Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Mnyamata Wogwidwa ndi Chiwanda Achiritsidwa
PAMENE Yesu, Petro, Yakobo, ndi Yohane ochoka, mwachidziŵikire ali pa malo okwezeka a Phiri la Hermone, ophunzira enawo alowa mu vuto. Pamene akubwerera, Yesu mwamsanga awona kuti chinachake chalakwika. Pali khamu losonkhana mozungulira ophunzira ake, ndipo alembi akukangana ndi iwo. Pa kumuwona Yesu, anthuwo adabwitsidwa kwambiri ndipo akuthamangira kukampatsa iye moni. “Mufunsana nawo chiyani?” iye akufunsa.
Akubwera kutsogolo kuchoka m’khamulo, mwamuna agwada pamaso pa Yesu ndi kulongosola kuti: “Mphunzitsi, ndadza naye kwa inu mwana wanga, ali nawo mzimu wosalankhula; ndipo ponse pamene umgwira umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka, ndipo ndinalankhula nawo ophunzira anu kuti atulutse; koma sanakhoza.”
Alembiwo mwachiwonekere akukulitsa nkhani chifukwa cha kulephera kwa ophunzirawo kuchiritsa mnyamatayo, mwinamwake kuseka zoyesayesa zawo. Panthaŵi yovutitsa imeneyi, Yesu afika. “Mbadwo wosakhulupirira inu,” iye akutero, “ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthaŵi yanji?”
Yesu akuwoneka ngati kuti akulankhula ndemangazi kwa aliyense amene alipo, koma mosakaikira izo zalunjikitsidwa mwapadera kwa Afarisi, omwe akhala akupangitsa vuto kaamba ka ophunzira ake. Kenaka, Yesu akunena kwa mnyamatayo: “Mudze naye kwa ine.” Koma pamene mnyamatayo akudza kwa Yesu, chiwanda chomgwiracho chinamgwetsa pansi ndi kumng’ambitsa kowopsya. Mnyamatayo abvimvinika ndi kuchita thovu.
“Chimenechi chinayamba kumgwira liti?” Yesu akufunsa.
“Chidayamba akali mwana,” tateyo akuyankha. “Ndipo kaŵirikaŵiri [chiwandacho] chikamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuwononga.” Kenaka tateyo akuchonderera: “Ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.”
Mwinamwake kwa zaka zingapo, tateyo anakhala akufunafuna thandizo. Ndipo tsopano, ndi kulephera kwa ophunzira a Yesu, kuvutitsa kwake kuli kwakukulu. Akumatenga pembedzero losowa chochita la munthuyo, Yesu molimbikitsa akunena kuti: “Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.”
“Ndikhulupirira!” Tateyo mwamsanga anafuula, ndipo akupempha kuti: “Thandizani kusakhulupirira kwanga!”
Akuzindikira kuti khamulo likuthamangira pamodzi kwa iwo, Yesu akudzudzula chiwandacho: “Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.” Pamene chiwandacho chikutuluka, icho kachiŵirinso chikupangitsa mnyamatayo kulira ndi kumng’ambitsa iye. Kenaka mnyamatayo anakhala pansi ngati wakufa, kotero kuti anthu ambiri anayamba kunena kuti: “Wamwalira!” Koma Yesu anagwira dzanja la mnyamatayo, ndi kumuwutsa.
Kumayambiriro, pamene ophunzirawo anatumizidwa kukalalikira, iwo anatulutsa ziwanda. Chotero tsopano, pamene iwo analowa mnyumba, iwo akufunsa Yesu mwachinsinsi kuti: “Nanga bwanji sitinakhoza ife kuutulutsa?”
Akusonyeza kuti kunali kusoweka kwa chikhulupiriro chawo, Yesu akuyankha kuti: “Mtundu uwu sukhoza kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.” Mwachiwonekere kukonzekera kunafunikira kuti atulutse chiwanda champhamvu mwapadera chokhudzidwa m’nkhaniyi. Chikhulupiriro champhamvu limodzi ndi pemphero kufunsa thandizo lopatsa mphamvu la Mulungu linafunikira.
Kenaka Yesu akuwonjezera kuti: “Indetu ndinena kwa inu, mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambewu kampiru, mudzati ndi phiri iri, ‘Senderapo umuke kuja,’ ndipo lidzasendera, ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosachitika.”
Ndi mwamphamvu chotani nanga mmene chikhulupiriro chingakhalire! Zokhumudwitsa ndi zovuta zomwe zimatsekereza kupita patsogolo mu utumiki wa Yehova zingawonekere kukhala zosakwereka ndi zosachotseka mofanana ndi phiri lalikulu lenileni. Komabe, Yesu akusonyeza kuti ngati tikulitsa chikhulupiriro m’mitima yathu, kuchithirira icho ndi kuchilimbikitsa icho kuti chikule, icho chidzafutukuka kufika ku uchikulire ndipo chidzatitheketsa ife kulaka zokhumudwitsa ndi mavuto onga mapiri oterowo. Marko 9:14-29; Mateyu 17:19, 20; Luka 9:37-43.
◆ Ndi mkhalidwe wotani umene Yesu akupeza pamene abwerera kuchokera ku Phiri la Hermone?
◆ Ndi chilimbikitso chotani chimene Yesu akupereka kwa atate wa mnyamata wogwidwa ndi chiwandayo?
◆ Nchifukwa ninji ophunzira alephera kutulutsa chiwandacho?
◆ Ndi mwamphamvu chotani mmene Yesu akusonyezera kuti chikhulupiriro chingakhale?