaeli, kalonga wamkulu wakumwamba amene anaima kutumikira ana a anthu a mtundu wa Danieli kale’lo m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., ndiye Mwana wa Mulungu amene anakhala Ambuye Yesu Kristu. (Danieli 10:13, 21; Yuda 9; Chibvumbulutso 12:7) Ana a anthu a mtundu wa Danieli kale’lo anali otsalira a Aisrayeli okhulupirika amene anachoka ku Babulo ndi kukamanga’nso Yerusalemu ndi kachisi wa Yehova kumene’ko.

5. Kodi ‘Mikaeli kalonga wamkulu’ akuima m’malo a yani tsopano?

5 Lero lino anthu a mtundu wa Danieli akakhala, osati Aisrayeli akuthupi odulidwa amene anakana Mesiya amene kuonekera kwake Danieli (9:24, 25) anakuneneratu, koma otsalira a Aisrayeli auzimu a lero lino, mboni Zachikristu zobadwa ndi mzimu za Yehova m’kati mwa zaka zino za zina la makumi awiri. M’malo mwa Aisrayeli auzimu amene’wa Yesu Mesiya wolemekezedwa’yo, monga ‘Mikaeli kalonga wamkulu’ kachiwiri’nso kumwamba, akuimirira, ndipo akugwiritsira ntchito mphamvu yake ndi ulamuliro m’malo mwa otsalira auzimu amene’wa. Kachitidwe kamene’ka ndiko kamene kakachititsa “nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija.”

6. Kodi ndani amene adzapulumuka “nthawi ya masautso”?

6 “Nthawi ya masautso” yosafanana ndi ina iri yonse’yo ndiyo “chisautso chachikulu” za chimene Chibvumbulutso mwa njira ya Yesu chimanena ndi chimene chinasonyezedwa mwa chitsanzo ndi chionongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. monga momwe kunanenedweratu ndi Yesu Kristu. (Chibvumbulutso 7:14, Mateyu 24:21, 22) Ndimo mwa “chisautso chachikulu” chimene’chi kuti “nthawi ya mapeto” imene tsopano ikutha’yo ikufika pa mapeto ake akulu! M’kati mwa “chisautso chachikulu” chosafanana ndi china chiri chonse chimene’cho kapena “nthawi ya masautso” “mfumu ya kumwela” ophiphiritsira’wo sadzapulumuka chionongeko, koma padzakhala ena amene adzapulumuka. Ndani? Anthu a mtundu wa Danieli a lero lino, otsalira a Aisrayeli auzimu, “yense amene am’peza wolembedwa m’bukhu.” (Onani Malaki 3:16 ndi Ahebri 12:23.) Ndipo’nso, Chibvumbulutso 7:9-17 chimatipatsa chitsimikiziritso chakuti “khamu lalikulu” la alambiri a Mulungu wa Danieli ndi okhulupirira Mesiya Yesu adzapulumuka limodzi ndi otsalira a Israyeli wauzimu. Mulungu amasunga mbiri ya alambiri ake okhulupirika.

7, 8. Kodi ndi motani m’mene akufa adzaukira kumka ku moyo wamuyaya kapena ku chitonzo?

7 Ha, ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chotani nanga chimene chiri patsogolo pathu! Pambuyo pa “nthawi ya masautso” imene’yo imene iribe yofanana nayo m’mbiri ya anthu padzayamba chiukiriro cha akufa, pansi pa boma la dziko la Mulungu lokhala m’manja mwa Mesiya wake Yesu, kapena ‘Mikaeli kalonga wamkulu.’ Imene’yi ndiyo ndandanda ya zochitika malinga ndi zimene mngelo anauza Danieli, amene tsopano akupitirizabe kusimba zimene mngelo ananena: “Ndipo ambiri a iwo ogona m’pfumbi lapansi adzauka, ena kumka ku moyo wosatha, ndi ena ku manyazi ndi mnyozo wosatha.”—Danieli 12:2.

8 Ndithudi, m’mene okhala pa dziko lapansi apapitapo amene’wa anachitira m’kati mwa moyo uno, kudzayambukira kaimidwe kao koyambirira pa dziko lapansi pansi pa boma la dziko Laumesiya. Koma m’mene pambuyo pake iwo akulinganizira miyoyo yao pansi pa boma la dziko la zaka chikwi limene’li kudzatsimikizira kaya iwo potsirizira pake adzaweruzidwa kukhala oyenerera moyo wosatha m’dziko lapansi la Paradaiso kapena oyenera chionongeko chamuyaya monga anthu onyozedwa ndi kunyansa kopanda mapeto. Yesu Kristu ananena za kuthekera kumene’ko kaamba ka akufa oukitsidwa, pa Yohane 5:28, 29.

9. Kodi ndi owala otani amene adzatembenuzira ambiri ku chilungamo? Liti?

9 Pamenepo aulemerero adzakhala malo ndi mwai wa “opatulika a Wam’mwamba-mwamba” kwa amene ufumu ndi ulamuliro wakumwamba ziyenera kuperekedwa limodzi ndi Mesiya Yesu, ‘Mikaeli kalonga wamkulu.’ Ponena za zimene’zi mngelo’yo anapitiriza kunena ndi Danieli kuti: “Ndipo anthu okhala ndi chidziwitso adzawala ngati kuwala kwa thambo; ndipo awo otembenuzira ambiri ku chilungamo, ngati nyenyezi ku nthawi yosatha, ngakhale kwamuyaya.” (Danieli 12:3, NW) Awo ofikitsidwa ku chilungamo pansi pa boma la dziko Laumesiya adzakhala anthu amene adzapeza “moyo wamuyaya” m’dziko lapansi la Paradaiso. Koma ngakhale tsopano, m’kati mwa “nthawi ya mapeto ino,” otsalira a “opatulika a Wam’mwamba-mwamba” akusonyeza chidziwitso chauzimu ndipo chifukwa cha chimene’cho ali otanganitsidwa ndi kutembenuzira “khamu lalikulu” ku chilungamo limodzi ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya pa dziko lapansi la Paradaiso.—Mateyu 25:46.

TSOPANO BUKHU LATSEGULIDWA

10. Kodi n’chifukwa ninji yathu ino iri nthawi ya chidziwitso chonena za ulosi wa Baibulo?

10 Kodi ife lero lino tiri pakati pa awo amene akutembenuzira ambiri ku chilungamo kapena pakati pa awo amene akutembenuziridwa ku chilungamo chimene chimapatsa lonjezo la moyo wosatha? Ngati kuli choncho, pamenepo tingathe kuzindikira kuti tikukhala ndi moyo m’nthawi yabwino kwambiri. Chiyambire pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914 takhala tikukhala ndi moyo mu “nthawi ya mapeto.” Iri nthawi ya chidziwitso chauzimu choonjezereka, yakuti ochuluka a maulosi osalongosoledwa a Baibulo Loyera, kuphatikizapo ulosi wa Danieli, azindikiritsidwe maganizo ndi mitima yathu. Yathu’yi ndiyo nthawi imene mngelo anasonya’ko pamene iye anati kwa Danieli: “Ndipo ponena za iwe, O Danieli, usaulule mau ndipo matira bukhu’lo, kufikira nthawi ya mapeto. Ambiri adzayenda-yenda, ndipo chidziwitso choona chidzachuluka.”—Danieli 12:4, NW.

11. Kodi ndani amene ali ‘oyenda-yenda ambiri’ onenedweratu m’Danieli 12:4?

11 Lero lino anthu mabiliyoni ambiri akuyenda pa liwiro lothamanga kwambiri mwa njira zonse zamakono za kuyenda kofulumira. Komabe amene’wa sindiwo “ambiri” onenedweratu m’Danieli 12:4. Koma Nkhondo Yoyamba ya Dziko itatha mu 1918, “ambiri” anali Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse amene anayamba “kuyenda-yenda,” motani? Mwamaganizo, m’phunziro lozama la maulosi a Baibulo, kuphatikizapo ulosi wa Danieli. Zinsinsi zobisika kwa nthawi yaitali za Mau a Mulungu tsopano zinali zitakwana nthawi yake yakuti zimasulidwe. Chotero ‘oyenda-yenda’ auzimu amene’wa anakhala ndi “chidziwitso cheni-cheni choona” cha Bukhu lotsegulidwa tsopano’lo la Mau a Mulungu ‘chochuluka’ kwa iwo. Mopanda dyera iwo akuwanditsa “chidziwitso choona” chimene’chi kuli konse mwa mau a pakamwa ndi mwa masamba osindikizidwa m’malo mwakuti onse amene akufuna moyo wosatha pansi pa boma la dziko la Mulungu achitepo kanthu pa chidziwitso chimene’chi ndipo motero kutembenuziridwa ku chilungamo.—Chibvumbulutso 22:17.

12, 13. Kodi mngelo’yo analumbira kuti ulosi’wo ukatenga “nthawi” zingati?

12 Limodzi ndi mneneri Danieli tiyeni timvetsere pamene mmodzi wa angelo a m’masomphenya ake akufunsa funso lokondweretsa kwa ife’nso kuti: “Chimariziro cha zodabwiza izi chidzafika liti?” Ndiko kuti, Kodi padzapita nthawi yaitali motani kuti zinthu zoopsya zoonedwa ndi Danieli zimene’zi zifike pa mapeto a kukwaniritsidwa kwake? Yankho la funso limene’li likuperekedwa ndi mngelo wina, amene akulumbira manja ake onse atakwezedwa kumwamba ponena za kutsimikizirika ndi kudalirika kwa yankho lake. Danieli akuti:

13 “Iye anakweza dzanja lake lamanja ndi dzanja lake lamanzere kumwamba ndi kulumbira mwa dzina la Uyo amene ali ndi moyo ku nthawi yosatha: ‘Kudzakhala kwa nthawi yoikidwiratu, nthawi zoikidwiratu ndi theka. Ndipo mwamsanga atatha kufafaniza mphamvu ya anthu oyera’wo, zinthu zonse’zi zidzafika pa mapeto ake.’”—Danieli 12:5-7, NW.

14. Kodi n’chifukwa ninji “oyera” anaperekedwa m’manja mwa nyanga “yaing’ono”?

14 Moyenerera “nthawi zitatu ndi theka zoikidwiratu” zimene’zo zimagwira ntchito ku nyengo ya nthawi yofanana ndi “nthawi” zitatu ndi theka zochulidwa mu Danieli 7:25, m’kati mwa zimene “nthawi” kapena “zaka” kapena “zaka” zimene “opatulika a Wam’mwamba-mwamba” obvutitsidwa’wo akuperekedwa m’manja mwa Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri, wophiphiritsiridwa ndi nyanga “yaing’ono” yokhala ndi maso ndi pakamwa pamutu pa ‘chirombo’ chachinai. Chifuno cha kupereka kwa Wam’mwamba-mwamba’yo ‘oyera’ ake m’manja mwa Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chiwiri kwa nyengo ya nthawi imene’yo chinali chakuti pakhale “kufafanizidwa kwa mphamvu ya anthu oyera’wo.” Kachitidwe kotero’ko kololedwa ndi Wam’mwamba-mwamba’yo kakasonyeza motsimikizirika mkhalidwe waudani wa nyanga “yaing’ono” (inde, ndipo’nso, ya “chirombo chachinai” chonse’cho) kulinga kwa “anthu oyera” amene amaumirira ku Ulamuliro wa Chilengedwe Chonse wa Wam’mwamba-mwamba’yo.

“NTHAWI ZOIKIDWIRATU” ZITATU NDI THEKA

15. Kodi ndi liti pamene mphamvu yophwanya ya nyanga’yo inatsimikizira kukhala yopanda mphamvu?

15 Mapeto a “nthawi zoikidwiratu” zitatu ndi theka’zo kapena zaka za miyezi yokhala zinayenera kusonyezedwa ndi “kutsirizidwa kwa kuphwanyidwa kwa mphamvu ya anthu oyera.” (Danieli 12:7, NW; Revised Standard Version; Rotherham; Young) Ndithudi, kumene’ku kukatanthauza’nso kuti kukhoza kwa oimira a ndale za dziko amene akuchita kuphwanya mphamvu ya “anthu oyera” a Yehova kudzayenera kukhala kutafika pa mapeto ake; kukhoza kwake kutero sikudzakhala’nso ndi nyonga kapena mphamvu. Monga momwe katembenuzidwe ka Baibulo kopangidwa ndi Dr. James Moffatt kamalitembenuzira: “Ikakhala zaka zitatu ndi theka, ndi kuti pamene mphamvu ya iye amene anaphwanya anthu opatulika itha, pamenepo mapeto a [zinthu] zonse ayenera kudza.” (Ndipo’nso, An American Translation; The New American Bible) Motero woimira wa ndale za dziko amene anachita kuphwanya’ko m’kati mwa zaka zitatu ndi theka anakhalabe ndi moyo pambuyo pake, koma kukhoza kwake kuphwanya mphamvu ya anthu oyera a Yehova kachiwiri’nso yafika pa mapeto. “Anthu oyera” ophwanyidwa kapena kubalalitsidwa’wo akasonkhana’nso ndi kulinganizidwa’nso ndipo sakagonjera ku kulandidwa “mphamvu” yao.

16. Kodi ndi liti pamene “mphamvu ya anthu oyera” inaphwanyidwa, ndipo motani?

16 “Kutsirizidwa kwa kuphwanyidwa kwa mphamvu ya anthu oyera” mwachionekere kunachitika pa June 21, 1918. Pa tsiku limene’lo khothi lalikulu lachitaganya la Amereka linaweruza Prezidenti ndi mlembi-msungi chuma wa Watch Tower Bible and Tract Society ndi anzao asanu a pa malikulu kuikidwa mu ukaidi wa nthawi yaitali, onse pamodzi zaka zokwanira 140. N’zoona kuti panali pa May 7, 1918, kuti akulu-akulu a Sosaite amene’wa ndi anzao ochuka anagwidwa ndi akulu-akulu a boma, koma iwo anali kuyembekezera chiweruzo ndi kupatsidwa chilango, osalolezedwa kupereka chikole. Chotero kutha kwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko pa November 11, 1918, kuncahitika oimira akulu asanu ndi awiri a Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse, ndi antchito anzao amene’wa, ali m’ndende yachibalo pa Atlanta, Georgia, U.S.A., kumene iwo ananyamulidwira’ko kuchokera ku Brooklyn, New York, pa July 4, 1918. Motero khothi lalikulu la Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka unapereka nkhonya yophwanya kwa “anthu oyera” a Yehova pa June 21, 1918.

17, 18.Chotero, kodi ndi liti pamene zaka zitatu ndi theka za mwezi wokhala zinayamba?

17 Chifukwa cha chimene’cho, kodi zaka zitatu ndi theka’zo, zimene zinayenera kutsirizidwa ndi kachitidwe kophwanya kamene’ko kotsutsana ndi Akristu odzipereka ndi obatizidwa, zinayamba liti? Kodi ndi motani m’mene kuyamba kumene’ko kunasonyezedwera?

18 Eya, malinga ndi kalendala ya Baibulo ya miyezi yokhala, June 21, 1918, anali pa Tammuz 11, 1918. Zaka zitatu za miyezi yokhala kubwerera m’mbuyo kuchokera pamenepo, kapena Tammuz 11, 1915, anali pa June 23, 1915. Ndiyeno theka la chaka cha miyezi yokhala, kapena miyezi yokhala isanu ndi umodzi, kubwerera m’mbuyo kuchokera pamenepo ikakhala Tebeth 11, 1914, amene analingana ndi December 28, 1914.—Onani The Universal Jewish Encyclopedia, pansi pa mutu wakuti “Jewish Calendar for 200 Years,” tsamba 634-639.

19. Kodi Photo-Drama of Creation inapereka chenjezo lotani pa mitundu?

19 Deti limene’lo, December 28, 1914, linali loyenerera kwambiri. M’kati mwa chaka’cho kuyambira kuchiyambi-yambi kwa January Watch Tower Bible and Tract Society inali kusonyeza Photo-Drama of Creation yochuka’yo. M’chisonyezero cha Baibulo chimene’cho, chimene chinali m’zigawo zinai za utali wa maora awiri chigawo chiri chonse, maganizo anasumikidwa pa loto la Nebukadinezara lonena za “fano” la ulamuliro wa dziko ndipo’nso ku loto la “zirombo” zinai za ndale za dziko zimene Danieli anaziona zikutuluka m’nyanja. Moyenerera, chenjezo linaperekedwa pa mitundu lonena za mapeto a Nthawi za Akunja, limodzi ndi tsoka lotsatirapo kwa mitundu yonse yaudziko. Ndipo’nso, nkhondo ya Armagedo inaperekedwa chenjezo, imene’yi inayenera ku tsatiridwa ndi “Miyamba Yatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano.” (Onani tsamba 50, 51, 92, 94 la Zirembo za Photo-Drama of Creation.) Pokwana pa mwezi wa October, m’mwezi umene Nthawi za Akunja zinatha ndipo Nkhondo Yoyamba ya Dziko inali kumawirima, Sewero’lo linali litasonyezedwa kwa anthu ochuluka mu Amereka, Great Britain, Germany, Switzerland, Denmark, Sweden, Finland, Australia, ndi New Zealand.—Kope (Lachingelezi) la Nsanja ya Olonda, la December 15, 1914, tsamba 371, 372.

20. Kodi kope lotsatirapo la Watch Tower pambuyo pa December 28, 1914, linanenanji ponena za mapemphero opemphedwa kuti Nkhondo Yoyamba ya Dziko ithe?

20 M’kope la January 1, 1914, m’kupereka “lingaliro lochokera ku Watch Tower,” magazini a Nsanja ya Olonda anayamba ndi kuti: “Pamene Prezidenti wathu wabwino kwambiri [Thomas Woodrow Wilson] ndipo’nso Papa Woyera anapempha anthu Achikristu kupemphera kwa Mulungu kuti nkhondo ya ku Yuropu ilekeke, ife tinalengeza kuti pemphero limene’lo silinali logwirizana ndi kakonzedwe ka Mulungu ndipo silikayankhidwa. Ife tinasonyeza kuti malinga ndi kunena kwa Malemba zaka 2520 za kulamulira kwa Akunja zinathera m’September, 1914; ndi kuti nkhondo’yo ndiyo imene inanenedweratu ‘Malemba monga yogwirizanitsidwa ndi Tsiku Lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse-“Tsiku la Kubwezera la Mulungu wathu.’ Tinasonyeza Mau a Ambuye kupyolera mwa Mneneri Yoweli onena za kusonkhanitisidwa kwa mitundu yonse ku Chigwa cha Yehosafati—chigwa cha imfa.—Yoweli 3:1-12.” Mogwirizana ndi lingaliro limene’li, nkhani yoyambirira yophunziridwa ya magazini amodzimodzi’wo inali ndi mutu wakuti “Nkhondo Yoyamba ya Armagedo.”—Tsamba 7.

21. Kodi ndi motani m’mene Lemba la Chaka la 1915 linasonyezera kuti kubvutika kunali kuyembekezeredwa?

21 Pamenepo chizunzo chinali kuyembekezeredwa ndi mipingo ya Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse, pakuti, pansi pa mutu wakuti “1915—Lemba Lathu la Chaka-1915,” kope limodzi-modzi’lo la Nsanja ya Olonda linayamba mwakumati: “Tasankha monga lemba la chaka mau a Ambuye onenedwa kupachikidwa Kwake pa mtanda kutangotsala pang’ono kwa ophunzira Ake awiri okondedwa, amene anapempha kukhala limodzi Naye mu Mpando Wake Wachifumu. Tasankha yankho la Ambuye monga lemba la chaka chino: ‘Kodi mungakhoze kumwera chikho Changa?’—Mateyu 20:20-23.” (Tsamba 11) Pofika pa nthawi imene’yo mitundu khumi ndi maufumu inali m’nkhondo ndipo yochuluka inali kumalowamo m’kati mwa 1915 ndi pambuyo pake kufikira potsirizira pake mitundu makumi awiri mphambu isanu ndi itatu ndi maufumu inali italowetsedwa m’Nkhondo Yoyamba ya Dziko. Chotero “anthu oyera” a Yehova, pa nthawi imene’yo ochedwa Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse, sakanatha kupewa zizunzo ndi mabvuto zonga zimene zikuphatikizidwa ‘m’kumwera chikho’ cha Ambuye wao, Yesu Kristu.

22. Chiyambire 1876 kodi anachenjeza mitundu za chiani ponena za 1914?

22 Chiyambire m’chaka cha 1876 awo amene anakhala ogwirizana ndi Watch Tower Bible And Tract Society ndi Gulu la Ophunzira Baibulo la m’Mitundu Yonse anakhala akulengeza poyera kuti Nthawi za Akunja zikatha kuchiyambi-yambi kwa mphakasa ya 1914. Chifukwa cha chimene’cho, iwo anachenjeza dziko lonse za chionongeko cha Mitundu Yachikunja kuti ipereke malo ku ufumu wa Mulungu wa zaka chikwi wokhala m’manja mwa Mwana wake wolemekezedwa Yesu Kristu. Pamene Akristu odzipereka, obatizidwa ndi odzozedwa ndi mzimu amene’wa anali atalengeza chionongeko chinalinkudza cha mitundu yonse yaudziko, kuphatikizapo Ufumu wa Britain ndi United States wa ku North America, mitundu imene’yi inayamba kuononga olengeza ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Kristu. Iyo inagwiritsira ntchito mkhalidwe umene unapangidwa ndi Nkhondo Yoyamba ya Dziko kuchita motero.—Onani Chibvumbulutso 11:3-10; 13:1,2,5, 7.

23. Mu 1917 kodi ndi bukhu lotani limene linapereka maziko oonjezereka a chizunzo?

23 Pa July 17, 1917, Watch Tower Bible and Tract Society inatulutsa bukhu lakuti “The Finished Mystery.” Bukhu limene’li linalongosola Chibvumbulutso ndi ulosi wa Ezekieli, ndipo, mosapeweka, linagogomezera kuonongedwa kwa Babulo Wamkulu wachipembedzo ndi mabwenzi ake a ndale za dziko, a magulu ankhondo, achiweruzo ndi amalonda. (Yakobo 4:4) Limene’li linapereka maziko ena kwa olamulira a ndale za dziko osonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo a Babulo Wamkulu, ‘kuphwanya mphamvu ya anthu oyera a Yehova.’ Kumeneku iwo anakuchita pofika pa mapeto a zaka zitatu ndi theka zonenedweratu’zo pa June 21, 1918. Chotero nyengo imene’yi inayamba pa December 28, 1914, m’dzinja loyamba la kumpoto la Nkhondo Yoyamba ya Dziko. Pofika pa nthawi imene’yo Ophunzira Baibulo a m’Mitundu Yonse, amene anali okana mwachikumbu mtima nkhondo yakuthupi, anaona chitsenderezo choonjezereka-onjezereka pa iwo chakuti agonjere ndi kulowa mu Ufumu wa Britain, Ufumu wa Jeremani, Ufumu wa Austria ndi Hungary, Ufumu wa Fransa, Belgium okonzekera nkhondo’wo, ndi mitundu ina isanu imene pa nthawi’yo inali kumeneyana m’nkhondo yomafalikira’yo ya dziko. Lemba lao la Baibulo losankhidwa kaamba ka 1915 linasonyeza cheni-cheni chimene’cho. Chotero nyengo ya “nthawi” zitatu ndi theka ikusonyezedwa bwino lomwe!

24. Kodi Danieli anazindikira masomphenya’wo? Kodi n’chifukwa chotani chimene chinaperekedwa?

24 Ndithudi, mneneri Danieli sakanatha kuona m’mene zinthu zonse zoopsya zimene zinabvumbulidwa kwa iye zikachitikira m’mbiri yamakono. Iye mwini anati: “Ndinachimva ichi, koma osachizindikira; pamenepo ndinati Mbuye wanga; chitsiriziro cha izi n’chiani? Ndipo anati, Pita Danieli; pakuti mau’wo atsekedwa, nakomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro. Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.”—Danieli 12:8-10.

25, 26. Chifukwa cha chimene’cho, kodi ndi m’kagulu kati kochulidwa m’kamene ife tikufuna kupezekamo?

25 Danieli ‘sanazindikire’ zimene iye anamva, m’nthawi yake. Koma ife, m’nthawi ino, mu “masiku otsiriza” ano chiyambire 1914, tikuzindikira. Koma osati ngati ife ‘tikuchita moipa! Pamenepa, kodi ndi motani m’mene, ife tikuchitira? Moipa, kapena mwa chidziwitso chauzimu? Zotulukapo zimasiyana!

26 Tiyeni tilingalire mwamphamvu zimene mngelo ananena ndi Danieli ponena za “nthawi ya masautso,” ndiko kuti, kuti ‘anthu a mtundu wa Danieli adzapulumutsidwa, yense wopezedwa wolembedwa m’bukhu.’ (Danieli 12:1) Kodi tikufuna kugwirizanitsidwa ndi “anthu” a Danieli? Pamenepo liri thayo lathu kupewa kupezeka pakati pa awo ochita moipa m’nthawi ya mapeto ino. Tikufuna kuti maina athu ‘apezedwa olembedwa m’bukhu’ la Mulungu. Kuti tifikire chonulirapo chimene’chi tifunikira kusonyeza “chidziwitso” mwa kusanthula Mau a Mulungu, kuphunzira uthenga wake wopatsa chilangizo kaamba ka nthawi yathu yobvuta ndiyeno kuchita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Tiyeni tilole ‘chidziwitso [choona]’ chichuluke!

MASIKU 1,290 NDI MASIKU 1,335

27-29. Kodi ndi nyengo zina zotani zimene zinanenedweratu ponena za “nthawi ya mapeto”?

27 Ponena za chidziwitso cholosera’cho choperekedwa kwa Danieli, mngelo’yo anati: “Mau’wo atsekedwa, nakomeredwa chizindikiro mpaka nthawi ya chitsiriziro.” (Danieli 12:9) Cheni-cheni chakuti “mau” obisika ndi osindikizidwa chizindikiro pa nthawi ina’wo tsopano atsegulidwa ndi kubvumbulidwa chimaonjezera ku umboni wochuluka’wo wakuti, chiyambire pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914, takhala tiri mu “nthawi ya mapeto” yochititsa nthumanzi. Tikuona m’mene “nthawi zoikidwiratu, nthawi zina zoikidwiratu ndi theka” za Danieli 12:7 zayeneranira ndi “nthawi ya mapeto imene’yi.” Ngakhale kuli kwakuti zaka zitatu ndi theka zimene’zo zinatha kale-kale, komabe izo zinasonyeza posinthira m’njira ya otsalira a “anthu” amakono a Danieli, kotero kuti zimene’zi zayambukira mboni Zachikristu za Yehova zimene ziri ndi moyo lero lino. Koma pali nyengo zina za nthawi zimene zaperekedwa ndi Yehova ku “nthawi ya mapeto” yokondweretsa imene’yi, ndipo Danieli 12:11, 12 tsopano akutisonyeza zimene’zi kuti:

28 “Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhala’nso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

29 “Wodala iye amene ayembekeza, nafikira ku masiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.”

30. Kodi ndani amene akuimika “chonyansa” chakupululutsa?

30 Pano, kaamba ka chitsogozo chathu m’kumvetsetsa zinthu, tiyenera kukumbukira kuti Babulo Wamkulu wachipembedzo’yo sakuika kapena kukhazikitsa “chonyansa chakupululutsa.” Magulu a ndale za dziko a dongosolo iri la zinthu akuchita chimene’chi. Kuti “masiku chikwin chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai” ayambe, zofunika zonse ziyenera kukwaniritsidwa, ndiko kuti, “nsembe yachikhalire” iyenera kuchotsedwa ndipo “chonyansa chakupululutsa” chiyenera kuikidwa m’malo ake. Kuchotsedwa kwa “nsembe yachikhalire” kunachitika m’kati mwa “nthawi yoikidwiratu, nthawi zina zoikidwiratu ndi theka” zimene zinakwana m’kati mwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko, kuyambira pa December 28, 1914, kufikira pa kulowa kwa dzuwa kwa pa June 21, 1918. “nsembe yachikhalire” inayenera kulowetsamo “anthu oyera” a Yehova, amene “mphamvu” yao yauzimu inaphwanyidwa kale’lo.

31. Kodi n’chiani chimene chinali “nsembe yachikhalire” yoperekedwa ndi anthu a Danieli?

31 Mu 537 B.C.E. anthu a mneneri Danieli anamasulidwa ku Babulo wakale ndi wogonjetsa Koresi Mperisi, ndipo iwo anabwerera ku dziko la Yuda kukabwezeretsa kulambiridwa kwa Yehova pa Yerusalemu. Kumeneko, pa mapeto a zaka makumi asanu ndi awiri a kukhala bwinja kwa dziko lakwao, iwo anapiritiza “kumanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israyeli, kupereka nsembe zoocha pa iro, mogwirizana ndi zimene zalembedwa m’chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu woona.” (Ezara 3:1, 2, NW) Kuyambira pa nthawi imene’yo kumkabe m’tsogolo “nsembe yachikhalire” ya tsiku liri lonse inaperekedwa ndi ansembe, kupatulapo kudodometsedwa kwa kanthawi kochitidwa ndi Asuri m’kati mwa masiku a Amakabeo Achilevi m’zaka za zana lachiwiri B.C.E. (Eksodo 29:38, 39) Komabe, kodi n’chiani, chimene chinali “nsembe yachikhalire” ya tsiku ndi tsiku imene Aisrayeli auzimu anali kupereka kwa Mulungu pa chiyambi cha “nthawi za mapeto” mu 1914?

32. Kodi “nsembe yachikhalire” inali ndi chiani chiyambire 1914 C.E.?

32 Iyo sinakhale ndi nsembe ya nyama zoperekedwa pa guwa la nsembe pa Yerusalemu m’Middle East. Nsembe zotero’zo zinalekeka kuperekedwa kumene’ko m’chaka 70 C.E. pa kuononedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi wake wokongola’yo kochitidwa ndi magulu ankhondo Achiroma. Zaka zambiri chimene’cho chisanachitike, mtumwi Wachikristu Petro analemba, akumanena kuti Aisrayeli auzimu odzozedwa “akumangidwa kukhala nyumba yauzimu kaamba ka chifuno cha unsembe woyera, kupereka nsembe zauzimu zolandirika kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu.” (1 Petro 2:5, 9, NW) “Nsembe zauzimu” zimene’zi zimaphitikizamo “nsembe ya chitamando, imene iri, chipatso cha miromo imene imapanga chilengezo chapoyera cha dzina lake.” (Ahebri 13:15, NW) Nthawi za Akunja zitatha mu 1914 ndipo ufumu wa Mulungu Waumesiya unabadwa kumwamba, “nsembe ya chitamando” monga mbali ya “nsembe yachikhalire” imene inaperekedwa ndi Aisrayeli auzimu kweni-kweni inali ndi kuchitira umboni ufumu wakumwamba wokhazikitsidwa’wo m’manja mwa Yesu Kristu.—Mateyu 24:3, 14, NW.

