Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • my nkhani 89
  • Yesu Ayeretsa Kachisi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Ayeretsa Kachisi
  • Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Anayeretsa Kachisi
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Changu cha Kulambira Yehova
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Anali Wodzipereka pa Kulambira Mulungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Nyama
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
my nkhani 89

NKHANI 89

Yesu Ayeretsa Kachisi

YESU akuoneka’di kukhala atakwiya pano, kodi si choncho? Kodi mukudziwa chifukwa chake? N’chifukwa chakuti amuna’wa pa kachisi wa Mulungu mu Yerusalemu ali adyera kwambiri. Iwo akuyesa kupanga ndalama zochuluka kuchokera kwa anthu amene adza pano kudzalambira.

Kodi mukuona makonyani, nkhosa ndi nkhunda’zo? Eya, anthu’wa akugulitsa zifuyo’zi panopo pa kachisi. Kodi mukudziwa chifukwa chake? N’chifukwa chakuti Aisrayeli amafuna zinyama ndi mbalame zoti apereke nsembe kwa Mulungu.

Chilamulo cha Mulungu chinati Muisrayeli akalakwa, ayenera kupereka nsembe kwa Mulungu. Panali’nso nthawi zina, pamene Aisrayeli anafunikira kupereka nsembe. Koma kodi Muisrayeli akanapeza kuti mbalame ndi zinyama zozipereka kwa Mulungu?

Aisrayeli ena anali ndi mbalame ndi zinyama. Chotero akanatha kuzipereka nsembe. Koma ena ambiri analibe zifuyo kapena mbalame ziri zonse. Ndipo ena anakhala kutali kwambiri ndi Yerusalemu kuti sakanatha kubwera ndi zinyama zao ku kachisi. Chotero anthu’wo anadza pano nagula zinyama kapana mbalame zimene anafuna. Koma anthu’wa anali kulipiritsa ndalama zochulukitsitsa. Iwo anali kunyenga anthu’wo. Ndipo’nso, iwo sanayenera kukhala akugulitsira m’kati mweni-mweni muno mwa kachisi wa Mulungu.

Ndizo zimene zikupsyetsa mtima Yesu. Chotero iye akugubuduza matebulo a anthu’wo okhala ndi ndalama namwaza ndalama zao. Ndipo’nso akupanga chikwapulo cha chingwe naingitsira kunja zinyama zonse. Iye akulamula anthu ogulitsa nkhunda kuti: ‘Zitulutseni muno! Lekani kupanga nyumba ya Atate wanga kukhala malo opangira ndalama zochuluka!’

Ena a atsatiri a Yesu ali naye pano pa kachisi m’Yerusalemu. Iwo akudabwa n’zimene akuona Yesu akuchita. Ndiyeno akukumbukira malo m’Baibulo pamene pamanena kuti ponena za Mwana wa Mulungu: ‘Chikondi cha pa nyumba ya Mulungu chidzamudya ngati moto.’

Ali kuno ku Yerusalemu kukhalapo pa Paskha, Yesu akuchita zozizwitsa zambiri. Kenako, Yesu akuchoka kumka ku Yudeya nayamba ulendo wake wobwerera ku Galileya. Koma pa ulendo wake, iye akudutsa chigawo cha Samariya. Tiyeni tione zimene zikuchitika kumene’ko.

Yohane 2:13-25; 4:3, 4.

Mafunso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena