Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 5/15 tsamba 24-25
  • Chikhulupiriro Chachikulu cha Kenturiyo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikhulupiriro Chachikulu cha Kenturiyo
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Chikhulupiliro Chachikulu cha Kazembe Wankhondo
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kapitawo wa Asilikali Anasonyeza Kuti Anali ndi Chikhulupiriro
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu Chimakulimbikitsani Kuchitapo Kanthu?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2010
Nsanja ya Olonda—1987
w87 5/15 tsamba 24-25

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Chikhulupiriro Chachikulu cha Kenturiyo

PAMENE Yesu akupereka Ulaliki wake wa pa Phiri, wafika pafupifupi theka la nthawi yauminisitala wake wapoyera. Zimenezi zitanthauza kuti watsaliridwa kokha ndi chaka chimodzi ndi miyezi isanu ndi inayi kuti amalize ntchito yake padziko lapansi.

Yesu tsopano akulowa mu mzinda wa Kapernao, wowonekera kukhala malo apakati a utumiki wake. Kunoku akulu Achiyuda akumfikira ndi pempho. Iwo atumidwa ndi kenturiyo m’gulu lankhondo la Roma amene ali Wakunja.

Mtumiki wokondedwa wa kenturiyo ali pafupi kufa ndi matenda akayakaya, ndipo akufuna kuti Yesu amchiritsire mtumiki wake. Ayudawo akuchonderera mwaphamphu m’malo mwa kazembeyo kuti:“Ayenera iye kuti mumchitire ichi,“ iwo akutero, “pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ife sunagoge.”

Mosazengereza, Yesu akupitira limodzi ndi amunawo. Komabe, pamene iwo afika pafupi, kenturiyoyo akutumiza mabwenzi kunena kuti: “Ambuye musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa tsindwi langa; chifukwa chake ine sindinadziyesere ndekha woyenera kudza kwa inu.”

Ndimawu odzichepetsa chotani nanga onenedwa ndi kenturiyo wozolowera kulamula ena! Koma iye mwinamwake akulingaliranso za Yesu, akumazindikira kuti mwambo umaletsa Ayuda kukhala ndi zigwirizano zochezera limodzi ndi osakhala Ayuda. Ngakhale Petro anati: “Mudziwa inu nokha kuti sikuloledwa kwa munthu Myuda adziphatike kapena kudza kwa munthu wamtundu wina.”

Mwinamwake mosafuna kuti Yesu avutike ndi zotulukapo za kuswa mwambo umenewu, kazembeyo akutumiza mabwenzi ake kumpempha kuti: “Nenani mawu, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa. Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera akulu anga, ndiri nawo asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita.”

Eya, pamene Yesu amva zimenezi akuzizwa. “Ndinena kwa inu,“ iye akutero,“sindinapeza ngakhale mwa Israyeli, chikhulupiriro chachikulu chotere.” Pambuyo pa kuchiritsa mtumiki wa kazembeyo, Yesu akugwiritsira ntchito nthawiyo kusimba mmene osakhala Ayuda achikhulupiriro adzalandirira madalitso amene amakanidwa ndi Ayuda opanda chikhulupiriro.

“Ambiri,“ Yesu akutero, “akummawa ndi akumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, mu ufumu wakumwamba; koma anawo a ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

‘Ana a ufumuwo . . . otayidwa kumdima wakunja’ ndiwo Ayuda akuthupi amene samavomereza mwawi woperekedwa kwa iwo choyamba wa kukhala olamulira limodzi ndi Kristu. Abrahamu, Isake, ndi Yakobo amaimira kakonzedwe ka Ufumu wa Mulungu. Motero Yesu akusimba mmene Akunja adzalandiridwira kukaseyama pagome lakumwamba, kunena kwake titero, “mu ufumu wakumwamba.” Luka 7:1-10; Mateyu 8:5-13; Machitidwe 10:28.

◆ Kodi nchifukwa ninji Ayuda anachondererera kenturiyo Wachikunja?

◆ Kodi nchifukwa ninji kenturiyo angakhale atapemphera kuti Yesu asalowe m’nyumba mwake?

◆Kodi nchiyani chimene Yesu anatanthauza mwa mawu ake omalizira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena