Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 76 tsamba 180-tsamba 181 ndime 2
  • Yesu Anayeretsa Kachisi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anayeretsa Kachisi
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Ayeretsa Kachisi
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yesu Anali Wodzipereka pa Kulambira Mulungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Changu cha Kulambira Yehova
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Anayeretsanso Kachisi
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 76 tsamba 180-tsamba 181 ndime 2
Yesu akugwiritsa ntchito chikwapu potulutsa nyama m’kachisi ndiponso anagubuduza matebulo a osintha ndalama

MUTU 76

Yesu Anayeretsa Kachisi

M’chaka cha 30 C.E., Yesu anapita ku Yerusalemu pa nthawi ya chikondwerero cha Pasika. Anthu enanso ambiri anapita ku Yerusalemuko kukachita chikondwererochi. Pa nthawiyi, anthu ankapereka nsembe za nyama pakachisi. Ena ankabweretsa nyamazi, koma ena ankagula ku Yerusalemu komweko.

Yesu atalowa m’kachisi anapeza kuti anthu akugulitsa nyama mmenemo. Tangoganiza! Ankachita malonda m’nyumba mwa Yehova mwenimwenimo! Ndiye kodi Yesu anatani? Nthawi yomweyo anatenga zingwe n’kupanga chokwapulira. Ndiyeno anayamba kuthamangitsa nkhosa ndi ng’ombe zimene zinali m’kachisimo. Anagubuduzanso matebulo a anthu amene ankachita malondawo komanso anakhuthulira pansi ndalama zawo. Iye anauza anthu amene ankagulitsa nkhunda kuti: ‘Chotsani izi muno! Nyumba ya Bambo anga musaisandutse malo ochitira bizinezi!’

Anthu anadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anachitazi. Ophunzira ake anakumbukira ulosi wonena za Mesiya wakuti: ‘Ndidzakhala wodzipereka kwambiri panyumba ya Yehova.’

M’chaka cha 33 C.E., Yesu anayeretsanso kachisi kachiwiri pothamangitsa anthu amene ankachita malonda panyumba ya Yehova. Iye sanalole kuti munthu aliyense azinyoza nyumba ya Yehova.

“Simungakhale akapolo a Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”​—Luka 16:13

Mafunso: Kodi Yesu anatani ataona anthu akuchita malonda m’kachisi? N’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

Mateyu 21:12, 13; Maliko 11:15-17; Luka 19:45, 46; Yohane 2:13-17; Salimo 69:9

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena