Mutu 61
Mnyamata Wogwidwa ndi Chiŵanda Achiritsidwa
PAMENE Yesu, Petro, Yakobo ndi Yohane atachokapo, ali mwinamwake pamwamba pa Phiri la Hermoni, ophunzira ena akugwera m’vuto. Pobwerera, Yesu mwamsanga akuwona kuti kanthu kena kalakwika. Pali gulu la anthu lozinga ophunzira ake, ndipo alembi akukangana nawo. Atawona Yesu, anthuwo akudabwa kwambiri namthamangira kuti amlonjere. “Mufunsana nawo chiyani?” iye akufunsa.
Atatulukira patsogolo pakhamulo, mwamuna wina akugwada pamaso pa Yesu nafotokoza kuti: “Mphunzitsi, ndadza naye kwa inu mwana wanga, ali nawo mzimu wosalankhula; ndipo ponse pamene umgwira umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nawo ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoza.”
Mwachiwonekere alembiwo akunyoza kulephera kwa ophunzirawo kuchiritsa mnyamatayo, mwinamwake akunyodola kuyesayesa kwawo. Pamphindi yeniyeni yovuta imeneyi, Yesu akufika. “Mbadwo wosakhulupilira inu,” iye akutero, “ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthaŵi yanji?”
Yesu akuwoneka ngati kuti akulankhula mawuŵa kwa aliyense wopezekapo, koma mosakayikira iwo akulunjikitsidwa makamaka kwa alembi, omwe akhala akuvutitsa ophunzira ake. Kenako, Yesu akunena za mnyamatayo kuti: “Mudze naye kwa ine.” Koma pamene mnyamatayo adza kwa Yesu, chiŵanda chomwe chamgwira chikumgwetsera pansi ndi kumvivinika. Mnyamatayo akukunkhulika pansi nachita thovu kukamwa.
“Chimenechi chinayamba kumgwira liti?” Yesu akufunsa motero.
“Chidayamba akali mwana,” akuyankha motero atateyo. “Kaŵirikaŵiri [chiŵandacho] chikamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuwononga.” Ndiyeno atatewo akuchondelera kuti: “Ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.”
Mwinamwake kwa zaka zingapo, atateyo wakhala akufunafuna thandizo. Ndipo tsopano, ophunzira a Yesu pokhala atalephera, akusoŵeratu chochita. Poyankha pempho la mwamunayo losoŵa chochita, Yesu momlimbikitsa akuti: “Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.”
“Ndikhulupirira;” atateyo mwamsanga akufuula motero, komabe akupempha kuti: “Thandizani kusakhulupirira kwanga.”
Atawona kuti khamulo lagwirizana kuwatsutsa, Yesu akudzudzula chiŵandacho kuti: “Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye ndipo usaloŵenso mwa iye.” Pamene chiŵandacho chikuchoka, chikuchititsanso mnyamatayo kufuula ndi kumamgwetsera pansi. Ndiyeno mnyamatayo ali kwala pansi mosatakasuka, kotero kuti unyinji wa anthuwo ukuyamba kunena kuti: “Wamwalira.” Koma Yesu akugwira mnyamatayo padzanja, nanyamuka.
Poyambapo, pamene ophunzirawo anatumidwa kukalalikira, anachotsa ziŵanda. Chotero tsopano lino, pamene akuloŵa m’nyumba, iwo akufunsa Yesu mtseri kuti: “Nanga bwanji sitinakhoza ife kuutulutsa?”
Posonyeza kuti chinali chifukwa cha kusoŵa kwawo chikhulupiliro, Yesu akuyankha kuti: “Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.” Mwachiwonekere padafunika kukonzekera kuti atulutse chiŵanda champhamvu kwenikweni chimenechi. Panafunikira chikhulupiliro cholimba limodzi ndi pemphero lopempha thandizo la Mulungu lopereka mphamvu.
Ndiyeno Yesu akuwonjezera kuti: “Indetu ndinena kwa inu, mukakhala nacho chikhulupiliro monga kambewu kampiru, mudzati ndi phiri ili, sendera umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosachitika kwa inu.” Mmene chikhulupiliro chingakhalire champhamvu nanga!
Zopinga ndi mavuto zimene zimatsekereza kupita patsogolo muutumiki wa Yehova zingawoneke kukhala zazikulu ndi zosasunthika monga phiri lenileni lalikulu. Komabe, Yesu akusonyeza kuti ngati tikulitsa chikhulupiliro m’mitima yathu, tikumachithirira ndi kuchilimbikitsa kukula, chidzafikira pakukhwima ndipo chidzatikhozetsa kugonjetsa zopingazo ndi mavuto onga phiri. Marko 9:14-29; Mateyu 17:19, 20; Luka 9:37-43.
▪ Kodi Yesu akukumana ndi mkhalidwe wotani pobwerera kuchokera ku Phiri la Hermoni?
▪ Kodi ndichilimbikitso chotani chimene Yesu akupereka kwa atate wa mnyamata wogwidwa ndi chiŵanda?
▪ Kodi nchifukwa ninji ophunzirawo sanali okhoza kutulutsa chiŵandacho?
▪ Kodi Yesu akusonyeza motani kuti chikhulupiliro chingakhale ndi mphamvu?