Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 56
  • Kodi Chimaipitsa Munthu Nchiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chimaipitsa Munthu Nchiyani?
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Nchiyani Chiipitsa Munthu?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Chimaipitsa Munthu N’chiyani?
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 56

Mutu 56

Kodi Chimaipitsa Munthu Nchiyani?

KUTSUTSA Yesu kukufikira kukhala kwamphamvu kwambiri. Sikokha kuti ambiri a ophunzira ake akuchoka koma Ayuda m’Yudeya akufunafuna kumupha, monga momwedi anachitira pamene iye anali ku Yerusalemu mkati mwa Paskha wa 31 C.E.

Tsopano ndinthaŵi ya Paskha wa 32 C.E. Mwachiwonekere, mogwirizana ndi lamulo la Mulungu lakuti ayenera kufikapo, Yesu akupita ku Paskhayo ku Yerusalemu. Komabe, iye akutero mochenjera chifukwa moyo wake uli paupandu. Pambuyo pake iye akubwerera ku Galileya.

Mwinamwake Yesu ali ku Kapernao pamene Afarisi ndi alembi ochokera ku Yerusalemu adza kwa iye. Iwo akufunafuna mpata womuimbira mlandu wa kuswa lamulo la chipembedzo. “Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo?” iwo akufunsa motero. “Pakuti sasamba manja pakudya.” Kumeneku sindiko chinthu china chofunidwa ndi Mulungu, komabe Afarisi akukulingalira kuti ndiko kuswa lamulo kwakukulu kusachita dzoma lamakolo limeneli, limene limaphatikizapo kusamba kufikira pazigongono.

Mmalo mwa kuwayankha za chinenezo chawocho, Yesu akusonya kukuipa kwawo ndi kuswa kwawo dala lamulo la Mulungu. “Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?” iye akufuna kudziŵa. “Pakuti, Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu. Koma inu munena, Amene aliyense anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu; iyeyo sadzalemekeza atate wake.”

Ndithudi, Afarisi amaphunzitsa kuti ndalama, chuma, kapena kanthu kalikonse kopatulidwa monga mphatso kwa Mulungu nkapakachisi ndipo sikangathe kugwiritsidwa ntchito kaamba ka chifuno chirichonse. Komabe, kwenikweni, mphatso yopatulidwayo imasungidwa ndi munthu woipatulirayo. Mwanjira iyi mwanayo, mwakungonena kuti ndalama zake kapena chuma chake ndicho “korban”—mphatso yopatulidwira Mulungu kapena ku kachisi—amazemba thayo lake lothandiza makolo ake okalamba, amene angakhale osoŵa kwambiri.

Atanyansidwa moyenerera kaamba ka kupotoza Chilamulo cha Mulungu koipa kwa Afarisi, Yesu akuti: “Mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. Onyenga inu Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso a anthu.”

Mwinamwake khamulo linali litafufunuka kulola Afarisiwo kufunsa Yesu. Tsopano, pamene Afarisi alibe yankho pazinenezo zamphamvu za Yesu kwa iwo, iye akuitanira khamulo pafupi. “Mverani ine,” iye akutero, “ndipo dziŵitsani: kulibe kanthu kunja kwa munthu kakulowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu.”

Pambuyo pake, pamene iwo aloŵa m’nyumba, ophunzira ake akufunsa kuti: “Mudziŵa kodi kuti Afarisi anakhumudwa pakumva chonenacho?”

“Mmera wonse, umene Atate wanga wakumwamba sanaubzala udzazulidwa,” Yesu akuyankha motero. “Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse aŵiri adzagwa m’mbuna.”

Yesu akuwonekera kukhala wodabwa pamene, moimira ophunzirawo, Petro akufunsa kumveketsedwa kwa chimene chimadetsa munthu. “Kodi nanunso mukhala chipulukire?” Yesu akuyankha motero. “Simudziŵa kodi kuti zonse zakuloŵa m’kamwa zipita m’mimba, ndipo zitayidwa kuthengo? Koma zakutuluka m’kamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu. Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, zaumboni wonama, zamwano, izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ayi.”

Panopa Yesu sakuletsa anthu ukhondo wozoloŵereka. Iye sakutsutsa kuti munthu safunikira kusamba m’manja asanayambe kukonza kapena kudya chakudya. Mmalomwake, Yesu akutsutsa chinyengo cha atsogoleri achipembedzo amene mwamachenjera akuyesa kupotoza malamulo olungama a Mulungu mwakuumirira gwagwagwa pamiyambo yosagwirizana ndi malemba. Inde, ziri ntchito zoipa zimene zimadetsa munthu, ndipo Yesu akusonyeza kuti zimenezi zimachokera mumtima mwamunthu. Yohane 7:1; Deuteronomo 16:16; Mateyu 15:1-20; Marko 7:1-23; Eksodo 20:12; 21:17; Yesaya 29:13.

▪ Kodi nchitsutso chotani chimene Yesu tsopano akuyang’anizana nacho?

▪ Kodi ndichinenezo chotani chimene Afarisi akupanga, koma malinga ndi kunena kwa Yesu, kodi ndimotani mmene Afarisi mwadala amaswera Lamulo la Mulungu?

▪ Kodi nchiyani chimene Yesu akuvumbula kuti ndizo zinthu zimene zimadetsa munthu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena