Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • my gawo 1
  • Chilengedwe Mpaka pa Chigumula

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilengedwe Mpaka pa Chigumula
  • Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Uchimo Uchotsera Anthu Chimwemwe
    Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Yehova Analenga Angelo Ambirimbiri
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Angelo Ena Anaukira Mulungu
    Kodi Mizimu ya Akufa Ilipodi?
  • Mulungu Ayamba Kupanga Zinthu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
my gawo 1

CHIGAWO 1

Chilengedwe Mpaka pa Chigumula

Kodi kumwamba ndi dziko lapansi zinachokera kuti? Kodi dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, ndipo’nso zinthu zochuluka za dziko lapansi’zo, zinakhalapo motani? Baibulo limapereka yankho loona pamene limati zinalengedwa ndi Mulungu. Chotero bukhu lathu lino likuyamba ndi nkhani za Baibulo za chilengedwe.

Timamva kuti, zolengedwa zoyamba za Mulungu, zinali anthu auzimu ofananirapo naye. Iwo anali angelo. Koma dziko lapansi linalengedwera anthu onga ife. Chotero Mulungu anaumba mwamuna ndi mkazi ochedwa Adamu ndi Hava nawaika m’munda wokongola. Koma iwo sanamvere Mulungu ndipo anataya kuyenera kwa kukhalabe ndi moyo.

Zonse pamodzi, kuyambira pa kulengedwa kwa Adamu mpaka pa Chigumula chachikulu, panali zaka 1656. M’nthawi’yi panali anthu ambiri oipa. Kumwamba, kunali anthu osaoneka auzimu, Satana ndi angelo ake oipa. Pa dziko lapansi panali Kaini ndi anthu ena ambiri oipa, kuphatikizapo ena amphamvu zodabwitsa. Koma panali’nso anthu abwino pa dziko lapansi—Abele, Enoke ndi Nowa. M’Chigawo CHOYAMBA tidzawerenga za anthu onse’wa ndi zochitika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena