Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Malinga nkunena kwa Mateyu 17:20, atumwi sanathe kuchiza mnyamata wozunzika ‘chifukwa cha chikhulupiriro chawo chaching’ono.’ Komabe, Marko 9:29 akufotokoza kuti iwo analephera chifukwa chakuti sanapemphere. Kodi nchifukwa ninji anapereka zifukwa zosiyana m’Mauthenga Abwino ameneŵa?
Kwenikweni, nkhani ziŵirizi nzogwirizana, nzosatsutsana. Choyamba, taonani pa Mateyu 17:14-20. Munthu wina anafotokoza kuti mwana wake anali kudwala khunyu ndipo ophunzira a Yesu analephera kuchiza mwanayo. Kenaka Yesu anachiza mnyamatayo mwa kutulutsa chiŵanda chimene chinali kumuvutitsa. Ophunzirawo anafunsa chifukwa chimene analepherera kutulutsa chiŵandacho. Malinga nkunena kwa nkhani ya Mateyu, Yesu anayankha kuti: ‘Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching’ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambewu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosachitika.’
Tsopano tsegulani Marko 9:14-29, pamene nkhaniyi yakambidwa mwatsatanetsatane. Mwachitsanzo, Marko 9:17 akufotokoza kuti panthaŵiyi kugwidwa ndi khunyuku kunali kuchitika chifukwa cha mzimu woipa. Zingakhalenso bwino kudziŵa kuti penapake Baibulo limati Yesu anachiza anthu akhunyu ndiponso ogwidwa ndi mizimu yoipa. (Mateyu 4:24) Pachochitika chapadera chimenechi, kugwidwako kunali kuchitika chifukwa cha “Mzimu wosalankhula ndi wogontha,” umenewo ndiwo mzimu woipa, zimene sing’anga Luka anavomereza. (Luka 9:39; Akolose 4:14) Onani kuti pa Marko 9:18 pali mawu akuti, “Ponse pamene umgwira [mzimu woipa].” Choncho, mnyamatayo sanali kugwidwa moŵirikiza ndi chiŵandacho ayi, koma ankagwidwa mwa apo ndi apo. Komabe, ophunzira analephera kutulutsa chiŵandacho ndipo mnyamatayo sanamchize. Atamfunsa chifukwa chimene iwo analepherera, Yesu anayankha kuti: “Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.”
Komabe, titaŵerenga mosamalitsa nkhani ya Marko, zikuonetsa kuti nkhaniyo sikutsutsana ndi zimene Mateyu analemba. Pa Marko 9:19, timaŵerenga kuti Yesu anadandaula chifukwa cha kusakhulupirira kwa mbadwo umenewo. Ndipo pavesi 23, analemba kuti iye anauza atate ake a mnyamatayo kuti: “Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.” Choncho, Marko akugogomezeranso za kufunika kwa chikhulupiriro. Zangokhala kuti pavesi 29 Marko analembapo mfundo yowonjezereka. Marko anawonjezerapo mawu a Yesu onena za pemphero, amene Mateyu ndi Luka sanalembe.
Nanga kodi tinganenenji pamenepa? Nthaŵi zina, atumwi 12 ndiponso ophunzira 70 anali kutulutsa mizimu yoipa. (Marko 3:15; 6:13; Luka 10:17) Koma panthaŵiyi, ophunzirawo analephera kutulutsa chiŵandacho. Chifukwa ninji? Ngati tiphatikiza mfundo zofotokozedwa m’nkhani zosiyanasiyanazi, tinganene kuti iwo anali asanakonzekere kuchita zimenezi panthaŵiyi. Mwinamwake vuto lina linali lokhudza mtundu wa chiŵandacho, pakuti zikuonetsa kuti ziŵanda zingakhale ndi maumunthu, zokonda, ngakhalenso mphamvu zosiyanasiyana. Koma chiŵanda ichi chinafunikira chikhulupiriro cholimba ndi kupemphera mwaphamphu kuti Mulungu athandizepo. Tikudziŵa kuti Yesu anali ndi chikhulupiriro chotero. Iye anathandizidwanso ndi Atate wake, Wakumva pemphero. (Salmo 65:2) Yesu sanali chabe ndi mphamvu yochiritsa mnyamata wozunzikayo mwakutulutsa chiŵandacho koma anamchiritsadi.