Mutu 2
Kuzani Yehova Monga Mulungu Wowona
1. (a) Kodi Mulungu wowona ndani? (b) Pamene tiphunzira za iye, kodi miyoyo yathu iyenera kuyambukiridwa motani?
KWA AKRISTU anzake mtumwi Paulo analemba kuti, ngakhale kuti pali ambiri otchedwa milungu, “kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate . . . ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu.” (1 Akor. 8:5, 6) “Mulungu mmodzi” amene Paulo anasonyako ndiye Yehova, Mlengi wa zinthu zonse. (Deut. 6:4; Chiv. 4:11) Anthu oyamikira amene amaphunzira za mikhalidwe yake ndi zinthu zimene wachitira mtundu wa anthu amadzipeza kukhala okokedwera pafupi naye mosapeweka. Nchotulukapo chotani? Kuli kokha kwachibadwa kwa iwo kutamanda Uyo amene iwo amakonda kwambiri motero, akumatero ponse pawiri mwa mawu ndi ntchito. Pamene chikondi chawo cha pa Mulungu chikula, amadziwona kukhala osonkhezeredwa kuuza ena za iye, ndipo kumlingo wothekera kwa iwo monga anthu amafuna kumtsanzira. Baibulo limalimbikitsa tonsefe kuchita zimenezo, kumati: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; ndipo yendani m’chikondi.” (Aef. 5:1, 2) Kugwiritsira ntchito uphungu umenewo, tifunikira kudziwa Yehova monga momwedi iye aliri.
Mtundu wa Munthu Amene Yehova Ali
2. Kodi ndi iti imene iri ina ya mikhalidwe yapadera ya Mulungu imene imatisonkhezera kumtamanda?
2 M’Baibulo lonse muli mawu olunjika osonyeza mikhalidwe yapadera ya Mulungu. Pamene muwerenga imeneyi, khalani ndi nthawi ya kulingalira za chimenedi mikhalidweyo iri ndi mmene iriri yofunika kwa inu. Mwachitsanzo: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yoh. 4:8) “Njira zake zonse ndi chiweruzo.” (Deut. 32:4) ‘Kwa iye kuli nzeru.’ (Yobu 12:13) Iye ali “ndi mphamvu zake zazikulu.” (Yes. 40:26) Pamene musinkhasinkha mikhalidwe imeneyi, kodi simumasonkhezeredwa, mochita chidwi ndi Mulungu, kumtamanda?
3. Kodi ndimbali zina ziti za umunthu wa Yehova zimene ziri zokondweretsa kwambiri?
3 Potidziwitsa mowonjezereka umunthu wake wochititsa kasowo, Baibulo limatiuza kuti Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekeleza, ndi waukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi.” (Eks. 34:6) “Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira.” (Sal. 86:5) “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lapansi, kudziwonetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi iye.” (2 Mbiri 16:9) “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Mac. 10:34, 35) Yehova “apatsa kwa onse modzala manja” ndipo ali “Mulungu wachimwemwe.” (Yak. 1:5; 1 Tim. 1:11, NW) Ha ndikotsitsimula chotani nanga mmene kuliri kutumikira Mulungu wosayerekezereka ameneyu ndikukhala ndi chisamaliro chake chachikondi!
4. (a) Kodi ndikudzipereka kwamtundu wanji kumene Yehova amafuna, ndipo kodi kuli kofunika motani? (b) Kodi Salmo 34:3 limatiitanira kukhala ndi mbali m’chiyani?
4 Choyenderana ndi mikhalidwe yake imeneyi ndicho chenicheni chakuti iye ali “Mulungu wofuna kudzipereka kotheratu.” (Eks. 20:5, NW) Kuti timtumikire movomerezeka tiyenera kumpatsa kudzipereka kwathu kwachikwanekwane. Sitingakondenso dziko limene Satana ali mulungu wake. (1 Yoh. 2:15-17; 2 Akor. 4:3, 4) Yehova amawona kunyengezera chilungamo kulikonse. Amadziwa bwino lomwe osati kokha zimene timachita komanso mmene timalingalilira za izo ndi mtundu wa anthu amene tikuyesa kukhala. Ngati tikondadi chilungamo, iye amatithandiza. (Yer. 17:10; Miy. 15:9) Chifukwa cha mtundu wamunthu amene Yehova ali, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi avomereza mokondwera chiitano cha wamasalmo wa Baibulo amene analemba kuti: “Bukitsani pamodzi ndi ine ukulu wa Yehova, ndipo tikweze dzina lake pamodzi.” (Sal. 34:3) Kodi inu ndinu mmodzi wa iwo?
5. Kodi nchiyani chidzatithandiza kupindula mokwanira ndi phunziro lathu la umunthu wa Yehova?
5 Chikhumbo chanu cha kulankhula za Mulungu chidzazama, ndipo mudzathandizidwa kwambiri m’zoyesayesa zanu za kumtsanzira ngati mupenda mosamalitsa mikhalidwe yake yapamwamba. Pezani (1) chimene kwenikweni mkhalidwe uliwonse uli, mwinamwake chimene chimaupangitsa kukhala wosiyana ndi mikhalidwe ina, (2) mmene Yehova wausonyezera ndipo kwa ayani, ndiponso (3) mmene mungausonyezere kapena mmene uyenera kuyambukirira lingaliro lanu.
6. Mukumagwiritsira ntchito chikondi monga chitsanzo, sonyezani mmene mungapendere mikhalidwe ya Yehova. Chitani ichi mwa kuyankha mafunso kumapeto kwa ndime ino, kuphatikizapo malemba m’mayankho anu.
6 Talingalirani panopa chitsanzo chimodzi chokha. Pamene Baibulo limati, “Mulungu ndiye chikondi,” kodi limatanthauzanji? (1 Yoh. 4:8) Ndithudi, pali mitundu ingapo ya chikondi. Liwu Lachigiriki logwiritsiridwa ntchito m’lemba ili ndilo a·gaʹpe, limene limanena mpangidwe wapamwamba koposa wa chikondi, monga momwe wasonyezedwera mwachitsanzo ndi Yehova Mulungu iye mwiniyo. Chikondi chotero chiri chisonyezero cha kupanda dyera kotheratu. Muli ndi zimenezo m’maganizo, pangani mayankho a inu mwini a mafunso ali pansipawa, mukumagwiritsira ntchito malemba operekedwa.
Kodi mkhalidwe uwu umasonyezedwa motani m’ntchito za Yehova za chilengedwe? (Mac. 14:16, 17)
Kodi nchiyani chimene chiri chitsanzo chapadera koposa cha chikondi cha Yehova kaamba ka anthu? (Yoh. 3:16, 17) Kodi chinali chifukwa cha ubwino wa anthu kuti Yehova anachita ichi? (Aroma 5:8)
Kodi ndimotani mmene zimene Yehova anachita kupyolera mwa Mwana wake ziyenera kusonkhezerera njira imene tikugwiritsirira ntchito nayo miyoyo yathu? (2 Akor. 5:14, 15, 18, 19)
Kodi ife monga Akristu tingasonyeze mwanjira zotani kuti tiri ndi mtundu umodzimodziwo wa chikondi kwa Akristu anzathu? (1 Akor. 13:4-7; 1 Yoh. 4:10, 11; 3:16-18)
Kodi nkwandaninso kumene tiyenera kusonyeza chikondi, ndipo chifukwa ninji? (Mat. 5:43-48; 28:19, 20; Agal. 6:10)
7. M’phunziro lanu laumwini, mungapeze bwanji mawu ofanana ponena za mikhalidwe yina ya Yehova?
7 Kodi mukakondanso kufufuza ina ya mikhalidwe ya Yehova? M’phunziro laumwini, kulekeranji kuyamba ndi “chiweruzo” ndi “nzeru,” ndiyeno mwinamwake “kukoma mtima kwa chikondi” ndi “chifundo.” Mogwiritsira ntchito zosonyezera mabukhu a Watch Tower ndi konkodansi ya Baibulo, mudzapeza nkhani zambiri zopereka chidziwitso.
Thandizani Ena Kuphunzira Chowonadi Chonena za Mulungu
8. (a) Kodi ndimilungu iti imene anthu adziko amalambira? (b) Kodi ndani amene akuchirikiza chisokonezo chonsechi, ndipo kodi nchifukwa ninji mukunena choncho?
8 Motsutsana ndi kulambiridwa kwa Mulungu wowona, mamiliyoni ambiri enieni a milungu ina ikulambiridwa ndi anthu. M’zaka za zana lachinayi, Dziko Lachikristu linavomereza chiphunzitso cha “Utatu,” chophunzitsidwa ndi Ababulo, Aigupto, Ahindu ndi Abudha nthawiyo isanafike. Kuwonjezera pa lingaliro la Mulungu limeneli, pali olamulira amphamvu, ochita masewera apadera ndi oyimba amene alambiridwa mofanana ndi milungu. Ndalama, munthu mwini ndi kugonana zafikiranso kukhala milungu kwa imene yapatsidwa kudzipereka kwa phamphu. Kodi ndani amene akuchirikiza zonsezi? “Mulungu wa nthawi ino ya pansi pano,” Satana Mdyerekezi. (2 Akor. 4:4; 1 Akor. 10:20) Mwanjira iriyonse yokhoza kulingaliridwa, yamachenjera iye amayesayesa kupatutsa anthu kuchoka kwa Yehova, kapena makamaka kugawanitsa kudzipereka kwawo.
9. Kodi ndiiti imene iri njira yabwino koposa yothandizira munthu aliyense kuphunzira za Mulungu?
9 Kodi ndimotani mmene tingathandizire anthu otere, kaya akhale odzinenera kukhala Akristu kapena ena, kuzindikira chowonadi chonena za Mulungu? Imodzi ya njira zabwino koposa ndiyo kuwasonyeza mwa dongosolo lothandiza chimene Baibulo lenilenilo limanena ponena za umunthu wa Mulungu wowona ndi mtundu wa munthu amene iye ali. Pamenepo tifunikira kuchirikiza zimenezi ndi khalidwe limene limasonyeza mikhalidwe yaumulungu m’miyoyo yathu.—1 Pet. 2:12.
10. Polankhula kwa okhulupirira Utatu, kodi nchifukwa ninji sikuli kwanzeru kuyerekezera kuti timadziwa zenizeni zimene amakhulupirira?
10 Koma bwanji ngati ena amene ali ziwalo za matchalitchi a Dziko Lachikristu atsutsana nanu, akumanena kuti chikhulupiriro chawo mu “Utatu” chiri Chamalemba? Choyamba, zindikirani kuti, ngakhale kuti pali mawu a ukumu onena za chiphunzitso cha “Utatu,” anthu ochuluka ali ndi malingaliro a iwo eni. Apempheni kulankhula momasuka, ndiyeno athandizeni kuyerekezera zikhulupiriro zawo ndi zimene ziri m’Baibulo lawo. M’nthawi yokwanira, alimbikitseninso kuyerekezera chiphunzitso chalamulo cha tchalitchi ndi Mawu a Mulungu.
11. Mukumatenga mfundo imodzi yokha mwa zisanu zazikuluzo panthawi, gwiritsirani ntchito mafunso ndi malemba ondandalikidwa m’ndime ino kulongosola kusagwirizana ndi malemba kwa chiphunzitso cha “Utatu.”
11 Pokhala ndi chikhumbo m’maganizo cha kuthandiza anthu owona mtima, lingalirani mmene mungagwiritsirire ntchito malemba osonyezedwa pansipa kusinkhasinkha mfundo pazimene malemba amenewa asonyezedwa:
(1) Okhulupirira mu Utatu ena amagogomezera lingaliro lakuti pali Anthu atatu aumulungu (Atate, Mwana ndi Mzukwa Woyera) koma Mulungu mmodzi yekha.
Koma kodi Machitidwe 2:4, 17 amasonyeza kuti “Mzukwa Woyera,” kapena “mzimu woyera,” ndiwo munthu?