33. Kodi ndi liti pamene kuchotsedwa kwa “nsembe yachikhalire” kunachititdwa?

33 Mwa kubvutitsa mboni za Ufumu zodzozedwa’zo ndipo potsirizira pake mwa kuononga “mphamvu” yao yauzimu yolalikirira ufumu wa Mulungu umene uyenera kuposa maboma onse opangidwa ndi anthu pa dziko lapansi, mitundu yomenyana’yo inatsendereza mboni za Ufumu’yo ndipo motero inachotsa “nsembe yachikhalire.” Zimene’zi zinachitidwa pofika pa June 21, 1918. Kwa miyezi isanu ndi itatu ndi masiku anai pambuyo pake akulu-akulu oweruzidwa’wo a Watch Tower Bible and Tract Society ndi antchito anzao anakhalabe m’ndende yachitaganya, kuyembekezera kumasulidwa kwao atalipira chikole kaamba ka kuimbidwa mlandu kwatsopano ndi kuchotseredwa zinenezo zonse zonama. Kuikidwa kwao m’ndende kosalungama kwa nthawi yaitali kunachita monga cholepheretsa chachikulu ku kupereka “nsembe yachikhalire” kochititdwa ndi mboni Zaufumu. Koma bwanji ponena za “chonyansa chakupululutsa” chimene chimapululutsa?

34. Kodi ndi motani m’mene “choyansa” chinapangidwira kukhalako?

34 “Chonyansa chakupululutsa” ndicho gulu la m’mitundu yonse la mtendere ndi chisungiko za dziko. Limene’li poyamba linalinganizidwa ndi msonkhano wa mtendere umene unasonkhaniridwa mu Versailles, Fransa, pa January 18, 1919. Mabwenzi opambana nkhondo’wo anapanga pangano la mtendere limene linaperekedwa kwa nthumwi za ku Jeremani pa May 7, 1919. Pa June 28, 1919, Ajeremani ndi nthumwi zogwirizana’zo anasaina pangano la mtendere limene’li pa Versailles. Gulu la m’Mitundu yonse la mtendere ndi chisungiko, pa nthawi imene’yo lochedwa Chigwirizano cha Mitundu, linali mbali yofunika kwambiri ya pangano la mtendere limene’lo, ndipo pamene maboma olowetsedwamo anabvomereza pangano la mtendere losainidwa’lo, Chigwirizano cha Mitundu chinayamba kugwira ntchito.

35. Kodi ndi motani m’mene atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko anachirikizira Chigwirizano cha Mitundu?

35 Zimene’zo zisanachitike, pamene msonkhano wa mtendere umene unalambula njira kaamba ka Chigwirizano cha Mitundu unasonkhana pa January 18, 1919, atsogoleri achipembedzo a Chalichi cha England ndi Chitaganya cha Upo wa Machalichi a Kristu mu Amereka ananena mobvomereza Chigwirizano cha Mitundu cholinganizidwa’cho ndipo anachirikiza kupangidwa kwake. Atsogoleri achipembedzo analitamanda kukhala “chisonyezero cha ndale za dziko cha Ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi.”

36. Chotero, kodi ndi liti pamene masiku 1,290 anayamba ndi kutha?

36 Ngati, tsopano, tiwerenga masiku 1,290 kuyambira padeti losonyezedwa limene’lo, January 18, 1919, pamene oimira asanu ndi atatu a Watch Tower Bible and Tract Society anali chikhalirebe mu ukaidi m’ndende yachibalo yachitaganya ya Atlanta, kodi tikufika pati? Malinga ndi kunena kwa Baibulo, masiku 1,290 amene’wo ali olingana ndi zaka za mwezi wokhala zitatu ndi miyezi ya mwezi wokhala isanu ndi iwiri. Malinga ndi kalenda ya mwezi wokhala, January 18, 1919, anakwana pa Shebat 17, 1919. Zaka zitatu za mwezi wokhala kuyambira pamenepo zikatifikitsa ku Shebat 17, 1922, kapena February 15, 1922. Miyezi isanu ndi iwiri ya mwezi wokhala yowerengedwa kuchokera pamenepo ikathera pa Elul 16, 1922, kapena pa kulowa kwa dzuwa, September 9, 1922. Chotero kodi masiku 1,290 kapena zaka zitatu za mwezi wokhala ndi miyezi isanu ndi iwiri anathera pa nthawi yapadera’yo? Zeni-zeni za mu mbiri zikuyankha kuti Inde!

37. Kodi ndi motani m’mene tsiku lotsatirapo’lo, September 10, 1922, linaliri lapadera?

37 Tsiku lotsatirapo, September 10, 1922, Sande, linatsimikizira kukhala tsiku lachisanu ndi chimodzi la msonkhano wa mitundu yonse wa International Bible Students Association wa masiku asanu ndi anai pa Cedar Point Ohio, U.S.A. Pa programu iro linachedwa “Tsiku la Ntchito.” Mbali yaikulu ya tsiku’lo inali nkhani yapoyera kwa omvetesera 18,000, yokambidwa ndi prezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society. Pa mapeto a nkhani yake, wokamba nkhani’yo anapereka kwa omvetsera ake chitsimikiziro chochedwa “Chilengezo,” chimene chinapereka chitokoso kwa olamuliro onse a dziko. Chilengezo chimene’chi chinali ndi cholinga, osati kokha kaamba ka ochita msonkhano’wo, koma kaamba ka dziko lonse, ndipo pambuyo pa msonkhano wa pa Cedar Point chinafalitsidwa mu mpangidwe wa trakiti ndi kugawiridwa makope mamiliyoni makumi ochuluka m’zinerero zambiri.

38. Kodi n’chiani chimene chinapangitsa September 9, 1922, weni-weni’yo, ndi September 8 kukhala wapadera?

38 Dzulo lake, Loweruka, September 9, linali ndi mutu wakuti “Tsiku Lopatulika” ndipo linapangitsidwa kukhala lapadera ndi ubatizo wa amuna ndi akazi ambiri-mbiri 361 mochitira chizindikiro kudzipereka kwao kwa Mulungu kupyolera mwa Kristu. Komabe, Lachisanu, September 8, linali ndi mutu wakuti “Tsiku’lo,” limene linasonyeza nkhani ya prezidenti wa Sosaite pa mutu wopezeka m’Mateyu 4:17: “Ufumu wa Kumwamba Wayandikira.” Chakumapeto kwa nkhani yake, wokamba nkhani’yo anati:

“Pamenepo, nchifukwa ninji, uthenga’wo, uyenera kuperekedwa kwa amene sakuumvetsetsa? Kodi ali yense adzamva? Mneneri wa Ambuye akuyankha kuti: “Tulutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu. Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ichi ndi kuonetsa ife zinthu zakale? atenge mboni zao, kuti abvomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi. Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina. Ine Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha. Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wachilendo pakati pa inu; chifukwa chake inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.’—Yesaya 43:8-12.

“Motero tikuona kuti awo a kagulu ka kachisi momvekera bwino akuchedwa mboni za Ambuye pa nthawi ino, kupereka uthenga wa chitonthozo kwa anthu, wakuti ufumu wa kumwamba wafika, . . .”

