Mutu 36
Chikhulupiliro Chachikulu cha Kazembe Wankhondo
PAMENE Yesu akupereka Ulaliki wake wa pa Phiri, iye wafikira pafupifupi theka la uminisitala wake wapoyera. Zimenezi zikutanthauza kuti iye wangotsaliridwa ndi chaka chimodzi ndi miyezi isanu ndi inayi kapena chapompo kuti amalize ntchito yake padziko lapansi.
Tsopano Yesu akuloŵa mumzinda wa Kapernao, malo otumikira monga malikulu a ntchito yake. Kunoko akulu Achiyuda akumfika ndi pempho. Iwo atumidwa ndi mkulu wina wa gulu lankhondo la Roma amene ali Wakunja, munthu wafuko lina losakhala Lachiyuda.
Mtumiki wina wokondedwa wa mkulu wa gulu lankhondoyo ali pafupi kufa chifukwa cha nthenda ina yaikulu, ndipo iye akufuna kuti Yesu achiritse mtumiki wakeyo. Mwakhama Ayuda ena akuchondelera m’malo mwa mkulu wa gulu lankhondoyo kuti: “Ayenera iye kuti mumchitire ichi,” iwo akunena kuti, “pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ife sunagoge.”
Mosazengeleza, Yesu akupita limodzi ndi amunawo. Komabe, pamene ayandikira, mkulu wa gulu lankhondo akutumiza mabwenzi kukanena naye kuti: “Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzaloŵe pansi pachindwi langa; chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa inu.”
Ndimawu odzichepetsa chotani nanga a mkulu wa gulu lankhondo amene ali wozoloŵera kulamulira ena! Komanso iye mwinamwake akuganizira za Yesu, akumazindikira kuti mwambo umaletsa Myuda kukhala ndi mgwirizano wachitaganya ndi osakhala Ayuda. Ngakhale Petro anati: “Mudziŵa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wa mtundu wina.”
Mwinamwake posafuna kuti Yesu avutike ndi zotulukapo za kuswedwa kwa mwambo umenewu, mkulu wa gulu lankhondoyo wapempha mabwenzi ake kukampemphera kuti: “Koma nenani mawu, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa. Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera akulu anga, ndiri nawo asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga, Tachita ichi, nachita.”
Eya, pamene Yesu amva zimenezi, akudabwa. “Ndinena kwa inu,” iye akutero, “sindinapeza, ngakhale mwa Israyeli, chikhulupiliro chachikulu chotere.” Atachiritsa mtumiki wa mkulu wa gulu lankhondoyo, Yesu akugwiritsira ntchito chochitikacho kusimba za mmene anthu achikhulupiliro osakhala Ayuda adzapatsidwira madalitso amene akanidwa ndi Ayuda opanda chikhulupiliro.
“Ambiri,” Yesu akutero, “akummaŵa ndi akumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, muufumu wakumwamba; koma anawo a ufumu adzatayidwa kumdima wakunja komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
‘Ana a ufumuwo . . . oponyeredwa kumdima’ ndiwo Ayuda akuthupi amene samavomereza mwaŵi woperekedwa choyamba kwa iwo kukhala olamulira limodzi ndi Kristu. Abrahamu, Isake, ndi Yakobo amaimira makonzedwe a Ufumu wa Mulungu. Motero Yesu akusimba za mmene Akunja adzalandiridwira kudzaseyama pagome lakumwamba, kunena kwake titero, “muufumu wakumwamba.” Luka 7:1-10; Mateyu 8:5-13; Machitidwe 10:28.
▪ Kodi nchifukwa ninji Ayuda ena akuchondelera mmalo mwa mkulu wa gulu lankhondo Wachikunja?
▪ Kodi nchiyani chimene chingafotokoze chifukwa chake mkulu wa gulu lankhondoyo sanaitane Yesu kuloŵa m’nyumba mwake?
▪ Kodi Yesu akutanthauzanji ndi ndemanga zake zotsiriza?