Kodi nchifukwa ninji kuli kothandiza kuwona kuchuluka kwa anthu ophatikizidwa mu lirilonse la malemba otsatirawa? (Yoh. 17:20-22; Mac. 7:56; Chiv. 7:10)
(2) Ena amakhulupirira kuti ziwalo zonse za “Utatu” ziri ndi ulemerero wofanana, kuti palibe chokulirapo kapena chocheperapo koposa china, kuti zonse ziri zofanana ndiponso zonse ziri ndi umuyaya wofanana.
Kodi Malemba amavomereza? (Kaamba ka yankho, wonani Yohane 14:28; Mateyu 23:36; Chivumbulutso 3:14.)
(3) Anthu ena amasonya ku Yohane 1:1 monga umboni wa “Utatu.” Iwo akutsutsa kuti panopa lemba Lachigiriki liribe mfotokozi (“yo”) ndi kuti chifukwa chake lembalo limati: “Mawu anali Mulungu,” mmalo mwa “mulunguyo.”
Koma kodi ndianthu angati akunenedwa mu Yohane 1:1? Atatu? Kapena awiri? Kodi ndimotani mmene Yohane 1:18 amatsutsanira ndi chiphunzitso cha “Utatu”?
Nzowona kuti Chigiriki chiribe mfotokozi, koma zinenero zambiri ziri naye, ndipo amagwiritsiridwa ntchito m’zinenerozo kuchitira kulongosola ziganizo molondola. Ngati munthu wina alingalira kuti kuli kulakwa kugwiritsira ntchito mfotokozi potembenuza Yohane 1:1, kodi iye akanafunanso kuti asiyidwe pa Machitidwe 28:6 malinga ndi King James Version ndi ena? (Njira yina yakutembenuzira Yohane 1:1, monga momwe kwasonyezedwera mu An American Translation, ndiyo “Mawu anali aumulungu,” ndiko kuti, anali ndi mikhalidwe yaumulungu yofanana ndi imene Mulungu ali nayo.)
(4) Okhulupirira mu Utatu amatsutsanso kuti pa Genesis 1:1, 26 liwu Lachihebri lotembenuzidwa “Mulungu” ndilo El·o·himʹ ndi kuti liwuli likuimira zochuluka m’Chihebri ndipo makamaka limatanthauza “Milungu.”
Kodi nchifukwa ninji limenelo silikuchirikiza chiphunzitso cha Anthu aumulungu atatu mwa “Mulungu mmodzi”?
Ngati pa Genesis 1:1 likusonyeza “Utatu,” kodi pa Oweruza 16:23 limasonyezanji, pomwe pamagwiritsiranso ntchito el·o·himʹ kaamba ka “mulungu,” pamene mneni Wachihebri akusonyeza chinthu chimodzi, osati zochuluka?
Kodi nchifukwa ninji mpangidwe wa zochuluka wa Mulungu umagwiritsiridwa ntchito m’malemba awa Achihebri? Iyi ndiyo njira imodzi imene Chihebri chimasonyezera lingaliro la kulemekeza kapena ulemu. Ngati munthu woposa mmodzi anatanthauzidwa, aneni otsatira akanakhalanso ochulukitsa, koma m’zochitika zapamwamba saali.
(5) Chifukwa cha chigogomezero chimene matchalitchi aika pa Yesu (limodzi ndi chenicheni chakuti dzinalo Yehova lachotsedwa m’matembenuzidwe a Baibulo ambiri) anthu ena amalingalira kokha za Yesu pamene Mulungu atchulidwa.
Koma kodi nchitsanzo chiti m’kulambira chimene Yesu anapereka kwa ife kutsanzira? (Luka 4:8)
12. Kodi nchifukwa ninji Yesu moyenerera anatcha Atate wake monga “Mulungu wowona yekha”?
12 Ngakhale kuti Yesu akunenedwa m’Malemba kukhala “mulunguyo,” ngakhale “Mulungu Wamphamvu,” komabe iye analemekeza Atate wake, akumamtchula kukhala “Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.” (Yoh. 1:1; 20:17; Yes. 9:6) Iye anavomerezana ndi Mose, amene poyamba ananena kuti: “Yehova ndiye Mulungu; palibe wina wopanda iye.” (Deut. 4:35) Yehova ali wosiyana kotheratu ndi zinthu zolambiridwa zoterozo monga mafano, anthu olambiridwa monga milungu ndi Satana Mdyerekezi. Mosiyana ndi zonsezo, Yehova ndiye “Mulungu wowona yekha,” monga momwe Yesu anamtchera.—Yoh. 17:3.
‘Yendani m’Dzina la Yehova’
13, 14. Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa mu “kudziwa” ndi ‘kuyenda mu’ dzina la Yehova?
13 Pambuyo pa zaka zambiri za chisokonezo ponena za kudziwika kwa Mulungu, anthu ambiri amapeza kukhala kosangalatsa pamene awona koyamba dzina laumwini la Mulungu, Yehova, m’Baibulo lawo. (Eks 6:3) Koma iwo adzapindula kosatha ndi chidziwitso ichi kokha ngati ‘ayenda m’dzina la Yehova kunthawi yonka muyaya.’ (Mika 4:5) Izi ziphatikizapo zowonjezereka koposa kungodziwa dzinalo Yehova kapena kunena kuti ali Mboni za Yehova.
14 Ponena za tanthauzo la dzina la Mulungu, Salmo 9:10 limati: “Iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira inu . . . Yehova.” Kodi zimenezo zimaphatikizapo chiyani? Zimaphatikizapo zambiri kuposa kokha kudziwa dzinalo Yehova, kumene mwaiko kokha sikumatanthauza kudalira mwa Yehova. Panopa “kudziwa” dzina la Mulungu kumatanthauza kuzindikira mtundu wa Mulungu amene Yehova ali, kulemekeza ulamuliro wake, kumvera malamulo ake. Mofananamo, ‘kuyenda m’dzina la Yehova’ kumatanthauza kukhala wodzipatulira kwa iye ndi kumuimira monga mmodzi wa alambiri ake, kugwiritsiradi ntchito moyo wa munthuwe kugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Luka 10:27) Kodi inu mukuchita zimenezo?
15. Kuphatikiza pa lingaliro lantchito, kodi nchiyani chimene chiri chofunika ngati titi titumikire Yehova kwamuyaya?
15 Ngati titi tidzatumikire Yehova ku umuyaya wonse, zoposa lingaliro lantchito ziyenera kutisonkhezera. Mtumwi Paulo analimbikitsa Timoteo, amene anali kutumikira kale Yehova kwa zaka zambiri kuti: “Udzizoloweretse kuchita chipembedzo.” (1 Tim. 4:7) Kupembedza kumachokera mumtima; kumasonkhezeredwa ndi kuyamikira munthu amene kukulunjikitsidwako. ‘Kudzipereka kwaumulungu’ ndiko ulemu wakuya kaamba ka Yehova iye mwiniyo. Kumasonyeza kumamatira kwachikondi kwa iye chifukwa cha chiyamikiro kaamba ka iye ndi njira zake. Kumatichititsa kufuna kuti aliyense achitire dzina lake ulemu waukulu. Tiyenera kukulitsa ‘kudzipereka kwaumulungu’ monga chonulirapo kapena cholinga m’miyoyo yathu ngati tidzayenda m’dzina la Yehova, Mulungu wowona, kwamuyaya.—Sal. 37:4; 2 Pet. 3:11.
Makambitsirano Openda
● Kodi Yehova ndimunthu wamtundu wanji? Kodi ndimotani mmene timapindulitsidwira mwa kupeza chidziwitso chomvekera bwino cha uliwonse wa mikhalidwe yake?
● Kodi ndimotani mmene tingathandizire anthu ena kuphunzira chowonadi chonena za Mulungu?
● Kodi nchiyani chimene chimaphatikizidwa mu “kudziwa” Yehova ndi ‘kuyenda m’dzina lake’?