Chotero, moyenera kotheratu, prezidenti wa Sosaite’yo anatsiriza nkhani yake yosonkhezera’yo ndi chisonkhezero ichi: “Lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake.”

39. Kodi ndi motani m’mene Lolemba, September 11, 1922, linakhalira lapadera?

39 Mwai wa pa nthawi yomwe’yo wa kulengeza unaperekedwa pa tsiku la pambuyo pa nkhani yapoyera’yo ndi chitsimikiziro chotokosa cholandiridwa ndi onse ochita msonkhano’wo. Lolemba limene’lo, September 11, 1922, linali ndi mutu wakuti “Tsiku la Utumuki,” ndipo ochita msonkhano’wo anabalalika kulowa mu utumiki wakumunda, ozindikira kotheratu koposa kale kuti iwo anali oimira olengeza pasadakhale ufumu waulemerero wa Mulungu.

40. Kodi ndi kusonyezedwa kotani kwa mkwiyo wa Mulungu kumene motero kunayambidwa poyera?

40 Pambuyo pake, kunazindikiridwa kuti uthenga wa onse ndi chitsimikiziro zolandiridwa mogwirizana ndi uthenga wa kwa anthu onse’wo zinali chiyambi cha kukwaniritsidwa kwa zimene zinanenedweratu m’Chibvumbulutso, chaputala chachisanu ndi chitatu kufikira cha khumi ndi chisanu ndi chimodzi. Kodi chimene’cho chinali chiani? Kulizidwa kwa malipenga asanu ndi awiri ndi kutsanulidwa kwa miliri yotsirizira isanu ndi iwiri ya mkwiyo wa Yehova pa dongosolo la zinthu loyembekezera kuonongedwa’li.

41. Kodi ndi mkangano waukulu wotani umene motero unali kutulukira poyera m’chilengedwe chonse?

41 Powerenga masiku 1,290 a Danieli 12:11 m’njira yoperekedwa pano’yi, kodi tikupeza kuti akuthera pa nthawi yapadera kwambiri? Tiri ndi chikhulupiriro chiri chonse chokhulupirira motero. Pangakhale popanda chikaikiro kuti masiku 1,290 owerengeredwa motero’wo amasonyeza chiyambi cha nyengo yatsopano kaamba ka “anthu oyera” a Yehova m’nthawi ya mapeto ino. Mkangano waukulu pamaso pa chilengedwe chonse pa nthawi imene’yo unali kutulukira poyera, ndiko kuti Ulamuliro wa Yehova wa m’Chilengedwe Chonse.

CHIMWEMWE PAMBUYO PA MASIKU 1,335

42. Kodi kutha kwa masiku 1,335 kunayenera kusonyezedwa ndi chiani?

42 Tsopano, bwanji, ponena za masiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu monga momwe asonyezedwera ndi Danieli 12:12? Mngelo’yo sananene kanthu ponena za nthawi imene masiku amene’wa adzayamba; iye anangosonyeza kuti iwo akathera pa kulowa kwa anthu oyembekezera’wo m’chimwemwe chachikulu kopambana: “Wodala iye amene ayembekeza, nafikira ku masiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.” Mwachionekere masiku 1,335 amene’wa ali kufutukulidwa kwa nthawi pa masiku 1,290 amene angochulidwa kumene’wo, amene anathera m’kati mwa msonkhano wa I.B.S.A. pa Cedar Point, Ohio, Mu 1922. Kufutukulidwa kwa nthawi kotero’ko—kwa masiku 1,335 oonjezereka—kunafunikiritsa chipiriro choonjezereka kwa otsalira a “anthu oyera” a Yehova amene anapulumuka Nkhondo Yoyamba ya Dziko. Iwo anali ndi lingaliro lochepa pa nthawi’yo ponena za chimwemwe chimene chikaperekedwa kwa iwo kaamba ka kupirira ndi kufika pa mapeto a masiku 1,335 amene’wo. Chotero-kodi ndi liti pamene masiku amene’wo anayamba ndi kutha?

43. Malinga ndi kalendala ya Baibulo, kodi ndi liti pamene masiku 1,335 anatha?

43 Msonkhano wachiwiri wa pa Cedar Point unatha pa September 13, 1922. Ngati, tsopano, tiwerenga kuchokera pa tsiku lotsatirapo, September 14, kapena, Elul 21, 1922, nthawi ya kalendala ya Baibulo, kodi masiku 1,335 akatha liti? Popeza kuti masiku 1,290 anakwana zaka zitatu za mwezi wokhala ndi miyezi isanu ndi iwiri, chotero masiku 1,335 akakwanira zaka zitatu za mwezi wokhala, miyezi isanu ndi itatu ndi masiku khumi ndi asanu. Powerenga tsopano kuchokera pa Elul 21 (kapens, September 14), 1922, tikupeza kuti zaka zitatu za mwezi wokhala kuchokera pa deti limene’lo zikathera pa Elul 20 (kapena, September 9), 1925. Ku zimene’zi tikuonjeza’ko miyezi isanu ndi itatu ya mwezi wokhala ndi masiku khumi ndi asanu ndipo tikufika pa deti la Sivan 6 (kapena, May 19), 1926. Tsiku limene’lo linali tsiku la chimwemwe la chaka ndi chaka lachi—1,893 la Pentekoste wa 33 C.E., pamene mzimu woyera unatsanuliridwa pa ophunzira a Yesu pa Yerusalemu.

44. Kodi n’chiani chimene chinayambirira ndipo n’chiani chimene chinatsatizana mwamsanga ndi tsiku limene’lo?

44 Limene’li lisanakwane, pa May 13-16, 1926, msonkhano wa onse unachitika pa m’Magderburg, Jeremani, pa umene prezidenti wa Watch Tower Society anakambira nkhani anthu osonkhana 25,000 pa mutu wa nkhani wakuti “Chitonthozo kaamba ka Anthu.” Tsopano, pa May 19, malinganizidwe anapiritirizidwabe kaamba ka kuchitidwa kwa msonkhano wapadera wa mitundu yonse wa 1926, umene’wo pa Alexandra Palace, London, England, May 25-31. Nthumwi zambiri zachimwemwe zinachokera ku maiko akutali.

45. Pofika pa nthawi imene’yo kodi Ophunzira Baibulo Achikristu anasankha kulemekeza yani?

45 Msonkhano wa ku London umene’wu unapanga kuthandizira kwakukulu ku chimwemwe cha anthu a mneneri Danieli, otsalira a Aisrayeli auzimu. Pa nthawi imene’yo, panalibe anthu ambiri amene anali okondwa ndi kutengedwa kwa Italiya ndi Afasisti. Mantha anasonkhezeredwa ndi kupita patsogolo kwa gulu la Nazi (National Socialist German Workers’ Party) m’Jeremani. Koma Chigwirizano cha Mitundu cha zaka zisanu ndi chimodzi’cho chinali kumakula-kula mphamvu ndipo chinali chitatsala pang’ono kulandira Jeremani wa pambuyo pa nkhondo’yo kukhala chiwalo chake-pa September 8, 1926. Mosasamala kanthu za zimene’zi International Bible Students Association (I.B.S.A.) inapitirizabe kubvumbula Chigwirizano’cho monga cholowa m’malo cha ndale za dziko chopangidwa ndi anthu cha ufumu wa Mulungu umene unayamba kulamulira kumwamba chiyambire pa mapeto a Nthawi za Akunja mu 1914. Ophunzira Baibulo Achikristu amenewa anali atayankha funso lakuti, “Kodi Ndani Amene Adzalemekeza Yehova?” limene kope la Nsanja ya Olonda (Lachingelezi) la January 1, 1926, linafunsa owerenga ake, ndipo anasankha kulemekeza Yehova ndi ufumu wake.

46. Kodi n’chiani chimene chinapangitsa Lachisanu, May 28, la msonkhano wa ku London wa 1926 kukhala lapadera?

46 Pa Lachisanu, May 28, J.F. Rutherford monga prezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society anapereka kwa ochita msonkhano pa London chitsimikiziro chokhala ndi mutu wakuti “Umboni kwa Olamulira a Dziko.” Chimene’chi chinali chachisanu mu mpambo wa zitsimikiziro zolandiridwa pa misonkhano ya chaka ndi chaka ya I.B.S.A. Chitsimikiziro cha ku London chimene’cho limodzi ndi uthenga wake wochichirikiza zinatsimikizira kukhala chiyambi cha kutsanulidwa kwa “mliri” wachisanu monga momwe kunanenedweratu m’Chibvumbulutso 16:10, 11. Mwapadera kwambiri mliri wachisanu umene’wo unayamba kutsanulidwa pa London, England, malikulu a Ufumu wa Britain, umene unali chiwalo cha Britain cha Ulamuliro Wachisanu ndi Chiwiri wa ulosi wa Baibulo, Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka, wamphamvu kopambana wa maulamuliro onse a m’mbiri. Maofesi a gulu la I.B.S.A. anali mu London.

47, 48. Kodi ndi ntchito yapadera yotani imene inapangitsa Loweruka, May 29, 1926 kukhala lapadera?

47 Pa Loweruka, May 29, tsiku lonse lathunthu linaperekedwa ku utumiki wakumunda. Programu yosindikizidwa ya msonkhano’wo inati: “Tsiku lino lapatulidwira utumiki wakumunda. Ali yense wopatulika wokhala pa msonkhano akupemphedwa kukhala ndi phande m’kulengeza Mfumu ndi Ufumu. Fikani ku Alexandra Palace mofulumira monga momwe kungathekere, ndi kuonekera kaamba ka utumiki ku Dipatimenti ya Utumiki. Maulendo a pa galimoto alinganizidwa kaamba ka malo akutali okachitirako utumiki.”

48 Awo a mwa ife amene tikali ndi moyo amene tinafika pa msonkhano wa ku London umene’wo tidzakumbukira m’mene tinakwerera mabasi a mzinda’wo m’timagulu ndipo tinatengeredwa ku malo athu mu mzinda wonse’wo kukagawira kabukhu katsopano m’makonde oyenda anthu ndi pa zipata za nyumba zapansi. M’njira imene’yi makope okwanira 120,000 a kabukhu kamene’ko The Standard for the People anaikidwa m’manja mwa oyendamo. Posimba za njira yachilendo pa nthawi’yo yolengezera Mfumu ndi Ufumu imene’yi, Nsanja ya Olonda (Yachingelezi) ya pa deti la July 15, 1926, inati: “Palibe chiri chonse chonga chimene’chi chinadziwidwa ndi kale lonse pa Tsiku la Utumiki pa msonkhano. Mabwenzi anali kuonjezeka m’kutenthedwa maganizo. Iwo analingalira kuti iwo anachita zonse zimene iwo akanatha kuchita kumvera lamulo la Yehova lakuti: ‘Inu ndinu mboni zanga pakuti Ine ndine Mulungu.’”

49. Kodi ndi zochitika zotani zimene zinapangitsa Sande, May 30, 1926, kukhala lapadera pa London?

49 Sande, May 30, linatsiriza chimwemwe ndi dalitso la msonkhano wopanga mbiri umene’wu, ndi ofikapo 4,000. Pa 2:00 koloko masana, panali ulaliki wa ubatizo pa Alexandra Palace, umene pambuyo pake 184 anamizidwa m’madzi monga mboni zodzipereka za Mulungu Wam’mwambamwamba. Usiku umene’wo, ochita msonkhano’wo anasamukira ku holo ya masewera yaikulu kopambana pa nthawi’yo ya Britain Royal Albert Hall, kaamba ka nkhani yapoyera yokambidwa ndi prezidenti wa I.B.S.A. J.F. Rutherford, pa mutu wa nkhani wakuti “Chifukwa Chake Maulamuliro a Dziko Akugwedezeka-Mankhwala.” Holo’yo inadzazidwa mpaka ena kukhala panja, ndi ofikapo 10,000. Pambuyo pa kuwerengedwa kwa chitsimikiziro’cho “Umboni kwa Olamuliro a Dziko,” Prezidenti Rutherford anapitiriza ndi nkhani yake. Iye anamka ku Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chitatu monga momwe kunanenedweratu mu ulosi wa Baibulo, kenako ku Chigwirizano cha Mitundu, ndi kusonyeza m’tsogolo ku kulephera kwa gulu la m’mitundu yonse kaamba ka mtendere ndi chisungiko za dziko limene’lo. Ulamuliro waumunthu wa mtundu wa anthu udzathera m’tsoka lalikulu kopambana la dziko, ndiyeno padzadza Mankhwala, Ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Kristu, wokhala ndi mtendere, ulemerero, thanzi, moyo ndi chimwemwe kaamba ka mtundu wonse wa anthu. Pomaliza, wokamba nkhani’yo anati:

50. Potsiriza, kodi n’chiani chimene wokamba nkhani yapoyera ananena mosonkhezera?

50 “Maufumu ndi olamulira a dziko lapansi apereketu tsopano chichirikizo chao ndi kudzipereka kwa Ambuye. Abvomerezetu Yehova monga Mulungu, ndi Yesu Kristu monga Mfumu yake yodzozedwa; ndipo motero iwo adzapereka utumiki weni-weni kwa anthu ndi kudziika mu mzera wa kulandira madalitso amuyaya a Yehova.” M’mawa mwake imodzi ya manyuzipepa a London inali ndi lipoti lokwanira la nkhani yapoyera imene’yi lokwana pa tsamba lathunthu kotero kuti zikwi zina zambiri zinawerenga uthenga wotokosa Waufumu umene’wu koposa amene anaumva pa Royal Albert Hall. Chotero “mliri” wachisanu wonenedwratu’wo unali’di kutsanulidwa!

51. Kodi ndi motani m’mene tsiku lotsirizira la msonkhano, May 31, linapangitsidwira kukhala lapadera?

51 Tsiku lotsirizira la msonkhano’wo, Lolemba, May 31, 1926, ochita msonkhano’wo anatuluka kulowa m’munda kukapereka m’manja mwa anthu Achiyuda okhala m’London bukhu la chikuto cha pepala lolembedwa mwapadera kaamba ka iwo. Usiku umene’wo ochita msonkhano’wo kachiwiri’nso anasamukira ku Royal Albert Hall kukamvetsera chimene chinatsimikizira kukhala chisonkhezero chachikulu chotsirizira cha kwa anthu onse kwa Ayuda kuti atembenukire kwa Mesiya wa Yehova, Mwana wake womalamulira tsopano’yo Yesu Kristu. Kumene’ko Ayuda zikwi zambiri analabadira ku kuitanidwa kwa anthu onse’ko ndipo anamva nkhani ya prezidenti wa Sosaite ndi kuwapatsa uthenga wosonkhezera umene unayenera kukhala wotonthoza kwa iwo. Chiyembekezo chao chokha chinali mwa Mesiya wa Yehova. Chosankha tsopano chinali kwa Aisrayeli achibadwidwe odulidwa’wo!

