Mutu 10
Maulendo a ku Yerusalemu
NGULULU yafika. Ndipo ndinthaŵi yakuti banja la Yosefe, limodzi ndi mabwenzi ndi achibale, apange ulendo wawo wachaka ndi chaka wopita ku Yerusalemu kukasunga Paskha. Pamene akuchoka paulendo umene uli pafupifupi makilomitala 100, pali kuchita chidwi kwa nthaŵi zonse. Tsopano Yesu ali ndi zaka 12 zakubadwa, ndipo akuyang’anira mtsogolo ndi chikondwerero chapadera kuphwandolo.
Kwa Yesu ndi banja lake, Paskha sali chochitika cha tsiku limodzi lokha. Iwo akukhalakonso kwa masiku asanu ndi aŵiri otsatira, kaamba ka Phwando la Mkate Wopanda Chotupitsa, limene akulingalira kukhala mbali ya nyengo ya Paskha. Monga chotulukapo, ulendo wonse wochokera kwawo ku Nazarete, kuphatikizapo kukakhala m’Yerusalemu umatenga pafupifupi masabata aŵiri. Koma chaka chino, chifukwa cha kanthu kena kamene kakuphatikizapo Yesu, ukutenga nthaŵi yotalikirapo.
Vutolo likudziŵika paulendo wobwerera kuchokera ku Yerusalemu. Yosefe ndi Mariya akulingalira kuti Yesu ali m’kagulu ka achibale ndi mabwenzi amene akuyenda nawo. Komabe iye sakuwoneka pamene akuima usiku, ndipo iwo akumfunafuna pakati pa atsamwali awo oyenda nawo. Iye sakupezeka kulikonse. Chotero Yosefe ndi Mariya akubwereranso ku Yerusalemu kukamfunafuna.
Kwa tsiku lathunthu iwo akumfunafuna, koma mosaphula kanthu. Tsiku lachiŵiri iwo sakumpezanso. Potsirizira, patsiku lachitatu, iwo akupita kukachisi. Kumeneko m’chimodzi cha zipinda zake, iwo akuwona Yesu atakhala pakati pa aphunzitsi Achiyuda, akumawamvetsera nawafunsa mafunso.
“Mwanawe, wachitiranji ife chotero?” Mariya akufunsa motero. “Tawona atate wako ndi ine tinali kufunafuna iwe ndi kuda nkhaŵa.”
Yesu akudabwa kuti iwo sanadziŵe kumene angampeze. ‘Kodi nchifukwa ninji munakandifunafuna?’ iye akufunsa motero. ‘Kodi simunadziŵe kuti ine ndiyenera kukhala m’nyumba ya Atate wanga?’
Yesu sangathe kumvetsetsa chifukwa chimene makolo ake sanadziŵire za ichi. Pamenepo Yesu, akubwerera kunyumba pamodzi ndi makolo ake napitirizabe kuwamvera. Iye akupitirizabe kupita patsogolo m’nzeru ndi m’kusinkhuka ndi kuyanjidwa ndi Mulungu ndi anthu. Inde, kuyambira paubwana wake kumka mtsogolo, Yesu akupereka chitsanzo chabwino kwambiri osati kokha m’kufunafuna zinthu zauzimu komanso m’kusonyeza ulemu kwa makolo ake. Luka 2:40-52; 22:7.
▪ Kodi ndiulendo wa m’ngululu wotani umene Yesu akupanga mokhazikika pamodzi ndi banja lake, ndipo ngwautali motani?
▪ Kodi nchiyani chimene chikuchitika paulendo umene akupanga pamene Yesu ali ndi zaka 12 zakubadwa?
▪ Kodi ndichitsanzo chotani chimene Yesu akupereka kwa achichepere lerolino?