52. Kodi ndi bukhu lokondweretsa lotani limene linatulutsidwa Lachisanu, May 28, 1926?

52 Pakati pa mbali zapadera za msonkhano wosangalatsa kopambana wa otsalira a Yehova a Aisrayeli auzimu umene’wu inali kutulutsiridwa kwa anthu pa Lachisanu, May 28, kwa bukhu latsopano la Sosaite lochedwa “Deliverance.” Kaamba ka chidziwitso cha Baibulo chimene bukhu limene’li linapereka, linali losangalatsa kwa anthu a Yehova. Mosafanana ndi m’mene bukhu lina liri lonse lakale linachitira, linachititsa gulu la Mulungu kuonekera bwino, monga momwe linaphiphiritsiridwira ndi mkazi m’Chibvumbulutso, chaputala cha khumi ndi chiwiri, ndipo linasonyeza kusiyana kwakukulu pakati pa gulu la Mulungu ndi gulu la Satana. Bukhu limene’li linali loyamba la mpambo wa mabukhu amene analowa m’malo mwa mavoliamu asanu ndi awiri a Studies in the Scriptures (a 1886-1917), amene anatumikira monga muyeso wa chilangizo cha Baibulo kufikira pa nthawi’yo. Chaka chotsatirapo panatuluka bukhu lakuti Creation (1927), pambuyo pake Reconciliation (1928), Government (1928), Life (1929), Light (m’mavoliamu awiri, 1930), Vindication (m’mavoliamu atatu, 1931, 1932), Preservation (1932), Preparation (1933), Jehovah (1934), ndi ena otero, mpaka kudzafika chaka chino.

53, 54. (a) Kodi ndi kufutukuka kotani kumene kunalinganizidwa pa msonkhano wa 1926 wa ku London? (b) Ndipo’nso, kodi ndi bukhu la chaka ndi chaka lotani limene linapititsidwa patsogolo?

53 Ndipo’nso, pa msonkhano wa 1926 wochitidwira m’malikulu a Ufumu wa Britain, prezidenti wa Watch Tower anaika amuna odziwa zinthu m’malo a ntchito a utumiki m’maiko achilendo, kuphatikizapo awiri amene anayenera kutsegula nthambi yatsopano m’Bombay, India, amene pa nthawi’yo anali dziko lolamulidwa ndi Britain. (Onani Year Book I.B.S.A., lolembedwa m’1926, tsamba 90.) Ndipo’nso anapanga malinganizidwe a kufalitsa lipoti la chaka ndi chaka la Sosaite mu mpangidwe wa bukhu. Chotero, m’nthawi yokwanira, m’malo mwakuti ntchito za Ufumu za anthu a Yehova ziikidwe m’zolembedwa kaamba ka chaka chapadera cha 1926, panatuluka “Year Book of International Bible Students Association lokhala ndi Malemba a Tsiku ndi Tsiku ndi Ndemanga.” (masamba 320) “Daily Heavenly Manna and Birthday Records,” zimene zinagwiritsiridwa ntchito m’kulambira kwa tsiku ndi tsiku kwa Akristu chiyambire pa kufalitsidwa kwao mu 1907, tsopano analeka kugwiritsiridwa ntchito, popeza kuti malemba a tsiku ndi tsiku atsopano ndi ndemanga zinatuluka m’Year Book iri yonse yotsatirapo yofalitisdwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society kufikira lero lino.

54 M’kati mwa zaka makumi asanu zapita’zo palibe Year Book imene inalephera kutulutsidwa pa kutha kwa chaka chiri chonse, kusonyeza mwatsatane-tsatane kwambiri ntchito za pa dziko lonse za mboni Zachikristu za Yehova m’kulalikira m’biri yabwino imene’yi ya Ufumu.—Mateyu 24:14, NW.

55. Kodi ndi programu ya kumanga yotani imene inaonjezera chimwemwe cha otsalira?

55 Chinthu china chofunika chimene chinaonjezera chiyembekezo chosangalatsa cha anthu a Yehova pa nthawi ya msonkhano wa mitundu yonse m’London chinali ichi: Malinganizidwe anali kuchita akuti Watch Tower Bible and Tract Society imange fakitale ya zipinda zosanja zisanu ndi zitatu za iyo yokha pa Brooklyn, New York, kuti ikwaniritsire zofunika za ntchito ya mboni yomafutukuka pa dziko lonse’yo. Pa July 23, 1926, malo eni-eni kaamba ka imene’yi potsirizira pake anagulidwa. Mosasamala kanthu za nyengo yachisanu yotsatirapo, kumangidwa kwa fakitale ya Sosaite imene’yi kunapitirizabe.

56. Kodi fakitale imene’yo inatsimikizira kukhala phata la chiani?

56 Chimwemwe cha ziwalo zogwira ntchito pa malikulu a Brooklyn chinali chachikulu pamene izo zinasamutsidwira m’fakitale ndi maofesi zolinganizidwa mwapadera, ndi zotakata zimene’zi m’February wa 1927. Chotero pa tsamba la afalitsi la magazini a Nsanja ya Olonda kope la February 1, 1927, ndi The Golden Age kope la February 9, 1927, panatuluka keyala ya afalitsi: 117 Adams Street, Brooklyn, New York. Nyumba imene’yi inayenera kuonjezeredwa pambuyo pake, ndipo inakhala phata la kufutukuka kwa mafakitale osindikizira makumi atatu mphambu awiri ogwirizanitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society pa dziko lonse lapansi. Kutulutsidwa kwa mabukhu othanidzira phunziro la Baibulo ndi mtandadza wozungulira dziko lonse lapansi wa kusindikiza umene’wu kufikira tsopano kwakhala kwakukulu kwambiri. Mwa njira imene’yo Paradaiso wauzimu wafalikira!

57. Kodi otsalira analowa m’chimwemwe cha utali wotani?

57 Ndithudi chaka cha 1926 chiyenera kukhala chapadera monga chimake cha chimwemwe cha mapeto a masiku 1,335. Awo a mwa “anthu” a Danieli amene anali kuyembekezerabe ndipo anafika mapeto a masiku 1,335 analowetsedwa m’chimwemwe chimene sichinazimiririke, koma kuti, mosasamala kanthu za chizunzo chomaonjezereka’cho ndi Nkhondo Yachiwiri ya Dziko (1939-1945) ndi mabvuto a dziko otsatirapo, chapitirizabe ndi kuonjezeka. Maka-maka kuyambira m’chaka chapadera chimene’cho 1926 alambiri odzipereka ndi obatizidwa a Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu alowa m’chimwemwe cha Paradaiso chosonyezedwa ndi wamasalmo wouziridwa’yo, pamene iye anati: “Wachimwemwe ndiwo mtundu umene Mulungu wake ali Yehova, anthu amene iye wawasankha monga cholowa chake.”—Salmo 33:12, NW; 144:15b.

58. Pambuyo pa “masiku” onse’wo, kodi Danieli adzalowa m’gawo lotani?

58 Mneneri Danieli sanapatsidwe mwai wa kuona ndi kulowa m’chimwemwe chimene’chi cha mboni Zachikristu za Mulungu wake, Yehova. Iye anauzidwa kusayembekezera kutero, kpakuti mngelo wa Mulungu anamuuza kuti: “Koma iwe, muka mpaka chimariziro; pakuti udzapumula, nudzaima m’gawo lako masiku otsiriza.” (Danieli 12:13) Kwa zaka zoposa 2,500 tsopano Danieli wapumula m’manda, m’tulo ta imfa. M’nthawi yokwanira iye adzaimirira m’chiukiriro kudzalandira gawo lake pansi pa ufumu Waumesiya wa Yehova Mulungu, za umene iye anauziridwa kuulosera modabwitsa kwambiri. (Ahebri 11:33-40) Ndipo’nso, nthawi yokwanira ya Mulungu ikuyandikira pafupi pamene, osati Danieli yekha, koma’nso Abrahamu, Isake, Yakobo, Mose ndi aneneri ena okhulupiririka a m’nthawi zakale adzaimirira kaamba ka “gawo” lao, kuuka kutulo ta imfa “kumka ku moyo wosatha” ndi ku mwai wa kutumikira monga “akalonga m’dziko lonse lapansi” pansi pa boma lathu la dziko likudza’lo.—Salmo 45:16, NW; Danieli 12:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena